Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Ololera Koma Mosapitirira Malire

Khalani Ololera Koma Mosapitirira Malire

Khalani Ololera Koma Mosapitirira Malire

“Pitiriza kuwakumbutsa . . . akhale ololera.”​—TITO 3:1, 2.

1, 2. Kodi Malemba amati chiyani pankhani ya kulolera, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenera?

YEHOVA, Atate wathu wachikondi wa kumwamba, ali ndi nzeru zopanda malire. Popeza ndife zolengedwa zake, timayang’ana kwa iye kuti atitsogolere pamoyo wathu. (Sal. 48:14) Yakobe, wophunzira wachikhristu, amatiuza kuti “nzeru yochokera kumwamba, choyamba, ndi yoyera, kenako yamtendere, yololera, yokonzeka kumvera, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yopanda chinyengo.”​—Yak. 3:17.

2 Paulo analangiza kuti: “Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse.” * (Afil. 4:5) Khristu Yesu ndi Mbuye ndiponso Mutu wa mpingo wachikhristu. (Aef. 5:23) Choncho aliyense wa ife afunika kukhala wololera mwa kugonjera malangizo a Khristu ndiponso pochita zinthu ndi anthu anzathu.

3, 4. (a) Perekani chitsanzo chosonyeza ubwino wa kulolera. (b) Kodi tikambirana chiyani?

3 Kukhala ndi mtima wololera m’njira yoyenera kuli ndi ubwino wake. Mwachitsanzo, atatulukira chiwembu chimene zigawenga zinakonza ku Britain, anthu ambiri oyenda pandege anali okonzeka kutsatira malamulo oletsa kunyamula zinthu zimene anali kuloledwa kunyamula kale. Tikamayendetsa galimoto, timaona kuti ndi bwino kulolera madalaivala ena, makamaka podutsa pa laundabauti. Timachita zimenezi popewa ngozi ndiponso kuti galimoto ziziyenda bwinobwino.

4 Ambirife zimativuta kukhala ololera. Pofuna kuthandizana, tiyeni tikambirane mbali zitatu zokhudza kulolera. Mbali zimenezi ndizo chifukwa chake tiyenera kukhala ololera, mmene timaonera ulamuliro ndiponso kudziwa malire a kulolera kwathu.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhala Ololera?

5. M’Chilamulo cha Mose, kodi n’chiyani chimene chikanalimbikitsa kapolo kusankha kukhalabe ndi mbuye wake?

5 Chitsanzo cha m’nthawi yakale Chikhristu chisanayambe, chimasonyeza chifukwa chabwino chimene tiyenera kukhalira ololera. M’Chilamulo cha Mose, Aheberi amene anali akapolo anayenera kumasulidwa m’chaka cha 7 cha ukapolo wawo kapena m’chaka Choliza Lipenga, malinga ndi chaka chimene chayambirira paziwirizi. Koma munthu anali ndi ufulu wosankha kukhalabe kapolo. (Werengani Eksodo 21:5, 6.) Kodi chikanalimbikitsa kapoloyo kuchita zimenezo n’chiyani? Chikondi ndi chimene chikanalimbikitsa munthu kusankha kukhalabe kapolo, pansi pa ulamuliro wa mbuye wake wabwino.

6. Kodi chikondi chimatithandiza bwanji kukhala ololera?

6 Mofanana ndi zimenezi, chikondi chathu pa Yehova chimatilimbikitsa kupereka moyo wathu kwa iye ndi kukwaniritsa kudzipereka kwathuko. (Aroma 14:7, 8) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.” (1 Yoh. 5:3) Chikondi chimenechi sichisamala zofuna zake zokha ayi. (1 Akor. 13:4, 5) Pochita zinthu ndi anthu anzathu, chikondi chathu pa anansi chimatilimbikitsa kukhala ololera ndi kuika zofuna zawo patsogolo. M’malo mokhala odzikonda, timaganizira zofuna za ena.​—Afil. 2:2, 3.

7. Kodi kukhala ololera kumathandiza bwanji muutumiki wathu?

7 Zolankhula zathu kapena zochita zathu siziyenera kukhumudwitsa ena. (Aef. 4:29) Inde, chikondi chimatilimbikitsa kupewa kuchita chilichonse chimene chingalepheretse anthu amitundu yosiyanasiyana kutumikira Yehova. Zimenezi zimafuna kuti tikhale ololera. Mwachitsanzo, alongo amene ndi amishonale ndipo anazolowera kugwiritsa ntchito zodzoladzola ndi kuvala sokosi zitalizitali zanailoni zogwira thupi, saumirira kuzigwiritsa ntchito m’madera kumene anthu angakhumudwe nazo kapena kukayikira khalidwe lawo.​—1 Akor. 10:31-33.

8. Kodi kukonda kwathu Mulungu kungatithandize bwanji kukhala ngati ‘aang’ono’?

8 Kukonda kwathu Yehova kumatithandiza kuti tisakhale odzikuza. Ophunzira ake atakangana pankhani yakuti wamkulu ndani, Yesu anatenga mwana wamng’ono ndi kumuimiritsa pakati pawo. Kenako anafotokoza kuti: “Aliyense wolandira mwana wamng’ono uyu m’dzina langa walandiranso ine, ndipo aliyense wolandira ine walandiranso amene anandituma ine. Pakuti aliyense wokhala ngati wamng’ono mwa inu nonse ndi amene ali wamkulu.” (Luka 9:48; Maliko 9:36) Mwina ifeyo patokha zimativuta kukhala ngati “wamng’ono.” Chibadwa chathu chopanda ungwiro ndi mtima wokonda kudzikuza zingatisonkhezere kufuna kutchuka, koma kudzichepetsa kungatithandize kukhala ololera.​—Aroma 12:10.

9. Kodi munthu wololera amazindikira chiyani?

9 Munthu wololera amazindikira ulamuliro woikidwa ndi Mulungu. Akhristu onse oona amazindikira mfundo yofunika kwambiri ya umutu. Mtumwi Paulo anafotokoza bwino lomwe mfundo imeneyi kwa Akorinto kuti: “Ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu; ndi mutu wa mkazi ndi mwamuna; ndi mutu wa Khristu ndiye Mulungu.”​—1 Akor. 11:3.

10. Kodi timasonyeza chiyani tikamagonjera ulamuliro wa Yehova?

10 Tikamagonjera ulamuliro wa Mulungu, timasonyeza kuti timamukhulupirira ndi kumudalira monga Atate wathu wachikondi. Iye amaona zonse zimene zimatichitikira ndipo angatipatse mphoto malinga ndi mmene waonera. Kukumbukira mfundo imeneyi kumatithandiza ngati anzathu sakutilemekeza kapena akakwiya n’kusaugwira mtima. Paulo analemba kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.” Ndiyeno potsindika uphunguwo, Paulo analangiza kuti: “Okondedwa, musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’”​—Aroma 12:18, 19.

11. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikugonjera umutu wa Khristu?

11 Mumpingo wachikhristu timafunikanso kugonjera ulamuliro woikidwa ndi Mulungu. Buku la Chivumbulutso chaputala 1 limasonyeza Khristu Yesu atagwira m’dzanja lake lamanja “nyenyezi” za mpingo. (Chiv. 1:16, 20) M’lingaliro lina, “nyenyezi” zimenezi zimaimiranso mabungwe a akulu, kapena kuti oyang’anira m’mipingo. Oyang’anira amenewo amagonjera utsogoleri wa Khristu ndipo amatsanzira kukoma mtima kwake pochita zinthu ndi anthu. Onse mumpingo amagonjera dongosolo limene Yesu anakhazikitsa lakuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” azipereka chakudya chauzimu panthawi yake. (Mat. 24:45-47) Ngati ifeyo panopa timaphunzira zinthu zimenezi mwakhama ndi kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzira, timasonyeza kuti tikugonjera umutu wa Khristu, ndipo zimenezi zimalimbikitsa mtendere ndi umodzi.​—Aroma 14:13, 19.

Kulolera Kuli ndi Malire

12. N’chifukwa chiyani kulolera kuli ndi malire?

12 Kukhala ololera sikufuna kuti tinyalanyaze chikhulupiriro chathu kapena mfundo za Mulungu. Kodi Akhristu oyambirira anachita chiyani atalamulidwa ndi atsogoleri achipembedzo kusiya kuphunzitsa m’dzina la Yesu? Petulo ndi atumwi ena molimba mtima anati: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Mac. 4:18-20; 5:28, 29) Masiku ano, akuluakulu a boma akatiletsa kulalikira uthenga wabwino, ifenso sitileka ngakhale kuti timasintha njira zolalikira pofuna kuchita mwanzeru. Akaletsa ulaliki wa nyumba ndi nyumba, ife timapeza njira zina zolankhulirana ndi eninyumba ndi kupitiriza kumvera lamulo la Mulungu. Ndiponso “olamulira aakulu” akaletsa misonkhano yathu, ife timasonkhana mwakabisira m’timagulu ting’onoting’ono.​—Aroma 13:1; Aheb. 10:24, 25.

13. Kodi Yesu ananena chiyani pankhani ya kugonjera anthu audindo?

13 Paulaliki wake wa paphiri, Yesu ananena kuti m’pofunika kugonjera anthu audindo. Iye anati: “Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako am’kati, m’patsenso akunja. Ndipo winawake waudindo akakulamula kumunyamulira katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire makilomita awiri.” (Mat. 5:40, 41) * Mtima woganizira ena ndi wofuna kuwathandiza umatilimbikitsanso kuwachitira zinthu zoposa zimene atipempha.​—1 Akor. 13:5; Tito 3:1, 2.

14. Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kulolera mpatuko?

14 Kukhala ololera sikuyenera kutichititsa kugwirizana ndi ampatuko m’pang’ono pomwe. Tifunika kulimba pankhani imeneyi kuti titeteze chiyero cha choonadi ndi umodzi wa mpingo. Polemba za “abale onyenga,” Paulo anati: “Amenewa sitinawagonjere, ngakhale kwa ola limodzi, kuti inuyo mupitirize kukhala ndi choonadi cha uthenga wabwino.” (Agal. 2:4, 5) Mpatuko suchitikachitika. Koma ukachitika, Akhristu enieni amaima ku mbali ya choonadi mosagwedera.

Oyang’anira Ayenera Kukhala Ololera

15. Kodi oyang’anira achikhristu angakhale bwanji ololera pamsonkhano wawo?

15 Kukhala ndi mtima wololera ndi chimodzi mwa ziyeneretso za anthu amene amaikidwa kukhala oyang’anira. Paulo analemba kuti: “Choncho woyang’anira akhale . . . wololera.” (1 Tim. 3:2, 3) Kukhala ololera kumafunika kwambiri abale oikidwawo akakumana kuti akambirane nkhani zokhudza mpingo. Asanamange mfundo, mkulu aliyense amakhala ndi ufulu wakuti alankhulepo maganizo ake. Ngakhale ndi choncho, si lamulo kuti mpaka mkulu aliyense alankhulepo. Akamakambirana, mkulu wina akhoza kusintha maganizo ake atamva mfundo za m’Malemba zokhudza nkhaniyo zimene akulu anzake atchula. M’malo motsutsa ndi kuumirira maganizo ake, mkulu wokhwima mwauzimu amalolera. Poyamba, iwo angakhale ndi maganizo osiyana, koma kuganizira bwino mfundozo ndi kupemphera kumalimbikitsa umodzi pakati pa akulu odziwa malire awo ndiponso ololera.​—1 Akor. 1:10; Werengani Aefeso 4:1-3.

16. Kodi woyang’anira wachikhristu ayenera kukhala ndi mtima wotani?

16 Pazochita zake zonse, mkulu wachikhristu amayesetsa kulemekeza dongosolo la Mulungu loyendetsera zinthu. Afunika kukhalanso ndi mtima umenewu poweta gulu la nkhosa, chifukwa ungamuthandize kukhala woganizira ena ndi wachifundo. Petulo analemba kuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe anakuikizani, osati mokakamizika, koma mwaufulu; osatinso chifukwa chofuna kupindulapo, koma ndi mtima wonse.”​—1 Pet. 5:2.

17. Kodi onse mumpingo angasonyeze bwanji mtima wololera pochita zinthu ndi ena?

17 Mumpingo, okalamba amayamikira thandizo limene ocheperapo msinkhu amapereka kwa iwo ndipo amawalemekeza. Nawonso achinyamata amalemekeza achikulire amene atumikira Yehova kwa zaka zambiri. (1 Tim. 5:1, 2) Akulu achikhristu amafufuza amuna oyenerera kuti awapatse ntchito zina pofuna kuwaphunzitsa kuti athandize kusamalira gulu la nkhosa za Mulungu. (2 Tim. 2:1, 2) Mkhristu aliyense ayenera kutsatira uphungu wouziridwa wa Paulo wakuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankha mlandu. Teroni kuti achite ntchito yawo mwa chimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuwonongani.”​—Aheb. 13:17.

Khalani Ololera M’banja

18. Kodi n’chifukwa chiyani mtima wololera umafunika m’banja?

18 Mtima wololera umafunikanso m’banja. (Werengani Akolose 3:18-21.) Baibulo limafotokoza udindo wa munthu aliyense m’banja lachikhristu. Tate ndiye mutu wa mkazi komanso ndiye ali ndi udindo waukulu wolangiza ana. Mkazi ayenera kuzindikira ulamuliro wa mwamuna wake, ana afunika kuyesetsa kukhala omvera, ndipo zimenezi Ambuye amakondwera nazo. Aliyense m’banja angalimbikitse umodzi ndi mtendere mwa kukhala wololera koma mosapitirira malire. Baibulo lili ndi zitsanzo zothandiza kumveketsa mfundo imeneyi.

19, 20. (a) Kodi chitsanzo cha Eli pankhani ya kukhala wololera chikusiyana bwanji ndi cha Yehova? (b) Kodi makolo angaphunzirepo chiyani pazitsanzo zimenezi?

19 Samueli ali kamnyamata, Eli anali mkulu wa ansembe mu Isiraeli. Komabe, ana aamuna a Eli, Hofeni ndi Pinehasi, anali “oipa” ndipo “sanadziwa Yehova.” Eli anamva mbiri yawo yoipa, kuphatikizapo kuti iwo anali kugonana ndi akazi amene anali kutumikira pa khomo la chihema chokumanako. Kodi Eli anachita chiyani? Anawauza kuti ngati achimwira Yehova, palibe munthu amene angawapembedzere. Ngakhale anatero, analephera kuwawongolera ndi kuwalanga. Motero, ana a Eli sanasiye njira zawo zoipa. Mapeto ake, Yehova potsata chilungamo anapereka chilango cha imfa. Eli atamva za imfa yawo, iyenso anamwalira. Zinali zomvetsa chisoni. Apa ndi zoonekeratu kuti Eli, analolera m’njira yolakwika zoipa zawo mwa kuwalola kupitiriza kutumikira, ndipo sanachite bwino.​—1 Sam. 2:12-17, 22-25, 34, 35; 4:17, 18.

20 Mosiyana ndi zimenezo, taganizirani za mmene Mulungu anachitira ndi ana ake, angelo. Mneneri Mikaya anaona masomphenya ochititsa chidwi a Yehova ali pamsonkhano ndi angelowo. Yehova anafunsa angelowo kuti ndani wa iwo amene akananyenga Mfumu Ahabu ya Isiraeli pofuna kuwononga mfumu yoipayo. Yehova anamvetsera maganizo osiyanasiyana a ana ake auzimu. Kenako mngelo wina ananena kuti iye adzachita zimenezo. Yehova anafunsa mngeloyo kuti adzachita bwanji zimenezo. Atakhutira ndi yankho lake, Yehova anatumiza mngeloyo kukachita zimenezo. (1 Maf. 22:19-23) Kodi pamenepa anthu m’banja sangaphunzirepo kanthu pankhani ya kukhala ololera? Mwamuna wachikhristu amenenso ndi tate ayenera kumvetsera maganizo a mkazi wake komanso a ana ake. Nayenso mkazi ndi ana ayenera kudziwa kuti ngati apereka maganizo awo, angafunikire kulolera ndi kulemekeza malangizo operekedwa ndi mwamunayo amene Malemba amamupatsa mphamvu yogamula.

21. Kodi nkhani yotsatira idzafotokoza chiyani?

21 Tikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha zikumbutso zake zachikondi ndi zanzeru pankhani ya kukhala ololera. (Sal. 119:99) Nkhani yathu yotsatira idzafotokoza mmene kukhala ololera m’njira yoyenera kumathandizira kuti ukwati ukhale wosangalatsa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito liwu lovuta kulimasulira ndi mawu amodzi. Buku lina limati: “Liwulo limanena za mtima umene umalolera kudzimana ufulu wako ndiponso woganizira ena komanso wachifundo.” Choncho mfundo ya liwulo imaphatikizapo kukhala wololera, osati kuumiriza munthu kuti atsatire malamulo mosaphonyetsako kapena kuumirira kuti ndi ufulu wanga kuchita zakutizakuti.

^ ndime 13 Onani nkhani yakuti “‘Akakukakamizani’ Kuchita Zinthu,” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 2005, masamba 23-26.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ubwino wa kukhala wololera ndi wotani?

• Kodi oyang’anira angasonyeze bwanji mtima wololera?

• Kodi n’chifukwa chiyani mtima wololera umafunika m’banja?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 4]

Akulu amatsanzira kukoma mtima kwa Khristu pochita zinthu ndi anthu

[Chithunzi patsamba 6]

Akulu akakhala pa msonkhano wawo, kuganizira bwino mfundo zawo, kupemphera ndiponso mtima wololera, zimalimbikitsa umodzi