Achinyamata, Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu
Achinyamata, Kumbukirani Mlengi Wanu Wamkulu
“Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”—MLAL. 12:1.
1. Kodi Yehova amasonyeza bwanji kuti amakhulupirira achinyamata amene amamulambira?
YEHOVA amaona kuti Akhristu achinyamata ndi amtengo wapatali ndiponso otsitsimula ngati mame. Iye analosera kuti tsiku la “chamuna” cha Mwana wake, anyamata ndi atsikana “adzadzipereka eni ake” kutumikira Khristu. (Sal. 110:3) Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa panopa pamene anthu ambiri ndi osaopa Mulungu, odzikonda ndi okonda ndalama, ndiponso osamvera. Koma Yehova anadziwa kuti achinyamata amene adzamulambira adzakhala osiyana ndi anthu onsewo. Inde, Yehova amakukhulupirirani kwambiri inu abale ndi alongo achinyamata.
2. Kodi kukumbukira Yehova kumatanthauza chiyani?
2 Mulungu amasangalala kwambiri kuona achinyamata akumukumbukira iye monga Mlengi wawo Wamkulu. (Mlal. 12:1) Monga mmene mukudziwira, kukumbukira Yehova kumatanthauza zambiri osati chabe kungoganizira za iye. Kumatanthauza kuchita zimene iye amakondwera nazo ndiponso kulola malamulo ndi mfundo zake kutitsogolera pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Kumatanthauzanso kukhulupirira Yehova, podziwa kuti iye amatifunira zabwino zokhazokha. (Sal. 37:3; Yes. 48:17, 18) Kodi umu ndi mmene inu mumaonera Mlengi wanu Wamkuluyu?
‘Khulupirirani Yehova ndi Mtima Wanu Wonse’
3, 4. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anakhulupirira Yehova, nanga n’chifukwa chiyani kukhulupirira Yehova kuli kofunika masiku ano?
3 Chitsanzo chabwino koposa cha munthu amene anakhulupirira Mulungu ndi Yesu Khristu. Iye anatsatira mawu a pa Miyambo 3:5, 6 akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.” Yesu atangobatizidwa, Satana anafika kwa iye ndipo anamuyesa mwa kumulonjeza kuti amupatsa ulamuliro wa dziko lapansi ndi ulemerero wake. (Luka 4:3-13) Yesu sanakopeke. Iye anadziwa kuti “chuma, ndi ulemu, ndi moyo” weniweni zimabwera chifukwa cha ‘kufatsa ndi kuopa Yehova.’—Miy. 22:4.
4 Masiku ano m’dzikoli, anthu ndi adyera ndi odzikonda. Popeza tikukhala m’dziko lotereli, ndi nzeru kutsatira chitsanzo cha Yesu. Komanso musaiwale kuti Satana akuyesetsa kwambiri kunyengerera atumiki a Yehova kuti awachotse pa msewu wopanikiza wa kumoyo. Iye angakonde kuona anthu onse akuyenda pa msewu waukulu wa kuchiwonongeko. Choncho, asakunyengeni. Ndiponso musasiye kukumbukira Mlengi wanu Wamkulu. Khulupirirani iye ndi mtima wanu wonse kuti mugwire zolimba “moyo weniweniwo,” umene ndi wodalirika ndiponso umene wayandikira.—1 Tim. 6:19.
Achinyamata, Chitani Mwanzeru
5. Kodi inu mukuganiza bwanji za tsogolo la dzikoli?
5 Achinyamata amene amakumbukira Mlengi wawo Wamkulu ndi anzeru kuposa anzawo. (Werengani Salmo 119:99, 100.) Popeza amaona zinthu mmene Mulungu amaonera, iwo akudziwa bwino kuti dzikoli chake palibe ndipo litha posachedwapa. Ngakhale kuti mulibe zaka zambiri, mosakayikira mwaona anthu ambiri akukhala ndi nkhawa ndi mantha. Ngati ndinu mwana wa sukulu, muyenera kuti mwamva za mavuto monga kudula mitengo mwachisawawa, kuwonongedwa kwa chilengedwe ndi kutentha kwa dziko. Anthu ali ndi nkhawa yaikulu chifukwa cha zimenezi, koma Mboni za Yehova zokha ndi zimene zikudziwa kuti zinthuzi ndi zina mwa zizindikiro zosonyeza kuti dziko la Satanali likutha.—Chiv. 11:18.
6. Kodi achinyamata ena anyengedwa ndi chiyani?
6 N’zomvetsa chisoni kuti atumiki a Mulungu ena achinyamata ayamba kuwodzera ndipo aiwala 2 Pet. 3:3, 4) Ena afika pochita machimo aakulu chifukwa choyanjana ndi anthu olakwika ndiponso chifukwa chokonda zinthu zolaula. (Miy. 13:20) Zingakhale zomvetsa chisoni kwambiri kusiya kuyanjidwa ndi Mulungu makamaka nthawi ino pamene mapeto atsala pang’ono kufika. Choncho, tenganipo phunziro pa zimene zinachitikira Aisiraeli mu 1473 B.C.E. pamene anali mu Chigwa cha Moabu, pakhomo penipeni pa Dziko Lolonjezedwa. Kodi chinachitika n’chiyani?
kuti dzikoli latsala pang’ono kutha. (Analephera Kulowa Atafika Kale
7, 8. (a) Kodi Satana anagwiritsa ntchito msampha wotani m’Chigwa cha Moabu? (b) Kodi masiku ano Satana akugwiritsa ntchito msampha wotani?
7 Kalelo, Satana anali kufuna kuti Aisiraeli asalandire cholowa chawo chimene analonjezedwa. Atalephera kuwatemberera kudzera mwa mneneri Balamu, Satana anagwiritsa ntchito msampha wovuta kuuzindikira. Iye anawachititsa zinthu zimene zinawalepheretsa kulandira madalitso a Yehova. Kuti awanyenge, iye anagwiritsa ntchito akazi okongola ndi okopa a ku Moabu, ndipo apa Mdyerekezi anapambana ndithu. Aisiraeli anayamba kugonana ndi ana aakazi a ku Moabu ndi kugwadira Baala wa ku Peori. Ngakhale kuti iwo anali pakhomo penipeni pa Dziko Lolonjezedwa, lomwe linali cholowa chawo chamtengo wapatali, Aisiraeli okwana 24,000 anataya moyo wawo. Koma ndiye zinali zachisoni!—Num. 25:1-3, 9.
8 Masiku ano, tikuyandikira kwambiri dziko lolonjezedwa labwino kuposa limenelo. Dzikolo ndi dongosolo latsopano la zinthu. Mwachizolowezi chake, Satana akugwiritsanso ntchito chiwerewere kudetsa nacho anthu a Mulungu. Anthu m’dzikoli atayirira kwambiri motero kuti amaona dama ngati labwinobwino ndipo kugonana amuna kapena akazi okhaokha ngati ufulu wa munthu. Mlongo wina anati: “Ndi kunyumba kokha komanso ku Nyumba ya Ufumu, kumene ana anga amaphunzira kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha ndiponso kugonana anthu osakwatirana, ndi kuchimwira Mulungu.”
9. Kodi chimachitika ndi chiyani “pachimake pa unyamata,” ndipo achinyamatawo angachite chiyani?
9 Achinyamata amene amakumbukira Mlengi wawo Wamkulu, amadziwa kuti kugonana ndi mphatso yopatulika imene imathandiza anthu kubereka ana kuti moyo upitirire. Choncho, amaona kuti anthu ayenera kugonana mu ukwati mokha, malinga ndi lamulo la Mulungu. (Aheb. 13:4) Komabe “pachimake pa unyamata,” nthawi imene chilakolako chofuna kugonana chimakhala champhamvu ndipo chingasokoneze kuganiza kwa munthu, imakhala nkhondo kuti munthu akhalebe woyera. (1 Akor. 7:36) Kodi muyenera kuchita chiyani maganizo olakwika akakubwererani? Pempherani mwakhama kuti Yehova akuthandizeni kusintha maganizo anu kuti muyambe kuganizira zinthu zabwino. Yehova nthawi zonse amamva mapemphero a anthu amene amafika kwa iye ndi mtima wonse. (Werengani Luka 11:9-13.) Kukambirana zinthu zolimbikitsa kungakuthandizeninso kuchotsa maganizo anu pa zinthu zolakwikazo.
Chitani Mwanzeru Posankha Zochita Pamoyo Wanu
10. Kodi ndi maganizo ati osayenera amene tifunika kupewa, ndipo tingachite bwino kudzifunsa mafunso otani?
10 Achinyamata ambiri m’dzikoli ndi osadziletsa ndipo amakonda zosangalatsa thupi. Chifukwa china ndi chakuti iwo alibe “chivumbulutso,” kapena kuti masomphenya. Zimenezi zikutanthauza kuti iwo satsogoleredwa ndi Mulungu kapena kuti alibe chiyembekezo cha m’tsogolo. (Miy. 29:18) Iwo ali ngati Aisiraeli osaopa Mulungu a mu nthawi ya Yesaya amene anali kukhalira “kukondwa, ndi kusekerera, . . . kudya nyama, ndi kumwa vinyo.” (Yes. 22:13) M’malo mosirira anthu ngati amenewo, bwanji osaganizira za chiyembekezo chamtengo wapatali chimene Yehova wapatsa anthu ake okhulupirika? Ngati ndinu mtumiki wachinyamata wa Mulungu, kodi mukuyembekezera mwachidwi dziko latsopano? Kodi mukuyesetsa ‘kukhala a maganizo abwino . . . pamene mukuyembekeza kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chosangalatsa’ chimene Yehova wakupatsani? (Tito 2:12, 13) Yankho lanu pa mafunso amenewa lingakhudze mmene mumaonera zolinga zanu ndi zinthu zimene mumati ndi zofunika kwa inu.
11. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu achinyamata amene ali pasukulu afunika kulimbikira maphunziro?
11 Anthu ambiri amafuna kuti achinyamata aziwonongera mphamvu zawo kufunafuna zinthu za dzikoli. Kunena zoona, inu amene muli pasukulu muyenera kulimbikira kwambiri kuti mukhale ndi maphunziro ofunikira. Musaiwale kuti cholinga chanu sikuti mudzapeze ntchito basi, koma kuti mudzakhalenso othandiza mumpingo ndiponso mukhale mlaliki wogwira mtima wa Ufumu. Kuti zimenezi zitheke, pamafunika kudziwa kulankhula bwino ndi anthu, kuganiza mwanzeru ndiponso kukambirana ndi anthu modekha ndi mwaulemu. Koma maphunziro apamwamba amapezeka m’Baibulo. Choncho achinyamata amene amaphunzira Baibulo ndi kumayesetsa kutsatira mfundo zake pamoyo wawo, ndi amene amapeza maphunziro abwino koposa. Ndipo maphunziro amenewa ndi maziko olimba a tsogolo labwino ndi losatha.—Werengani Salmo 1:1-3. *
12. Kodi mabanja achikhristu angachite bwino kutsatira chitsanzo chiti?
12 M’nthawi ya Isiraeli, kuphunzitsa ana kunali udindo wofunika kwambiri kwa makolo. Maphunziro amenewo anakhudza zinthu zambiri, makamaka zinthu zauzimu. (Deut. 6:6, 7) Motero, Aisiraeli achinyamata amene anamvera makolo awo ndi anthu ena achikulire oopa Mulungu, sanangodziwa zinthu koma anakhalanso anzeru, ozindikira, omvetsa zinthu ndiponso anali ndi luso la kulingalira. Makhalidwe amenewa ndi osowa ndipo amapezeka kokha kudzera m’maphunziro a Mulungu. (Miy. 1:2-4; 2:1-5, 11-15) Mabanja achikhristu masiku ano amafunikanso kuona maphunziro mwa njira imeneyi.
Mverani Anthu Amene Amakukondani
13. Kodi achinyamata ena amalandira malangizo otani, nanga n’chifukwa chiyani amafunika kusamala?
13 Achinyamata amalandira malangizo kwa anthu osiyanasiyana, ngakhale alangizi apasukulu othandiza achinyamata kusankha ntchito. Nthawi zambiri alangizi amenewa amangolimbikitsa achinyamata kukhala anthu otsogola m’dzikoli. Polingalira za malangizo awo, musamaiwale kupemphera ndipo muzigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu ndi mabuku amene gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limatulutsa, musanasankhe chochita. Chifukwa cha kuphunzira kwanu Baibulo, Gen. 3:1-6.
inu mukudziwa kuti Satana amalimbana kwambiri ndi achinyamata ndiponso anthu omwe sadziwa zambiri. Mwachitsanzo m’munda wa Edene, Hava yemwe sanali kudziwa zambiri anamvera Satana, amene anali ngati mlendo ndipo analibe chikondi pa iye ngakhale pang’ono. Zinthu zikanakhala bwino kwambiri Hava akanamvera Yehova, amene anamusonyeza chikondi m’njira zambiri.—14. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kumvera Yehova ndi makolo athu okhulupirira?
14 Nayenso Mlengi wanu Wamkulu amakukondani, ndipo chikondi chakecho ndi chopanda mpeni kumphasa. Iye akufuna kuti mukhale osangalala, osati lero lokha komanso mpaka muyaya. Ndiye chifukwa chake pokhala ndi mtima wa kholo, akulankhula ndi inu ndiponso anthu onse amene amalambira iye, kuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.” (Yes. 30:21) Ngati makolo anu ndi Akhristu ndipo amakondadi Yehova, mulinso ndi mwayi. Alemekezeni mwa kumvera uphungu wawo posankha zochita pamoyo wanu. (Miy. 1:8, 9) Musaiwale kuti iwo akufuna mukapeze moyo, umene ndi wofunika kwambiri kuposa chuma ndi kutchuka m’dzikoli.—Mat. 16:26.
15, 16. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira Yehova? (b) Kodi nkhani ya Baruki ikutiphunzitsa mfundo yofunika yotani?
15 Anthu amene amakumbukira Mlengi wawo Wamkulu safuna zambiri pamoyo, chifukwa amakhulupirira kuti Yehova sadzawasiya “mulimonse” ngakhale kuwataya “konse.” (Werengani Aheberi 13:5.) Popeza kuti maganizo amenewa ndi osiyana ndi a dzikoli, tifunika kusamala kuti tisatengere mzimu wa dziko. (Aef. 2:2) Pankhani imeneyi, ganizirani Baruki mlembi wa Yeremiya, amene anakhala ndi moyo m’masiku otsiriza a Yerusalemu pamene mzindawo unatsala pang’ono kuwonongedwa mu 607 B.C.E. Nthawi imeneyi inali yovuta kwambiri.
16 Mwina Baruki anafuna kutukula moyo wake ndi kukhala ndi chuma. Yehova anaona zimenezo ndipo anachenjeza Baruki kuti asafunefune “zinthu zazikulu.” Baruki anadzichepetsa ndipo anachita mwanzeru, chifukwa anamvera Yehova, kenako anapulumuka chiwonongeko cha Yerusalemu. (Yer. 45:2-5) Koma anzake a Baruki amene anapeza “zinthu zazikulu” zakuthupi ndi kuiwala Yehova, posapita nthawi anataya zinthu zawo zonse pamene Akaldayo (Ababulo) anaukira mzindawo. Ambirinso anataya moyo wawo. (2 Mbiri 36:15-18) Nkhani ya Baruki ikutithandiza kuona kuti chofunika kwambiri kuposa chuma ndi kutchuka m’dzikoli ndicho ubale wathu ndi Mulungu.
Tsatirani Anthu Amene Ndi Zitsanzo Zabwino
17. N’chifukwa chiyani Yesu, Paulo ndi Timoteyo ali zitsanzo zabwino kwa atumiki a Yehova masiku ano?
17 Pofuna kutithandiza pamene tikuyenda pa njira ya kumoyo, Mawu a Mulungu amatipatsa zitsanzo zambiri zabwino. Yesu anali ndi luso kuposa munthu wina aliyense padziko lapansi, koma iye anaika mtima wake pa ntchito imene ingathandize anthu kupeza moyo wosatha. Ntchito imeneyi inali yolakira “uthenga wabwino wa ufumu.” (Luka 4:43) Kuti atumikire Yehova ndi moyo wonse, mtumwi Paulo anasiya ntchito ya ndalama zambiri ndipo anagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zake kulalikira uthenga wabwino. Timoteyo, ‘mwana weniweni m’chikhulupiriro,’ anatsatira chitsanzo cha Paulo. (1 Tim. 1:2) Kodi Yesu, Paulo ndi Timoteyo anadandaula kuti sanasankhe bwino? Sanadandaule ngakhale pang’ono. M’malo mwake, Paulo ananena kuti zimene dzikoli limapereka ndi “mulu wa zinyalala” kuyerekeza ndi mwayi wotumikira Mulungu.—Afil. 3:8-11.
18. Kodi m’bale wina wachinyamata anasintha bwanji moyo wake, ndipo n’chifukwa chiyani sadandaula ngakhale pang’ono?
18 Akhristu ambiri achinyamata masiku ano amatsatira chitsanzo cha Yesu, Paulo ndi Timoteyo. Mwachitsanzo, m’bale wina wachinyamata yemwe anali kugwira ntchito ya ndalama zambiri ananena kuti: “Chifukwa chotsatira mfundo zabwino za m’Baibulo, sipanatenge nthawi kuti andikweze pantchito. Komabe, ngakhale kuti ndinali kulandira ndalama zambiri, ndinali kungosautsa mtima. Nditauza mabwana anga kuti ndikufuna kusiya ntchito kuti ndiyambe utumiki wa nthawi zonse, mwamsanga anandilonjeza kuti andiwonjezera malipiro, poganiza kuti ndisintha maganizo. Koma sindinasinthe. Anthu ambiri sanamvetse chifukwa chimene ndinasiyira ntchito ya ndalama zambiri ndi kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Chifukwa chake ndi chakuti ndinadzipereka kwa Mulungu ndipo ndikufuna kukwaniritsa zimenezo. Popeza kuti chachikulu pamoyo wanga tsopano ndi kutumikira Mulungu, ndine munthu wosangalala ndipo ndimakhutira ndi zimene ndili nazo. Ndalama kapena kutchuka sizingandipatse zimenezi.”
19. Kodi achinyamata akulimbikitsidwa kuchita chiyani?
19 Padziko lonse, achinyamata ambiri asankhanso zinthu mwanzeru. Motero inu achinyamata, mukamaganizira za tsogolo lanu, musaiwale kuti tsiku la Yehova layandikira. (2 Pet. 3:11, 12) Musamasirire anthu amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino m’dzikoli. M’malo mwake, mverani anthu amene amakukondanidi. Chinthu chofunika kwambiri chimene mungachite ndi kukundika ‘chuma kumwamba,’ ndipo chuma chimenechi ndi chimene mungapindule nacho kosatha. (Mat. 6:19, 20; werengani 1 Yohane 2:15-17.) Inde, kumbukirani Mlengi wanu Wamkulu ndipo mukatero, Yehova adzakudalitsani.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri za maphunziro apamwamba ndi ntchito yolembedwa, onani Nsanja ya Olonda ya October 1, 2005, masamba 26-31.
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Mulungu?
• Kodi maphunziro apamwamba kwambiri ndi ati?
• Kodi tikuphunzira chiyani kwa Baruki?
• Kodi ndi anthu ati ofunika kuwatsatira monga zitsanzo zabwino, ndipo chifukwa chiyani?
[Mafunso]
[Zithunzi patsamba 13]
Yehova ndi amene amatipatsa maphunziro apamwamba kwambiri
[Chithunzi patsamba 15]
Baruki anamvera Yehova ndipo anapulumuka chiwonongeko cha Yerusalemu. Kodi mukuphunzirapo chiyani?