Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Palibe Chida Chosulidwira Inu Chimene Chidzapambane

Palibe Chida Chosulidwira Inu Chimene Chidzapambane

Palibe Chida Chosulidwira Inu Chimene Chidzapambane

“Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula.”​—YESAYA 54:17.

1, 2. Kodi zimene zinachitikira Mboni za Yehova ku Albania zikusonyeza bwanji kuti mawu a pa Yesaya 54:17 ndi oona?

ZAKA makumi angapo zapitazo, m’dziko laling’ono la m’dera la mapiri kum’mwera cha kum’mawa kwa Ulaya, kunali kagulu kolimba mtima ka Akhristu. Anthu a boma la chikomyunizimu osakhulupirira Mulungu anayesetsa kuti afafanize Akhristuwa. Komabe, analephera ngakhale ankawazunza, kuwaika m’ndende ndiponso kuwaipitsira mbiri pofalitsa nkhani zabodza. Kodi Akhristuwo anali ndani? Anali Mboni za Yehova za ku Albania. Ngakhale kuti kusonkhana ndi kulalikira kunali kovuta kwambiri, kupirira kwawo m’zaka zonsezi kunachititsa kuti Chikhristu chilemekezedwe ndiponso dzina la Yehova litamandidwe. M’chaka cha 2006, popatulira maofesi a nthambi yawo yatsopano, Mboni ina yomwe yakhala yokhulupirika kwa nthawi yaitali inati: “Ngakhale Satana atayesetsa bwanji kutizunza sangapambane koma Yehova sadzalephera nthawi zonse.”

2 Umenewu ndi umboni weniweni wotsimikizira kuti zimene Mulungu analonjeza anthu ake pa Yesaya 54:17 n’zoona. Lembali limati: “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m’chiweruzo udzalitsutsa.” Zochitika zikutsimikizira kuti palibe chimene dziko la Satanali lingachite chimene chingaletse atumiki odzipereka kulambira Yehova Mulungu.

Zida za Satana Sizingapambane

3, 4. (a) Kodi zina mwa zida za Satana ndi ziti? (b) Kodi n’chiyani chasonyeza kuti zida za Mdyerekezi sizingapambane?

3 Zida zimene Satana amagwiritsa ntchito polimbana ndi olambira oona ndi zinthu monga, ziletso, ziwawa, ndende ndiponso kupanga ‘chovuta kukhala lamulo.’ (Salmo 94:20) Ndipotu, tikunena pano m’mayiko ena, Akhristu oona ‘akuyesedwa’ chifukwa cha kukhulupirika kwawo.​—Chivumbulutso 2:10.

4 Mwachitsanzo, ofesi ina ya nthambi ya Mboni za Yehova inanena kuti m’chaka chimodzi chokha panali malipoti 32 akuti atumiki a Mulungu anamenyedwa ali mu utumiki. Komanso, panali malipoti ena 59 amene apolisi anamanga a Mboni, ana ndi achikulire omwe chifukwa cholalikira. Ena mwa iwo anatengedwa zidindo za zala zawo, ena kujambulidwa ndi kuponyedwa m’ndende ngati kuti anali zigawenga. Mboni zinanso zinamenyedwa. Panopo m’dziko lina muli malipoti oposa 1,100 okhudza Mboni za Yehova zimene zinamangidwa, kulipitsidwa kapenanso kumenyedwa. Pa malipoti amenewa, oposa 200 anachitika panthawi imene Akhristu amachita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Komabe, mzimu wa Yehova wathandiza anthu ake kupirira zovuta zimenezi, m’mayiko amenewa ndi m’mayiko enanso. (Zekariya 4:6) Nkhanza za adani amenewa sizingatseke pakamwa anthu otamanda Yehova. Inde tili ndi chikhulupiriro choti palibe chida chimene chingalepheretse cholinga cha Mulungu.

Kutsutsa Lilime Lonama

5. Kodi atumiki a Yehova m’nthawi ya atumwi anaukiridwa bwanji ndi lilime lonama?

5 Yesaya analosera kuti anthu a Mulungu adzatsutsa lilime lililonse lomwe lingalimbane nawo. Nthawi zambiri Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankanamiziridwa ndi kuonedwa ngati anthu oipa. Mawu a pa Machitidwe 16:20, 21 akusonyeza bwino zimenezi. Mawuwa amati: “Anthu awa akusokoneza mzinda wathu kwambiri, . . . ndipo akufalitsa miyambo imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatira kapena kuichita, popeza ndife Aroma.” Nthawi ina, anthu achipembedzo omwe anali otsutsa anayesetsa kulimbikitsa olamulira m’mizinda kulimbana ndi otsatira Khristu, akumati: “Anthu awa amene ayalutsa dziko lapansi kumene kuli anthu, tsopano akupezekanso kuno, ndipo akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara.” (Machitidwe 17:6, 7) Mtumwi Paulo ankatchedwa ‘wovutitsa kwabasi’ ndiponso mtsogoleri wa mpatuko amene ankayambitsa zoukira maboma “onse padziko lapansi kumene kuli anthu.”​—Machitidwe 24:2-5.

6, 7. Kodi ndi njira imodzi iti imene Akhristu oona amatsutsira mabodza?

6 N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti Akhristu oona masiku ano amanamiziridwa kwambiri. Kodi timatsutsa bwanji mabodza amenewa?​—Yesaya 54:17.

7 Khalidwe lathu labwino monga Mboni za Yehova nthawi zambiri limatsutsa mabodza amenewa. (1 Petulo 2:12) Akhristu akakhala nzika zomvera malamulo ndiponso akhalidwe labwino ndipo akamachita zinthu zoganizira anzawo, zimene anthu amawanamizirazo zimaoneka zokha kuti sizoona. Khalidwe lathu labwino limatichitira umboni. Anthu akamaona khama lathu pantchito zabwino, nthawi zambiri amalemekeza Atate wathu wakumwamba ndipo amazindikira kuti atumiki ake ali ndi khalidwe labwino.​—Yesaya 60:14; Mateyo 5:14-16.

8. (a) Kodi nthawi zina tingafunike kuchita chiyani kuti titeteze mfundo zathu za m’Baibulo? (b) Potsanzira Khristu, kodi timatsutsa bwanji lilime lonama?

8 Kuwonjezera pa khalidwe lathu lachikhristu, nthawi zina zingakhale bwino kuteteza molimba mtima mfundo zathu za m’Baibulo. Njira imodzi imene tingachitire zimenezi ndi kukadandaula ku boma ndiponso ku khoti. (Estere 8:3; Machitidwe 22:25-29; 25:10-12) Yesu ali padziko lapansi pano, nthawi zina ankatsutsa poyera adani ake ndiponso kuvumbula chinyengo chawo. (Mateyo 12:34-37; 15:1-11) Potsanzira Yesu, timasangalala kukhala ndi mwayi wofotokozera ena momveka bwino zimene timakhulupirira ndi mtima wonse. (1 Petulo 3:15) Choncho, tisasiye kulengeza choonadi cha Mawu a Mulungu chifukwa chakuti anthu kusukulu, kuntchito, kapena achibale amene ali osakhulupirira akutinyoza.​—2 Petulo 3:3, 4.

Yerusalemu Ndiwo “Mwala Wolemetsa”

9. Kodi “mwala wolemetsa” wotchulidwa pa Zekariya 12:3, ukunena Yerusalemu wake uti, ndipo ndani padziko lino akuimira Yerusalemu ameneyu?

9 Ulosi wa Zekariya umanena chifukwa chimene anthu a mitundu amalimbanirana ndi Akhristu oona. Taonani zimene zili pa Zekariya 12:3. Lembali limati: “Kudzachitika tsiku ilo, ndidzaika Yerusalemu akhale mwala wolemetsa mitundu yonse ya anthu.” Kodi ulosiwu ukunena za Yerusalemu uti? Ulosi wa Zekariya ukunena za “Yerusalemu wakumwamba,” yemwe ndi Ufumu wa kumwamba umene Akhristu odzozedwa aitanidwa kuti akalamulire nawo. (Aheberi 12:22) Anthu ochepa a m’kagulu ka olamulira mu Ufumu wa Mesiya amenewa adakali padziko lapansi pano. Iwo pamodzi ndi anzawo a “nkhosa zina,” akulimbikitsa anthu kuti akhale kumbali ya Ufumu wa Mulungu nthawi isanathe. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 11:15) Kodi anthu a mitundu achita chiyani ndi uthenga umenewu? Ndipo kodi Yehova akuthandiza bwanji olambira ake oona masiku ano? Tiyeni tione zimenezi pamene tikukambirana tanthauzo la mawu a m’chaputala 12 cha Zekariya. Kuchita zimenezi kutithandiza kukhala ndi chikhulupiriro chakuti ‘palibe chida chingapindule’ polimbana ndi odzozedwa a Mulungu ndi abale awo okhulupirika.

10. (a) Kodi n’chifukwa chiyani amitundu akuukira anthu a Mulungu? (b) Kodi anthu amene amayesa kuchotsa “mwala wolemetsa” zinthu zimawathera bwanji?

10 Pa Zekariya 12:3 pamasonyeza kuti anthu amitundu ‘adzalasidwa’ kwambiri. Kodi zimenezi zikuchitika bwanji? Mulungu walamula kuti uthenga wabwino wa Ufumu ulalikidwe padziko lapansi. Mboni za Yehova sizimaona ntchito imeneyi mopepuka. Komabe, ntchito yolalikira za Ufumu womwe ndi chiyembekezo chokha cha anthu ndi “mwala wolemetsa” kwa amitundu. Iwo amayesa kuuchotsa posokoneza anthu olalikira za Ufumuwo. Pochita zimenezi, mitunduyi ‘yadzilasa yokha’ n’kukhala ndi mabala okhaokha. Ngakhale mbiri yawo yaipa kumene chifukwa chakuti alephera mochititsa manyazi kukwaniritsa zolinga zawo. Sangakwanitse kutseka pakamwa olambira oona, amene amasangalala kukhala ndi mwayi wolalikira “uthenga wabwino wosatha” wa Ufumu wa Mulungu wa Mesiya, dongosolo lino la zinthu lisanathe. (Chivumbulutso 14:6) Woyang’anira ndende wina m’dziko lina ku Africa kuno ataona nkhanza zimene atumiki a Yehova anali kuchitiridwa anati: ‘Mukungotaya nthawi yanu pozunza anthu awa. Sangasinthe maganizo awo koma anthu amenewa azingochuluka basi.’

11. Kodi Mulungu wakwaniritsa bwanji lonjezo lake la pa Zekariya 12:4?

11 Werengani Zekariya 12:4. Yehova akulonjeza kuti adzachititsa khungu lophiphiritsa ndipo ‘adzadabwitsa’ amene amalimbana ndi atumiki ake a Ufumu olimba mtima. Izitu n’zimene iye wakhala akuchita. Mwachitsanzo, m’dziko lina limene choonadi chinali choletsedwa, anthu otsutsa sanathe kulepheretsa atumiki a Mulungu kulandira chakudya chauzimu. Nyuzipepala ina inanena kuti Mboni za Yehova zinkagwiritsa ntchito zibaluni polowetsa mabuku ofotokoza Baibulo m’dziko lawolo. Mawu amene Mulungu analonjeza atumiki ake okhulupirika anali oona. Mawuwo amati: “Ndidzatsegulira maso anga nyumba ya Yuda, ndi kukantha kavalo aliyense wa mitundu ya anthu akhale wakhungu.” Popeza adani a Ufumuwa adzachititsidwa khungu ndi mkwiyo wawo, sadzadziwa kolowera. Komabe, tili ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova adzasunga anthu ake monga gulu ndipo adzawasamalira.​—2 Mafumu 6:15-19.

12. (a) Kodi Yesu anakoleza bwanji moto padziko lapansi? (b) Kodi otsalira odzozedwa akoleza bwanji moto mwauzimu, nanga zotsatira zake n’zotani?

12 Werengani Zekariya 12:5, 6Mawu akuti “akalonga a Yuda” akunena anthu amene ali oyang’anira pakati pa anthu a Mulungu. Yehova wapatsa anthu amenewa changu choyaka ngati moto pochita zinthu zogwirizana ndi Ufumu padziko lino lapansi. Nthawi ina, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndinabwera kudzakoleza moto padziko lapansi.” (Luka 12:49) Ndithudi, Yesu anakoleza moto. Uthenga wa Ufumu wa Mulungu unali nkhani yaikulu imene Yesu ankalalikira mwachangu. Ndipo zimenezi zinautsa mapiri pachigwa pakati pa mtundu wonse wa Yuda. (Mateyo 4:17, 25; 10:5-7, 17-20) Chotero, mofanana ndi “phale la moto pansi pa nkhuni, ndi ngati muuni wamoto mwa mitolo ya tirigu,” anthu amene amatsatira mapazi a Khristu masiku ano amakoleza moto mwauzimu. Buku lina lofalitsidwa mu 1917 (lakuti The Finished Mystery *) linavumbula chinyengo chonse cha Matchalitchi Achikristu. Izi zinawapalamula atsogoleri achipembedzo. Posachedwapa kapepala ka Uthenga wa Ufumu Na. 37, kakuti “Mapeto a Chipembedzo Chonyenga Ayandikira!” kachititsa anthu ambiri kusankha kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu kapena ayi.

Kupulumutsa “Mahema a Yuda”

13. Kodi mawu akuti “mahema a Yuda” akusonyeza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova adzawapulumutse?

13 Werengani Zekariya 12:7, 8Mu Isiraeli wakale, mahema anali ofala ndipo nthawi zina munkakhala abusa ndi alimi. Anthu amenewa ndi amene akanayamba kuwonongedwa ngati kukanabwera adani kudzaukira mzinda wa Yerusalemu. Mawu akuti “mahema a Yuda” akusonyeza mophiphiritsa kuti otsalira odzozedwa m’nthawi yathu ino ndi osatetezeka, sali m’malo obisika. Iwo akuteteza mopanda mantha zinthu za Ufumu wa Mesiya. Yehova wa makamu adzapulumutsa ‘koyamba mahema a Yuda’ chifukwa ndi omwe Satana akuwafunitsitsa.

14. Kodi Yehova amateteza bwanji anthu a ‘m’mahema a Yuda’ kuti asapunthwe?

14 Ndithudi, zochitika zikusonyeza kuti Yehova akuteteza akazembe odzozedwa a Ufumu ‘m’mahema’ mwawo. * Iye amawateteza kuti asapunthwe ndipo amawathandiza kuti akhale ngati mfumu ya nkhondo, Davide.

15. N’chifukwa chiyani Yehova ‘adzayesa kuwononga amitundu onse,’ ndipo adzachita liti zimenezi?

15 Werengani Zekariya 12:9. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova ‘adzayesa kuwononga amitundu onse’? Iwo adzaweruzidwa chifukwa chakuti amangokhalira kutsutsa Ufumu wa Umesiya komanso chifukwa chozunza anthu a Mulungu. Posachedwapa magulu a Satana a padziko lapansi pano adzaukira komaliza olambira oona a Mulungu. Izi zidzapangitsa kuti zimene Baibulo limati Haramagedo zichitike. (Chivumbulutso 16:13-16) Zikadzatero, Woweruza Wamkulu adzateteza atumiki ake ndiponso adzayeretsa dzina lake kwa anthu a mitundu yonse.​—Ezekieli 38:14-18, 22, 23.

16, 17. (a) Kodi “cholowa cha atumiki a Yehova” n’chiyani? (b) Kodi kupirira kwathu Satana akamatiukira kumatsimikizira chiyani?

16 Satana alibe chida chimene chingafooketse kapena kuchepetsa changu cha anthu a Mulungu padziko lonse. Tili ndi mtendere wauzimu womwe ndi “cholowa cha atumiki a Yehova” chifukwa timadziwa kuti Iye ali ndi mphamvu zopulumutsa. (Yesaya 54:17) Palibe angatilande mtendere umenewu ndiponso chuma chauzimu chimene tili nacho. (Salmo 118:6) Satana apitiriza kukolezera moto kuti anthu azititsutsa ndiponso kutizunza. Kupitiriza kwathu kupirira kumatsimizira kuti tili ndi mzimu wa Mulungu. (1 Petulo 4:14) Uthenga wabwino woti Ufumu wa Yehova unakhazikitsidwa ukulalikidwa padziko lonse. Mofanana ndi zida zimene zimaponyedwa kuti zisokoneze anthu ena, anthu a Mulungu akuponyeredwa “miyala” yambiri yophiphiritsa. Komabe chifukwa cha mphamvu ya Yehova, iwo akupirira nayo miyalayo ndipo sikuwasokoneza ngakhale pang’ono. (Zekariya 9:15) Palibe munthu amene adzaimitse ntchito ya otsalira odzozedwa ndi anzawo okhulupirika.

17 Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene Mdyerekezi sadzatiukiranso. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri chifukwa talonjezedwa kuti ‘palibe chida chosulidwira ife chimene chidzapindule; ndipo lilime lililonse limene lidzakangana nafe m’chiweruzo tidzalitsutsa.’

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri pa mfundoyi, onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses​—Proclaimers of God’s Kingdom masamba 675 ndi 676, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti zida za Satana sizingapambane?

• Kodi Yerusalemu wakumwamba wakhala bwanji “mwala wolemetsa”?

• Kodi Yehova amapulumutsa bwanji “mahema a Yuda”?

• Pamene tikuyandikira Aramagedo, kodi n’chiyani chimene chili chotsimikizirika?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 21]

Anthu a Yehova ku Albania anakhalabe okhulupirika ngakhale kuti Satana ankawaukira

[Chithunzi patsamba 23]

Yesu anavumbula chinyengo

[Zithunzi patsamba 24]

Palibe chida chosulidwira anthu olengeza uthenga wabwino chimene chidzapambane