Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Oyenerera” Akulabadira

Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Oyenerera” Akulabadira

Anthu Amene Ali ndi “Maganizo Oyenerera” Akulabadira

“Onse amene anali ndi maganizo oyenerera moyo wosatha anakhala okhulupirira.”​—MAC. 13:48.

1, 2. Kodi Akhristu oyambirira analabadira bwanji ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse kumene kuli anthu?

M’BUKU la m’Baibulo la Machitidwe muli nkhani yochititsa chidwi. Nkhani imeneyi imasimba mmene Akhristu oyambirira analabadirira ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. (Mat. 24:14) Alaliki okangalika amenewo analambula njira kuti onse obwera m’mbuyo mwawo awatsatire. Ophunzira a Yesu atachitira umboni mwachangu mu Yerusalemu, anthu zikwizikwi, kuphatikizapo “ansembe ambirimbiri,” analowa mu mpingo woyambirira.​—Mac. 2:41; 4:4; 6:7.

2 Amishonale oyambirira anathandiza anthu enanso ambiri kuyamba Chikhristu. Mwachitsanzo, Filipo anapita ku Samariya ndipo kumeneko makamu a anthu anamvetsera uthenga wake. (Mac. 8:5-8) Paulo limodzi ndi anzake osiyanasiyana anayenda maulendo ataliatali polalikira uthenga wachikhristu ku Kupuro, madera ena a Asia Minor, Makedoniya, Girisi ndi Italiya. Ayuda ndi Agiriki ambirimbiri anayamba kukhulupirira m’mizinda imene iye analalikirako. (Mac. 14:1; 16:5; 17:4) Tito anali kulalikira ku Kerete. (Tito 1:5) Petulo anali kugwira ntchito mwakhama ku Babulo, ndipo pamene analemba kalata yake yoyamba, cha m’ma 62-64 C.E., ntchito ya Akhristu inali kudziwika ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asia ndi Bituniya. (1 Pet. 1:1; 5:13) Imeneyo inali nthawi yosangalatsa kwambiri. Akhristu oyambirira amenewo anali alaliki okangalika kwambiri motero kuti adani awo anati iwo “ayalutsa dziko lapansi kumene kuli anthu.”​—Mac. 17:6; 28:22.

3. Kodi masiku ano ntchito yolengeza Ufumu ikubala zipatso zotani, ndipo inu mukumva bwanji?

3 Masiku anonso, mpingo wachikhristu ukuwonjezeka kwambiri. Kodi simulimbikitsidwa mukawerenga lipoti la pachaka la Mboni za Yehova ndi kuona mmene anthu akuwonjezekera pa dziko lonse lapansi? Kodi simukusangalala kudziwa kuti olengeza Ufumu anachititsa maphunziro a Baibulo oposa 6,000,000 m’chaka chautumiki cha 2007? Ndiponso, chiwerengero cha anthu amene anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Khristu chinasonyeza kuti anthu pafupifupi 10,000,000 amene si Mboni za Yehova, anachita chidwi ndi uthenga wabwino mpaka kupezeka pa mwambo wofunika kwambiri umenewu. Zimenezi zikusonyeza kuti ntchito ilipobe yambiri.

4. Kodi ndi anthu otani amene akulabadira uthenga wa Ufumu?

4 Masiku ano, mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, “onse amene [ali] ndi maganizo oyenerera moyo wosatha” akulabadira uthenga wa choonadi. (Mac. 13:48) Yehova akusonkhanitsira anthu otero m’gulu lake. (Werengani Hagai 2:7.) Kodi tiyenera kukhala ndi maganizo otani pautumiki wachikhristu kuti tigwire mokwanira ntchito yosonkhanitsa anthu imeneyi?

Lalikirani Mopanda Tsankho

5. Kodi Yehova amayanja anthu otani?

5 Akhristu oyambirira anazindikira kuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Kuti munthu akhale pa ubale ndi Yehova, amafunika kukhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu. (Yoh. 3:16, 36) Ndipo chifuniro cha Yehova ndi chakuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”​—1 Tim. 2:3, 4.

6. Kodi alaliki a Ufumu ayenera kupewa chiyani, ndipo chifukwa chiyani?

6 Si bwino kuti olengeza uthenga wabwino aziweruziratu anthu chifukwa cha mtundu wawo, zinthu zimene ali nazo, maonekedwe awo, zipembedzo zawo, kapena makhalidwe awo. Tadzifunsani kuti: Kodi ine sindikuyamikira kuti munthu amene anayamba kulankhula nane choonadi cha m’Malemba analibe tsankho? Ndiye n’kulekeranji kuuza aliyense amene angamvetsere uthenga wopulumutsa moyo?​—Werengani Mateyo 7:12.

7. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruza anthu amene timawalalikira?

7 Yehova waika Yesu kukhala Woweruza, choncho ife tilibe udindo woweruza aliyense. Zimenezi ndi zomveka, popeza ife timangoweruza “monga apenya maso” athu kapena “mwamphekesera,” koma Yesu amadziwa zenizeni zimene zili m’maganizo ndi mumtima wa munthu.​—Yes. 11:1-5; 2 Tim. 4:1.

8, 9. (a) Kodi Saulo anali munthu wotani asanakhale Mkhristu? (b) Kodi nkhani ya mtumwi Paulo ikutiphunzitsa chiyani?

8 Anthu amtundu uliwonse akhala atumiki a Yehova. Chitsanzo chimodzi chapadera ndi Saulo wa ku Tariso, amene anadzakhala mtumwi Paulo. Saulo ali Mfarisi, anali kutsutsa koopsa Akhristu. Chifukwa chokhulupirira ndi mtima wonse kuti mpingo wachikhristu unali wolakwa, iye anauzunza. (Agal. 1:13) Kwa anthu, iye ayenera kuti anaoneka ngati sangakhale Mkhristu. Koma Yesu anaona zabwino mumtima wa Saulo ndipo anamusankha kuti achite ntchito yapadera. Mapeto ake, Saulo anakhala mmodzi wa anthu achangu ndi okangalika mumpingo woyambirira wachikhristu.

9 Kodi nkhani ya mtumwi Paulo ikutiphunzitsa chiyani? M’gawo lathu, mungakhale anthu amene amaoneka kuti amadana ndi uthenga wathu. Mwina zingakhale zokayikitsa kuti anthu amenewo angadzakhale Akhristu oona, komabe tisasiye kukambirana nawo. Zimachitika kuti anthu amene sitikuwaganizira n’komwe amalabadira uthenga wathu. Ntchito yathu ndi yolalikira anthu onse “mwakhama.”​—Werengani Machitidwe 5:42.

Anthu Amene Amalalikira “Mwakhama” Amadalitsidwa

10. N’chifukwa chiyani sitiyenera kusiya kulalikira anthu amene akuoneka oopsa? Perekani zitsanzo za m’dera lanu.

10 Maonekedwe amapusitsa. Mwachitsanzo, Ignacio * anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ali kundende m’dziko lina la ku South America. Anthu anali kumuopa chifukwa anali wachiwawa. Choncho, akaidi anzake amene anali kupanga ndi kugulitsa zinthu kwa akaidi ena, anali kuuza Ignacio kuti aziwatengera ngongole kwa anthu amene amazengereza kubweza. Koma Ignacio atayamba kupita patsogolo mwauzimu ndiponso kugwiritsa ntchito zimene anali kuphunzira, munthu amene anali wachiwawa ndi wovutitsa anzake ameneyu, anasintha n’kukhala munthu wachifundo. Palibenso amene amamuuza kuti akamutengere ngongole. Ignacio akuona kuti choonadi cha m’Baibulo ndiponso mzimu wa Mulungu, ndi zimene zasintha khalidwe lake. Iye akuyamikira kwambiri kupanda tsankho kwa olengeza Ufumu amene anayesetsa kuphunzira naye.

11. N’chifukwa chiyani timapita mobwerezabwereza kwa anthu amene timawalalikira?

11 Chifukwa china chimene timapitira mobwerezabwereza kwa anthu amene tinawalalikira uthenga wabwino ndi chakuti khalidwe ndiponso zochitika pamoyo zimasintha. N’kutheka kuti pambuyo powalalikira, ena angakumane ndi mavuto monga matenda aakulu, kuchotsedwa ntchito kapena imfa ya wokondedwa wawo. (Werengani Mlaliki 9:11.) Mavuto a m’dzikoli angachititse anthu kuganizira mozama za tsogolo lawo. Zinthu ngati zimenezi zingachititse munthu amene poyamba analibe chidwi kapena amene anali wotsutsa, kulabadira uthenga wathu. Choncho tisasiye kulalikira uthenga wabwino kwa anthu pa mpata uliwonse umene ungapezeke.

12. Kodi tiziwaona bwanji anthu amene timawalalikira, ndipo chifukwa chiyani?

12 Anthufe timakonda kuweruza anzathu ndi kuganiza kuti akutiakuti sangalabadire choonadi. Koma Yehova amaona mmene munthu aliyense payekha alili. Amaona zabwino zimene munthu aliyense angathe kuchita. (Werengani 1 Samueli 16:7.) Tikakhala mu utumiki, ifenso tizichita chimodzimodzi. Zokumana nazo za anthu ambiri zimasonyeza kuti tikakhala ndi maganizo osakondera kwa anthu amene timawalalikira, zotsatira zake zimakhala zabwino.

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani mpainiya wina analibe chidwi ndi mayi amene anakumana naye muutumiki? (b) Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani?

13 Mpainiya wina dzina lake Sandra, anali mu ulaliki wa nyumba ndi nyumba pachilumba china cha ku Caribbean. Mlongo ameneyu anakumana ndi Ruth, amene anali kukonda kwambiri kuchita zikondwerero zovina mumsewu. Kawiri konse Ruth anawinapo mpikisano wa dzikolo chifukwa chodziwa kuvina pazikondwerero zimenezo. Iye anachita chidwi kwambiri ndi zimene Sandra anali kulankhula, ndipo anakonza zakuti aziphunzira naye Baibulo. Sandra anati: “Nditalowa m’chipinda chake chochezeramo, ndinangoona chithunzi chachikulu cha Ruth atavala zovala zonse zovinira. Munalinso mphoto zimene analandira. Nditaona zimenezo, ndinaganiza molakwa kuti munthu wotchuka ndiponso wokonda zikondwerero zovina mumsewu ngati ameneyo sangapitirize kuchita chidwi ndi choonadi. Choncho ndinasiya kupitako.”

14 Patapita nthawi, Ruth uja anabwera ku Nyumba ya Ufumu. Misonkhano itatha, anafunsa Sandra kuti, “N’chifukwa chiyani munasiya kuphunzira nane?” Sandra anapepesa ndipo anayambiranso kuphunzira naye. Ruth anapita patsogolo mofulumira, anachotsa zithunzi zake zija, anayamba kuchita nawo ntchito zonse za mpingo ndipo anapereka moyo wake kwa Yehova. Mosakayikira Sandra anazindikira kuti zimene anachita poyamba zinali zolakwika.

15, 16. (a) Kodi chinachitika ndi chiyani wofalitsa wina atalalikira wachibale wake? (b) N’chifukwa chiyani zochita za wachibale wathu siziyenera kutilepheretsa kumulalikira?

15 Anthu ena ambiri amene alalikira kwa achibale awo osakhulupirira, apeza zotsatirapo zabwino ngakhale achibalewo anaoneka kuti sangalabadire uthenga wathu. Mwachitsanzo, taganizirani nkhani ya Joyce, mlongo wa ku United States. Mlamu wake wamwamuna anakhala akumangidwa kuyambira ali wachinyamata. Joyce anati: “Anthu anali kunena kuti iyeyo anali wachabechabe chifukwa chakuti anali kugulitsa mankhwala osokoneza bongo, kuba ndipo anali kuchita zoipa zambirimbiri. Ngakhale anali wotero, ine ndinali kumuuzabe choonadi cha m’Baibulo kwa zaka 37.” Kuleza mtima ndiponso khama lake pothandiza wachibale wakeyo, zinapindula kwambiri pamene wachibaleyo anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anasintha kwambiri moyo wake. Posachedwapa, mlamu wa Joyce uja anabatizidwa pa msonkhano wachigawo ku California, m’dziko la United States, ali ndi zaka 50. Joyce anati: “Ndinalira chifukwa cha chisangalalo. Ndine wosangalala kwambiri kuti sindinatope naye.”

16 Mwina mungazengereze kuuza achibale ena choonadi cha m’Baibulo chifukwa cha zimene iwo amachita. Koma Joyce sanazengereze kulankhula ndi mlamu wake. Ndi iko komwe, ungadziwe bwanji zimene zili mu mtima mwa munthu wina? Mwina munthu ameneyo angakhale akufufuza choonadi ndi mtima wonse. Choncho musamumane mwayi wopeza choonadi.​—Werengani Miyambo 3:27.

Buku Lothandiza Pophunzira Baibulo

17, 18. (a) Kodi malipoti ochokera m’mayiko osiyanasiyana akusonyeza chiyani za ubwino wa buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? (b) Kodi inu mwakumana ndi zinthu zolimbikitsa zotani pogwiritsa ntchito buku limeneli?

17 Malipoti ochokera m’mayiko osiyanasiyana akusonyeza kuti anthu ambiri amtima wabwino akulikonda kwambiri buku lophunzirira Baibulo lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Mpainiya wina ku United States dzina lake Penni, anayamba kuphunzira buku limeneli ndi anthu angapo. Awiri mwa anthuwo anali okalamba ndiponso okonda kwambiri chipembedzo chawo. Mlongo wathu Penni sanadziwe kuti anthuwo achita chiyani akamva mfundo za choonadi cha m’Malemba zomwe zili m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngakhale iye anali ndi nkhawa imeneyo, analemba kuti: “Popeza kuti bukuli limafotokoza mfundo zake momveka, motsatirika ndi mwachidule, iwo sanavutike kuvomereza kuti zimene anali kuphunzirazo ndi choonadi. Iwo sanatsutse kapena kukwiya.”

18 Pat, wofalitsa wa ku Britain, anayamba kuphunzira Baibulo ndi mayi wina yemwe anathawa kwawo kudziko lina la ku Asia. Mayiyo anathawa m’dziko lawo ataona kuti mwamuna wake ndi ana ake atengedwa ndi zigawenga ndipo sanawaonenso. Moyo wake unali pa ngozi, nyumba yake inatenthedwa ndipo gulu la amuna linamugwirira. Chifukwa cha zimenezi, anaganiza kuti palibe chifukwa chokhalira ndi moyo ndipo anayesa kudzipha kangapo. Koma atayamba kuphunzira Baibulo, anakhala ndi chiyembekezo. Pat analemba kuti: “Iye anakhudzidwa kwambiri ndi mfundo komanso mafanizo osavuta kumva a m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.” Wophunzirayo anapita patsogolo mofulumira, anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo anati akufuna kubatizidwa pa msonkhano wotsatira. Zimasangalatsa kwambiri kuthandiza anthu amtima wabwino kumvetsa ndi kuyamikira chiyembekezo chimene Malemba amapereka.

“Tisaleke Kuchita Zabwino”

19. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ifunika kugwiridwa mwachangu?

19 Tsiku lililonse likadutsa, nthawi yakuti tigwire ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira imachepa. Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri amaganizo oyenerera amalabadira ife tikamalalikira. Komatu “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” Zimenezi zikutanthauza kuti anthu amene adakali mu mdima wauzimu akupita kokaphedwa.​—Zef. 1:14; Miy. 24:11.

20. Kodi aliyense wa ife ayenera kulimbikira kuchita chiyani?

20 Anthu oterewa tingawathandizebe. Kuti tichite zimenezi, tifunika kutengera chitsanzo cha Akhristu oyambirira amene “anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.” (Mac. 5:42) Tengerani chitsanzo chawo mwa kulimbikira kulalikira ngakhale mukukumana ndi mavuto, kuyang’anira ‘luso lanu la kuphunzitsa’ ndiponso kulalikira anthu onse mopanda tsankho. “Tisaleke kuchita zabwino” chifukwa tikalimbikira, tidzadalitsidwa kwambiri mwa kuyanjidwa ndi Mulungu.​—2 Tim. 4:2; werengani Agalatiya 6:9.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Mayina ena tawasintha.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndi anthu otani amene akulabadira uthenga wabwino?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kuweruziratu anthu amene timawalalikira?

• Kodi pakukhala zotsatira zotani pogwiritsa ntchito buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

Anthu ambirimbiri amtima wabwino akulabadira uthenga wabwino

[Zithunzi patsamba 15]

Kodi kusintha kwa mtumwi Paulo kukutiphunzitsa chiyani?

[Chithunzi patsamba 16]

Olengeza uthenga wabwino saweruziratu anthu