Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufalitsa Uthenga Wabwino M’mapiri a Andes

Kufalitsa Uthenga Wabwino M’mapiri a Andes

Kufalitsa Uthenga Wabwino M’mapiri a Andes

IFE anthu okwana 18 tinali gone pansi m’nyumba yopanda simenti. Tinali kunjenjemera chifukwa cha kuzizira, uku phokoso la chimvula likumveka pa malata. Mmene kanyumbako kanali kuonekera, tinaganiza kuti mwina tinali anthu oyamba kugonamo.

N’chifukwa chiyani ife anthu 18 tinapita kumeneko? Tinachita izi potsatira lamulo la Yesu lakuti uthenga wabwino uyenera kulalikidwa “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8; Mat. 24:14) Tinali kulalikira kugawo lakutali m’mapiri a Andes ku Bolivia.

Ndi Kovuta Kukafikako

Vuto loyamba linali lakuti tipita bwanji kumeneko. Tinamva kuti galimoto zopita kumeneko zinali zosadalirika. Basi yathu itafika, tinapeza kuti ndi yaing’ono kwambiri motero kuti ambirife tinakhala choimirira. Ngakhale zinali choncho, tonse tinakafika ndithu.

Cholinga chathu chinali chakuti tikafike ku midzi ya m’mapiri a Andes ku Bolivia. Titatsika basiyo, tinanyamula katundu wathu n’kumayenda mondondozana mutinjira tokwera m’mapirimo.

Ngakhale kuti midziyo inali ing’onoing’ono, inali yotalikirana kwambiri motero kuti tinali kuyenda maola ambiri tisanafike pa mudzi wina. Tikayenda kwambiri kufika pa nyumba ina, tinali kuonanso nyumba ina patali kutsogolo kwathu. Tinali kusochera kawirikawiri mutinjira tambiri tosokoneza, todutsa m’minda.

“Munali Kuti Nthawi Yonseyi?”

Mayi wina anachita chidwi ndi mtunda umene tinayenda, ndipo anatilola kugwiritsa ntchito khitchini ndi nkhuni zake kuti tiphike chakudya chathu chamasana. Mwamuna wina atadziwa zimene Baibulo limaphunzitsa za akufa anafunsa kuti, “Munali kuti nthawi yonseyi?” Iye anachita chidwi kwambiri mpaka anatiperekeza pochoka m’mudzi wawo kuti azifunsabe mafunso m’njiramo. Mwamuna winanso anali asanamvepo za Mboni za Yehova ndipo anasangalala kwambiri ndi mabuku athu. Iye anatithokoza kwambiri chifukwa chofika kumeneko ndipo anatipatsa makiyi a kanyumba kena kuti tigonemo usikuwo.

Tsiku lina usiku, tinaika matenti athu pamalo ena, osadziwa kuti pali nyerere zikuluzikulu zakuda. Nyererezo zinalusa ndipo sizinachedwe kuyamba kutiluma. Koma chifukwa cha kutopa, tinakhalabe pomwepo ndipo posapita nthawi, nyerere zija zinangotisiya.

Poyamba tinali kumva kupweteka msana ndi m’nthiti chifukwa chogona pansi, koma usiku thupi linazolowera. Kutacha, tinaiwala za ululu wonse uja titaona zigwa zokongola ndi mitambo ikukwera pang’onopang’ono m’mapirimo ndiponso nsonga zokongola za mapiriwo chapatali, zitakutidwa ndi chipale chofewa. Kunali zii, ndipo phokoso lomwe linali kumveka linali la madzi a mumtsinje ndi kuimba kwa mbalame basi.

Titasamba mu mtsinjemo, tinakambirana lemba la tsiku, kenako tinadya chakudya cham’mawa. Titatero, tinanyamuka kukwerabe mapiriwo kupita ku midzi ina ya kutali kwambiri. Ulendowu unali waphindu. Tinakumana ndi mayi wina wokalamba, ndipo atadziwa kuti m’Baibulo muli dzina la Mulungu lakuti Yehova, anagwetsa misozi. Iye anakhudzidwa mtima kwambiri. Tsopano amatchula dzina la Mulungulo popemphera.

Mwamuna wina wokalamba ananena kuti Mulungu wamukumbukira, ndipo anagundika nayo nyimbo yonena kuti angelo ndi amene atituma. Mwamuna winanso amene sanali kutuluka m’nyumba yake chifukwa chodwala, anatiuza kuti palibe munthu aliyense wa m’mudzimo amene anapita kukamuona. Anadabwa kwambiri atamva kuti tinachokera komwe ku La Paz. Mwamuna winanso anachita chidwi kwambiri kuona kuti Mboni za Yehova zimayendera anthu m’nyumba zawo pomwe matchalitchi ena amangoitana anthu ndi belu.

Kuderali nyumba zonse zilibe magetsi, motero anthu amagona mdima ukangogwa ndipo amadzuka dzuwa likatuluka. Chifukwa cha zimenezi, tinafunika kuyamba kulalikira 6 koloko m’mawa kuti tipeze anthu. Kungochedwa pang’ono, tikanapeza anthu onse atapita kumunda. Komabe anthu ena amene anali atayamba kale kugwira ntchito, anali kusiya ntchito zawo kuti amvetsere uthenga wathu wa m’Mawu a Mulungu. Zimenezi zinali kupereka mpata wakuti ng’ombe zokoka pulawo zipumeko. Anthu ambiri amene tinawapeza pakhomo anali kuyala zikopa za nkhosa kuti tikhalepo ndipo anali kuitana banja lonse kuti lidzamvetsere. Alimi ena anali kupereka matumba akuluakulu a chimanga poyamikira mabuku ofotokoza Baibulo amene tinawasiyira.

“Simunandiiwale?”

Kuti munthu apite patsogolo kuphunzira Baibulo, amafunika kumuyendera maulendo angapo. Ambiri anatichonderera kuti tidzapitenso kukawaphunzitsa zambiri. Motero, tapita maulendo angapo kudera limeneli la Bolivia.

Paulendo wina, mayi wokalamba anasangalala titafikanso ndipo anati: “Inu muli ngati ana anga. Zoona kuti simunandiiwale?” Mwamuna wina anayamikira ntchito yathu ndipo anatiuza kuti tikadzapita ulendo wina, tikafikire ku nyumba kwawo. Titamva kuti mayi wina amene tinamulalikira pa maulendo oyamba anasamukira mu mzinda ndipo akulalikira uthenga wabwino, tinadziwa kuti khama lathu lonse lija lapindula kwambiri.

Tsiku lomaliza la ulendo wathu woyamba, palafini amene tinali kuphikira anatha ndipo tinatsala ndi chakudya chochepa. Tinatola nkhuni ndi kusonkha moto ndipo tinaphika ndi kudya chakudya chotsalacho, kenako tinauyamba wapansi kubwerera kwathu. Panali mtunda wautali ndithu kuti tikafike ku tawuni kokwerera basi ndipo tinakafika kutada.

Ulendo Wobwerera Kwathu

Ulendo wathu wobwerera unalinso ndi mavuto ake chifukwa basi inafa. Kenako tinakwera kumbuyo kwa lole ina kumene kunali anthu tho! Zimenezi zinatipatsa mpata wolalikira anthu amene tinakwera nawo loleyo. Anthuwo anafuna kudziwa chifukwa chimene tinapitira kumeneko. Ngakhale kuti anthu kumeneko ndi amanyazi mwachibadwa, amadziwa kulandira alendo ndipo ndi ansangala.

Titayenda pa loleyo maola 9, tinafika kwathu titanyowa ndiponso titakongwa kwambiri. Ngakhale ndi choncho, ulendowo unali waphindu. Tili m’njira, tinapangana ndi mayi wina amene amakhalanso mumzindawo kuti tiziphunzira naye Baibulo.

Tinali ndi mwayi waukulu kulalikira kwa anthu a m’dera lakutali kwambiri limeneli. Tinalalikira m’midzi inayi ikuluikulu komanso midzi ing’onoing’ono yambiri. Sitikanachitira mwina koma kukumbukira mawu akuti: “Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso.”​—Yes. 52:7; Aroma 10:15.

[Chithunzi patsamba 17]

Titakonzeka kukalalikira uthenga wabwino