Zamkatimu
Zamkatimu
February 15, 2008
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MLUNGU WA:
March 17-23, 2008
Ikani Yehova Patsogolo Panu Nthawi Zonse
TSAMBA 3
NYIMBO ZOIMBA: 37, 26
March 24-30, 2008
TSAMBA 7
NYIMBO ZOIMBA: 138, 57
March 31, 2008–April 6, 2008
Yesu Khristu—Mmishonale Woposa Amishonale Onse
TSAMBA 12
NYIMBO ZOIMBA: 172, 72
April 7-13, 2008
Tsanzirani Mmishonale Woposa Amishonale Onse
TSAMBA 16
NYIMBO ZOIMBA: 211, 209
April 14-20, 2008
Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?
TSAMBA 21
NYIMBO ZOIMBA: 168, 21
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
Nkhani Zophunzira 1, 2 MASAMBA 3-11
Tikamasinkhasinkha nkhani za m’Baibulo, chikhulupiriro chathu chimalimba. Tikamaika Yehova patsogolo pathu, iye amayankha mapemphero athu. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kumvera Mulungu ndi kumukhulupirira nthawi zonse. Tikamayenda m’njira zake, tidzakhala anthu odalirika, odzichepetsa, olimba mtima ndi osamala zofuna za ena.
Nkhani Zophunzira 3, 4 MASAMBA 12-20
Yesu Khristu anali Mmishonale woposa amishonale onse. Dziwani mmene iye anaphunzitsidwira, mmene anali kuphunzitsira ndi chifukwa chimene anthu anali kumukondera. Werengani zimene tiyenera kuchita kuti titsanzire Yesu ndi kuphunzitsa mogwira mtima anthu amene timawalalikira uthenga wabwino.
Nkhani Zophunzira 5 MASAMBA 21-25
Dziwani chifukwa chimene tinganenere kuti nthawi ya kukhalapo kwa Khristu ndi yaitali. Fufuzani umboni wa m’Malemba wotithandiza kudziwa anthu a “m’badwo uwu,” umene Yesu anatchula. (Mat. 24:34) Ndipo onani chifukwa chake zilili zosatheka kuwerengetsa zaka za “m’badwo uwu.”
M’MAGAZINI INO MULINSO:
Titengerepo Phunziro Pazolakwa za Aisiraeli
TSAMBA 26
Mawu a Yehova Ndi Amoyo—Mfundo Zazikulu za M’buku la Maliko
TSAMBA 28
Omaliza Maphunziro a Gileadi Akulimbikitsidwa Kuti “Ayambe Kukumba”
TSAMBA 31