Akhristu Akamapetedwa Ngati Tirigu
Akhristu Akamapetedwa Ngati Tirigu
ATATSALA pang’ono kuphedwa, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Ndithu Satana akufuna anthu inu, kuti akupeteni ngati tirigu.” (Luka 22:31) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?
M’nthawi ya Yesu, ntchito yokolola tirigu inali yowawa kwambiri. Choyamba, okololawo ankaunjika pamodzi tirigu yense amene wadulidwa m’munda. Kenaka, ankamupuntha pomumenyetsa pa chinachake kapena pogwiritsira ntchito zida zokokedwa ndi ziweto. Akatero, ankauluza mankhusu, kapena kuti zosafunikira za m’tiriguyo. Tirigu weniweniyo ankagwera pansi, pamene mankhusu aja ankauluzika ndi mphepo. Pomaliza ankapeta tiriguyo.
Mogwirizana ndi mawu a Yesu aja, Satana analimbana nawo zedi ophunzira a Yesu panthawiyo ndipo amalimbananso ndi ifeyo masiku ano. (Aef. 6:11) Inde, sikuti zovuta zathu zonse amaziyambitsa ndi Satana. (Mlal. 9:11) Komabe Satana amachita chilichonse chimene angathe kuti awononge kukhulupirika kwathu. Mwachitsanzo, angatiyese ndi chuma, zosangalatsa zosayenera, kapena zinthu monga chiwerewere. Angagwiritsenso ntchito anzathu a kusukulu kapena a kuntchito ndiponso abale athu osakhulupirira kutilimbikitsa kuti tizilimbana kwambiri ndi kupeza zinthu zonse za m’dzikoli zokhudza maphunziro ndiponso ntchito zapamwamba. Komanso Satana angagwiritse ntchito chizunzo chenicheni pofuna kuti tisiye kukhulupirika kwa Mulungu. Komabe, pali njira zinanso zosiyanasiyana zimene Satana amagwiritsira ntchito kuti atipete.
Kodi tingalimbane naye bwanji mdani wamphamvuyu? Satana sitingaimitsane naye patokha, koma tikudziwa kuti Yehova samuona Satana ngati kanthu. Yehova amatithandiza kulimbana bwinobwino ndi Satana tikamam’dalira mosakayika ngakhale pang’ono, tikamadalira malangizo ake, ndiponso tikamapemphera ndi mtima wonse kuti atipatse nzeru ndi kutilimbitsa mtima kuti tipirire.—Sal. 25:4, 5.
Tikamayesedwa tizitha “kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika” kuti tipewe kusocheretsedwa ndi Satana. (Aheb. 5:13, 14) Yehova angatithandize kuti tizitha kutero. Ndiyeno tiziyesetsa kuchita zoyenerazo, ngakhale zitavuta bwanji. Tikamatsatira malangizo a Yehova, iye sangalephere kutithandiza poona kulimba mtima kwathu pankhani yochita zinthu zoyenera.—Aef. 6:10.
Satana amayesa kutipeta ngati tirigu. Koma mwa mphamvu ya Yehova, tingathe kulimbana naye n’kukhala olimba m’chikhulupiriro. (1 Pet. 5:9) Inde, Mawu a Yehova amatitsimikizira kuti: “Tsutsani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani.”—Yak. 4:7.