Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mateyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mateyo

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Mateyo

MUNTHU woyamba kulemba nkhani yochititsa chidwi ya moyo wa Yesu ndiponso utumiki wake anali Mateyo. Iyeyu anali mnzake wapamtima wa Yesu Khristu ndipo panthawi ina anali wokhometsa msonkho. Uthenga Wabwino wa Mateyo anaulemba m’Chiheberi ndipo kenako unadzamasuliridwa m’Chigiriki. Anamaliza kuulemba cha mu 41 C.E. ndipo buku limeneli ndilo limagwirizanitsa Malemba Achiheberi ndi Malemba Achigiriki Achikhristu.

Zikuoneka kuti kwenikweni Mateyo anali kuganizira zoti Ayuda ndiwo akawerenge buku lakeli ndipo bukuli ndi lokhudza mtima komanso lothandiza kwambiri. Limasonyeza kuti Yesu ndiye Mesiya amene analonjezedwa, komanso Mwana wa Mulungu. Kutsatira mosamala uthenga wa m’bukuli kungalimbitse chikhulupiriro chathu mwa Mulungu woona, Mwana wake, ndiponso malonjezo Ake.​—Aheb. 4:12.

“UFUMU WA KUMWAMBA WAYANDIKIRA”

(Mat. 1:1–20:34)

Mateyo anatsindika kwambiri nkhani yokhudza Ufumu ndiponso zimene Yesu ankaphunzitsa, ngakhale kuti zimenezi zinachititsa kuti asatsatire ndondomeko yeniyeni ya mmene nkhanizo zinachitikira. Mwachitsanzo, ulaliki wa pa phiri uli cha kumayambiriro kwenikweni kwa bukuli, ngakhale kuti ulaliki umenewu unachitika cha m’katikati mwa utumiki wa Yesu.

Akulalikira ku Galileya, Yesu anachita zozizwitsa zambiri, analangiza atumwi 12 za mmene ayenera kuchitira utumiki wawo, anadzudzula Afarisi komanso ananena mafanizo osiyanasiyana okhudza Ufumu. Kenaka anachoka ku Galileya n’kubwera “ku madera a ku malire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano.” (Mat. 19:1) Ali m’njira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Tikukwezekaku tsopano ndi ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa munthu akamuweruza kuti aphedwe ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwa.’​—Mat. 20:18, 19.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

3:16—Kodi “kumwamba kunatseguka” motani pamene Yesu anali kubatizidwa? Zikuoneka kuti mawu amenewa akutanthauza kuti panthawiyo Yesu anayambanso kukumbukira zinthu zonse zokhudza nthawi imene anali kumwamba asanabwere padziko lapansi n’kudzakhala munthu.

5:21, 22—Kodi kuchita zinthu zosonyeza kupsa mtima n’koopsa kuposa kupitiriza kusunga mkwiyo mumtima? Yesu anachenjeza kuti munthu amene akupitiriza kupsera mtima m’bale wake amapalamula mlandu waukulu kwambiri. Koma, anati kuchita zinthu mopsa mtima ponena mawu onyoza n’koopsa kuposa pamenepa, moti munthu wochita zimenezi amapalamula mlandu wa ku khoti lapamwamba.

5:48—Kodi n’zothekadi kuti tikhale “angwiro, monga Atate [wathu] wa kumwamba ali wangwiro”? Inde tingati n’zotheka ndithu. Pamenepa, Yesu anali kunena za nkhani ya chikondi, ndipo ankauza anthu amene ankamumvetsera kuti atsanzire Mulungu pokhala ndi chikondi changwiro kapena kuti chokwanira. (Mat. 5:43-47) Kodi akanachita bwanji zimenezi? Akanatero poyamba kukondanso ngakhale adani awo.

7:16—Kodi ndi “zipatso” zotani zimene zimazindikiritsa chipembedzo choona? Zipatso zimenezi sizitanthauza khalidwe lathu lokha ayi, koma zimatanthauzanso ziphunzitso zimene timatsatira.

10:34-38—Kodi uthenga wa m’Malemba ndiwo umachititsa kuti mabanja azigawanika? Ayi si choncho. M’malo mwake kugawanika kotereku kumachitika chifukwa cha mmene anthu a m’banjamo akhudzidwira ndi uthengawo. Iwo angaganize zosaumvera kapenanso zotsutsa Chikhristu, ndipo zimenezi zingagawanitse banjalo.​—Luka 12:51-53.

11:2-6—Ngati Yohane anadziwa kale kuti Yesu ndi Mesiya pomva mawu ochokera kwa Mulungu omuvomereza, n’chifukwa chiyani iye anafunsa ngati Yesu anali “Wobwerayo”? N’kutheka kuti Yohane anafunsa zimenezi pofuna kudzimvera yekha kwa Yesu. Koma n’kuthekanso kuti kwenikweni iye ankafuna kudziwa ngati padzakhalenso “wina” amene adzabwere ndi mphamvu za Ufumu n’kukwaniritsa zinthu zonse zimene Ayuda ankayembekezera. Yankho la Yesu linasonyeza kuti sipadzakhalanso wina ayi.

19:28—Kodi mawu akuti “mafuko 12 a Isiraeli” amene adzaweruzidwe akuimira chiyani? Awa si mafuko 12 a Isiraeli wauzimu. (Agal. 6:16; Chiv. 7:4-8) Atumwi amene Yesu ankawauza zimenezi patsogolo pake anadzakhala m’gulu la Isiraeli wauzimu, osati oweruza a gululo. Yesu ‘anachita nawo chipangano cha ufumu,’ ndipo ichi chinali chipangano choti adzakhale ‘ansembe kwa Mulungu.’ (Luka 22:28-30; Chiv. 5:10) Anthu a m’gulu la Isiraeli wauzimu ‘adzaweruza dziko.’ (1 Akor. 6:2) Motero, zikuoneka kuti “mafuko 12 a Isiraeli,” amene anthu okhala pa mipando ya kumwamba akuweruza, akuimira dziko la anthu amene alipo masiku ano, amene ali kunja kwa gulu la ansembe achifumuwa. Mafuko 12 a pa Tsiku la Chitetezo anali ngati chithunzithunzi cha gulu limeneli.​—Lev., chap. 16.

Zimene Tikuphunzirapo:

4:1-10. Nkhani imeneyi ikutiphunzitsa kuti Satana ndi weniweni osati mkhalidwe woipa chabe ayi. Iye amagwiritsira ntchito “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo” potiyesa. Komano, kugwiritsira ntchito mfundo za m’Malemba kumatithandiza kukhala okhulupirika kwa Mulungu.​—1 Yoh. 2:16.

5:1–7:29. Zindikirani zosowa zanu zauzimu. Khalani amtendere. Kanizani maganizo osayenera. Sungani malonjezo anu. Muzipempherera kwambiri za zinthu zauzimu osati zakuthupi. Khalani olemera kwa Mulungu. Funani Ufumu choyamba ndi chilungamo cha Mulungu. Musakhale ndi mtima wokonda kutola ena zifukwa. Chitani chifuniro cha Mulungu. Inde, tingaphunzire zinthu zambiri zothandiza pa ulaliki wa pa phiri.

9:37, 38. Tikamachita mwakhama ntchito yopanga ophunzira ndiye kuti tikugwirizanadi ndi pempho limene timauza Mbuye wathu, lakuti “atumize antchito kukakolola.”​—Mat. 28:19, 20.

10:32, 33. Tisamaope ngakhale pang’ono kuuza ena za chikhulupiriro chathu.

13:51, 52. Tikamvetsetsa choonadi cha Ufumu timakhala ndi udindo wophunzitsa ena choonadicho ndi kuwathandiza kuchimvetsa.

14:12, 13, 23. Nthawi yokhala patokha n’njofunika kwambiri kuti tizisinkhasinkha.​—Maliko 6:46; Luka 6:12.

17:20. Timafunika kukhala ndi chikhulupiriro kuti tithane ndi mavuto aakulu ngati mapiri omwe angatisokoneze mwauzimu ndi kutilepheretsa kuthana ndi zovuta zosiyanasiyana. Tisamanyalanyaze kukulitsa ndiponso kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova ndi malonjezo ake.​—Maliko 11:23; Luka 17:6.

18:1-4; 20:20-28. Ophunzira a Yesu ankaganizira kwambiri za udindo chifukwa cha kupanda ungwiro ndiponso chifukwa cha zipembedzo zawo zakale zomwe zinkatsindika kwambiri nkhani ya udindo. Tiyenera kuyesetsa kukhala odzichepetsa popewa makhalidwe oipa ndipo tiziona m’njira yoyenerera mwayi wosiyanasiyana wa utumiki mumpingo ndiponso maudindo apadera amene tapatsidwa.

“MWANA WA MUNTHU ADZAPEREKEDWA”

(Mat. 21:1–28:20)

Yesu anafika ku Yerusalemu pa Nisani 9, 33 C.E., ‘atakwera pa bulu.’ (Mat. 21:5) Tsiku lotsatira, iye anafika ku kachisi ndipo anakayeretsako. Pa Nisani 11, anaphunzitsa m’kachisimo, kudzudzula Afarisi, ndipo kenaka anauza ophunzira ake za “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 24:3) Tsiku lotsatira, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa kuti pasika achitika pakangopita masiku awiri, ndipo Mwana wa munthu adzaperekedwa kuti akapachikidwe.”​—Mat. 26:1, 2.

Pa Nisani 14, Yesu atamaliza kukhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake imene inali itayandikira kwambiri, anaperekedwa, kumangidwa, kuweruzidwa, n’kupachikidwa. Patsiku lachitatu, iye anaukitsidwa. Asanapite kumwamba, Yesu analamula otsatira ake kuti: “Choncho pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse.”​—Mat. 28:19.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

22:3, 4, 9—Kodi ndi nthawi zitatu ziti zimene anthu anaitanidwa kuti apite ku phwando laukwati? Nthawi yoyamba kuitana anthu a m’gulu la mkwatibwi inali pamene Yesu ndi otsatira ake anayamba kulalikira mu 29 C.E., ndipo anapitiriza kuwaitana mpaka mu 33 C.E. Nthawi yachiwiri inayambira pamene ophunzira analandira mzimu woyera pa Pentekosite mu 33 C.E. ndipo inatha mu 36 C.E. Panthawi ziwiri zonsezi, oitanidwawo anali Ayuda, anthu otembenukira ku Chiyuda ndiponso Asamariya. Komano nthawi yachitatu anaitana anthu amene anali m’misewu ya kunja kwa mzinda, kutanthauza anthu osadulidwa, omwe sanali Ayuda. Zimenezi zinayamba kuchitika mu 36 C.E. panthawi imene Koneliyo, yemwe anali kapitawo wa gulu la asilikali achiroma anatembenuka ndipo zikupitirira mpaka pano.

23:15—N’chifukwa chiyani Afarisi akatembenuza munthu, munthuyo ankakhala “woyenera kuponyedwa m’Gehena kuwirikiza kawiri kuposa” Afarisiwo? Ena mwa anthu amene ankatembenuzidwa ndi Afarisiwo anali atachita machimo aakulu zedi m’mbuyomo. Ndiyeno anthuwo akatembenuka n’kuyamba kutsatira mfundo zonyanyira za Afarisi, ankachita kuipiratu chifukwa mwina ankafika poposa aphunzitsi awowo potsatira kwambiri mfundo zonyanyira. Motero, ankakhala oyenera kwambiri “kuponyedwa m’Gehena” poyerekezera ndi Afarisiwo.

27:3-5—Kodi n’chiyani chimene chinam’chititsa Yudasi kuti avutike mumtima mwake? Palibe mfundo iliyonse yosonyeza kuti Yudasi anavutika mumtima chifukwa cholapa zenizeni. M’malo mopempha Mulungu kuti amukhululukire, iye anakaulula tchimo lake kwa ansembe aakulu ndiponso akulu. Yudasi anadzimva kuti n’ngolakwa kwambiri ndipo anavutika maganizo zedi. Mpake kutero chifukwa iyeyu anachita “tchimo lobweretsa imfa.” (1 Yoh. 5:16) Chinam’chititsa kuti avutike mtima chinali kuthedwa nzeru basi.

Zimene Tikuphunzirapo:

21:28-31. Chinthu chofunika kwambiri kwa Yehova n’chakuti tizichita chifuniro chake. Mwachitsanzo, tizilimbikira kwambiri kuchita ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Mat. 24:14; 28:19, 20.

22:37-39. Malamulo awiri aakulu koposa amanena mwachidule zedi zimene Mulungu amafuna kuti anthu om’lambira azichita.

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi mukulimbikira kwambiri pantchito yokolola?

[Mawu a Chithunzi]

© 2003 BiblePlaces.com

[Chithunzi patsamba 31]

Buku la Mateyo limatsindika kwambiri nkhani yokhudza Ufumu