Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo Wawo Unakhala Waphindu Nanga Inuyo Bwanji?

Moyo Wawo Unakhala Waphindu Nanga Inuyo Bwanji?

Moyo Wawo Unakhala Waphindu Nanga Inuyo Bwanji?

M’BALE wina wa ku Canada dzina lake Marc, analembedwa ntchito kukampani ina yopanga makina apamwamba omwe mabungwe ofufuza za kuthambo amagwiritsa ntchito. Anali kugwira ntchito maola ochepa ndipo anali mpainiya wokhazikika. Kenako, bwana ake anauza Marc kuti amukweza pantchito koma azigwira ntchitoyo tsiku lonse. Ntchitoyo inali ya ndalama zambiri. Kodi Marc anatani atamva zimenezi?

Mlongo wina wa ku Philippines dzina lake Amy, anali kuchita upainiya wokhazikika ali pafupi kumaliza maphunziro ake. Atamaliza maphunziro akewo, analonjezedwa ntchito ya pamwamba. Ntchitoyi inali yofuna nthawi yambiri koma malipiro ake anali ambirinso. Kodi Amy anatani?

Marc ndi Amy anasankha zinthu zosiyana, ndipo zotsatira zake zikusonyeza kuti malangizo amene Akhristu a ku Korinto anapatsidwa ndi anzeru. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Amene amagwiritsa ntchito dzikoli azikhala ngati amene sakuligwiritsa ntchito mokwanira.”​—1 Akor. 7:29-31.

Musagwiritse Ntchito Dzikoli Mokwanira

Tisanakambirane zimene zinachitikira Marc ndi Amy, tiyeni tione mwachidule tanthauzo la mawu akuti “dziko” (kapena kuti, koʹsmos m’Chigiriki) amene Paulo anagwiritsa ntchito m’kalata yake kwa Akorinto. Pamavesi a m’Baibulo amenewa, mawu akuti koʹsmos amanena za dongosolo limene tikukhalali, kutanthauza anthu ndi zochitika zawo zonse, kuphatikizapo zinthu zofunika masiku onse monga nyumba, chakudya ndi zovala. * Kuti tikhale ndi zinthu zofunika pamoyo zimenezi, tiyenera kugwira ntchito. Ndithudi, sitingachitire mwina koma kugwiritsa ntchito dzikoli kuti tikwaniritse udindo wathu wa m’Malemba wodzisamala ndi kusamala banja lathu. (1 Tim. 5:8) Ngakhale zili choncho, timadziwa kuti “dziko likupita.” (1 Yoh. 2:17) Motero, timagwiritsa ntchito dzikoli moyenera koma osati “mokwanira.”​—1 Akor. 7:31.

Potsatira malangizo a m’Baibulo akuti tigwiritse ntchito dziko moyenera, abale ndi alongo ambiri aganiziranso za moyo wawo, achepetsa nthawi imene amagwira ntchito ndipo asintha moyo wawo ndi kukhala ndi zinthu zochepa. Atangochita zimenezo, anaona kuti moyo wawo wakhala waphindu chifukwa chakuti anali ndi nthawi yambiri yocheza ndi mabanja awo ndiponso yotumikira Yehova. Anaonanso kuti chifukwa chokhala ndi zochepa, anayamba kudalira kwambiri Yehova m’malo modalira dzikoli. Kodi inunso mungachite zimenezi ndi kusintha moyo wanu kuti mukhale ndi zinthu zochepa pofuna kuika patsogolo zinthu za Ufumu wa Mulungu?​—Mat. 6:19-24, 33.

“Ubale Wathu ndi Yehova Walimba Kwambiri Kuposa Kale”

Marc amene tamutchula poyamba uja, anatsatira malangizo a Baibulo akuti tisagwiritse ntchito dzikoli mokwanira. Anakana kukwezedwa pantchito ngakhale kuti akanapeza ndalama zambiri. Patadutsa masiku angapo, bwana ake anamulonjeza kuti awonjezeranso malipiro atsopanowo pofuna kumukopa kuti avomere ntchito yatsopanoyo. Marc anati: “Chinali chiyeso chovuta, koma ndinakanabe.” Pofotokoza chifukwa chake, iye anati: “Ine ndi mkazi wanga Paula, tinali kufuna kugwiritsa ntchito moyo wathu wonse potumikira Yehova mmene tingathere. Motero tinaganiza zosintha moyo kuti tikhale ndi zinthu zochepa. Tinapempha nzeru kwa Yehova kuti tikwanitse zolinga zathu ndipo tinakhazikitsa tsiku lakuti tiyambe kutumikira Yehova mmene tingathere.”

Paula anati: “Ndinali kugwira ntchito ya usekiritale kuchipatala kwa masiku atatu pamlungu ndipo malipiro ake anali abwino. Ndinalinso mpainiya wokhazikika. Koma mofanana ndi Marc, inenso ndinafuna kukatumikira Yehova kulikonse kumene kunali kufunika olengeza Ufumu ambiri. Nditapereka kalata yanga yosiyira ntchito, bwana anga anandiuza kuti pali mwayi wakuti ndikhale sekiritale wamkulu. Ntchito imeneyi inali ya ndalama zambiri pachipatalapo, komabe sindinasinthe maganizo anga osiya ntchito. Nditauza bwana anga chifukwa chimene sindinafune kufunsira ntchitoyo, anatamanda chikhulupiriro changa.”

Posapita nthawi, Marc ndi Paula anatumizidwa kukachita upainiya wapadera mumpingo waung’ono kudera lina lakutali m’dziko la Canada. Kodi zinthu zinawayendera bwanji? Marc anati: “Nditasiya ntchito yabwino imene ndinagwira kwa nthawi yaitali, ndinali ndi nkhawa, koma Yehova anadalitsa utumiki wathu. Tikusangalala kwambiri chifukwa chogawira ena mphatso zauzimu. Utumiki wa nthawi zonse walimbitsanso banja lathu. Timakonda kukambirana zinthu zauzimu zomwe ndi zofunika kwambiri. Ubale wathu ndi Yehova walimba kwambiri kuposa kale.” (Mac. 20:35) Nayenso Paula anati: “Ukasiya ntchito komanso nyumba yabwino imene unaizolowera, uyenera kudalira Yehova ndi mtima wako wonse. Izi ndi zimene tinachita, ndipo Yehova anatidalitsa. Abale ndi alongo athu okondedwa mumpingo wathu watsopano amatikonda ndipo amationa kuti ndife anthu ofunika. Panopo ndimagwiritsa ntchito mphamvu zanga zomwe ndinali kuthera pa ntchito kuthandiza anthu mwauzimu. Ndine wosangalala kwambiri kugwira ntchito imeneyi.”

‘Moyo Wosasowa Kanthu Koma Wosasangalatsa’

Amy amene tamutchula poyamba uja, anasankha zosiyana. Anavomera ntchito ya ndalama zambiri imene anapatsidwa. Amy anati: “Chaka choyamba, ndinali wokangalika muutumiki. Koma kenako moyo wanga unayamba kusintha pang’ono ndi pang’ono mpaka ndinayamba kuiwala zinthu za Ufumu ndi kumangoganiza zokwezedwa pantchito. Anali kundilonjeza kuti andikweza pa ntchito ndipo zinali zokopa kwambiri. Ndinayamba kugwira ntchito kwambiri pofuna udindo wapamwamba. Udindo wanga kuntchito utayamba kuwonjezeka, nthawi yochitira utumiki inayamba kuchepa. Mapeto ake, ndinasiyiratu kulalikira.”

Pokumbukira nthawi imeneyo, Amy anati: “Sindinali kusowa ndalama. Akakhala maulendowa, ndiye osanena. Kutchukanso, ndinatchuka chifukwa cha ntchito yanga yapamwamba. Koma sindinali wosangalala. Ndinali ndi mavuto ambiri ngakhale kuti ndinali ndi ndalama zambiri. Sindinadziwe kuti chikuvuta ndi chiyani. Kenako ndinazindikira kuti ndinatsala pang’ono ‘kusocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro’ chifukwa chofuna ntchito yapamwamba m’dzikoli. Choncho, malinga ndi zimene Mawu a Mulungu amanena, ndinali kuvutika ndi ‘zopweteka zambiri.’”​—1 Tim. 6:10.

Kodi Amy anachita chiyani? Iye anati: “Ndinapempha akulu kuti andithandize kukhala wolimbanso mwauzimu ndi kuyambanso kusonkhana. Nthawi ina nyimbo ikuimbidwa pa msonkhano, ndinayamba kulira. Ndinakumbukira chisangalalo chimene ndinali nacho pazaka zisanu zomwe ndinali kuchita upainiya, ngakhale kuti nthawi imeneyo ndinali wosauka. Ndinazindikira kuti ndiyenera kusiya moyo wofunafuna ndalama ndipo ndiyenera kuika zinthu za Ufumu patsogolo. Ndinalolera ntchito yotsika imene malipiro ake anali theka la malipiro a ntchito ya poyamba. Ndipo ndinayambanso kulalikira.” Mosangalala, Amy anati: “Ndinasangalala kuchita upainiya kwa zaka zingapo. Moyo wanga panopo ndi watanthauzo kwambiri kusiyana ndi mmene unalili panthawi imene ndinali kugwirira ntchito dzikoli.”

Kodi inu mungasinthe moyo wanu kuti mukhale ndi zinthu zochepa? Mukagwiritsa ntchito nthawi imene mungakhale nayo kuti mupititse patsogolo zinthu za Ufumu, inunso moyo wanu udzakhala waphindu.​—Miy. 10:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Onani Insight on the Scriptures, Voliyumu 2, masamba 1207 ndi 1208.

[Mawu Otsindika patsamba 19]

Kodi inu mungasinthe moyo wanu kuti mukhale ndi zinthu zochepa?

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 19]

“Ndayamba Kale Kusangalala!”

Mkulu wina wachikhristu wa ku United States dzina lake David, anali kufuna kuchita utumiki wa nthawi zonse limodzi ndi mkazi wake ndi ana ake. Kukampani imene anali kugwira, anagwirizana zakuti azigwira ntchito maola ochepa, ndipo anayamba upainiya wokhazikika. Kodi moyo wake unakhala waphindu chifukwa cha kusintha kumeneku? Patapita miyezi ingapo, David analembera mnzake kalata kuti: “Palibenso chinthu chosangalatsa kwambiri kuposa kutumikira Yehova mokwanira limodzi ndi banja lako. Ndinali kuganiza kuti zidzanditengera nthawi yaitali kuti ndizolowere upainiya, koma ndayamba kale kusangalala! Zimenezi ndi zotsitsimula kwambiri.”

[Chithunzi patsamba 18]

Marc ndi Paula ali mu utumiki