Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yendani M’njira za Yehova

Yendani M’njira za Yehova

Yendani M’njira za Yehova

“Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.”​—SAL. 128:1.

1, 2. Kodi tikudziwa bwanji kuti munthu atha kukhala wosangalala?

ALIYENSE amafuna kukhala wodala, kapena kuti wosangalala. Ngakhale zili choncho, inu mosakayika mukudziwa kuti tikamangolakalaka kapena kufunafuna chisangalalo sindiye kuti tikusangalala.

2 Komatu n’zotheka kukhala wosangalala. Lemba la Salmo 128:1 limati: “Wodala yense wakuopa Yehova, wakuyenda m’njira zake.” Timakhala odala, kapena kuti osangalala, ngati tikulambira Mulungu ndi kuyenda m’njira zake mwa kuchita chifuniro chake. Kodi kuchita zimenezi kumakhudza bwanji khalidwe lathu?

Khalani Munthu Wodalirika

3. Ngati ndife munthu wodalirika, kodi tidzatani ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu?

3 Anthu amene amaopa Yehova amakhala odalirika ngati mmene iye alili. Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza Aisiraeli. (1 Maf. 8:56) Kudzipereka kwathu kwa Mulungu ndi lonjezo lofunika kwambiri limene tinachita kuposa lonjezo lina lililonse, ndipo kupemphera nthawi zonse kumatithandiza kulisunga. Tingapemphere ngati mmene wamasalmo Davide anachitira. Iye anati: “Mulungu, mudamva zowinda zanga . . . Ndidzaimba zolemekeza dzina lanu ku nthawi zonse, kuti ndichite zowinda zanga tsiku ndi tsiku.” (Sal. 61:5, 8; Mlal. 5:4-6) Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera kukhala anthu odalirika.​—Sal. 15:1, 4.

4. Kodi Yefita ndi mwana wake wamkazi anachita chiyani mogwirizana ndi chowinda chimene iye anachita kwa Yehova?

4 M’masiku a Oweruza m’Isiraeli, Yefita anawinda kuti Yehova akamuthandiza kugonjetsa Aamoni, adzapereka munthu woyamba kukumana naye akamachokera ku nkhondo ngati “nsembe yopsereza.” Munthuyo anapezeka kuti ndi mwana wake wamkazi, ndipo Yefitayo anali ndi mwana mmodzi yekhayo. Chifukwa chokhulupirira Yehova, Yefita ndi mwana wake wamkazi wosakwatiwayo anakwaniritsa chowinda chake. Aisiraeli anali kuona ukwati ndi kubereka ana kukhala zinthu zofunika kwambiri. Ngakhale zinali choncho, mwana wamkazi wa Yefita anasankha kusakwatiwa ndipo anakhala ndi mwayi wochita utumiki wopatulika pachihema cha Yehova.​—Ower. 11:28-40.

5. Kodi Hana anakhala wodalirika pankhani iti?

5 Hana, mkazi woopa Mulungu, anali wodalirika. Iye anali kukhala ku dera lamapiri la Efraimu ndi mwamuna wake Elikana Mlevi ndi mkazi wake wachiwiri, Penina. Penina anali ndi ana angapo ndipo anali kunyodola Hana yemwe anali wosabereka, makamaka akapita ku chihema. Ulendo wina, Hana anawinda kuti akabereka mwana wamwamuna, adzamupereka kwa Yehova. Posapita nthawi, anakhala ndi pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna n’kumupatsa dzina lakuti Samueli. Ataleka kuyamwa, Hana anamupereka kwa Mulungu ku Silo. Inde, anapereka Samueli kwa Yehova “masiku onse a moyo wake.” (1 Sam. 1:11) Mwa kuchita zimenezi, anakwaniritsa chowinda chake ngakhale sanadziwe kuti adzakhalanso ndi ana ena m’tsogolo.​—1 Sam. 2:20, 21.

6. Kodi Tukiko anasonyeza bwanji kuti anali munthu wodalirika?

6 Mkhristu wa m’nthawi ya atumwi dzina lake Tukiko, anali munthu wodalirika ndiponso “mtumiki wokhulupirika.” (Akol. 4:7) Tukiko anayenda ndi mtumwi Paulo kuchokera ku Girisi kudzera ku Makedoniya kupita ku Asia Minor. Ndipo mwina anakafika ku Yerusalemu. (Mac. 20:2-4) N’kutheka kuti iye anali “m’bale” amene anathandiza Tito kusamalira mphatso zokathandizira okhulupirira anzawo amene anali osowa ku Yudeya. (2 Akor. 8:18, 19; 12:18) Ulendo woyamba umene Paulo anali m’ndende ku Roma, anapatsa Tukiko nthumwi yake yodalirika, kalata zopita kwa okhulupirira anzake ku Efeso ndi Kolose. (Aef. 6:21, 22; Akol. 4:8, 9) Ulendo wachiwiri umene Paulo anali m’ndende ku Roma, anatumiza Tukiko ku Efeso. (2 Tim. 4:12) Ngati ndife odalirika, nafenso tidzalandira madalitso potumikira Yehova.

7, 8. N’chifukwa chiyani tikunena kuti Davide ndi Jonatani anali mabwenzi enieni?

7 Mulungu amafuna kuti tikhale mabwenzi odalirika. (Miy. 17:17) Jonatani mwana wa Mfumu Sauli anakhala bwenzi la Davide. Atamva kuti Davide anapha Goliati, “mtima wa Jonatani unalumikizika ndi mtima wa Davide, ndipo Jonatani anam’konda iye monga moyo wa iye yekha.” (1 Sam. 18:1, 3) Jonatani anachenjezanso Davide pamene Sauli anafuna kumupha. Davide atathawa, Jonatani anakakumana naye ndi kuchita pangano. Iye anatsala pang’ono kutaya moyo wake chifukwa cholankhula za Davide kwa Sauli. Ngakhale ndi choncho, anthu awiriwa anakumananso ndi kulimbitsa ubwenzi wawo. (1 Sam. 20:24-41) Ulendo womaliza umene anakumana, Jonatani analimbitsa dzanja la Davide “mwa Mulungu.”​—1 Sam. 23:16-18.

8 Jonatani anafera ku nkhondo polimbana ndi Afilisti. (1 Sam. 31:6) Poimba nyimbo ya maliro, Davide anati: “Ndipsinjika mtima chifukwa cha iwe, m’bale wanga Jonatani; wandikomera kwambiri; chikondi chako, ndinadabwa nacho, chinaposa chikondi cha anthu aakazi.” (2 Sam. 1:26) Umu ndi mmene mabwenzi enieni amakonderana. Zoonadi, Davide ndi Jonatani anali mabwenzi enieni.

Khalani ndi “Maganizo Odzichepetsa” Nthawi Zonse

9. Kodi lemba la Oweruza chaputala 9 likusonyeza bwanji kufunika kwa kudzichepetsa?

9 Kuti tikhale mabwenzi a Mulungu, tiyenera kukhala ndi “maganizo odzichepetsa.” (1 Pet. 3:8; Sal. 138:6) Lemba la Oweruza chaputala 9 limasonyeza kufunika kwa kudzichepetsa. Yotamu mwana wa Gideoni anati: “Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu.” Anatchula mtengo wa azitona, wa mkuyu ndi wa mpesa. Mitengo imeneyi inaimira anthu oyenerera amene sanafune kulamulira Aisiraeli anzawo. Koma mtengo wa mkandankhuku, umene unali kugwira ntchito monga nkhuni basi, unaimira ufumu wa Abimeleki wodzikuza amene anali munthu wambanda ndi wokonda kupondereza ena. Ngakhale kuti iye ‘anakhala kalonga wa Isiraeli zaka zitatu,’ anafa imfa yosayembekezereka. (Ower. 9:8-15, 22, 50-54) Choncho ndi bwino kukhala ndi “maganizo odzichepetsa.”

10. Kodi nkhani ya Herode yolephera ‘kupereka ulemerero kwa Mulungu,’ yakuphunzitsani chiyani?

10 M’nthawi ya atumwi, panali kusamvana pakati pa Mfumu Herode Agripa yodzikuza ya ku Yudeya ndi nzika za ku Turo ndi Sidoni. Nzikazi zinafuna kupempha mtendere kwa iye. Tsiku lina Herode akulankhula ndi anthu, iwo anafuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu ayi!” Herode sanatsutse mawu omutamanda amenewa, ndipo mngelo wa Yehova anamukantha. Iye anafa imfa yoipa “chifukwa ulemererowo sanaupereke kwa Mulungu.” (Mac. 12:20-23) Mwina ife tingakhale ndi luso lokamba nkhani kapena lophunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Ngati ndi choncho, tizilemekeza Mulungu chifukwa cha zimene watilola kuchita.​—1 Akor. 4:6, 7; Yak. 4:6.

Khalani Olimba Mtima ndi Amphamvu

11, 12. Kodi nkhani ya Enoke ikusonyeza bwanji kuti Yehova amathandiza atumiki ake kukhala olimba mtima ndi amphamvu?

11 Tikamayenda m’njira za Yehova modzichepetsa, iye adzatithandiza kukhala olimba mtima ndi amphamvu. (Deut. 31:6-8, 23) Enoke, amene anali munthu wa chi 7 pamzera wa makolo kuchokera pa Adamu, anayenda ndi Mulungu molimba mtima mwa kukhala ndi moyo wolungama pakati pa anthu oipa. (Gen. 5:21-24) Yehova anapatsa Enoke mphamvu yolengeza uthenga wachiweruzo kwa anthuwo chifukwa cha mawu awo onyoza ndi ntchito zawo zoipa. (Werengani Yuda 14, 15.) Kodi inu ndinu wolimba mtima? Kulengeza ziweruzo za Mulungu kumafuna kulimba mtima.

12 Yehova anaweruza anthu oipawo pa Chigumula chapadziko lonse cha m’masiku a Nowa. Ulosi wa Enoke umatilimbikitsanso ife, chifukwa chakuti anthu oipa a masiku ano adzawonongedwa posachedwapa ndi zikwizikwi za oyera a Mulungu. (Chiv. 16:14-16; 19:11-16) Poyankha mapemphero athu, Yehova amatithandiza kukhala olimba mtima kuti tilengeze uthenga wake, kaya uthengawo ndi wa ziweruzo zake kapena wa madalitso a Ufumu wake.

13. N’chifukwa chiyani tili ndi chikhulupiriro chakuti Mulungu angatithandize kukhala olimba mtima ndi amphamvu kuti tipirire mavuto?

13 Timafunikira kulimba mtima ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu kuti tipirire mavuto. Esau atakwatira akazi awiri Ahiti, ‘iwo anapweteka mtima wa [makolo ake] Isake ndi Rebeka.’ Mpaka Rebeka anadandaula kuti: “Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Heti: [Yakobo mwana wathu akatenga] mkazi wa ana aakazi a Heti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?” (Gen. 26:34, 35; 27:46) Isake sanalekerere nkhaniyo koma anatumiza Yakobo kukapeza mkazi pakati pa anthu olambira Yehova. Ngakhale kuti Isake ndi Rebeka sakanasintha zimene Esau anachita, Mulungu anawapatsa nzeru ndi mphamvu ndipo anawathandiza kulimba mtima kuti akhalebe okhulupirika kwa iye. Ngati tipempha Yehova kuti atithandize, iye adzachitanso chimodzimodzi.​—Sal. 118:5.

14. Kodi mtsikana wamng’ono wa ku Isiraeli anasonyeza motani kulimba mtima?

14 Patadutsa zaka zambiri, mtsikana wamng’ono wa ku Isiraeli anagwidwa ndi achifwamba ndipo anakhala mdzakazi m’nyumba ya Namani, kazembe wa khamu la nkhondo la Aramu. Kazembeyu anali ndi khate. Podziwa za zozizwitsa zimene Mulungu anachita kudzera mwa mneneri Elisa, mtsikanayo molimba mtima anauza mkazi wa Namani kuti: ‘Mbuye wanga akanapita ku Isiraeli, mneneri wa Yehova akanam’chiritsa khate lake.’ Namani anapitadi ku Isiraeli ndipo anachiritsidwa mozizwitsa. (2 Maf. 5:1-3) Mtsikana ameneyu ndi chitsanzo chabwino kwa achinyamata amene amadalira Yehova kuti awathandize kukhala olimba mtima ndi kulalikira aphunzitsi, anzawo a kusukulu ndi anthu ena.

15. Kodi Obadiya, mdindo wa nyumba ya Ahabu, anachita chiyani molimba mtima?

15 Kulimba mtima kumene timakhala nako chifukwa cha Mulungu kumatithandiza kupirira chizunzo. Taganizirani za Obadiya, mdindo wa nyumba ya Mfumu Ahabu. Iye anakhalako m’nthawi ya mneneri Eliya. Mfumukazi Yezebeli atalamula kuti aneneri a Mulungu aphedwe, Obadiya anabisa aneneri 100 m’magulu a “makumi asanuasanu m’phanga.” (1 Maf. 18:13; 19:18) Kodi inu mungalimbe mtima ndi kuthandiza Akhristu anzanu amene akuzunzidwa, ngati mmene Obadiya anathandizira aneneri a Yehova?

16, 17. Kodi Arisitako ndi Gayo anachita chiyani atakumana ndi chizunzo?

16 Ngati tikuzunzidwa, tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova adzatithandiza. (Aroma 8:35-39) M’bwalo la masewera ku Efeso, Arisitako ndi Gayo, antchito anzake a Paulo, anayang’anizana ndi chipwirikiti cha khamu la anthu masauzande angapo. Amene anayambitsa chipwirikiticho anali Demetiriyo wapachipala wosula siliva. Iye ndi amisiri anzake anali ndi malonda opanga ndi kugulitsa tiakachisi tasiliva ta mulungu wamkazi Atemi. Iwo anaona kuti malonda awo alowa pansi chifukwa chakuti anthu ambiri mumzindawo anasiya kupembedza mafano atalalikidwa ndi Paulo. Khamulo linagwira Arisitako ndi Gayo n’kuwakokera ku bwalo la masewera ndipo linali kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi wa Aefeso!” Apa Arisitako ndi Gayo ayenera kuti anaganiza kuti afa basi, koma woyang’anira mzinda anathetsa chipwirikiticho.​—Mac. 19:23-41.

17 Mukanakhala inuyo, kodi mukanachita mantha n’kuyesa kufuna moyo wopanda mavuto? Palibe umboni wosonyeza kuti Arisitako kapena Gayo anasiya kulimba mtima. Popeza kuti Arisitako anali wa ku Tesalonika, anali kudziwa kuti kulalikira uthenga wabwino kungayambitse chizunzo. Nthawi ina m’mbuyomo Paulo atalalikira ku Tesalonika, kunabuka chisokonezo. (Mac. 17:5; 20:4) Popeza kuti Arisitako ndi Gayo anayenda m’njira za Yehova, anapirira chizunzo chifukwa cha mphamvu ndi kulimba mtima zochokera kwa Mulungu.

Samalani Zofuna za Ena

18. Kodi Purisikila ndi Akula ‘anasamala’ zofuna za ena m’njira yotani?

18 Kaya panopa tikuzunzidwa kapena ayi, tiyenera kusamala za Akhristu anzathu. Purisikila ndi Akula ‘anasamala’ zofuna za ena. (Werengani Afilipi 2:4.) Banja lochita bwino limeneli liyenera kuti linapatsa Paulo malo ku Efeso, kumene Demetiriyo wapachipala wosula siliva anayambitsa chipwirikiti takambirana chija. Mwina chifukwa cha zochitika zimenezo, Akula ndi Purisikila “anaika moyo wawo pachiswe” kuti athandize Paulo. (Aroma 16:3, 4; 2 Akor. 1:8) Masiku ano kukonda abale athu amene akuzunzidwa kumatichititsa kukhala “ochenjera ngati njoka.” (Mat. 10:16-18) Timapitiriza ntchito yathu mochenjera ndipo sitipereka mayina a abale athu kapena kuulula zinthu zina kwa anthu ozunza.

19. Kodi ndi zinthu zabwino zotani zimene Dorika anachitira anthu ena?

19 Kusamala zofuna za ena kumachitika m’njira zosiyanasiyana. Akhristu anzathu angakhale ndi zosowa, ndipo ife tingawathandize kupeza zimene akusowazo. (Aef. 4:28; Yak. 2:14-17) Mumpingo wa m’nthawi ya atumwi ku Yopa, munali mayi wina woolowa manja dzina lake Dorika. (Werengani Machitidwe 9:36-42.) Dorika “anali kuchita ntchito zabwino zambiri, ndi kupereka mphatso za chifundo zochuluka” zimene mwachionekere zinaphatikizapo kusokera zovala akazi amasiye. Dorika atamwalira mu 36 C.E., akazi amasiye anali ndi chisoni chachikulu. Mulungu anagwiritsa ntchito Petulo kuukitsa Dorika, ndipo mayiyu ayenera kuti analalikira uthenga wabwino mosangalala ndi kuchitira ena zinthu zabwino pamoyo wake wonse padziko lapansi. Ndife osangalala kuti masiku ano tili ndi akazi achikhristu odzimana ngati Dorika.

20, 21. (a) Kodi munthu wosamala zofuna za ena amachita chiyani? (b) Kodi mungalimbikitse ena pochita chiyani?

20 Timasamala zofuna za ena mwa kuwalimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Sila, wantchito mnzake wa Paulo, anali munthu wolimbikitsa kwambiri. Nkhani ya mdulidwe itagamulidwa cha mu 49 C.E., bungwe lolamulira ku Yerusalemu linatumiza nthumwi kukapereka kalata kwa okhulupirira anzawo a kumadera ena. Sila, Yudasi, Baranaba ndi Paulo anapita ndi kalatayo ku Antiokeya. Kumeneko Sila ndi Yudasi “analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndi kuwapatsa mphamvu.”​—Mac. 15:32.

21 Pambuyo pake, Paulo ndi Sila anaponyedwa m’ndende ku Filipi koma anamasulidwa kutachitika chivomezi. Iwo anasangalala kuchitira umboni ndiponso kuona woyang’anira ndende ndi banja lake atakhala okhulupirira. Asanachoke mu mzindawo, Sila ndi Paulo analimbikitsa abale. (Mac. 16:12, 40) Mofanana ndi Paulo ndi Sila, yesetsani kulimbikitsa ena popereka ndemanga, pokamba nkhani ndi pochita utumiki wa kumunda mwachangu. Ndipo mukakhala ndi “mawu alionse olimbikitsa nawo anthu, alankhuleni.”​—Mac. 13:15.

Pitirizani Kuyenda M’njira za Yehova

22, 23. Kodi tingachite chiyani kuti tipindule kwambiri ndi nkhani zolembedwa m’Baibulo?

22 Ndife osangalala kwambiri ndi nkhani zochitikadi zimene zalembedwa m’Mawu a Yehova, “Mulungu wa chilimbikitso chonse.” (2 Akor. 1:3, Byington) Kuti tipindule ndi nkhani zimenezi, tifunika kutsatira mfundo zimene Baibulo limaphunzitsa pamoyo wathu ndiponso kulola mzimu woyera wa Mulungu kuti uzititsogolera.​—Agal. 5:22-25.

23 Kusinkhasinkha nkhani za m’Baibulo kumatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Kumalimbitsa ubale wathu ndi Yehova amene amatipatsa “nzeru ndi chidziwitso ndi chimwemwe.” (Mlal. 2:26) Ndipo tidzakondweretsa mtima wa Mulungu wathu wachikondi. (Miy. 27:11) Tiyeni tilimbikire kuchita zimenezi mwa kupitiriza kuyenda m’njira za Yehova.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi muyenera kuchita chiyani kusonyeza kuti ndinu wodalirika?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi “maganizo odzichepetsa”?

• Kodi nkhani za m’Baibulo zingatithandize bwanji kukhala olimba mtima?

• Kodi tingasamale zofuna za ena m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Yefita ndi mwana wake wamkazi anali anthu odalirika ndipo anakwaniritsa chowinda chake ngakhale kuti kuchita zimenezo kunali kovuta

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi achinyamata mwaphunzira zotani pankhani ya mtsikana wa ku Isiraeli?

[Chithunzi patsamba 11]

Kodi Dorika anathandiza bwanji Akhristu osowa?