Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pangano Lofunika Kwambiri

Pangano Lofunika Kwambiri

Pangano Lofunika Kwambiri

NDINE mayi wachitsikana wa ku Spain. Ndinachita pangano lofunika kwambiri. Ndiloleni ndifotokoze zimene zinandilimbikitsa kuchita pangano limenelo.

M’banja la makolo anga munalibe mtendere. Banja lathu linali ndi chisoni chachikulu pamene mlongo wanga wamng’ono anamwalira pangozi yoopsa kwambiri ali ndi zaka zinayi. Komanso atate anali ndi makhalidwe oipa ndipo anali kusowetsa mtendere mayi anga. Zimenezi sizinalepheretse mayiwo kuphunzitsa ine ndi mchimwene wanga mfundo za makhalidwe abwino.

M’kupita kwa nthawi, mchimwene wanga uja anakwatira, inenso ndinakwatiwa. Posapita nthawi, mayi anga anapezeka ndi matenda a khansa ndipo anamwalira ndi matendawa. Koma asanamwalire, anatisiyira chuma chamtengo wapatali.

Mnzawo wina wa mayi anawauza za chiyembekezo cha m’Malemba chonena za kuuka kwa akufa, ndipo iwo anavomera kuti aziphunzira Baibulo. Uthenga wa chiyembekezo wopezeka m’Baibulo unawathandiza kudziwa chifukwa chokhalira ndi moyo ndiponso kupeza chimwemwe kumapeto kwa moyo wawo.

Ine ndi mchimwene wanga titaona kuti uthenga wa m’Baibulo wathandiza mayiwo, ifenso tinayamba kuphunzira Mawu a Mulungu. Ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova kutatsala mwezi umodzi kuti mwana wanga wachiwiri abadwe. Mwanayu anali wamkazi, wokongola ndipo tinamupatsa dzina lakuti Lucía.

Tsiku limene ndinabatizidwa linali lofunika kwambiri. Chifukwa choyamba chinali chakuti, popeza kuti ndinali nditadzipereka kwa Yehova kuti ndimutumikire kosatha, ndinali munthu wake. Chifukwa chachiwiri ndi chakuti kuyambira pamenepo ndinatha kuphunzitsa ana anga okondedwa, wamwamuna ndi wamkaziyo, za chikhulupiriro changa.

Koma posapita nthawi, chimwemwe chimene ndinali nacho pachifukwa chachiwirichi chinasokonezeka. Lucía ali ndi zaka zinayi, anayamba kumva kupweteka kwambiri m’mimba. Dokotala atamuunika maulendo angapo, ananena kuti chiwindi chake chili ndi chotupa chachikulu ngati lalanje. Dokotalayo ananena kuti Lucía ali ndi khansa yoopsa kwambiri imene inali kukula mofulumira. Kuyambira nthawi imeneyo, Lucía anakhala moyo wozunzika polimbana ndi khansa kwa zaka 7, ndipo nthawi zambiri tinali kukhala kuchipatala nthawi yaitali.

Anali ndi Mtima Wodzipereka

Pazaka zovuta zimenezi, Lucía anali kundilimbikitsa kwambiri mwa kundikumbatira mwachikondi ndiponso kundipsompsona. Ogwira ntchito m’chipatala anachita chidwi kwambiri ndi mmene anapiririra matendawa. Iye anali kukonda kugwira ntchito ndi manesi powathandiza kuperekera yogati, zakumwa ndi zinthu zina kwa ana ena odwala m’chipatalamo. Manesi anafika pomupatsa yunifolomu yoyera ndi baji yosonyeza kuti anali “wothandizira manesi.”

Munthu wina wogwira ntchito kuchipatala ananena kuti “Lucía anali kundisangalatsa kwambiri. Anali mwana wachangu, waluso ndipo anali kukonda kujambula zithunzi. Iye anali wokonda kucheza ndipo anali kuchita zinthu ngati munthu wamkulu.”

Mawu a Mulungu anathandiza Lucía kukhala wolimba mtima. (Aheb. 4:12) Iye anakhulupirira zimene Mawu a Mulunguwo amalonjeza kuti m’dziko latsopano, “imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chiv. 21:4) Iye anali ndi chidwi ndi anthu ena, ndipo anali kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuwauza uthenga wa m’Baibulo. Chifukwa chokhulupirira kuti akufa adzauka, Lucía sanataye mtima ndipo anali wosangalalabe ngakhale anali kudziwa kuti mwina sachira. (Yes. 25:8) Iye anakhala ndi maganizo amenewa mpaka pamene anamwalira ndi matenda a khansa.

Tsiku limene anamwaliralo ndi limene ndinachita naye pangano lofunika kwambiri. Lucía anali kulephera kuyang’ana. Ine ndinamugwira dzanja lina, ndipo atate ake anamugwira linalo. Ndinamunong’oneza kuti: “Usadandaule, sindikusiya. Uzingopuma pang’onopang’ono. Ukadzadzuka udzakhala bwino. Sudzamvanso kupweteka ndipo ine ndidzakhala nawe.”

Tsopano ndikuyesetsa kusunga pangano limenelo. Ndikudziwa kuti kudikira ndi kovuta. Koma ndikudziwanso kuti ngati ndileza mtima ndi kudalira Yehova ndiponso kukhalabe wokhulupirika, ndidzakhalapo pamene Lucía adzaukitsidwa.

Lucía Anatilimbikitsa

Kulimba mtima kwa Lucía ndiponso zimene mpingo unachita, zinakhudza kwambiri mwamuna wanga amene panthawiyo sanali wa Mboni. Tsiku limene Lucía anamwalira, mwamuna wangayo anandiuza kuti tsopano akufuna kuganiza mofatsa za moyo wake. Patangodutsa milungu yochepa, iye anapempha mkulu mumpingo wathu kuti aziphunzira naye Baibulo. Posapita nthawi, mwamuna wanga anayamba kupezeka pamisonkhano yonse. Yehova anamuthandiza ndipo iye anasiya kusuta ngakhale kuti m’mbuyomo zinali kumuvuta kuti asiye.

Ndimamvabe chisoni ndi imfa ya Lucía koma ndimayamikira Yehova chifukwa cha mmene Lucía anatilimbikitsira. Ine ndi mwamuna wanga timatonthozana ndi chiyembekezo chosangalatsa chakuti akufa adzauka, ndipo timakhala ngati tikumuona Lucía atauka, akutiyang’ana ndi maso ake aakulu, okongola ndi ochenjera, komanso akumwetulira m’masaya mwake mutalowa m’kati.

Mayi wina amene anali kutidziwa, anachita chidwi ndi nkhani yomvetsa chisoni ya mwana wanga. Loweruka lina m’mawa, kukugwa mvula, mayiyo amene mwana wake anali kuphunzira sukulu imodzi ndi Lucía, anabwera kunyumba kwathu. Mwana wake wina anali atamwalira m’mbuyomo. Kenako mwana wake wina wa zaka 11 anamwaliranso ndi matenda omwewa. Atamva zimene zinachitikira Lucía, mayiyo anafufuza kumene tinali kukhala ndipo anabwera kudzationa. Iye anafuna kudziwa kuti zinthu zili bwanji pambuyo pa imfa ya Lucía, ndipo anati tikhazikitse kabungwe kuti kazitonthoza amayi amene agweredwa mavuto ngati athuwa.

Ndinamuuza kuti chimene chimanditonthoza ndi limodzi mwa malonjezo a m’Baibulo. Lonjezoli limaposa malonjezo onse amene anthu angapereke. Nkhope yake inawala nditamuwerengera mawu a Yesu olembedwa pa Yohane 5:28, 29. Iye anavomera kuti ndiziphunzira naye Baibulo ndipo posapita nthawi, anayamba kupeza “mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira.” (Afil. 4:7) Nthawi zambiri tikamaphunzira Baibulo, timaima kaye n’kumaganizira zakuti tikulandira okondedwa athu amene anamwalira ataukitsidwa m’dziko latsopano.

Ngakhale kuti moyo wa Lucía unali waufupi, zimene anachita zimatilimbikitsabe. Chikhulupiriro chake chathandiza banja lathu kukhala logwirizana pakulambira Mulungu ndipo chathandiza inenso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Kunena zoona, tonse amene okondedwa athu anamwalira ndipo tikuyembekeza kuti adzaukitsidwa, tili ndi pangano lofunika kwambiri limene tiyenera kulikwaniritsa.

[Chithunzi patsamba 20]

Chithunzi cha paradaiso chimene Lucía anajambula