Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Titengerepo Phunziro Pazolakwa za Aisiraeli

Titengerepo Phunziro Pazolakwa za Aisiraeli

Titengerepo Phunziro Pazolakwa za Aisiraeli

AISIRAELI anali kudziwa zimene Yehova an’kafuna kuti iwo achite pamene anali kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Kudzera mwa Mose, Mulungu anali atawalamula kuti: “Mupitikitse onse okhala m’dziko pamaso panu, ndi kuwononga mafano awo onse a miyala, ndi kuwononga mafano awo onse oyenga, ndi kupasula misanje yawo yonse.”​—Num. 33:52.

Aisiraeli sanayenere kuchita pangano ndi nzika za dzikolo, kapena kukwatirana nawo. (Deut. 7:2, 3) Anthu a Mulungu anachenjezedwa mwamphamvu kuti: “Dzichenjere ungachite pangano ndi anthu a ku dziko limene umukako, lingakhale msampha pakati panu.” (Eks. 34:12) Ngakhale ndi choncho, Aisiraeli sanamvere Mulungu ndipo anakodwa mu msampha umenewu. Kodi chinachitika ndi chiyani kuti iwo agwe? Kodi tikupezapo chenjezo lotani pa zimene zinawachitikira?​—1 Akor. 10:11.

Anayamba ndi Kucheza Kenako Kupembedza Mafano

Polanda Dziko Lolonjezedwa, Aisiraeli poyamba anali kugonjetsa nzika za dzikolo. Koma ana a Isiraeli analephera kumverabe malamulo a Mulungu. Sanapitikitse adani awo m’dzikolo. (Ower. 1:1–2:10) M’malo mwake, Aisiraeliwo anayamba kukhala pakati pa “mitundu isanu ndi iwiri” imene inali m’dzikolo. Ndipo chifukwa chochita zinthu nthawi ndi nthawi ndi anthu a mitunduyo, iwo anakhala mabwenzi awo. (Deut. 7:1) Kodi zimenezi zinawakhudza motani Aisiraeliwo? Baibulo limati: “[A]nakwatira ana aakazi a iwowa, napereka ana awo aakazi kwa ana aamuna a iwowa natumikira milungu yawo. Ndipo ana a Israyeli anachita choipa pamaso pa Yehova, naiwala Yehova Mulungu wawo, natumikira Abaala ndi zifanizo.” (Ower. 3:5-7) Chifukwa chocheza ndi nzika za dzikolo, Aisiraeli anayamba kukwatirana nawo ndi kupembedza mafano. Atangoyamba kukwatirana, basi zinakhala zosatheka kuti Aisiraeliwo apitikitse anthu akunjawo m’dzikolo. Kulambira koona kunaipitsidwa ndipo Aisiraeli anayamba kulambira milungu yonyenga.

Nzika za Dziko Lolonjezedwa zitakhala mabwenzi awo, zinakhala zoopsa kwambiri chifukwa zikanatha kusokoneza moyo wauzimu wa Aisiraeli kuposa nthawi imene zinali adani awo. Tiyeni tikambirane njira ina imenenso mwina inaipitsa chipembedzo cha Aisiraeli.

Atayamba Ulimi Anayambanso Kupembedza Baala

Atalowa m’Dziko Lolonjezedwa, ana a Isiraeli anasiya moyo woyendayenda ndipo ambiri anakhala alimi. Ulimi umene iwo anayamba uyenera kuti unali wofanana ndi wa anthu amene anali kale m’dzikolo. Zikuoneka kuti chifukwa cha kusintha kumeneku, iwo sanangotengera ulimi wa Akanani. Chifukwa choyanjana ndi anthuwo, Aisiraeli anakopeka mpaka anatengeranso kapembedzedwe kawo kokhudzana ndi zaulimi.

Akanani anali kulambira Abaala ambiri ndipo anali kukhulupirira kuti milunguyo inali kuwonjezera chonde m’nthaka. Kuwonjezera pa kulima nthakayo ndi kukolola, Aisiraeli anayambanso kulemekeza milungu ya Akanani poganiza kuti imapatsa zokolola zambiri. Choncho Aisiraeli ambiri anali kuoneka ngati akulambira Yehova, koma zenizeni zinali zakuti anali atayamba mpatuko woipa kwambiri.

Chenjezo Lamphamvu kwa Ife Masiku Ano

Pamene Aisiraeli anayamba kuchita zinthu ndi anthu a m’Dziko Lolonjezedwa, sikuti cholinga chawo chinali kuyamba kulambira Baala ndi kutengera khalidwe lawo loipa. Koma izi ndi zimene zinachitika chifukwa cha mayanjano awo. Ngati ife ticheza ndi anthu amene ndi aubwenzi koma si Akhristu anzathu ndipo amayendera mfundo zawo, kodi sitingakumanenso ndi mavuto ofanana ndi amenewa? Apa sitikunena kuti tisachite zinthu zina zofunika ndi anthu osakhulupirira kaya ndi kuntchito, kusukulu, kapena ngakhale panyumba. Koma zimene zinachitikira Aisiraeli ndi chenjezo kwa ife kuti kukhala ndi mtima wokonda kuyanjana ndi anthu otero, ndi kuitana dala mavuto. Baibulo limanena mfundo yosatsutsika yakuti: “Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.”​—1 Akor. 15:33.

Masiku ano, timakumana ndi ziyeso zofanana ndi zimene Aisiraeli anakumana nazo. M’dziko lamakonoli, anthu ali ndi milungu yawo. Milungu imeneyi ndi monga ndalama, akatswiri a zosangalatsa ndi a masewero, ndale, atsogoleri ena a zipembedzo ndipo mwinanso achibale. N’zotheka kukondetsa zinthu zimenezi kapena anthu amenewa pamoyo wathu ndi kumalamulidwa nawo. Kukhala mabwenzi apamtima a anthu amene sakonda Yehova kungatipweteke mwauzimu.

Kupembedza Baala kunaphatikizapo kuchita chiwerewere ndipo Aisiraeli ambiri anakopeka nacho. Misampha yotereyi ikukolanso anthu ena a Mulungu masiku ano. Mwachitsanzo, munthu amene ali ndi mtima wakuti bwanji ndione kapena wachibwana, angawononge chikumbumtima chake chabwino mwa kungodina timabatani pakompyuta ali m’nyumba kwa yekha. Zingakhale zachisoni ngati Mkhristu angakopeke ndi zolaula za pa Intaneti.

“Odala Iwo Akusunga Mboni Zake”

Pankhani ya mayanjano, munthu aliyense ayenera kusankha yekha kumvera kapena kusamvera Yehova. (Deut. 30:19, 20) Choncho, ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimacheza ndi anthu otani panthawi yosangalala? Kodi anthuwo amayendera mfundo zotani ndipo makhalidwe awo ndi otani? Kodi amalambira Yehova? Kodi kucheza nawo kudzandithandiza kukhala Mkhristu wabwino?’

Wamasalmo anaimba kuti: “Odala angwiro m’mayendedwe awo, akuyenda m’chilamulo cha Yehova. Odala iwo akusunga mboni zake, akumufuna ndi mtima wonse.” (Sal. 119:1, 2) Zoonadi, “wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.” (Sal. 128:1) Pankhani yosankha mabwenzi, tiyeni titengerepo phunziro pazolakwa za Aisiraeli ndipo tizimvera Yehova ndi mtima wonse.​—Miy. 13:20.

[Chithunzi patsamba 26]

Tingayambe kupembedza mafano chifukwa chocheza ndi anthu amene sakonda Yehova