Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Mkhristu aziona bwanji nkhani ya kusaka kapena kusodza?

Baibulo sililetsa kusaka kapena kusodza. (Deuteronomo 14:​4, 5, 9, 20; Mateyo 17:27; Yohane 21:6) Komabe, Akhristu amene amasaka nyama kapena kuwedza nsomba ayenera kuganizira mfundo zingapo za m’Malemba.

Mulungu anavomereza Nowa ndi mbumba yake kuti azipha nyama ndi kudya, pokhapokha ngati akhetsa magazi. (Genesis 9:​3, 4) Lamulo limeneli linagogomezera mfundo yakuti moyo wa zinyama uyenera kulemekezedwa podziwa kuti unachokera kwa Mulungu. Motero, Akhristu sayenera kupha nyama pofuna kungosewera basi kapena kungosangalala. Komanso sayenera kupha nyama mosalemekeza moyo.​—Miyambo 12:10.

Palinso mbali ina yoyenera kuiganizira yokhudza mmene timaonera nkhaniyi. Atumwi amene anali asodzi ayenera kuti ankasangalala zedi akapha nsomba zambiri. Koma Baibulo silisonyeza kuti iwowa ankadzitama chifukwa cha luso lawo lopha nsomba kapena kusaka nyama. Ndipo silinenanso kuti ankachita mpikisano wosodza, pofuna kusonyeza kuti anali katswiri, kapena pofuna kungosangalala n’kupha nsomba kapena nyama.​—Salmo 11:5; Agalatiya 5:26.

Motero tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimapereka chitsanzo chabwino pankhani yolemekeza moyo monga mmene Yehova amauonera? Kodi ndimangokhalira kuganiza kapena kukamba nkhani zokhudza kusaka kapena kusodza? Kodi pamoyo wanga ndimadziwika monga mlenje, kapena monga mtumiki wa Mulungu? Kodi kupha nyama kapena kuwedza nsomba kumachititsa kuti ndizikhala nthawi yaitali ndi anthu osakhulupirira kapena kunyalanyaza banja langa?’​—Luka 6:45.

Anthu ena amene amasaka nyama kapena kuwedza nsomba pofuna chakudya angaone kuti palibe vuto kunyalanyaza nkhani zauzimu panyengo yosaka kapena yosodza. Koma dziwani kuti timasonyeza kukhulupirira ndiponso kudalira Mulungu tikamayesetsa kusalola chilichonse kukhala chofunika koposa zofuna zake. (Mateyo 6:33) Chinanso n’chakuti Akhristu amamvera malamulo onse a “Kaisara” okhudza kusaka nyama ndi kupha nsomba, ngakhale ngati aboma saonetsetsa kuti malamulowa akutsatiridwa.​—Mateyo 22:21; Aroma 13:1.

Mwina kuti enafe tiyambe kuona nkhani yosaka kapena yosodza monga mmene Yehova amaionera, tiyenera kusintha maganizo athu pankhani ya miyezo ya Yehova. (Aefeso 4:​22-24) Komabe m’pofunika kuti tizilemekeza maganizo a anzathu pankhani zogwirizana ndi chikumbumtima chawo. Zimenezi zikugwirizana kwambiri ndi malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Tisamaweruzane wina ndi mnzake, koma m’malo mwake khalani otsimikiza mtima kusaikira m’bale chokhumudwitsa kapena chopunthwitsa.” (Aroma 14:13) Kusonyeza chikondi ndiponso ulemu woterewu, kumalimbikitsa mtendere mumpingo ndipo kumasangalatsa Mlengi wathu, yemwe ali Chitsime cha chinthu chilichonse chamoyo.​—1 Akorinto 8:13. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onaninso “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 1990.