Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Magazini Yophunzira Yatsopano ya Nsanja ya Olonda

Magazini Yophunzira Yatsopano ya Nsanja ya Olonda

Magazini Yophunzira Yatsopano ya Nsanja ya Olonda

MAGAZINI imene mukuwerengayi ndi magazini yophunzira yoyamba ya Nsanja ya Olonda. Tikufuna tikufotokozereni zinthu zatsopano m’magaziniyi.

Magazini yophunzira ndi ya Mboni za Yehova ndiponso ophunzira Baibulo amene akupita patsogolo. Magaziniyi izituluka kamodzi pamwezi ndipo izikhala ndi nkhani zophunzira zinayi kapena zisanu. Ndandanda yophunzirira nkhani zimenezi izikhala pa tsamba loyamba la magaziniyi. Mosiyana ndi magazini yogawira ya Nsanja ya Olonda, magazini yophunzira siizikhala ndi zithunzi zosiyanasiyana pa chikuto mwezi uliwonse. Izi zili choncho chifukwa chakuti si yogawira m’munda.

Patsamba 2 la magaziniyi, pazikhala mawu achidule othandiza kwambiri ofotokoza cholinga cha nkhani yophunzira iliyonse kapena nkhani zophunzira zingapo komanso nkhani zina zimene zilimo. Mbali imeneyi izithandiza kwambiri abale ochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda pokonzekera kuti phunziro la nkhanizo likakhale logwira mtima pamsonkhano wa mpingo.

Muona kuti nkhani zophunzira ndi zofupikirapo kuyerekeza ndi kale. Choncho, pa Phunziro la Nsanja ya Olonda pazikhala nthawi yambiri yokambirana malemba amene ali ndi mfundo zazikulu. Tikukulimbikitsani kuti mlungu uliwonse, muziona malemba onse osagwidwa mawu. Malemba ena osagwidwa mawu alembedwa kuti, “werengani” ndipo muyenera kuwawerenga ndi kukambirana pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Mungawerengenso malemba ena ngati muli ndi nthawi. M’nkhani zina, mudzapeza malemba olembedwa kuti, “yerekezerani ndi.” Si nthawi zonse pamene malemba oterowo aziwerengedwa pa msonkhano wa mpingo. Chifukwa chake ndi chakuti umboni umene amapereka wotsimikizira mfundo zazikulu zimene zili pa ndimeyo, si wachindunji. Komabe, malemba olembedwa kuti, “yerekezerani ndi” ali ndi mfundo zina zowonjezera zochititsa chidwi komanso m’njira ina angachirikize mfundo zimene mukuphunzira. Tikukulimbikitsani kuwawerenga pokonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda kuti mwina mungatchule mfundo zake popereka ndemanga zanu.

Kuyambira chaka cha 2008, mu Nsanja ya Olonda simuzikhalanso lipoti la pachaka. M’malo mwake, lipotilo lizikhala mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndiponso mu Yearbook. Ngakhale zili choncho, maganizi yophunzira izikhala ndi nkhani zina malinga ndi zimene tanena kale. Tikukulimbikitsani kuwerenga nkhanizo mosamala, ngakhale kuti pamisonkhano ya mpingo sitidzakambirana zambiri mwa nkhani zimenezo. Nazonso ndi chakudya chauzimu chochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mat. 24:45-47.

Pomaliza, dziwani kuti magazini yophunzira ndiponso yogawira ya Nsanja ya Olonda si magazini awiri osiyana. Magazini onsewo ndi Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova. Patsamba 2 pali ndime zofanana zofotokoza cholinga cha Nsanja ya Olonda. Baundi voliyumu ya pachaka izikhala ndi magazini onsewo. Ndiponso mfundo zochokera m’magazini onsewo zizipezeka m’nkhani yakuti, “Kodi Mukukumbukira?” imene izituluka m’magazini yophunzira.

Kuyambira mu 1879, Nsanja ya Olonda yakhala ikulengeza mokhulupirika mfundo za choonadi cha Ufumu wa Mulungu. Yachita zimenezi ngakhale kuti pazaka zonsezo kwakhala nkhondo, mavuto a zachuma, ndi chizunzo. Pemphero lathu ndi lakuti Yehova adalitse magaziniyi kuti ipitirize kulengeza Ufumu. Adalitsenso inu owerenga pamene mukugwiritsa ntchito mwanzeru magazini yophunzira yatsopano ya Nsanja ya Olonda.