Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko

Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko

PAMABUKU anayi a Uthenga Wabwino, buku la Maliko ndi lalifupi kwambiri. Buku limeneli linalembedwa ndi Yohane Maliko patadutsa zaka pafupifupi 30 kuchokera pa imfa ya Yesu Khristu ndi kuuka kwake. Limasimba zinthu zambiri zosangalatsa zimene zinachitika pa zaka zitatu ndi theka za utumiki wa Yesu.

Zikuoneka kuti buku la Maliko linalembedwera anthu amene sanali Ayuda, makamaka Aroma. N’chifukwa chake bukuli pofotokoza za Yesu, limasonyeza kuti iye anali Mwana wa Mulungu wochita zozizwitsa amene anali kugwira ntchito yolalikira mwakhama. Bukuli limatsindika kwambiri zimene Yesu anachita m’malo mwa zimene anaphunzitsa. Kuwerenga Uthenga Wabwino wa Maliko kudzalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Mesiya ndi kutilimbikitsa kukhala achangu muutumiki polalikira uthenga wa Mulungu.​—Aheb. 4:12.

UTUMIKI WAPADERA KU GALILEYA

(Maliko 1:1–9:50)

Atamaliza kufotokoza za ntchito ya Yohane Mbatizi ndi za masiku 40 amene Yesu anakhala m’chipululu m’mavesi 14 okha, Maliko anayamba kufotokoza nkhani yosangalatsa ya utumiki wa Yesu ku Galileya. Anagwiritsa ntchito mawu akuti “nthawi yomweyo” mobwerezabwereza, ndipo zimenezi zimachititsa kuti powerenga munthu aziona kuti nkhaniyo ndi yachangu.​—Maliko 1:10, 12.

Pazaka zosakwana zitatu, Yesu anayenda maulendo atatu okalalikira ku Galileya. Pofotokoza nkhani yakeyo, Maliko anatsatira ndondomeko ya nthawi imene zinthuzo zinali kuchitika. Sanatchule za ulaliki wa paphiri ngakhalenso maulaliki ambiri ataliatali a Yesu.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:15—Kodi “nthawi yoikika” imene inakwaniritsidwa inali ya chiyani? Apa Yesu anali kunena kuti nthawi yoikika yakwana yakuti ayambe utumiki wake. Popeza kuti iye anali pomwepo monga Mfumu yosankhidwiratu, Ufumu wa Mulungu unali utayandikira. Choncho anthu amtima woongoka akanatha kulabadira ulaliki wake ndi kuchita zinthu zonse zofunika kuti Mulungu awayanje.

1:44; 3:12; 7:36—N’chifukwa chiyani Yesu sanafune kuti anthu afalitse zozizwitsa zimene anachita? Yesu sanafune kuti anthu amukhulupirire atamva malipoti okokomeza kapenanso opotoza mfundo zake, koma anafuna kuti iwo adzionere okha kuti iye ndi Khristu ndi kusankha chochita malinga ndi umboni. (Yes. 42:1-4; Mat. 8:4; 9:30; 12:15-21; 16:20; Luka 5:14) Nkhani yokhudza munthu amene kale anali ndi ziwanda m’dziko la Agerasa inali yosiyana ndi zimenezi. Yesu anauza munthuyo kupita kwawo ndi kukauza achibale ake zonse zimene zinachitika. Anthu akumeneko anali atauza Yesu kuchoka m’deralo, choncho panalibe mpata wakuti iye angaonane ndi anthuwo. Kukhalapo kwa munthu amene Yesu anamuchiritsa ndiponso umboni umene munthuyo akanapereka, zikanathandiza kutsutsa nkhani zoipa zokhudza kuwonongeka kwa nkhumba.​—Maliko 5:1-20; Luka 8:26-39.

2:28—N’chifukwa chiyani Yesu akutchedwa “Mbuye wa sabata”? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilamulo chili ndi mthunzi chabe wa zinthu zabwino zimene zikubwera.” (Aheb. 10:1) Malinga ndi Chilamulo, Sabata inali kukhalako patadutsa masiku 6 amene anthu anali kugwira ntchito, ndipo Yesu anachiritsa anthu ambiri patsikulo. Zimenezi zinaimira mtendere, mpumulo ndi madalitso ena amene anthu adzakhala nawo mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu umene udzayamba utatha ulamuliro wopondereza wa Satana. Choncho, Mfumu ya Ufumuwo ndiyenso “Mbuye wa sabata.”​—Mat. 12:8; Luka 6:5.

3:5; 7:34; 8:12—Kodi zinatheka bwanji Maliko kudziwa mmene Yesu anamvera? Maliko sanali mmodzi wa atumwi 12 komanso sanali mnzake wapamtima wa Yesu. Mbiri yakale imanena kuti mtumwi Petulo, yemwe anali mnzake wapamtima wa Maliko, ndi amene anauza Maliko zambiri zokhudza Yesu.​—1 Pet. 5:13.

6:51, 52—Kodi “tanthauzo la mitanda ya mkate,” limene ophunzira sanamvetse linali lotani? Maola angapo izi zisanachitike, Yesu anali atadyetsa anthu 5,000, osaphatikizapo akazi ndi ana, mikate isanu ndi nsomba ziwiri. “Tanthauzo la mitanda ya mkate,” limene ophunzira anayenera kumvetsa zitachitika zimenezo, linali lakuti Yehova Mulungu anali atapatsa Yesu mphamvu yochita zozizwitsa. (Maliko 6:41-44) Akanakhala kuti anazindikira kuchuluka kwa mphamvu zimene Yesu anapatsidwa, sakanadabwa kwambiri pamene Yesu anayenda pa madzi mozizwitsa.

8:22-26—N’chifukwa chiyani Yesu anachita zinthu ziwiri pochiritsa munthu wakhungu? Yesu ayenera kuti anachita zimenezi pochita chifundo ndi munthuyo. Kuchiritsa mwapang’onopang’ono munthu amene anali wosaona kwa nthawi yaitali, kukanathandiza munthuyo kuti azolowere kuwala kwa dzuwa.

Zimene Tikuphunzirapo:

2:18; 7:11; 12:18; 13:3. Maliko anafotokoza miyambo, mawu, zikhulupiriro, ndi malo amene ayenera kuti anali osadziwika kwa anthu omwe sanali Ayuda. Ananena momveka bwino kuti Afarisi “anali kusala kudya,” khobani inali “mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,” Asaduki “amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa” ndiponso kuti kachisi anali ‘kuonekera bwino m’Phiri la Maolivi.’ Popeza kuti Ayuda ndi amene anali kufuna kudziwa mzera wobadwira wa Mesiya, iye sanalembe za zimenezo. Apa Maliko akutipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Tiyenera kuganizira zimene omvera athu akudziwa kale tikakhala muutumiki wachikhristu kapena pokamba nkhani pa misonkhano ya mpingo.

3:21. Achibale a Yesu anali osakhulupirira. N’chifukwa chake iye amamvetsa ndiponso kuchitira chifundo anthu amene amatsutsidwa kapena kunyozedwa ndi achibale osakhulupirira chifukwa cha chipembedzo chawo.

3:31-35. Paubatizo wake, Yesu anakhala Mwana wauzimu wa Mulungu, ndipo “Yerusalemu wam’mwambamwamba” anali mayi ake. (Agal. 4:26) Kuchokera pamenepo, Yesu anali kukonda kwambiri ophuzira ake kuposa achibale ake. Zimenezi zikutiphunzitsa kuti tiziika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wathu.​—Mat. 12:46-50; Luka 8:19-21.

8:32-34. Tiyenera kuzindikira mwamsanga ndi kukana kukoma mtima kolakwika kumene anthu ena angatisonyeze. Munthu wotsatira Khristu ayenera kukhala wokonzeka ‘kudzikana yekha,’ kutanthauza kuti ayenera kukana zilakolako kapena zolinga zake zadyera. Azikhala wokonzeka “kunyamula mtengo wake wozunzikirapo,” kutanthauza kuvutika, ngati zingafunike kutero, kapena kuchititsidwa manyazi, kuzunzidwa ngakhale kuphedwa kumene chifukwa chokhala Mkhristu. Ndipo ayenera ‘kutsatira Yesu mosalekeza,’ kutanthauza kukhala ndi moyo motsanzira Yesu. Kukhala wophunzira kumafuna kuti tikhale ndi mtima wodzimana umene Khristu Yesu anali nawo.​—Mat. 16:21-25; Luka 9:22, 23.

9:24. Tisachite manyazi kuuza ena za chikhulupiriro chathu kapena kupempherera chikhulupiriro chowonjezereka.​—Luka 17:5.

MWEZI WOMALIZA

(Maliko 10:1–16:8)

Chakumapeto kwa 32 C.E., Yesu anafika ku “madera a ku malire kwa Yudeya kutsidya la Yorodano,” ndipo khamu la anthu linasonkhananso kwa iye. (Maliko 10:1) Atalalikira kumeneko, anapita ku Yerusalemu.

Pa Nisani 8, Yesu anali ku Betaniya. Atakhala pa chakudya, kunabwera mkazi wina amene anathira mafuta onunkhira pamutu pake. Maliko anafotokoza zochitikazo kuyambira pamene Yesu analowa ndi chikondwerero mu Yerusalemu mpaka kuuka kwake malinga ndi ndondomeko ya nthawi imene zinachitika.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

10:17, 18—N’chifukwa chiyani Yesu anawongolera munthu amene anatcha Yesuyo kuti “Mphunzitsi Wabwino”? Mwa kukana dzina laulemu lomugomera limeneli, Yesu anapereka ulemerero kwa Yehova ndipo anasonyeza kuti Mulungu woona ndiye gwero la zabwino zonse. Ndiponso Yesu anasonyeza mfundo yofunika kwambiri ya choonadi yakuti Yehova Mulungu, Mlengi wa zonse, ndiye yekha amene ali ndi udindo wokhazikitsa mfundo zosonyeza chabwino ndi choipa.​—Mat. 19:16, 17; Luka 18:18, 19.

14:25—Kodi Yesu anatanthauza chiyani pamene anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mpesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu”? Yesu sanali kunena kuti kumwamba kuli vinyo. Koma popeza kuti vinyo nthawi zina amaimira chisangalalo, Yesu anali kunena za chisangalalo chimene adzakhala nacho mu Ufumuwo limodzi ndi otsatira ake odzozedwa akaukitsidwa.​—Sal. 104:15; Mat. 26:29.

14:51, 52—Kodi mnyamata amene ‘anathawa wamaliseche’ anali ndani? Maliko yekha ndi amene amatchula za nkhani imeneyi, choncho tingathe kunena kuti anali kunena za iye mwini.

15:34—Kodi mawu a Yesu akuti “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” akusonyeza kuti iye analibe chikhulupiriro? Ayi. Ngakhale sitikudziwa cholinga cha Yesu ponena zimenezi, mawu akewo angasonyeze kuti Yesu anazindikira kuti Yehova anali atasiya kumuteteza kuti kukhulupirika kwa Mwana wakeyo kuyesedwe mokwanira. N’zothekanso kuti Yesu ananena zimenezi chifukwa chofuna kukwaniritsa zimene lemba la Salmo 22:1 linalosera za iye.​—Mat. 27:46.

Zimene Tikuphunzirapo:

10:6-9. Cholinga cha Mulungu ndi chakuti ukwati usamathe. Choncho, m’malo mothamangira kusudzulana, mwamuna ndi mkazi wake ayenera kuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti athetse mavuto alionse m’banja mwawo.​—Mat. 19:4-6.

12:41-44. Chitsanzo cha mkazi wamasiye chikutiphunzitsa kuti tiyenera kuchirikiza kulambira koona mosaumira.

[Chithunzi patsamba 29]

N’chifukwa chiyani Yesu anauza mwamunayu kuti akauze achibale ake zonse zimene zinamuchitikira?