Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kugwirizana kwa Ulamuliro wa Yehova ndi Ufumu wa Mulungu

Kugwirizana kwa Ulamuliro wa Yehova ndi Ufumu wa Mulungu

Kugwirizana kwa Ulamuliro wa Yehova ndi Ufumu wa Mulungu

“Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova . . . ufumu ndi wanu, Yehova.”​—1 MBIRI 29:11.

1. N’chifukwa chiyani Yehova ali woyenera kulamulira chilengedwe chonse?

“YEHOVA anakhazika mpando wachifumu wake Kumwamba; ndi ufumu wake uchita mphamvu ponsepo.” (Salmo 103:19) Palembali wamasalmo anatchula mfundo yosatsutsika yokhudza ulamuliro. Yehova Mulungu ndi Mlengi, choncho ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse.

2. Kodi Danieli anafotokoza motani ulamuliro wa Yehova pa zolengedwa zake zauzimu?

2 Wolamulira aliyense amafunika kukhala ndi ena oti aziwalamulira. Poyamba Yehova ankalamulira zolengedwa zauzimu zimene iye analenga. Woyamba anali Mwana wake wobadwa yekha ndipo kenako makamu a angelo. (Akolose 1:​15-17) Nthawi ina mneneri Danieli anaona m’masomphenya Yehova akulamulira. Iye analemba kuti: “Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, . . . zikwizikwi anam’tumikira, ndi unyinji wosawerengeka unaima pamaso pake.” (Danieli 7:​9, 10) Kwa zaka zosawerengeka Yehova, yemwe ndi “Nkhalamba ya kale lomwe,” wakhala akulamulira banja la zolengedwa zauzimu zambirimbiri ndiponso zadongosolo. Zolengedwa zimenezi zinkagwira ntchito monga “atumiki” ochita chifuniro chake.​—Salmo 103:​20, 21.

3. Kodi Yehova anawonjezera motani ulamuliro wake mu chilengedwe chonse?

3 Kenako, Yehova anawonjezera ulamuliro wake mwa kulenga chilengedwe chachikulu ndi chodabwitsa, kuphatikizapo dziko lapansili. (Yobu 38:​4, 7) Zolengedwa zakuthambo n’zadongosolo kwambiri moti anthu angaone kuti sipafunikanso winawake woti aziziyang’anira. Koma wamasalmo analemba kuti: “[Yehova] analamulira, ndipo zinalengedwa. Anazikhazikanso ku nthawi za nthawi; anazipatsa chilamulo chosatumphika.” (Salmo 148:​5, 6) Nthawi zonse Yehova wakhala akusonyeza ulamuliro wake mwa kutsogolera ndi kuyang’anira ntchito za zolengedwa zauzimu ndiponso zolengedwa zina zonse.​—Nehemiya 9:6.

4. Kodi Yehova amasonyeza motani ulamuliro wake pa anthu?

4 Mulungu anasonyezanso ulamuliro wake m’njira ina. Iye anatero mwa kulenga anthu awiri oyambirira. Yehova anawapatsa zinthu zonse zofunika kuti akhale ndi moyo wabwino komanso wosangalala. Kuwonjezera pamenepo, anawapatsanso mphamvu zolamulira zolengedwa zina padziko lapansi. (Genesis 1:​26-28; 2:​8, 9) Zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ndi wolamulira wabwino ndiponso wachifundo komanso amalemekeza zolengedwa zake. Ngati Adamu ndi Hava akanagonjera ulamuliro wa Yehova akanakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi.​—Genesis 2:​15-17.

5. Kodi mungafotokoze bwanji za mmene Yehova amasonyezera ulamuliro wake?

5 Kodi tikuphunzira chiyani pamfundo zimenezi? Choyamba, Yehova wakhala akulamulira chilengedwe chake chonse. Chachiwiri, Mulungu ndi wolamulira wabwino komanso amalemekeza amene akuwalamulira. Ndipo chachitatu, tidzapeza madalitso osatha ngati timvera ndi kukhala ku mbali ya ulamuliro wa Mulungu. M’pake kuti Mfumu Davide ya Isiraeli wakale inati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse.”​—1 Mbiri 29:11.

N’chifukwa Chiyani Ufumu wa Mulungu ndi Wofunika?

6. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa ulamuliro wa Mulungu ndi Ufumu wake?

6 N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uli wofunika ngakhale kuti Yehova wakhala akusonyeza mphamvu zake monga Wolamulira wa Chilengedwe Chonse? Nthawi zambiri wolamulira amakhala ndi njira imene amasonyezera ulamuliro wake pa anthu amene akuwalamulira. Motero, Ufumu wa Mulungu ndi njira imene Mulungu amagwiritsa ntchito posonyeza ulamuliro wake pa zolengedwa zake.

7. N’chifukwa chiyani Yehova anakonza njira yatsopano yosonyezera ulamuliro wake?

7 Yehova wakhala akusonyeza ulamuliro wake m’njira zambiri panthawi zosiyanasiyana. Iye anakonza njira yatsopano yosonyezera ulamuliro wake chifukwa cha zinthu zina zimene zinachitika. Nthawi imeneyo Satana, mwana wauzimu wopanduka wa Mulungu, anachititsa kuti Adamu ndi Hava apandukire ulamuliro wa Yehova. Mwakuchita zimenezi iye anatsutsa ulamuliro wa Mulungu. Kodi zimenezi zinachitika motani? Pamene anauza Hava kuti ‘sadzafa’ akadya chipatso choletsedwa, Satana anasonyeza kuti Yehova ndi wabodza ndiponso wosadalirika. Satana anapitiriza kuuza Hava kuti: “Adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” Satana anali kutanthauza kuti Adamu ndi Hava akanatha kukhala ndi moyo wabwino kwambiri mwa kunyalanyaza lamulo la Mulungu ndi kukhala moyo wosadalira Yehova kuti awatsogolere. (Genesis 3:​1-6) Zimene anachitazi zinatsutsiratu mfundo yakuti Mulungu ndiye woyenera kulamulira. Kodi Yehova akanatani pamenepa?

8, 9. (a) Kodi wolamulira angatani ngati anthu ena agalukira ulamuliro wake? (b) Kodi Yehova anatani ndi kupanduka kumene kunachitika mu Edene?

8 Kodi wolamulira angatani ngati anthu ena amene akuwalamulira amugalukira? Anthu amene akudziwa bwino mbiri yakale angakumbukire zimene zimachitika. Ngakhale wolamulira atakhala wabwino kwambiri sangalekerere zoterezi. Iye angaimbe mlandu anthu ogalukirawo. Ndiyeno, wolamulirayo angapatse mphamvu munthu wina kuti agonjetse anthu ogalukirawo n’cholinga chokhazikitsa mtendere. Mofananamo, Yehova anasonyeza mphamvu zake mwa kuchitapo kanthu nthawi yomweyo. Iye anaweruza opandukawo ndipo anauza Adamu ndi Hava kuti sadzakhalanso ndi moyo wosatha komanso anawathamangitsa m’munda wa Edene.​—Genesis 3:​16-19, 22-24.

9 Poweruza Satana, Yehova anatchula njira yatsopano yosonyezera ulamuliro wake. Njira imeneyi ndi imene idzabweretsanso bata ndi mtendere m’chilengedwe chonse. Mulungu anauza Satana kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:15) Motero, Yehova anasonyeza kuti chinali cholinga chake kupereka mphamvu kwa “mbewu” kuti idzawononge Satana ndi gulu lake, ndipo zimenezi zidzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.​—Salmo 2:​7-9; 110:​1, 2.

10. (a) Kodi ndani anadzakhala “mbewu” yolonjezedwa? (b) Kodi Paulo ananena chiyani za kukwaniritsidwa kwa ulosi woyamba?

10 Yesu Khristu anadzakhala “mbewu” imeneyi pamodzi ndi kagulu ka anthu ena amene adzalamulira naye pamodzi. Yesu pamodzi ndi kagulu kameneka amapanga Ufumu wa Mulungu Wolamulidwa ndi Mesiya. (Danieli 7:​13, 14, 27; Mateyo 19:28; Luka 12:32; 22:​28-30) Koma zonsezi zinatenga nthawi yaitali kuti zidziwike. Kukwaniritsidwa kwa ulosi woyamba umenewu kunali “chinsinsi chopatulika chimene chakhala chobisika kuyambira nthawi zakale.” (Aroma 16:25). Kwa zaka zambiri anthu okhulupirika ankayembekezera nthawi imene “chinsinsi chopatulika” chidzadziwika ndiponso kukwaniritsidwa kwa ulosi woyambawu. Kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu kudzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira.​—Aroma 8:​19-21.

“Chinsinsi Chopatulika” Chinadziwika Pang’onopang’ono

11. Kodi n’chiyani chimene Yehova anauza Abulahamu?

11 M’kupita kwanthawi Yehova anavumbula pang’onopang’ono mfundo zina zokhudza “chinsinsi chopatulika cha ufumu wa Mulungu.” (Maliko 4:11) Abulahamu, amene anatchedwa “bwenzi la Yehova,” anali mmodzi wa anthu amene Yehova anawavumbulira chinsinsichi. (Yakobe 2:23) Yehova analonjeza Abulahamu kuti mwa iye mudzatuluka mtundu waukulu. Kenako, Mulungu anamuuza kuti ‘mafumu adzatuluka mwa iye’ komanso kuti ‘m’mbewu zake mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.’​—Genesis 12:​2, 3; 17:6; 22:​17, 18.

12. Kodi mbewu ya Satana inadziwika motani pambuyo pa Chigumula?

12 Pofika m’nthawi ya Abulahamu, anthu anali atayamba kale kulamulira ndi kupondereza anzawo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za Nimrode yemwe anali mdzukulu wa Nowa kuti: “Iye anayamba kukhala wamphamvu pa dziko lapansi. Iye ndiye mpalu wamphamvu pamaso pa Yehova.” (Genesis 10:​8, 9) N’zodziwikiratu kuti Nimrode komanso anthu ena omwe anadziika okha kukhala olamulira anali kutsogoleredwa ndi Satana. Olamulirawa komanso owatsatira awo anakhala mbali ya mbewu ya Satana.​—1 Yohane 5:19.

13. Kodi Yehova analosera chiyani kudzera mwa Yakobo?

13 Yehova akupitirizabe kuchita cholinga chake ngakhale kuti Satana akuyesetsa kuika anthu olamulira. Kudzera mwa Yakobo, yemwe anali mdzukulu wa Abulahamu, Yehova anati: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Mawu akuti “Silo” amatanthauza kuti “Mwini Wake; Iye Amene Chili Chake.” Choncho mawu aulosi amenewa anasonyeza kuti kudzabwera wina amene anali woyenera kulandira “ndodo yachifumu” kapena kuti ulamuliro pa anthu amitundu yonse. Kodi ameneyu anali ndani?

“Kufikira Atadza Silo”

14 Kodi ndi pangano lotani limene Yehova anachita ndi Davide?

14 Pa mbadwa zonse za Yuda, Davide, mwana wa Jese, yemwenso anali m’busa, anali woyamba kusankhidwa ndi Yehova kukhala mfumu ya anthu a Mulungu. * (1 Samueli 16:​1-13) Ngakhale kuti Davide anachita machimo komanso analakwitsa zinthu zina, anali kukondedwa kwambiri ndi Yehova chifukwa anali wokhulupirika ku ulamuliro wa Yehova. Pofotokoza bwino ulosi wa mu Edene, Yehova anachita pangano ndi Davide. Iye anati: “Ine ndidzaukitsa mbewu yako pambuyo pako, imene idzatuluka m’matumbo mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.” Zimenezi zinaphatikizapo anthu enanso kuwonjezera pa Solomo, mwana wa Davide yemwe anali kudzamulowa m’malo. Izi zili choncho chifukwa panganolo linati: “Ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthawi zonse.” Pangano limene Mulungu anachita ndi Davide linasonyeza kuti “mbewu” ya Ufumu yolonjezedwayo m’kupita kwanthawi idzachokera mumzera wa banja la Davide.​—2 Samueli 7:​12, 13.

15. N’chifukwa chiyani ufumu wa Yuda unali kuonedwa kuti ndi chitsanzo cha Ufumu wa Mulungu?

15 Davide anayambitsa mzera wa mafumu omwe mkulu wa ansembe ankachita kudzoza ndi mafuta opatulika. Motero, mafumuwa anali kutchedwa odzozedwa kapena kuti mesiya. (1 Samueli 16:13; 2 Samueli 2:4; 5:3; 1 Mafumu 1:39) Mafumuwa akamalamulira ku Yerusalemu ankaonedwa kuti ali pa mpando wachifumu wa Yehova ndipo akulamulira m’malo mwake. (2 Mbiri 9:8) Mwa njira imeneyi, ufumu wa Yuda unaimira Ufumu wa Mulungu ndipo unali chitsanzo cha ulamuliro wa Yehova.

16. Kodi zotsatirapo za ulamuliro wa mafumu a Yuda zinali zotani?

16 Ngati mfumu komanso anthu ake agonjera ulamuliro wa Yehova, Iye anali kuwateteza ndi kuwadalitsa. Mu ulamuliro wa Solomo anthu anali pa mtendere ndipo zinthu zinali kuyenda bwino kwambiri kusiyana ndi kale lonse. Zimenezi zinapereka chithunzi chabwino cha ulosi wonena za kulamulira kwa Ufumu wa Mulungu, nthawi imene ntchito zonse za Satana zidzachotsedwa ndipo zimenezi zidzatsimikizira kuti Yehova ndiye woyenera kulamulira. (1 Mafumu 4:​20, 25) Koma ndi zomvetsa chisoni kuti ambiri mwa mafumu a mumzera wa Davide analephera kuchita zinthu mogwirizana ndi zofuna za Yehova, ndipo anthu anayamba kupembedza mafano ndi kuchita chiwerewere. Zotsatira zake, Yehova analola kuti Ababulo awononge ufumu wa Yuda mu 607 B.C.E. Pamenepa, Satana anaoneka ngati wapambana pa zoyesayesa zake zofuna kulepheretsa ulamuliro wa Yehova.

17. N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anali akulamulirabe ngakhale kuti ufumu wa Davide unali utawonongedwa?

17 Kuwonongedwa kwa ufumu wa Davide komanso ufumu wakumpoto wa Isiraeli sikunali umboni wakuti Yehova ndi wosayenera kulamulira kapena kuti walephera kulamulira bwino. Koma unali umboni wakuti pamakhala zotsatira zomvetsa chisoni anthu akasankha kuchita zofuna za Satana kapena akasankha kuti azidzilamulira okha popanda kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Miyambo 16:25; Yeremiya 10:23) Posonyeza kuti Iye ndi amene anali kulamulirabe, Yehova kudzera mwa mneneri Ezekieli anati: ‘Chotsa chilemba, vula korona. . . . Ndidzagubuduza gubuduza ufumu uno, sudzakhalanso kufikira akadza Iye mwini chiweruzo; ndipo ndidzaupereka kwa Iye.’ (Ezekieli 21:​26, 27) Mawu amenewa akusonyeza kuti “mbewu” yolonjezedwa yomwe ndi “mwini chiweruzo” inali kudzabwera m’tsogolo.

18. Kodi ndi uthenga wotani womwe mngelo Gabiriele anapereka kwa Mariya?

18 Tsopano tiyeni tione zimene zinachitika patatha zaka pafupifupi 600 chichitikireni zimenezi. Mngelo Gabiriele anatumizidwa kwa namwali Mariya wa ku Nazarete, mzinda womwe unali ku Galileya, kumpoto kwa Palesitina. Mngeloyo anati: “Mvetsera! Udzakhala ndi pathupi nudzabereka mwana wamwamuna, ndipo udzam’patse dzina lakuti Yesu. Ameneyu adzakhala wamkulu nadzatchedwa Mwana wa Wam’mwambamwamba. Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake, ndipo adzalamulira monga mfumu pa nyumba ya Yakobo kwa muyaya, mwakuti ufumu wake sudzatha konse.”​—Luka 1:​31-33.

19. Pamene Yesu ankabadwa, kodi ndi nthawi ya zochitika zochititsa chidwi ziti imene inali itatsala pang’ono kukwana?

19 Tsopano nthawi yoti “chinsinsi chopatulika” chivumbulidwe inali itatsala pang’ono kukwana. Munthu wofunika kwambiri woimira “mbewu” yolonjezedwa anali atatsala pang’ono kuonekera. (Agalatiya 4:4; 1 Timoteyo 3:16) Satana anali kudzalalira chitende chake. Koma “mbewu” imeneyi inali kudzalalira mutu wa Satana, ndipo zimenezi zinatanthauza kuti Satana komanso omutsatira ake adzawonongedwa. Kuwonjezera pamenepo, iye adzachitiranso umboni kuti kudzera mu Ufumu wa Mulungu zoipa zonse zomwe Satana akuchita zidzathetsedwa ndipo zimenezi zidzasonyeza kuti ndi Yehova yekha yemwe ali woyenera kulamulira. (Aheberi 2:14; 1 Yohane 3:8) Komano kodi Yesu adzakwanitsa bwanji kuchita zimenezi? Nanga ndi chitsanzo chotani chomwe iye anatisiyira kuti titsatire? Tipeza mayankho a mafunso amenewa m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Sauli yemwe anali woyamba kusankhidwa ndi Mulungu kukhala mfumu ya Isiraeli, anali wochokera m’fuko la Benjamini.​—1 Samueli 9:​15, 16; 10:1.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi n’chiyani chimapangitsa Yehova kukhala woyenera kulamulira chilengedwe chonse?

• Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakonza zokhazikitsa Ufumu?

• Fotokozani momwe Yehova mwapang’onopang’ono anavumbulira “chinsinsi chopatulika.”

• N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anali kulamulirabe ngakhale kuti ufumu wa Davide unali utawonongedwa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi Yehova ananeneratu za chiyani kudzera mwa Abulahamu?

[Chithunzi patsamba 25]

N’chifukwa chiyani kuwonongedwa kwa ufumu wa Davide sikunasonyeze kuti ulamuliro wa Yehova walephera?