Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kanani Zinthu “Zopanda Pake”

Kanani Zinthu “Zopanda Pake”

Kanani Zinthu “Zopanda Pake”

“Wotsata anthu opanda pake [“zinthu zopanda pake,” NW] asowa nzeru.”​—MIY. 12:11.

1. Tchulani zinthu zina zamtengo wapatali zimene tili nazo. Kodi njira yabwino kwambiri yomwe tingazigwiritsire ntchito ndi iti?

AKHRISTUFE tili ndi zinthu zosiyanasiyana zamtengo wapatali. Zinthuzi ndi monga moyo wathanzi ndiponso mphamvu zathu, luso lobadwa nalo, kapena chuma. Chifukwa chakuti timakonda Yehova, timasangalala kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi pomutumikira. Tikamachita zimenezi, timakhala tikumvera malangizo ouziridwa akuti: “Lemekeza Yehova ndi chuma chako.”​—Miy. 3:9.

2. Kodi Baibulo limapereka chenjezo lotani pazinthu zopanda pake, ndipo chenjezolo limagwira ntchito bwanji pazinthu zakuthupi?

2 Baibulo limanenanso za zinthu zopanda pake ndipo limatichenjeza kuti tisawawanye zinthu zathu zamtengo wapatali pofunafuna zinthu zopanda pakezo. Pankhani imeneyi, tiyeni tione mawu a pa Miyambo 12:11. Lembali limati: “Zakudya zikwanira wolima minda yake; koma wotsata anthu opanda pake [“zinthu zopanda pake”] asowa nzeru.” Apa ndi zosavuta kuona tanthauzo la lembali. Munthu amene amathera nthawi ndi mphamvu zake akugwira ntchito molimbika kuti adyetse banja lake, kawirikawiri banja lakelo silisowa kanthu. (1 Tim. 5:8) Koma ngati amangosakaza nthawi ndi mphamvu zake pazinthu zopanda pake, ndiye kuti alibe nzeru ndipo zolinga zake si zabwino. Munthu wotero amasauka.

3. Kodi chenjezo la Baibulo lokhudza zinthu zopanda pake limagwira ntchito bwanji pakulambira kwathu?

3 Tsopano tiyeni tigwiritse ntchito mfundo ya palembalo pakulambira kwathu. Timaona kuti Mkhristu amene amatumikira Yehova mwakhama ndiponso mokhulupirika amakhala wosatekeseka. Amakhulupirira kuti Mulungu adzamudalitsa panopa ndipo amakhala ndi chiyembekezo chodalirika cha m’tsogolo. (Mat. 6:33; 1 Tim. 4:10) Koma Mkhristu amene amatengeka ndi zinthu zopanda pake, angawononge ubale wake ndi Yehova ndipo angataye chiyembekezo chake cha moyo wosatha. Kodi tingapewe bwanji zimenezi? Tifunikira kuzindikira zinthu pamoyo wathu zomwe ndi “zopanda pake” kenako ndi kuzikana kwa mtu wagalu.​—Werengani Tito 2:11, 12.

4. Kodi zinthu zopanda pake zingakhale ngati chiyani?

4 Ndiyeno, kodi zinthu zopanda pake ndi chiyani? Zinthuzo zingakhale zilizonse zimene zingatilepheretse kutumikira Yehova ndi moyo wathu wonse. Zimenezi ndi zinthu monga zosangalatsa zosiyanasiyana. Kunena zoona, zosangalatsa ndi zofunika pamoyo wa munthu. Koma ngati timatayira nthawi yaitali pa zinthu zosangalatsa ndi kuiwala kulambira kwathu, ndiye kuti zosangalatsazo ndi zopanda pake, chifukwa zikuwononga moyo wathu wauzimu. (Mlal. 2:24; 4:6) Pofuna kupewa zimenezi, Mkhristu amakhala ndi malire ndipo amagwiritsa ntchito nthawi yake yamtengo wapatali mosamala. (Werengani Akolose 4:5.) Komabe, pali zinthu zina zopanda pake zomwe ndi zoopsa kwambiri kuposa zosangalatsa. Zina mwa izo ndi milungu yonyenga.

Kanani Milungu Yopanda Pake

5. Kodi nthawi zambiri mawu akuti “zopanda pake” mu Chiheberi choyambirira amanena za chiyani?

5 Chochititsa chidwi ndi chakuti mu Chiheberi choyambirira, nthawi zambiri mawu akuti “zopanda pake” amanena za milungu yonyenga. Mwachitsanzo, Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Musamadzipangira mafano [“milungu yopanda pake,” NW], kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m’dziko mwanu kuugwadira umene.” (Lev. 26:1) Ndipo Mfumu Davide inalemba kuti: “Yehova ali wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse. Pakuti milungu ya mitundu ya anthu ndiyo mafano [“milungu yopanda pake,” NW]; koma Yehova analenga zakumwamba.”​—1 Mbiri 16:25, 26.

6. Kodi ndi chifukwa chiyani milungu yonyenga ili yopanda pake?

6 Monga mmene Davide anasonyezera, umboni wakuti Yehova ndi wamkulu uli ponseponse. (Sal. 139:14; 148:1-10) Aisiraeli anali pa ubale ndi Yehova chifukwa chakuti anachita nawo pangano. Umenewo unali mwayi wapadera kwambiri. Ngakhale zinali choncho, iwo anamusiya Yehovayo ndi kuyamba kugwadira mafano osema ndi zipilala zopatulika. Zimene anachitazi zinali zopanda nzeru. Panthawi yamavuto, milungu yawo yonyenga ija inakhaladi yopanda pake, chifukwa sinathe kuwapulumutsa kapena kudzipulumutsa yokha.​—Ower. 10:14, 15; Yes. 46:5-7.

7, 8. Kodi zingatheke bwanji “Chuma” kukhala mulungu?

7 Masiku ano, anthu m’mayiko ambiri amagwadirabe mafano opangidwa ndi anthu, ndipo milungu imeneyo ndi yopanda ntchito ngati mmene inalili kale. (1 Yoh. 5:21) Komabe, kuwonjezera pa mafano Baibulo limatchulanso zinthu zina kuti ndi milungu. Mwachitsanzo, taganizirani mawu a Yesu akuti: “Kapolo sangatumikire ambuye awiri; pakuti adzadana ndi mmodzi ndi kukonda winayo, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”​—Mat. 6:24.

8 Kodi zingatheke bwanji “Chuma” kukhala mulungu? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tiganizire za mwala umene uli m’munda, m’nthawi ya Aisiraeli. Mwala umenewo akanatha kumangira nyumba kapena mpanda. Koma mwala womwewo akanati aupange “choimiritsa” kapena “mwala wozokota,” ukanakhala chopunthwitsa anthu a Yehova. (Lev. 26:1) Mofanana ndi zimenezi, ndalama zili ndi ntchito yake. Timafunikira ndalama kuti tipeze zofunika pamoyo, ndipo tingazigwiritse ntchito bwino potumikira Yehova. (Mlal. 7:12; Luka 16:9) Koma mtima wathu ukakhala pa kufunafuna ndalama m’malo motsogoza utumiki wathu wachikhristu, pamenepo ndalamazo zimakhala mulungu wathu. (Werengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Popeza kuti anthu m’dzikoli amafuna kwambiri kulemera, ifeyo tionetsetse kuti nkhani ya ndalamayi tikuiona bwino.​—1 Tim. 6:17-19.

9, 10. (a) Kodi Mkhristu amawaona bwanji maphunziro? (b) Kodi maphunziro apamwamba ali ndi vuto lotani?

9 Chinthu china chofunika koma chimene chingakhale chopanda pake ndi maphunziro akusukulu. Ife timafuna kuti ana athu aphunzire kuti akaphunzira, adzakhale ndi moyo wodzidalira. Chofunika kwambiri ndi chakuti, Mkhristu amene waphunzira bwino amatha kuwerenga Baibulo ndi kulimvetsa. Akakumana ndi mavuto, amaganizira mofatsa ndi kupeza njira zowathetsera, ndiponso Mkhristu wotero amaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo momveka komanso mokopa anthu. Zimatenga nthawi yaitali kuti munthu aphunzire bwino, koma zimenezi ndi zofunika.

10 Nanga bwanji za maphunziro apamwamba a kukoleji kapena kuyunivesite? Anthu ambiri amakhulupirira kuti maphunziro amenewa ndi ofunika kwambiri kuti munthu atukule moyo wake. Komabe, ambiri amene amachita maphunzirowa amadzaza mitu yawo ndi nzeru zopanda phindu za dzikoli. Maphunziro otero amangowononga zaka zamtengo wapatali za unyamata zimene munthu akanazigwiritsa ntchito bwino kutumikira Yehova. (Mlal. 12:1) Mwina ndiye chifukwa chake m’mayiko amene anthu ambiri amachita maphunziro apamwamba, ndi anthu ochepa kwambiri amene amakhulupirira Mulungu. Koma Mkhristu pofuna kukonza tsogolo lake, amadalira Yehova osati maphunziro apamwamba a dzikoli.​—Miy. 3:5.

Musalole Kuti Chilakolako cha Thupi Chikhale Mulungu Wanu

11, 12. Kodi ndi chifukwa chiyani pofotokoza za anthu ena, Paulo anati: “Mulungu wawo ndi mimba yawo”?

11 Polembera kalata Afilipi, mtumwi Paulo anatchula chinthu china chimene chingakhalenso mulungu. Anafotokoza za olambira anzake ndipo anati: “Alipo ambiri amene ndinali kuwatchula kawirikawiri, koma tsopano ndikuwatchula ndi misozi, amene akuyenda monga adani a mtengo wozunzikirapo wa Khristu. Amenewo mathero awo ndi chiwonongeko, ndipo mulungu wawo ndi mimba yawo . . . Ndipo maganizo awo ali pa zinthu za dziko lapansi.” (Afil. 3:18, 19) Kodi zingatheke bwanji kuti mimba ya munthu ikhale mulungu?

12 Zikuoneka kuti vuto la anzake a Paulowo linali lakuti anakulitsa mtima wofuna kukhutiritsa zilakolako zawo za thupi, m’malo motumikira Yehova limodzi ndi Paulo. Mwina ena anali kudya ndi kumwa mopitirira muyeso mpaka kukhala anthu osusuka kapena zidakwa. (Miy. 23:20, 21; yerekezerani ndi Deuteronomo 21:18-21.) Mwinanso ena anapezerapo mwayi pa mpata wotukula moyo wawo ndi wosangalala, umene dziko linapereka kalelo ndipo anasiya kutumikira Yehova. Ifeyo tisalole mtima wofuna zinthu zimene anthu amati ndiye moyowo kuti utilepheretse kutumikira Yehova ndi moyo wonse.​—Akol. 3:23, 24.

13. (a) Kodi kusirira kwa nsanje ndi chiyani, ndipo Paulo anakufotokoza bwanji? (b) Kodi tingapewe bwanji kusirira kwa nsanje?

13 Paulo anatchulanso mbali ina ya kulambira konyenga. Analemba kuti: “Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.” (Akol. 3:5) Kusirira kwa nsanje ndiko kulakalaka mwamphamvu chinthu chomwe si chathu. Munthu angasirire mwansanje chuma. Ngakhalenso chilakolako chofuna kugonana ndi munthu amene suli naye pabanja ndi kusirira kwa nsanje. (Eks. 20:17) Kodi pamenepa sitinganene kuti imeneyi ndi nkhani yaikulu, tikaganizira kuti munthu amene ali ndi zilakolako zoterezi amapembedza mafano kapena kuti amalambira milungu yonyenga? Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lamphamvu kwambiri pofuna kusonyeza kuti tifunika kuchita chilichonse chotheka kuti tithetse zilakolako zoipa.​—Werengani Maliko 9:47; 1 Yoh. 2:16.

Chenjerani ndi Mawu Opanda Pake

14, 15. (a) Kodi “chinthu chachabe” chimene chinapunthwitsa anthu ambiri m’nthawi ya Yeremiya ndi chiyani? (b) Kodi ndi chifukwa chiyani mawu a Mose anali aphindu?

14 Mawunso angakhale m’gulu la zinthu zopanda pake. Mwachitsanzo, Yehova anauza Yeremiya kuti: ‘Aneneri anenera zonama m’dzina langa; sindinatuma iwo, sindinauza iwo, sindinanena nawo; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wawo.’ (Yer. 14:14) Aneneri onyengawo anali kunamiza anthu kuti akulankhula m’dzina la Yehova, pamene anali kulankhula za m’mutu mwawo. Motero mawu awo anali “chinthu chachabe.” Anali opanda pake ndipo anali owononga mwauzimu. Mu 607 B.C.E., anthu ambiri amene anatsatira mawu opanda pakewo anaphedwa mosayembekezeka ndi asilikali a ku Babulo.

15 Mosiyana ndi aneneriwo, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Ikani mitima yanu pa mawu onse ndikuchitirani nawo mboni lero . . . Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu, ndipo mwa chinthu ichi mudzachulukitsa masiku anu m’dziko limene muwolokera Yordano, kulilandira.” (Deut. 32:46, 47) Indedi, mawu a Mose anali ouziridwa ndi Mulungu. Motero anali aphindu ndi ofunika kwambiri ku mtunduwo kuti zinthu ziwayendere bwino. Anthu amene anamvera mawuwo anakhala ndi moyo wautali ndi wotukuka. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizikana mawu opanda pake ndipo tizimvera mawu aphindu a choonadi.

16. Kodi mfundo zotsutsana ndi Mawu a Mulungu zimene asayansi amanena timaziona bwanji?

16 Kodi ife masiku ano timamva anthu akulankhula mawu opanda pake? Inde timamva. Mwachitsanzo, asayansi ena amanena kuti chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusinthika ndiponso zinthu zosiyanasiyana zimene iwo apeza, zikusonyeza kuti palibenso chifukwa chokhulupirira kuti kuli Mulungu, komanso zikusonyeza kuti zinthu zonse zinangokhalako zokha. Kodi ife tiyenera kuda nkhawa ndi mawu otumbwa ngati amenewa? Ayi. Nzeru za anthu ndi zosiyana ndi za Mulungu. (1 Akor. 2:6, 7) Ndiponso ife timadziwa kuti ziphunzitso za anthu zikasiyana ndi zimene Mulungu watiphunzitsa, ziphunzitso za anthuzo nthawi zonse ndi zimene zimakhala zolakwika. (Werengani Aroma 3:4.) Ngakhale kuti sayansi yapita patsogolo m’zinthu zambiri, zimene Baibulo limanena pa nzeru za anthu sizisintha. Ilo limati: “Kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa.” Inde, nzeru za anthu ndi zopanda pake ndipo sizingafanane ngakhale pang’ono ndi nzeru za Mulungu zopanda malire.​—1 Akor. 3:18-20.

17. Kodi mawu a atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu ndiponso a anthu ampatuko tiyenera kuwaona bwanji?

17 Mawu enanso opanda pake amalankhulidwa ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu. Iwo amati amalankhula m’dzina la Mulungu, koma zambiri zimene amalankhula sizichokera m’Malemba, ndipo zimakhala zachabechabe. Ampatuko nawonso amalankhula mawu opanda pake ndipo amaganiza kuti ali ndi nzeru zambiri kuposa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anachita kusankhidwa. (Mat. 24:45-47) Komatu, ampatuko amalankhula za m’mutu mwawo ndipo mawu awo ndi opanda pake, ndiponso angapunthwitse munthu aliyense wowamvetsera. (Luka 17:1, 2) Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti asatisocheretse?

Kodi Tingakane Bwanji Mawu Opanda Pake?

18. Kodi uphungu wopezeka pa 1 Yohane 4:1 tingautsatire bwanji?

18 Mtumwi wokalamba Yohane, anapereka uphungu wabwino pankhani imeneyi. (Werengani 1 Yohane 4:1.) Mogwirizana ndi uphungu wa mtumwiyu, timalimbikitsa anthu onse amene timakumana nawo tikamalalikira kuti aziyesa zimene amaphunzitsidwa poziyerekeza ndi Baibulo. Mfundoyi ndi yabwinonso kwa ife. Tikamva mawu onyoza choonadi kapena oipitsa mbiri ya mpingo, ya akulu kapena ya m’bale wathu aliyense, sitithamangira kukhulupirira mawuwo. M’malo mwake timadzifunsa kuti: “Kodi munthu amene akufalitsa nkhanizi, akuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena? Kodi nkhanizi zikupititsa patsogolo zolinga za Yehova? Kodi zikulimbikitsa mtendere mumpingo? Chilichonse chimene tingamve chomwe chimapasula ubale wathu, m’malo momanga ubalewo, ndi chinthu chopanda pake.​—2 Akor. 13:10, 11.

19. Kodi akulu amaonetsetsa bwanji kuti mawu awo asakhale opanda pake?

19 Pankhani ya mawu opanda pake, akulunso ayenera kutengapo phunziro lofunika kwambiri. Akamapereka uphungu kwa munthu, amakumbukira kuti iwonso ndi anthu omwe amalephera ndiponso sadziwa zonse. Choncho, sapereka uphunguwo kuchokera mu nkhokwe ya nzeru zawo. Koma nthawi zonse iwo ayenera kugwiritsa ntchito zimene Baibulo limanena. Mtumwi Paulo ananena mfundo yofunika kwambiri yakuti: “Musapitirire zinthu zolembedwa.” (1 Akor. 4:6) Akulu sayenera kupitirira zinthu zolembedwa m’Baibulo. Ndiponso, sayenera kupitirira uphungu wa m’Baibulo wolembedwa m’mabuku a kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.

20. Kodi chingatithandize ndi chiyani kukana zinthu zopanda pake?

20 Zinthu zopanda pake, kaya zikhale “milungu,” mawu kapena china chilichonse, ndi zoipa ndithu. Pachifukwa chimenechi, tiyenera nthawi zonse kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kuzindikira zinthu zopanda pake ndi kudalira malangizo ake kuti tikane zinthuzo. Tikamachita zimenezi, timagwirizana ndi zimene wamasalmo ananena, kuti: “Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe, mundipatse moyo mu njira yanu.” (Sal. 119:37) Mu nkhani yotsatira, tidzapitiriza kukambirana ubwino wotsatira malangizo a Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi ndi “zinthu zopanda pake” ziti zimene tiyenera kuzikana?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ndalama zisakhale mulungu wathu?

• Kodi zilakolako zathupi zingakhale bwanji kupembedza mafano?

• Kodi tingakane bwanji mawu opanda pake?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 3]

Aisiraeli analimbikitsidwa ‘kulima minda yawo,’ osati kutsata zinthu zopanda pake

[Chithunzi patsamba 5]

Musalole mtima wofuna zinthu zakuthupi kuti ukulepheretseni kutumikira Yehova

[Chithunzi patsamba 6]

Mawu a akulu angakhale opindulitsa kwambiri