Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muli ndi Mlangizi pa Zauzimu?

Kodi Muli ndi Mlangizi pa Zauzimu?

Kodi Muli ndi Mlangizi pa Zauzimu?

UZIYA anakhala mfumu ya ufumu wa kum’mwera wa Yuda ali ndi zaka 16 zokha. Analamulira kwa zaka zoposa 50, kuyambira mu 829 B.C.E. mpaka mu 778 B.C.E. Kuyambira ali mwana, Uziya ‘anachita zoongoka pamaso pa Yehova.’ Kodi n’chiyani chinam’thandiza kuchita zinthu zoyenera? Nkhani ya m’Baibulo imati: ‘Uziya anali munthu wakufuna Mulungu m’masiku a Zekariya, . . . [wolangiza kuopa Mulungu woona] ndipo masiku akufunira Yehova iye, Mulungu anam’lemereza.’​—2 Mbiri 26:1, 4, 5.

Ndi nkhani yokhayi m’Baibulo imene imafotokoza za Zekariya yemwe anali mlangizi wa mfumu. Komabe, Zekariya monga “wolangiza kuopa Mulungu woona,” anathandiza kwambiri mfumu yachinyamatayo kuchita zoyenera pa maso pa Yehova Mulungu. Buku lina lofotokoza Baibulo (lotchedwa Expositor’s Bible) limati, n’zodziwikiratu kuti Zekariya “anali munthu wodziwa bwino malemba ndiponso zinthu zauzimu komanso wodziwa kuphunzitsa zimene ankadziwazo.” Katswiri wina wa Baibulo anafika ponena za Zekariya kuti: “Ankadziwa kwambiri maulosi ndiponso . . . anali wanzeru, wodzipereka, munthu wabwino, ndipo zikuoneka kuti iyeyu ndi amene anathandiza kwambiri Uziya.”

Uziya anadalitsidwa kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwakeku ndipo “analimbika chilimbikire” chifukwa “Mulungu anam’thandiza.” Ndithudi, Uziya zinthu zinkamuyendera bwino kwambiri ‘m’masiku a Zekariya’ chifukwa ankakonda zinthu zauzimu. (2 Mbiri 26:6-8) Komano Uziya atalemera kwambiri, anasiya kumvera mlangizi wake, Zekariya. Mtima wake “unakwezeka momuwononga, nalakwira Yehova.” Uziya atachita zinthu zosayenera, anakanthidwa ndi nthenda ya pakhungu yoopsa kwambiri ndipo anapunduka moti ankalephera kugwira ntchito zake bwinobwino monga mfumu.​—2 Mbiri 26:16-21.

Kodi pali munthu winawake amene amakulangizani ndiponso kukuthandizani ‘kufuna Mulungu’? Mungakhale ndi munthu wokuthandizani pa nkhani zauzimu kaya ndinu mnyamata kapena mtsikana. Sonyezani kuti mumayamikira zimene mlangizi wanuyo amakuuzani popeza cholinga chake n’chokuthandizani kuti mupitirize kuchita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova. Mumvereni mlangizi wanu wachikhristuyo chifukwa amadziwa zambiri. Choncho tiyeni tisasiye kumvera mawu a nzeru a mlangizi wathu amene ‘amatilangiza kuopa Mulungu woona.’​—Miyambo 1:5; 12:15; 19:20.