Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Onetsetsani Kuti Mukusamala Utumiki Umene Munaulandira mwa Ambuye

Onetsetsani Kuti Mukusamala Utumiki Umene Munaulandira mwa Ambuye

Onetsetsani Kuti Mukusamala Utumiki Umene Munaulandira mwa Ambuye

“Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.”​—AKOL. 4:17.

1, 2. Kodi Akhristu ali ndi udindo wotani kwa anthu onse?

TILI ndi udindo waukulu kwa anthu anzathu. Malinga ndi zimene anthuwo akusankha panopa, angapulumuke kapena kufa pa “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:14) Wolemba buku la Miyambo anauziridwa kunena kuti: “Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse; omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa.” Amenewa ndi mawu okhudza mtima kwambiri. Tikalephera udindo wathu wochenjeza anthu pa zimene ayenera kusankha, tingakhale ndi mlandu wa magazi. Pajatu lemba lomwelo limati: “Ukanena, Taonani, sitinadziwa chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake?” Zoonadi, atumiki a Yehova sanganene kuti ‘sadziwa’ za tsoka limene anthu adzakumana nalo.​—Miy. 24:11, 12.

2 Yehova amaona moyo kukhala wamtengo wapatali. N’chifukwa chake amalimbikitsa atumiki ake kuchita zonse zimene angathe kuti apulumutse miyoyo yambiri. Mtumiki aliyense wa Mulungu ayenera kulalikira uthenga wopulumutsa moyo umene umapezeka m’Mawu a Mulungu. Ntchito yathuyi imafanana ndi ya mlonda amene akaona zinthu zoopsa zikubwera, amachenjeza anthu. Ifetu sitikufuna kukhala ndi mlandu wa magazi a anthu omwe angawonongeke. (Ezek. 33:1-7) Choncho, tifunika kulimbikira ‘kulalika mawu.’​—Werengani 2 Timoteyo 4:1, 2, 5.

3. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino ndi nkhani ziwiri zotsatira?

3 M’nkhani ino, tikambirana mmene mungagonjetsere mavuto okulepheretsani kuchita utumiki wopulumutsa moyo. Tikambirananso mmene mungathandizire anthu ambiri. M’nkhani yotsatira, tidzakambirana zimene mungachite kuti mupeze luso la kuphunzitsa ena mfundo zofunika za choonadi. Nkhani yachitatu idzasimba zinthu zina zolimbikitsa zimene olengeza Ufumu akuchita padziko lonse. Koma tisanakambirane nkhani zimenezo, tiyeni tione chifukwa chake masiku athu ano ali ovuta kwambiri.

N’chifukwa Chiyani Ambiri Alibe Chiyembekezo?

4, 5. Kodi anthu akukumana ndi zotani, ndipo ambiri amachita chiyani?

4 Zimene zikuchitika padziko lonse zikusonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu” ndipo mapetowo afika posachedwa. Anthu akukumana ndi zinthu zimene Yesu ndi ophunzira ake anati zidzakhala chizindikiro cha “masiku otsiriza.” “Masautso,” monga nkhondo, njala, zivomezi ndi mavuto ena, zikuvutitsa anthu. Anthu kulikonse ndi osamvera malamulo, adyera ndiponso saopa Mulungu. ‘Nthawi ino ndi yovuta’ ngakhale kwa anthu amene akuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo.​—Mat. 24:3, 6-8, 12; 2 Tim. 3:1-5.

5 Anthu ambiri sakudziwa kuti n’chifukwa chiyani dzikoli lili m’mavuto chonchi. Motero ambiri amada nkhawa za moyo wawo ndi wa mabanja awo. Amazunzika mnzawo kapena wachibale akamwalira, kapenanso iwo akakumana ndi mavuto ena. Anthuwa sadziwa bwinobwino chifukwa chake zinthu zimenezi zikuchitika ndiponso mmene zidzathera, choncho alibe chiyembekezo.​—Aef. 2:12.

6. N’chifukwa chiyani “Babulo Wamkulu” sakuthandiza anthu ake?

6 “Babulo Wamkulu,” kutanthauza ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, sakuthandiza anthu ngakhale pang’ono. M’malo mwake, iye wamwetsa anthu ambirimbiri “vinyo wa dama lake” ndipo iwo akudzandira posokonezeka mwauzimu. Ndiponso pokhala ngati mkazi wachiwerewere, chipembedzo chonyenga chakopa ndi kulamulira “mafumu a dziko lapansi.” Icho chikugwiritsanso ntchito ziphunzitso zonyenga ndi zamizimu polimbikitsa anthu kuti azigonjera andale m’chimbulimbuli. Mwanjira imeneyi, chipembedzo chonyenga chakhala champhamvu ngakhale kuti chimakaniratu choonadi cha Baibulo.​—Chiv. 17:1, 2, 5; 18:23.

7. Kodi anthu ambiri akupita kuti, nanga ena angathandizidwe bwanji?

7 Yesu anaphunzitsa kuti anthu ambiri akuyenda pa msewu waukulu wopita kuchiwonongeko. (Mat. 7:13, 14) Anthu ena ali pa msewu waukuluwo chifukwa chakuti asankha okha kusatsatira zimene Baibulo limaphunzitsa. Koma ena ambiri ali pa msewuwo chifukwa chonamizidwa, kapena kuti ali mu mdima ndipo sadziwa zimene Yehova amafuna kuti iwowo achite. Mwina ena angasinthe moyo wawo atapatsidwa zifukwa zomveka za m’Malemba. Koma amene sakuchoka m’Babulo Wamkulu ndiponso amene akupitiriza kusatsatira mfundo za m’Baibulo, sadzapulumuka “chisautso chachikulu.”​—Chiv. 7:14.

Musasiye Kulalikira “Mwakhama”

8, 9. Kodi Akhristu oyambirira anatani potsutsidwa, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?

8 Yesu ananena kuti ophunzira ake adzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Choncho kuyambira kale, Akhristu oona amakhulupirira kuti kuchita ntchito yolalikira ndi kofunika kwambiri pachikhulupiriro chawo ndipo kumasonyeza kukhulupirika kwawo kwa Mulungu. N’chifukwa chake otsatira a Yesu oyambirira sanasiye kulalikira ngakhale pamene anali kutsutsidwa. Iwo anadalira mphamvu ya Yehova ndipo anamupempha kuti awathandize kuti “alankhulebe mawu [ake] molimba mtima.” Poyankha pemphero lawo, Yehova anawapatsa mzimu woyera ndipo iwo analankhula mawu a Mulungu molimba mtima.​—Mac. 4:18, 29, 31.

9 Anthu amene anali kuwatsutsa atayamba chiwawa, kodi otsatira a Yesu anachita mantha ndi kusiya kulalikira uthenga wabwino? Ayi. Atsogoleri achipembedzo cha Chiyuda atakwiya ndi ulaliki wa atumwi, anagwira atumwiwo, kuwaopseza ndi kuwakwapula. Koma atumwiwo “anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu, Yesu.” Anatero chifukwa chozindikira kuti ayenera “kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Mac. 5:28, 29, 40-42.

10. Kodi Akhristu masiku ano amakumana ndi mavuto otani, nanga chingachitike ndi chiyani chifukwa cha khalidwe lawo labwino?

10 Masiku ano atumiki a Mulungu ochuluka sanakwapulidwepo kapena kuponyedwa m’ndende chifukwa cholalikira. Ngakhale zili choncho, Akhristu onse oona amayesedwa m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, chifukwa cha chikumbumtima chanu chophunzitsidwa Baibulo, mungakhale ndi khalidwe limene ena sangasangalale nalo kapena losiyana kwambiri ndi la anzanu. Mabwenzi anu, anzanu a kusukulu, kapena anansi anu angamakudabweni chifukwa chochita zinthu motsatira mfundo za m’Baibulo. Kaya anzanuwo achita chiyani, inu musafooke. Dzikoli lili mu mdima wauzimu, koma Akhristu “[amawala] monga zounikira.” (Afil. 2:15) Mwina anthu ozindikira adzaona ndi kusirira ntchito zanu zabwino ndipo mapeto ake, adzalemekeza Yehova.​—Werengani Mateyo 5:16.

11. (a) Kodi anthu ena angachite chiyani tikamawalalikira? (b) Kodi mtumwi Paulo anatsutsidwa m’njira zotani, ndipo iye anatani?

11 Kuti tisasiye kulalikira uthenga wa Ufumu, tifunika kulimba mtima. Anthu ena, ngakhale achibale, angakunyodoleni kapena angayese kukugwetsani ulesi mwanjira zina. (Mat. 10:36) Mtumwi Paulo anamenyedwa kangapo chifukwa chochita utumiki wake mokhulupirika. Onani zimene iye anachita atakumana ndi zimenezo. Analemba kuti: “Titavutika ndi kuchitidwa za chipongwe . . . , tinalimba mtima mwa Mulungu wathu kulankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikira kwambiri.” (1 Ates. 2:2) Kunena zoona, sichinali chinthu chapafupi kuti Paulo apitirize kulankhula za uthenga wabwino pambuyo pa kugwidwa, kuvulidwa zovala, kukwapulidwa ndi ndodo ndiponso kuponyedwa m’ndende. (Mac. 16:19-24) Kodi zinatheka bwanji kuti alimbe mtima ndi kupitiriza kulalikira? Zinatheka chifukwa chakuti anali ndi mtima wofunitsitsa kuchita ntchito yolalikira imene Mulungu anamupatsa.​—1 Akor. 9:16.

12, 13. Kodi ena amakumana ndi mavuto otani, nanga achita zotani polimbana ndi mavutowo?

12 Zingativutenso kukhala achangu m’magawo amene anthu sapezekapezeka pa nyumba kapena kumene anthu ambiri alibe chidwi ndi uthenga wa Ufumu. Kodi tingachite chiyani pamenepo? Mwina tingafunike kulimba mtima kwambiri kuti tilankhule ndi anthu powalalikira mwamwayi. Mwinanso tingasinthe nthawi yolalikira kapena kuyesetsa kukalalikira m’madera amene mungapezeke anthu ambiri.​—Yerekezerani ndi Yohane 4:7-15; Machitidwe 16:13; 17:17.

13 Mavuto ena amene anthu ambiri amalimbana nawo ndi ukalamba ndi matenda. Chifukwa cha zimenezi, iwo sangachite zambiri pantchito yolalikira. Ngati inu muli m’gulu limeneli, musataye mtima. Yehova akudziwa zimene simungathe kuchita ndipo amayamikira zimene mumakwanitsa. (Werengani 2 Akorinto 8:12.) Ngakhale mutakumana ndi mavuto otani, kaya kutsutsidwa, anthu opanda chidwi, kapena matenda, chitani zonse zimene mungathe kuti muuze ena uthenga wabwino.​—Miy. 3:27; yerekezerani ndi Maliko 12:41-44.

Onetsetsani Kuti Mukusamala Utumiki Wanu

14. Kodi mtumwi Paulo anapereka chitsanzo chotani kwa Akhristu anzake, nanga anapereka malangizo otani?

14 Mtumwi Paulo anasamala utumiki wake ndipo analimbikitsa okhulupirira anzake kuchita zomwezo. (Mac. 20:20, 21; 1 Akor. 11:1) Munthu wina amene Paulo analimbikitsa mwapadera anali Arikipo, Mkhristu wa m’nthawi ya atumwi. Polembera kalata Akolose, Paulo anati: “Arikipo mumuuze kuti: ‘Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.’” (Akol. 4:17) Sitikudziwa kuti Arikipo anali munthu wotani ndiponso kuti moyo wake unali wotani. Koma zikuonekeratu kuti analandira utumiki. Ngati inuyo ndinu Mkhristu wodzipereka kwa Mulungu, nanunso munalandira utumiki. Kodi mukupitiriza kusamala utumikiwo kuti muukwaniritse?

15. Kodi Mkhristu akadzipereka ndiye kuti wachita chiyani, ndipo zimenezi zikubweretsa mafunso ati?

15 Tisanabatizidwe, tinapereka moyo wathu kwa Yehova ndipo tinachita zimenezo mwa kupemphera ndi mtima wonse. Izi zinatanthauza kuti tinali okonzeka kuchita chifuniro chake. Choncho ndi bwino kudzifunsa panopo kuti, ‘Kodi ndimaona kuti kuchita chifuniro cha Mulungu ndi chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanga?’ Mwina tingakhale ndi udindo wina umene Yehova amafuna kuti tikwaniritse, monga kusamalira banja. (1 Tim. 5:8) Koma kodi nthawi yathu yotsala ndiponso mphamvu zathu timazigwiritsa ntchito bwanji? Kodi chofunika kwambiri pamoyo wathu ndi chiyani?​—Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.

16, 17. Kodi ndi zinthu zotani zimene Akhristu achinyamata kapena amene ali ndi udindo wochepa angachite?

16 Kodi ndinu Mkhristu wodzipereka ndiponso wachinyamata amene wamaliza kapena watsala pang’ono kumaliza sukulu? Ngati ndi choncho, muyenera kuti mulibe udindo waukulu wosamalira banja. Ndiye mukufuna kuchita chiyani pamoyo wanu? Kodi ndi zosankha zotani zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa lonjezo lanu lakuti mudzachita chifuniro cha Yehova? Ambiri asintha zina ndi zina pamoyo wawo kuti achite upainiya ndipo akusangalala kwambiri.​—Sal. 110:3; Mlal. 12:1.

17 Mwina ndinu wachikulirepo ndipo mumagwira ntchito yolembedwa koma mulibe udindo wambiri kupatulapo kudzipezera zofunika pamoyo. Mosakayika mumasangalala kugwira ntchito ndi mpingo malinga ndi mpata umene mumakhala nawo. Kodi mungakonde kuwonjezera chisangalalo chanu? Kodi mwaganizapo zofutukula utumiki wanu? (Sal. 34:8; Miy. 10:22) Mpaka pano, m’madera ena muli ntchito yambiri yofunika kuti ichitike, yofikira aliyense ndi uthenga wopatsa moyo wa choonadi. Kodi zingatheke kuti musinthe zina ndi zina pamoyo wanu n’cholinga chakuti mukatumikire kumene kukufunika olengeza Ufumu ambiri?​—Werengani 1 Timoteyo 6:6-8.

18. Kodi banja lina lachinyamata linatani, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

18 Tsopano tiyeni tione chitsanzo cha Kevin ndi Elena a ku United States. * Monga mmene zimakhalira kwawoko ndi achinyamata oti angokwatirana kumene, iwo anaganiza zogula nyumba. Onse anali pa ntchito ndipo anali ndi moyo wapamwamba. Ngakhale zinali choncho, ntchito yawo komanso ntchito za pakhomo sizinawapatse mpata wolalikira. Iwo anazindikira kuti anali kuthera nthawi ndi mphamvu zawo zonse pazinthu zimene anali nazo. Koma ataona chisangalalo cha banja lina la apainiya omwe analibe zinthu zambiri, Kevin ndi Elena anaganiza zosintha moyo wawo. Atapempha Yehova kuti awathandize pa nkhani imeneyi, anagulitsa nyumba yawo ndi kukakhala m’nyumba yaing’ono. Elena anayamba kugwira ntchito yolembedwa kwa maola ochepa ndipo anayamba upainiya. Chifukwa cholimbikitsidwa ndi zinthu zosangalatsa zimene mkazi wake anali kukumana nazo, Kevin anasiya ntchito ndi kuyamba upainiya. Patapita nthawi, anasamukira ku dziko lina la ku South America kuti akatumikire kumene kukufunikira alaliki ambiri a Ufumu. Kevin anati: “M’mbuyo monsemu, banja lathu linali losangalala. Koma titayamba kulimbikira zinthu zauzimu, chisangalalo chathu chinawonjezeka kwambiri.”​—Werengani Mateyo 6:19-22.

19, 20. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira uthenga wabwino ili yofunika kwambiri masiku ano kuposa ntchito ina iliyonse?

19 Kulalikira uthenga wabwino ndi ntchito yofunika kwambiri imene ikuchitika pa dziko lapansi masiku ano kuposa ntchito ina iliyonse. (Chiv. 14:6, 7) Imathandiza kuti dzina la Yehova liyeretsedwe. (Mat. 6:9) Uthenga wa m’Baibulo umathandiza anthu ambiri amene akuulandira chaka chilichonse kukhala ndi moyo wabwino, ndipo chifukwa cha zimenezi angadzapulumuke. Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Adzamva bwanji . . . popanda wina kulalikira?” (Aroma 10:14, 15) N’zodziwikiratu kuti sizingatheke. Bwanji osalimbikira kuchita zimene mungathe kuti mukwaniritse utumiki wanu?

20 Pali njira inanso imene mungathandizire anthu kumvetsa chifukwa chake nthawi yathu ino ili yovuta, ndiponso kuwathandiza kuzindikira kuti zosankha zawo zili ndi zotsatirapo zake. Njira imeneyo ndi kuyesetsa kukhala mphunzitsi waluso. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mmene mungachitire zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Mayina tawasintha.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Akhristu ali ndi udindo wotani kwa anthu onse?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani ndi mavuto otilepheretsa kugwira ntchito yathu yolalikira?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikwaniritse utumiki umene tinaulandira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 5]

M’pofunika kulimba mtima kuti tilalikire akamatitsutsa

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi mungatani ngati anthu sapezekapezeka pa nyumba m’magawo amene mumalalikira?