Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyenda Molowera ku Dziko Latsopano

Kuyenda Molowera ku Dziko Latsopano

Mbiri ya Moyo Wanga

Kuyenda Molowera ku Dziko Latsopano

Yosimbidwa Ndi Jack Pramberg

M’chigawo chapakati cha dziko la Sweden muli katauni kokongola kwambiri, kotchedwa Arboga. Kunja kwa katauni kameneka kuli ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, ndipo pa ofesiyi pali anthu oposa 80 ogwira ntchito mongodzipereka. Ine ndi mkazi wanga Karin timakhala ndiponso kugwira ntchito pa ofesi imeneyi. Koma kodi tinafika bwanji kunoko?

CHAKUMAPETO kwa zaka za m’ma 1800, mtsikana wina wa ku Sweden, yemwe anali ndi zaka 15 anasamukira ku United States. Kumeneko anakumana ndi woyendetsa sitima yapamadzi wina wa ku Sweden, pa malo a anthu othawa kwawo ku New York City. Anthuwa anakondana n’kukwatirana kenaka n’kubereka mwana wamwamuna. Mwanayo ndi ineyo. Ndipo zimenezi zinachitika m’kati mwa nkhondo yoyamba ya padziko lonse mu 1916, m’dera la Bronx ku New York, m’dziko la United States.

Posakhalitsa, tinasamukira ku Brooklyn, chapafupi kwambiri ndi dera lotchedwa Brooklyn Heights. Nditasinkhuka, bambo anga anandiuza kuti panthawi inayake anakwera nane kaboti kamene iwowo ankakayesa ndipo tinadutsa pafupi ndi mlatho wa Brooklyn, pomwe mumatha kuona bwinobwino likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Panthawiyi, sindinazindikire ngakhale pang’ono kuti zimene zimachitika ku likululi zidzasintha kwambiri moyo wanga.

Mu 1918, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inatha ndipo anasiya zopulula anthu ambirimbiri osalakwa ku Ulaya. Asilikali atabwerera kwawo anakapeza kuti kuli adani ena. Adani amenewa anali ulova ndi umphawi. Bambo anga anaona kuti njira yabwino n’kungobwerera kumudzi ku Sweden, ndipo tinaterodi mu 1923. Tinakakhala ku Erikstad, kamudzi kakang’ono ka kufupi ndi siteshoni ya njanji yomwe ili m’chigawo cha Dalsland. Kumeneku bambo anga anatsegula shopu yokonzerapo zinthu zoyendera injini, ndipo n’kumene ndinakulira komanso kupita kusukulu.

Mbewu Inadzalidwa

Shopu ya bambo ija siinkayenda bwino. Motero chakumayambiriro kwa m’ma 1930, anayambiranso ntchito yawo yoyendetsa sitima ija. Ine ndi mayi tinkangokhala tokhatokha. Mayi ankangokhalira kuda nkhawa ndipo ineyo anandisiyira ntchito yoyang’anira shopuyo. Tsiku lina mayi anapita kukaona alamu awo, bambo anga aang’ono, dzina lawo a Johan. Poona mmene zinthu zinaipira padziko lonse mayi anafunsa kuti: “Kodi alamu, mukuona kuti zinthu zidzasintha?”

Ndiyeno iwo anayankha kuti: “Inde mlamu zidzasintha.” Anapitiriza kuwauza za lonjezo la Mulungu lothetsa zoipa n’kubweretsa ulamuliro wolungama padziko lonse pogwiritsa ntchito Ufumu umene Yesu Khristu adzakhale Mfumu yake. (Yesaya 9:​6, 7; Danieli 2:44) Anafotokoza kuti Ufumu umenewu ndi umene Yesu anati tiziupempherera ndipo umatanthauza ulamuliro, kapena kuti boma lolungama limene lidzasinthe dziko kuti likhale paradaiso.​—Mateyo 6:​9, 10; Chivumbulutso 21:​3, 4.

Malonjezo a m’Baibulo amenewa anawakhudza mtima kwambiri mayi anga. Anabwerera ku nyumba ndipo njira yonseyo ankangothokoza Mulungu. Komano, ineyo ndi bambo sitinasangalale titaona kuti mayi ayamba kukonda kwambiri zinthu zachipembedzo. Chapanthawi yomweyi, m’ma 1935, ndinasamukira ku Trollhättan kumadzulo kwa dziko la Sweden, ndipo kumeneko ndinayamba ntchito pa shopu ina yaikulu yokonzerapo zinthu. Posakhalitsa mayi ndi bambo anasamukira komweko, bambo atangobwera kumene kunyanja. Pamenepa banja lathu linayambanso kukhalira limodzi.

Pofuna kuthetsa njala yawo yauzimu, mayi anayamba kufunafuna Mboni za Yehova m’deralo. Panthawiyi a Mboni za Yehova ankasonkhana m’nyumba zawo, monga mmene ankachitira Akhristu a m’nthawi ya atumwi. (Filemoni 1, 2) Itakwana nthawi yoti anthuwo akasonkhane kwathu, mayi anapempha bambo mwamantha. Bambo anayankha kuti: “Ngati ali anzako ndiye kuti ndi anzanganso.”

Motero anthuwa anali olandiridwa pakhomo pathu. Komabe, anthuwo akayamba kufika ndinkachokapo. Komano posakhalitsa ndinayamba kukhalapo. Khalidwe la nsangala la Mbonizo ndiponso kufotokoza kwawo mosavuta zinthu za m’Baibulo kunathetseratu makani onse amene ndinali nawo. Mbewu inadzalidwa mumtima mwanga n’kuyamba kuphuka. Iyi inali mbewu ya chiyembekezo cham’tsogolo.

Kupita ku Nyanja

Poti amati mwana mbuu make mbuu, nanenso ndinayamba ntchito yoyenda pamadzi. Ndinayambanso kuganizira kwambiri za moyo wanga wauzimu. Nthawi zonse sitima ikafika kumtunda, ndinkayesetsa kukumana ndi Mboni za Yehova. Ku Amsterdam, dziko la Holland (tsopano amati ku Netherlands), ndinapita pa positi ofesi kukafunsa kumene kumapezeka Amboni. Nditakambirana ndi a positi ofesi, anandiuza mmene ndingayendere kuti ndikapeze Amboni ndipo nthawi yomweyo ndinayambapo ulendo. Ndinafika panyumba ina pamene ndinalandiridwa mwansangala ndi kamtsikana ka zaka khumi. Ngakhale kuti sitinkadziwana ndinali womasuka kwambiri ndi kamtsikanaka komanso anthu am’banja lake. Uku kunali kuulawa chabe ubale wa padziko lonse wa Mboni za Yehova.

Ngakhale kuti sitinkamvana chifukwa cha chinenero, iwo anatenga kalendala ndi ndandanda yosonyeza kayendedwe ka sitima yapamtunda n’kuyamba kujambula mapu. Atatero ndinadziwa kuti akundiuza zoti kuchitika msonkhano ku Haarlem, dera lapafupi ndi kumeneku. Ndinapita ku msonkhanowo ndipo unandinasangalatsa kwambiri ngakhale kuti sindinatolepo chilichonse. Nditaona Amboni akugawira anthu timapepala towaitanira ku nkhani ya anthu onse ya Lamlungu, ndinafuna kugwira nawo ntchitoyi. Motero ndinayamba kutolera timapepala timene anthu ena anataya n’kumatigawiranso kwa anthu ena.

Sitima yathu itafika mumzinda wa Buenos Aires, ku Argentina, ndinafika pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Inali nyumba imene inali ndi ofesi imodzi ndi chipinda chosungiramo katundu. Ndinaona mzimayi atakhala pa tebulo akuluka ndipo poteropo panali kamtsikana komwe mwina kanali kamwana kake, kakusewera ndi chidole. Kunali kutada ndithu, ndipo ndinaonanso munthu akutenga mabuku kuchoka pa shelefu. Pamabukuwa panalinso buku la Creation koma la m’Chiswidishi. Nditaona nkhope zawo zansangala ndinalakalaka nditakhala m’gulu la anthu amenewa.

Pobwerera kumudzi, sitima yathu inatenganso anthu amene anali m’ndege ina ya ku Canada yomwe inagwera m’mphepete mwa chilumba cha Newfoundland. Patatha masiku angapo, tinafika kufupi ndi ku Scotland ndipo asilikali apamadzi a ku England anagwira sitima yathu. Anapita nafe ku Kirkwall, pa zilumba za Orkney, kuti akatifunse mafunso. Apa n’kuti nkhondo yachiwiri ya padziko lonse itayamba, ndipo asilikali a Hitler, a chipani cha Nazi anali atalanda kale dziko la Poland mu September 1939. Patatha masiku angapo, anatimasula ndipo tinabwerera ku Sweden popanda vuto lililonse.

Ndinafikanso kumudzi m’njira ziwiri, mwakuthupi komanso mwauzimu. Ndinali wofunitsitsa kukhala m’gulu la anthu a Mulungu ndipo sindinafune kusiya kusonkhana nawo. (Aheberi 10:​24, 25) Ndimasangalala ndikamakumbukira kuti panthawi imene ndinali pamadzi ndinkalalikira kwa oyendetsa sitima anzanga, ndipo ndikudziwa kuti mmodzi wa iwowa anadzakhalanso Mboni.

Utumiki Wapadera

Kumayambiriro kwa 1940, ndinapita kukaona ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Stockholm. Ndinalandiridwa ndi Johan H. Eneroth, yemwe panthawiyo anali kuyang’anira ntchito yolalikira ku Sweden. Ndinamuuza kuti ndikufuna nditakhala mpainiya kuti ndizigwira nawo ntchito yolalikira kwa nthawi zonse. Anandiyang’ana mwachidwi n’kundifunsa kuti: “Kodi umakhulupirira kuti limeneli ndi gulu la Mulungu?”

Ndinayankha kuti: “Inde.” Chifukwa cha yankho langali ndinabatizidwa pa June 22, 1940, ndipo zimenezi zinachititsa kuti ndikhale ndi mwayi waukulu wotumikira pa nthambi pamodzi ndi anthu a makhalidwe abwino kwambiri. Masiku a Loweruka ndi Lamlungu ankathera muutumiki. Panthawi yachilimwe, nthawi zambiri tinkakwera njinga n’kupita m’madera akutali ndipo tinkalalikira Loweruka ndi Lamlungu lonse, n’kumagona m’misasa ya maudzu.

Komabe nthawi zambiri tinkangolalikira khomo ndi khomo mumzinda wa Stockholm kapena m’madera ozungulira mzindawu. Panthawi ina ndinaona munthu wina ali m’chipinda cha pansi panyumba, akumata thanki yakudenga yotenthetsera madzi osamba. Motero ndinapinda shati yanga n’kuyamba kumuthandiza. Titamaliza kumata thankiyo munthuyo anandiyang’ana mothokoza n’kunena kuti: “Ndiyesa chilipo chimene mwabwerera. Tiyeni tisambe m’manja kuti tikambirane bwinobwino kwinaku tikumwa khofi.” Ndinaterodi ndipo ndinayamba kumulalikira kwinaku tikumwa khofi. Patsogolo pake munthuyu anadzakhala Mkhristu.

Ngakhale kuti dziko la Sweden silinalowerere nawo m’nkhondoyi, anthu a ku Sweden anakhudzidwa. Amuna ambiri anaitanidwa kuti akayambe usilikali, kuphatikizapo ineyo. Chifukwa chokana kuphunzira usilikali, ndinamangidwa nthawi zingapo, koma kwa kanthawi chabe. Kenaka ananditumiza ku ndende kuti ndikagwire ntchito ya kalavulagaga. Nthawi zambiri Amboni achinyamata ankaitanidwa pamaso pa oweruza, ndipo ankatha kuchitira umboni za Ufumu wa Mulungu. Zimenezi zinali zogwirizana ndi ulosi wa Yesu wakuti: “Adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa amitundu.”​—Mateyo 10:18.

Moyo Wanga Unasintha

Mu 1945 nkhondo inatha ku Ulaya. Chakumapeto kwa chaka chomwecho, m’bale Nathan H. Knorr, yemwe anali kutsogolera ntchito padziko lonse, anabwera kudzatiyendera kuchoka ku Brooklyn. Iye anabwera ndi mlembi wake, m’bale Milton Henschel. Ulendo umenewu unathandiza kwambiri kuti ntchito yolalikira iyambenso kuyenda molongosoka ku Sweden, ndipo unandithandizanso kwambiri ineyo pandekha. Nditamva kuti n’zotheka kupita ku Sukulu ya Gileadi Yophunzitsa Baibulo, ndinalemba kalata yofunsira sukuluyi nthawi yomweyo.

Chaka chotsatira, ndinayamba sukuluyi, yomwe panthawiyo inali pafupi kwambiri ndi ku South Lansing, mumzinda wa New York. Kosi ya miyezi isanu imeneyi inandiphunzitsa kuona kufunika kwa Baibulo ndiponso gulu la Mulungu. Ndinaona kuti abale amene anali kutsogolera ntchito yolalikira padziko lonse anali omasuka ndi anthu ndiponso oganizira ena. Ankagwira ntchito mwakhama, pamodzi ndi ena tonsefe. (Mateyo 24:14) Ngakhale kuti zimenezi sizinandidabwitse, ndinasangalala kwambiri kuti ndaona ndekha ndi maso anga.

Posakhalitsa tsiku lomaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi linafika. Tsiku lake linali February 9, 1947. M’bale Knorr analengeza mayiko onse amene ophunzirafe titumizidweko. Atafika pa ine, anati: “M’bale Pramberg abwerera ku Sweden kuti akatumikire abale ake kumeneko.” Kunena zoona, sindinasangalale kwambiri kubwerera kwathu.

Ndinapatsidwa Ntchito Yovuta

Nditabwerera ku Sweden, ndinamva kuti pali ntchito ina imene yayamba kuchitika m’mayiko ambiri padziko lonse. Iyi inali ntchito yoyang’anira zigawo. Ndinaikidwa kukhala woyang’anira chigawo woyamba ku Sweden, ndipo ntchito yanga inali yoyang’anira zigawo za dziko lonselo. Ndinkakonza ndi kuyang’anira misonkhano yonse imene patsogolo pake inadzayamba kutchedwa kuti misonkhano yadera. Misonkhano imeneyi inkachitika m’mizinda ndi m’matawuni osiyanasiyana a ku Sweden. Ntchito imeneyi inali itangoyamba kumene motero panalibe malangizo ambiri omwe ndikanatsatira. Ineyo ndi m’bale Eneroth tinakhala pansi n’kukonza pulogalamu yonse m’njira imene timaona kuti inali yabwino kwambiri. Nditalandira utumiki umenewu, ndinachita mantha kwambiri ndipo ndinapemphera kwa Yehova kambirimbiri. Ndinakhala ndi mwayi woyang’anira zigawo kwa zaka 15.

Masiku amenewo, kupeza malo osonkhanapo kunali kovuta kwambiri. Motero tinkangosonkhana m’maholo oviniramo ndiponso malo ena otere. Nthawi zambiri malo amenewa ankakhala ozizira kwambiri ndipo sankakhala olongosoka. Pali malo ena otere amene tinachitirapo msonkhano ku Rökiö, m’dziko la Finland. Holo yake inali bwinja limene kale, anthu a m’deralo ankachitiramo zinthu zosiyanasiyana. Kunja kunali kugwa chipale chofewa, ndipo kunkazizira kuposa m’firiji. Motero tinayatsa mbaula ziwiri zikuluzikulu za migolo ya mafuta n’kuziika pansi pa chumuni cha m’holoyo. Koma sitinadziwe kuti m’kati mwa chumunicho munali zisa za mbalame. Zisazo zinkalepheretsa utsi kutuluka, moti holo yonseyo inadzaza utsi wokhawokha. Komabe aliyense anangokhala phee n’kumangotikita maso chifukwa cha utsiwo, kwinaku akukokera khoti limene wavala. Chifukwa cha zimenezi, msonkhanowu suiwalika.

Ena mwa malangizo amene tinapatsidwa pokonza misonkhano yadera ya masiku atatu imeneyi anali akuti tidzakonze chakudya choti opezeka pamsonkhanopo adzadye. Poyamba, tinalibe zipangizo zokwanira zogwirira ntchito yaikulu chonchi, yomwe tinali tisanaigwirepo n’kale lonse. Koma abale ndi alongo anachita zamphamvu. Moti tsiku loti msonkhano uchitika mawa, iwo anali werawera kusenda mbatata zomwe zinali m’beseni, kwinaku nkhani zili pakamwa. Abale ndi alongo ambiri anadziwanirana pompo n’kukhala mabwenzi kwa nthawi yaitali.

Mbali ina ya ntchito yathu panthawiyi inali kuyenda ndi zikwangwani zolengeza misonkhano yadera. Tinkayenda mondondozana kudutsa m’matawuni kapena m’midzi, n’kumaitana anthu kuti akamvere nkhani ya anthu onse. Nthawi zambiri anthu ankatipatsa ulemu. Tsiku lina tili m’tauni yotchedwa Finspång, tinaona mumsewu muli anthu ambirimbiri ochokera pa fakitale inayake. Mwadzidzidzi mmodzi wa anthuwo anakuwa, amveke: “Taonani gulu limene ngakhale Hitler analilephera!”

Chinthu Chosaiwalika Pamoyo Wanga

Posakhalitsa moyo wanga monga mtumiki woyendayenda unasintha nditakumana ndi Karin, yemwe anali mtsikana wosowetsa tulo. Monga ine, nayenso anaitanidwa ku msonkhano wa mayiko womwe unachitikira kubwalo la masewera la Yankee, mumzinda wa New York City, mu July 1953. Kumeneko n’kumene m’bale Milton Henschel anamangitsa ukwati wathu, panthawi yopuma podikirira chigawo cha masana. Ili linali Lolemba pa July 20. Zinali zodabwitsa kumangitsa ukwati m’kati mwa bwalo lotchuka kwambiri la masewera a mpira wa manja wa amuna. Ndinachita utumiki woyendayenda pamodzi ndi mkazi wanga mpaka mu 1962. Kenaka anatiitana kuti tikatumikire ku Beteli ya ku Sweden. Poyamba ndinkagwira ntchito ku dipatimenti ya magazini. Kenaka, chifukwa choti ndinkadziwa za umakaniko, ndinakhala woyang’anira makina osindikizira ndi makina ena amene anali panthambipo. Kwa zaka zambiri ndithu, Karin anagwira ntchito mu dipatimenti yochapa zovala. Koma kenaka anayamba kugwira ntchito mu dipatimenti yowerenga ndi kukonza zolakwika m’mabuku, ndipo wakhala akugwira ntchito imeneyi kwa zaka zambiri.

Pazaka 54 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova pamodzi ndi mkazi wanga, moyo wathu wakhala wosangalatsa ndiponso wopindulitsa kwambiri. Ndithu Yehova wadalitsa gulu la atumiki ake achikondi, ndiponso olimbikira ntchito. Kale mu 1940, nditayamba kutumikira pa ofesi ya nthambi, ku Sweden kunali Mboni 1,500 zokha. Koma tsopano kuli Mboni zopitirira 22,000. M’madera ena a padziko lapansi Mboni zawonjezeka kuposa pamenepa, moti tsopano padziko lonse pali Mboni zopitirira 6 miliyoni ndi theka.

Mzimu wa Yehova ndiwo ukukankha ntchito yathu kuti ipite patsogolo, monga mmene mphepo imakankhira chombo cha panyanja choyendera m’mphepo. Chifukwa cha chikhulupiriro sitichita mantha tikaona anthu akutekeseka kwambiri ndi zinthu ngati nyanja yolusa. Timayenda molowera kutsogolo, chifukwa dziko latsopano la Mulungu tikutha kuliona bwinobwino poteropo. Ine ndi Karin tikuthokoza Mulungu chifukwa cha zabwino zonse zimene watichitira ndipo tsiku lililonse timapemphera kuti atipatse mphamvu zoti tikhalebe okhulupirika n’kufika bwinobwino pamapeto pa ulendo wathu. Mapeto ake ndiwo kuyanjidwa ndi Mulungu ndi kulandira moyo wosatha.​—Mateyo 24:13.

[Chithunzi patsamba 12]

Ndili pa miyendo ya amayi anga

[Chithunzi patsamba 13]

Kumene tinakwera sitima imene bambo ankayesa cha kumayambiriro kwa m’ma 1920

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi a Herman Henschel (bambo awo a a Milton Henschel) ku Gileadi, mu 1946

[Zithunzi patsamba 16]

Tinakwatirana pa July 20, 1953 mu bwalo lamasewera la Yankee