Yehova Amamva Kulira Kwathu Ndipo Amatithandiza
Yehova Amamva Kulira Kwathu Ndipo Amatithandiza
“Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake achereza kulira kwawo.”—SAL. 34:15.
1, 2. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano amamva bwanji? (b) N’chifukwa chiyani ife sitidabwa ndi zimenezi?
KODI mukukumana ndi mavuto? Ngati ndi choncho, simuli nokha. Anthu ambiri akulimbana ndi mavuto a tsiku ndi tsiku omwe amakumana nawo m’dongosolo la zinthu loipali. Ena amaona kuti n’zosatheka kupirira. Iwo amamva mmene anamvera wamasalmo Davide, yemwe analemba kuti: “Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa: Ndabangula chifukwa cha kumyuka mtima wanga. Mtima wanga ugundagunda, mphamvu yanga yachoka: Ndipo kuunika kwa maso anga, ndi iko komwe kwandichokera.”—Sal. 38:8, 10.
2 Akhristufe, sitidabwa ndi mavuto amene timakumana nawo. Timadziwa kuti “masautso, ngati mmene zimayambira zopweteka za kubereka,” ndi chizindikiro china cha kukhalapo kwa Yesu chimene chinaloseredwa. (Maliko 13:8; Mat. 24:3) Mawu akuti ‘masautso ngati zopweteka za kubereka,’ akufotokoza bwino kukula kwa mavuto amene anthu akukumana nawo m’nthawi ino “yovuta” ndi yoopsa.—2 Tim. 3:1.
Yehova Amamvetsa Mavuto Athu
3. Kodi anthu a Mulungu amadziwa bwino za chiyani?
3 Anthu a Yehova amadziwa bwino kuti iwo sangapewe mavuto amenewa, ndi kuti zinthu zingathe kuipiraipirabe. Kuwonjezera pa mavuto amene anthu onse amakumana nawo, atumiki a Mulungufe tilinso ndi ‘mdani wathu Mdyerekezi,’ amene cholinga chake ndi kuwononga chikhulupiriro chathu. (1 Pet. 5:8) Choncho m’posavuta kumva ngati mmene anamvera Davide yemwe anati: “Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe: Ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.”—Sal. 69:20.
4. Kodi chimatitonthoza mtima ndi chiyani tikamakumana ndi mavuto?
4 Kodi Davide anali kutanthauza kuti analibe chiyembekezo ngakhale pang’ono? Ayi. Tamverani mawu ake otsatira mu salmo limenelo: “Yehova amvera aumphawi, ndipo sapeputsa am’ndende ake,” kapena kuti anthu ake omwe ali m’ndende. (Sal. 69:33) Nthawi zina, tingamve ngati tili m’ndende chifukwa cha mavuto kapena masautso athu. Tingaone ngati kuti ena sakumvetsa bwinobwino mavuto athu, ndipo n’kuthekadi kuti sakumvetsa. Koma mofanana ndi Davide, mtima wathu ungatonthozedwe podziwa kuti Yehova amamvetsa bwino kwambiri mavuto athu.—Sal. 34:15.
5. Kodi Mfumu Solomo inali kukhulupirira kuti chiyani?
5 Solomo mwana wa Davide, anatsindika mfundo imeneyi popereka kachisi ku Yerusalemu. (Werengani 2 Mbiri 6:29-31.) Iye anachonderera Yehova kuti amve pemphero la munthu aliyense woona mtima amene anapemphera kwa iye za “chinthenda chake, ndi chisoni chake.” Kodi Mulungu akanatani ndi mapemphero a anthu ovutika amenewo? Solomo anasonyeza chikhulupiriro chake kuti Mulungu adzamva mapemphero awo ndi kuwathandiza. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti iye amadziwa “mitima ya ana a anthu.”
6. Kodi tingapirire motani nkhawa zathu, ndipo chifukwa chiyani?
6 Ifenso tingapemphere kwa Yehova za ‘chinthenda chathu, ndi chisoni chathu,’ zomwe 1 Pet. 5:7) Yehova amakhudzidwa ndi zimene zimatichitikira. Yesu anatsindika mfundo yakuti Yehova amatikonda ndi kutisamalira. Iye anati: “Kodi mpheta ziwiri samazigulitsa kakobili kamodzi kochepa mphamvu? Koma palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Koma tsitsi lenilenilo la m’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”—Mat. 10:29-31.
ndi mavuto athu. Timalimbikitsidwa podziwa kuti iye amamvetsa mavuto athu ndiponso amasamala za ife. Mtumwi Petulo anatsimikizira zimenezi pamene ananena kuti: ‘Mum’tulire nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.’ (Dalirani Thandizo la Yehova
7. Kodi tikutsimikiza kuti tingalandire thandizo lotani?
7 Tidziwe kuti Yehova ndi wokonzeka ndipo amatha kutithandiza tikakumana ndi mavuto. “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.” (Sal. 34:15-18; 46:1) Kodi Mulungu amapereka bwanji thandizo limenelo? Taonani zimene lemba la 1 Akorinto 10:13 limanena. Limati: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” Yehova angachititse zinthu kusintha kuti mavuto athu athe, kapena angatipatse mphamvu kuti tipirire. Inde, amatithandiza m’njira zonse ziwirizi.
8. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atithandize?
8 Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze thandizo limenelo? Onani zimene tikulangizidwa kuchita. ‘Mutulireni nkhawa zanu zonse.’ Zimenezi zikutanthauza kuti mophiphiritsa, timatenga udindo wosamalira nkhawa zathu zonse ndi kuupereka kwa Yehova. Timayesetsa kusada nkhawa ndipo moleza mtima timadalira iye kuti asamalire zosowa zathu. (Mat. 6:25-32) Kumudalira kumeneku kumafuna kudzichepetsa, osati kudalira mphamvu kapena nzeru zathu. Mwa kudzichepetsa “pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu,” timasonyeza kuti tikuzindikira kuti patokha sitingakwanitse. (Werengani 1 Petulo 5:6.) Zimenezi zimatithandiza kupirira zilizonse zimene Mulungu walola kuti zichitike. Mwina tingalakelake kuti mavutowo athe msanga, koma timakhulupirirabe kuti Yehova akudziwa nthawi yeniyeni imene adzatithandiza ndi mmene adzatithandizira.—Sal. 54:7; Yes. 41:10.
9. Kodi ndi nkhawa yotani imene Davide anafunikira kusenzetsa Yehova?
9 Kumbukirani mawu a Davide olembedwa pa Salmo 55:22. Iye anati: “Um’senze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” Pamene Davide anali kulemba mawuwa, anali pa mavuto aakulu. (Sal. 55:4) Zikuoneka kuti Davide analemba salmo limeneli mwana wake Abisalomu atachita chiwembu chofuna kumulanda ufumu. Ahitofeli, phungu wodalirika wa Davide, anachita nawo chiwembucho. Pofuna kupulumutsa moyo wake, Davide anathawa kuchoka ku Yerusalemu. (2 Sam. 15:12-14) Ngakhale zinthu zinavuta choncho, Davide sanasiye kukhulupirira Mulungu, ndipo sanagwiritsidwe mwala.
10. Kodi tiyenera kuchita chiyani tikakumana ndi mavuto?
10 Ifenso mofanana ndi Davide, tifunikira kupemphera kwa Yehova za mavuto amtundu uliwonse amene tingakumane nawo. Tiyeni tione zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuchita Afilipi 4:6, 7.) Kodi chimachitika n’chiyani tikamapemphera mochokera pansi pa mtima mwanjira imeneyi? “Mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Khristu Yesu.”
pa nkhani imeneyi. (Werengani11. Kodi “mtendere wa Mulungu” umateteza bwanji mtima ndi maganizo athu?
11 Kodi pemphero lingasinthe zinthu kukhala bwino? Mwina lingatero. Koma tiyenera kukumbukira kuti si nthawi zonse pamene Yehova amayankha mapemphero athu mmene ife tikufunira. Ngakhale ndi choncho, pemphero limatithandiza kusunga maganizo athu kuti mavuto athuwo asatitayitse mtima. “Mtendere wa Mulungu” ungatikhazikitse mtima pansi ngati tili ndi nkhawa chifukwa cha mavuto athu. Mofanana ndi asilikali amene ali pa ntchito yoteteza mzinda kwa adani, “mtendere wa Mulungu” umateteza mtima ndi maganizo athu. Umatithandiza kuti tisamakayikire, tisakhale ndi mantha ndiponso kuti tisamapsinjike maganizo. Umatithandizanso kuti tisachite zinthu mopupuluma ndi mopanda nzeru.—Sal. 145:18.
12. Perekani fanizo losonyeza mmene munthu angakhalire ndi mtendere wa mumtima.
12 Kodi zingatheke bwanji kukhala ndi mtendere wa mumtima pamene tikuvutika? Tiyeni tikambirane fanizo limene m’mbali zina likufanana ndi mmene zinthu zilili kwa ife. Munthu wina amagwira ntchito ndi manijala woipa mtima. Kenako, munthuyo akupeza mpata wofotokoza mavuto ake kwa mwini kampani yemwe ndi wokoma mtima ndi womvetsa zinthu. Mwini kampaniyo akutsimikizira munthuyo kuti akumvetsa mavuto akewo ndipo akumuuza kuti manijalayo achotsedwa ntchito posachedwa. Kodi munthuyo angamve bwanji? Pokhulupirira zimene wauzidwazo ndiponso podziwa zimene zichitike, adzalimba mtima ndi kupitiriza kugwira ntchito yake, ngakhale kuti panthawiyo angakumanebe ndi mavuto ena ndi ena. Mofanana ndi zimenezo, ife tikudziwa kuti Yehova amamvetsa mavuto athu ndipo akutitsimikizira kuti posachedwapa “wolamulira wa dzikoli aponyedwa kunja.” (Yoh. 12:31) Zimenezi ndi zolimbikitsa kwambiri.
13. Kodi tikapemphera, tiyeneranso kuchita chiyani?
13 Kodi pamenepa kungomuuza Yehova mavuto athu m’pemphero ndi kokwanira? Ayi, tifunika kuchitanso zina. Tifunika kuchita zinthu mogwirizana ndi mapemphero athuwo. Mfumu Sauli itatuma anthu kunyumba kwa Davide kuti akamuphe, Davide anapemphera kuti: “Ndilanditseni kwa adani anga, Mulungu wanga: Ndiikeni pamsanje kwa iwo akundiukira. Mundilanditse kwa ochita zopanda pake, ndipo ndipulumutseni kwa anthu olira mwazi.” (Sal. 59:1, 2) Atapemphera, Davide anamveranso mkazi wake ndipo anachita mogwirizana ndi zimene anapemphazo n’kuthawa. (1 Sam. 19:11, 12) Ifenso tingapemphe nzeru yochitira zinthu zimene zingatithandize kupirira mavuto athu kapena kuchepetsako mavutowo.—Yak. 1:5.
Tingapeze Bwanji Mphamvu Kuti Tipirire?
14. Kodi chingatithandize kupirira ndi chiyani tikamakumana ndi mavuto?
14 Mwina mavuto athu sangathe msanga ndipo angapitirire kwa kanthawi. Zikatero, kodi chingatithandize kupirira ndi chiyani? Choyamba ndi kukumbukira kuti tikapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika tikakhala pa mavuto, timasonyeza kuti timamukonda. (Mac. 14:22) Musaiwale kuti Satana ananeneza Yobu kuti: “Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe? Kodi simunam’chinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pom’zinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kum’khudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.” (Yobu 1:9-11) Chifukwa cha kukhulupirika kwake, Yobu anasonyeza kuti zonena za Satana ndi bodza lamkunkhuniza. Tikamapirira mavuto amene timakumana nawo, ifenso timakhala ndi mwayi wosonyeza kuti Satana ndi wabodza. Kenako, chifukwa cha kupirira kwathu, chiyembekezo ndi chikhulupiriro chathu chimalimba.—Yak. 1:4.
15. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zingatilimbikitse?
15 Chachiwiri, kumbukirani kuti “anzanunso m’gulu lonse la abale anu m’dzikoli akukumananso ndi masautso ngati amenewo.” (1 Pet. 5:9) Zoonadi, “palibe mayesero amene mwakumana nawo osakhala amene amagwera anthu.” (1 Akor. 10:13) Choncho ngati musinkhasinkha zitsanzo za ena m’malo moganizira kwambiri za mavuto anu, zingakuthandizeni kupeza mphamvu ndi kukhala wolimba mtima. (1 Ates. 1:5-7; Aheb. 12:1) Pezani nthawi yoganizira za zitsanzo za anthu amene mukuwadziwa omwe apirira mavuto aakulu mokhulupirika. Kodi mwafufuzapo mbiri za moyo wa anthu zimene zafalitsidwa, kuti mupeze nkhani za anthu amene akumanapo ndi mavuto ngati anuwo? Zimenezi zingakulimbikitseni kwambiri.
16. Kodi Mulungu amatilimbikitsa bwanji tikakumana ndi mayesero amitundumitundu?
16 Chachitatu, kumbukirani kuti Yehova ndi “Tate wa chifundo chachikulu ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, amene amatitonthoza m’masautso athu onse, kuti tikathe kutonthoza amene ali m’masautso a mtundu uliwonse mwa chitonthozo chimene nafenso Mulungu akutitonthoza nacho.” (2 Akor. 1:3, 4) Zili ngati kuti Mulungu waima pafupi nafe kuti atilimbikitse “m’masautso athu onse,” osati chabe m’masautso amene tili nawo panopa. Zimenezi zimatithandiza ifenso kutonthoza anzathu amene ali “m’masautso a mtundu uliwonse.” Mawu amenewa ndi oona ndipo zimenezi n’zimene zinamuchitikira Paulo.—2 Akor. 4:8, 9; 11:23-27.
17. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kupirira mavuto amene timakumana nawo?
17 Chachinayi, tili ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, amene ndi “opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:16, 17) Sikuti Mawu a Mulungu amangotithandiza kukhala “woyenera” ndi ‘wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.’ Amatithandizanso kupirira mavuto amene timakumana nawo. Amatithandiza kukhala “woyenera mokwanira” ndi “wokonzeka bwino lomwe.” M’chinenero choyambirira, tanthauzo lenileni la mawu omasuliridwa kuti “wokonzeka bwino lomwe” ndilo “kukhala ndi zinthu zokwanira.” Zikuoneka kuti kalelo, mawu amenewa anali kuwagwiritsa ntchito pofotokoza za bwato lokhala ndi zinthu zonse zokwanira zofunika paulendo kapena za makina otha kuchita ntchito yake bwinobwino. Mofanana ndi zimenezo, Yehova kudzera m’Mawu ake, amatipatsa zinthu zonse zimene timafunikira kuti tithe kupirira chilichonse chimene tingakumane nacho. Choncho m’pake kunena kuti, “Ngati Mulungu walola vutoli, nditha kulipirira ndipo adzandithandiza.”
Kupulumutsidwa ku Mavuto Athu Onse
18. Kodi ndi kusaiwala chiyani kumene kungatithandizenso kupirira mokhulupirika?
18 Chachisanu, musaiwale mfundo yosangalatsa yakuti Yehova posachedwapa adzamasula anthu onse ku mavuto awo. (Sal. 34:19; 37:9-11; 2 Pet. 2:9) Mulungu akadzatipulumutsa, sikuti tidzangopulumuka mavuto amene tikukumana nawowa koma tidzakhalanso ndi mwayi wolandira moyo wosatha, kaya kumwamba limodzi ndi Yesu kapena m’paradaiso padziko lapansi.
19. Kodi zingatheke bwanji kuti munthu apirire mokhulupirika?
19 Nthawi imeneyo isanafike, tiyeni tipitirize kupirira mavuto a m’dziko loipali. Tikuyembekezera mwachidwi nthawi imene mavuto onsewa adzatha. (Sal. 55:6-8) Tisaiwale kuti tikamapirira mokhulupirika, timasonyeza kuti Mdyerekezi ndi wabodza. Tiyeni tipeze mphamvu kuchokera m’mapemphero athu ndi kwa abale athu achikhristu, pokumbukira kuti abale athu akukumana ndi mayesero ngati athuwo. Pitirizani kukhala woyenera mokwanira ndi wokonzeka bwino lomwe mwa kugwiritsa ntchito bwino Mawu a Mulungu. Musasiye kukhulupirira kuti “Mulungu wa chitonthozo chonse” amakukondani ndipo amasamala za inu. Kumbukirani kuti “maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake achereza kulira kwawo.”—Sal. 34:15.
Kodi Mungayankhe?
• Kodi Davide anamva bwanji atakumana ndi mavuto?
• Kodi Mfumu Solomo inali kukhulupirira kuti chiyani?
• Kodi n’chiyani chingatithandize kupirira mavuto amene Yehova walola?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 13]
Solomo anali ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzathandiza anthu ake ovutika
[Chithunzi patsamba 15]
Davide anasenzetsa Yehova nkhawa zake mwa kupemphera ndipo anachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lakelo