Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukwatira Ndiponso Kukhala ndi Ana M’nthawi Yamapeto Ino

Kukwatira Ndiponso Kukhala ndi Ana M’nthawi Yamapeto Ino

Kukwatira Ndiponso Kukhala ndi Ana M’nthawi Yamapeto Ino

“Nthawi yotsalayi yafupika.”​—1 AKOR. 7:29.

1. (a) Kodi zinthu zasintha bwanji ‘m’nthawi yovuta’ ino? (b) Kodi n’chifukwa chiyani kusintha kwa zinthu m’banja kukudetsa nkhawa?

MAWU a Mulungu ananeneratu za “nthawi ya chimaliziro” kuti kudzakhala nkhondo, zivomezi, njala ndi miliri. (Dan. 8:17, 19; Luka 21:10, 11) Baibulo linachenjezanso kuti nthawi yovuta imeneyi m’mbiri ya anthu, zinthu zidzasintha kwambiri. Linati mavuto a m’banja adzakhala zina mwa zinthu ‘zovuta m’masiku otsiriza.’ (2 Tim. 3:1-4) N’chifukwa chiyani zimenezi zikudetsa nkhawa? N’chifukwa chakuti zikuchitika kulikonse ndipo zili ndi mphamvu kwambiri yosintha mmene Akhristu masiku ano amaonera kukwatira ndi kukhala ndi ana. Motani?

2. Kodi anthu ambiri m’dzikoli amauona bwanji ukwati ndi kusudzulana?

2 Masiku ano, kusudzulana si kovuta ndipo kwafala kwambiri. M’mayiko ambiri anthu amene akusudzulana akuchuluka. Komabe ife tiyenera kukumbukira bwino kuti Yehova Mulungu amaona ukwati ndi kusudzulana mosiyana kwambiri ndi mmene anthu ambiri m’dzikoli amaonera. Kodi Yehova amaiona bwanji nkhani imeneyi?

3. Kodi Yehova ndi Yesu Khristu amauona bwanji ukwati?

3 Yehova Mulungu amafuna kuti anthu okwatirana akhale okhulupirika. Yehova atakwatitsa mwamuna ndi mkazi pachiyambi, anati ‘mwamuna . . . adzadziphatika kwa mkazi wake, ndipo adzakhala thupi limodzi.’ Yesu Khristu ananenanso zimenezi ndipo anawonjezera kuti: “Choncho, chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” Kenako iye anati: “Aliyense wosudzula mkazi wake ndi kukwatira wina achita chigololo.” (Gen. 2:24; Mat. 19:3-6, 9) Motero, Yehova ndi Yesu amaona ukwati kuti ndi mgwirizano wa moyo wonse, umene umatha wina akamwalira. (1 Akor. 7:39) Popeza kuti ukwati ndi wopatulika, chisudzulo si nkhani yamasewera. Ndipotu, Mawu a Mulungu amati Yehova amadana ndi kusudzulana popanda zifukwa za m’Malemba. *​—Werengani Malaki 2:13-16; 3:6.

Ukwati Si Nkhani Yamasewera

4. N’chifukwa chiyani Akhristu ena achinyamata amadandaula kuti anathamangira kukwatira?

4 Dziko losaopa Mulungu limene tikukhalali limakonda zachiwerewere. Tsiku ndi tsiku timaona zinthu zolaula. Ndipo zinthu zimenezi zingatikhudze, makamaka achinyamata athu mumpingo. Ndiyeno kodi Akhristu achinyamata angachite chiyani ndi zinthu zimenezi, zimene zimayambitsa chilakolako cha kugonana ngakhale ngati mtima wawo sukufuna? Pofuna kuti asamavutike ndi chilakolakocho, ena amakwatira ali ndi zaka zochepa kwambiri. Iwo amaganiza kuti kuchita zimenezi kungawathandize kupewa chiwerewere. Koma pasanapite nthawi, ambiri amayamba kudandaula kuti anafulumira kukwatira. N’chifukwa chiyani amatero? Amati chisangalalo chakuti alowa mu ukwati chikangotha, amayamba kuzindikira kuti akusiyana maganizo pa zinthu zambiri. Zikatero, amakhala pa mavuto aakulu.

5. Kodi n’chiyani chingathandize okwatirana kukhalabe okhulupirika pa malumbiro awo a ukwati? (Onani mawu a m’munsi.)

5 Kukwatirana ndi munthu yemwe alibe makhalidwe amene munali kuyembekezera, ngakhale atakhala Mkhristu mnzanu, kungayambitse mavuto aakulu. (1 Akor. 7:28) Koma kaya zinthu zivute bwanji, Akhristu oona amadziwa kuti kusudzulana popanda chifukwa cha m’Malemba, si njira yabwino yothetsera mavuto a m’banja. Choncho, anthu amene amayesetsa kuti ukwati wawo usathe chifukwa chofuna kukhalabe okhulupirika pa malumbiro awo a ukwati, amafunika kuyamikiridwa ndi kuthandizidwa ndi mpingo wachikhristu. *

6. Kodi Akhristu achinyamata ayenera kuiona bwanji nkhani yokwatira?

6 Kodi ndinu wachinyamata wosakwatira? Ngati ndi choncho, kodi nkhani yokwatira muyenera kuiona bwanji? Mungapewe mavuto ngati mudikira mpaka mutakula ndi kukhwima m’maganizo ndi mwauzimu, musanayambe chibwenzi ndi Mkhristu mnzanu. Ndi zoona kuti Malemba sanena zaka zimene munthu ayenera kukwatira. * Komabe, Baibulo limasonyeza kuti ndi bwino kudikira mpaka itadutsa nthawi imene chilakolako cha kugonana chimakhala champhamvu kwambiri. (1 Akor. 7:36) N’chifukwa chiyani mufunikira kudikira? Chifukwa chilakolako champhamvu cha kugonana chingasokoneze kuganiza kwanu ndipo mungachite zinthu mopanda nzeru, mpaka kugwa m’mavuto. Kumbukirani kuti malangizo a Yehova a ukwati a m’Baibulo ndi anzeru ndipo angakuthandizeni kukhala ndi moyo wosangalala.​—Werengani Yesaya 48:17, 18.

Kukhala ndi Ana Ndi Udindo Waukulu

7. Kodi anthu amene amakwatirana ali ana amakumana ndi zotani, ndipo zimenezi zingayambitse mavuto otani?

7 Ambiri amene amalowa m’banja ali ana, amapezeka kuti akuyembekezera mwana iwo asanakule n’komwe. Pamene mwana akubadwa, yemwe amafuna chisamaliro usana ndi usiku, iwo amakhala asanadziwane bwinobwino. Mayiyo mwachibadwa amasamala kwambiri za mwanayo, ndipo mwamunayo amayamba nsanje. Ndiponso chifukwa chosowa tulo, iwo amatopa ndipo amayamba kukangana pafupipafupi. Kenako amazindikira kuti alibenso ufulu umene anali nawo. Tsopano satha kuyenda mmene akufunira ndi kuchita zinthu mwaufulu ngati kale. Kodi iwo angachite chiyani ndi kusintha kwa zinthu kumeneku?

8. Kodi kukhala ndi ana tiyenera kukuona bwanji, ndipo n’chifukwa chiyani?

8 Mofanana ndi ukwati, kukhala ndi ana ndi mwayi komanso ndi udindo waukulu wochokera kwa Mulungu. Kaya moyo wa makolo achikhristu usinthe bwanji mwana akabadwa, iwo amafunika kuchita zinthu mwauchikulire. Popeza kuti Yehova ndi amene anapatsa anthu mphamvu yotha kukhala ndi ana, makolo ayenera kuona mwana wawo wakhanda monga “cholandira cha kwa Yehova.” (Sal. 127:3) Makolo achikhristu amayesetsa kukwaniritsa udindo wawo “mwa Ambuye.”​—Aef. 6:1.

9. (a) Kodi kulera mwana kumafuna chiyani? (b) Kodi mwamuna angathandize bwanji mkazi wake kukhalabe wolimba mwauzimu?

9 Kulera mwana mpaka kukula kumatenga zaka zambiri ndipo kumafuna kudzipereka. Kumafuna nthawi ndiponso mphamvu. Mwamuna wachikhristu amafunika kumvetsa kuti kwa zaka zingapo mwana akabadwa, mkazi wake azidodometsedwa pa misonkhano ndipo azikhala ndi nthawi yochepa yophunzira Baibulo ndi kusinkhasinkha. Chifukwa cha zimenezi angafooke mwauzimu. Kulera bwino mwana kumafuna kuti mwamuna achite chilichonse chimene angathe kuti athandize mkazi wake kusamalira mwanayo. Pofuna kuthandiza mkaziyo kuti mfundo zina za kumsonkhano zisamam’pite, mwamuna amafunika kukambirana naye mfundozo kunyumba. Angafunikirenso kuthandiza mkazi wake kusamalira mwanayo kuti mkaziyo akhale ndi nthawi yokwanira yolalikira za Ufumu.​—Werengani Afilipi 2:3, 4.

10, 11. (a) Kodi ana angaphunzitsidwe bwanji ‘kalingaliridwe ka Yehova’? (b) N’chifukwa chiyani makolo ambiri achikhristu amafunika kuyamikiridwa?

10 Kulera bwino ana kumafuna zambiri osati kungowapatsa chakudya, zovala, pogona ndi thandizo la mankhwala. Makamaka m’nthawi yovuta ino yamapeto, ana ayenera kuphunzitsidwa mfundo za makhalidwe abwino kuyambira ali aang’ono. Ayenera kuleredwa “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aef. 6:4) Kuphunzitsa mwana “kalingaliridwe” kameneka kumatanthauza kutenga maganizo a Yehova ndi kuwaika m’mtima mwake, kungoyambira ali khanda mpaka zaka zovuta zaunyamata.​—2 Tim. 3:14, 15.

11 Pamene Yesu anauza ophunzira ake kuti ‘apange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse,’ n’zosakayikitsa kuti anafunanso kuti makolo apange ana awo kukhala ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Kuchita zimenezi n’kovuta chifukwa achinyamata akukumana ndi zambiri m’dzikoli. Choncho, makolo amene amakwanitsa kulera bwino ana awo mpaka kukhala Akhristu odzipereka, amafunika kuyamikiridwa kwambiri ndi onse mumpingo. Iwo ‘agonjetsa’ dziko chifukwa cha chikhulupiriro chawo ndiponso chifukwa chosanyalanyaza udindo wawo.​—1 Yoh. 5:4.

Chifukwa Chabwino Chokhalira Wosakwatira Kapena Wopanda Ana

12. N’chifukwa chiyani Akhristu ena amatenga zaka zambiri asanakwatire?

12 Popeza “nthawi yotsalayi yafupika” ndiponso “zochitika za padzikoli zikusintha,” Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuganizira za ubwino wokhala wosakwatira. (1 Akor. 7:29-31) Pachifukwa chimenechi, Akhristu ena amasankha kusakwatira moyo wawo wonse kapena kukhala zaka zambiri asanakwatire. N’zosangalatsa kuti sagwiritsa ntchito modzikonda ufulu umene munthu wosakwatira amakhala nawo. Ambiri amakhala osakwatira kuti atumikire Yehova “popanda chocheutsa.” (Werengani 1 Akorinto 7:32-35.) Akhristu ena osakwatira akuchita upainiya kapena ali pa Beteli. Enanso ambiri amapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, kuti athandize kwambiri m’gulu la Yehova. Ndipotu anthu amene anachita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri asanakwatire ndipo kenako n’kukwatira, nthawi zambiri amaona kuti zimene anaphunzira panthawiyo zikuwathandiza kwambiri mu ukwati wawo panopa.

13. N’chifukwa chiyani mabanja ena achikhristu asankha kusakhala ndi ana?

13 M’mayiko ena, moyo wa banja wasintha chifukwa anthu ambiri akusankha kusakhala ndi ana. Ena amachita zimenezi chifukwa cha mavuto a zachuma kapena chifukwa chofuna kukhala ndi mpata wabwino wopitiriza maphunziro. Palinso Akhristu ena amene amasankha kusakhala ndi ana. Koma iwo amachita zimenezi kuti akhale ndi mpata wokwanira wotumikira Yehova. Zimenezi sizikutanthauza kuti Akhristu amenewa sasangalala ndi ukwati wawo. Iwo amasangalala, koma kungoti amafuna kuika zinthu za Ufumu patsogolo pa madalitso amene angapeze m’banja. (1 Akor. 7:3-5) Ena a mabanja amenewa akutumikira Yehova ndi abale awo m’ntchito yadera, yachigawo kapena pa Beteli. Ena ndi apainiya kapena amishonale. Yehova sadzaiwala ntchito yawo ndi chikondi chimene amachisonyeza pa dzina lake.​—Aheb. 6:10.

“Nsautso M’thupi”

14, 15. Kodi “nsautso m’thupi” imene makolo achikhristu angakumane nayo ndi chiyani?

14 Mtumwi Paulo anauza Akhristu okwatira kuti adzakhala ndi “nsautso m’thupi mwawo.” (1 Akor. 7:28) Zimenezi zingaphatikizepo iwowo kudwala, ana awo kapena makolo awo okalamba. Mwinanso zingakhale mavuto okhudzana ndi kulera ana. Monga tanenera kumayambiriro kwa nkhani ino, Baibulo linaneneratu kuti nthawi ya “masiku otsiriza” idzakhala “yovuta.” Ena mwa mavutowa ndi ana “osamvera makolo.”​—2 Tim. 3:1-3.

15 Kulera ana ndi ntchito yaikulu kwa makolo achikhristu. Mavuto a “nthawi yovuta” ino amatikhudza. N’chifukwa chake kuti ateteze ana awo, makolo achikhristu amafunika kupitirizabe kumenya nkhondo yolimbana ndi zinthu zoipa za “dongosolo la zinthu la m’dzikoli.” (Aef. 2:2, 3) Ndipo nthawi zina sapambana nkhondoyo. Mwana wa m’banja lachikhristu akasiya kutumikira Yehova, makolo amene ayesetsa kulera mwanayo m’choonadi amakhala ndi “nsautso.”​—Miy. 17:25.

“Kudzakhala Chisautso Chachikulu”

16. Kodi Yesu ananeneratu za “chisautso” chotani?

16 “Nsautso,” kapena kuti mavuto alionse amene munthu angakumane nawo pankhani ya ukwati ndi kulera ana, ndi ochepa poyerekeza ndi chisautso chachikulu chimene chikubwera. Mu ulosi wonena za kukhalapo kwake ndi mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anati: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:3, 21) Kenako, Yesu anadzavumbula kuti khamu lalikulu lidzapulumuka “chisautso chachikulu” chimenechi. Komabe panthawi imeneyo, dongosolo la Satana lidzapitiriza kulimbana ndi Mboni za Yehova zokonda mtendere. Mosakayikira, nthawi imeneyi idzakhala yovuta kwa tonsefe, ana ndi akulu omwe.

17. (a) Kodi ndi chifukwa chiyani sitiyenera kuda nkhawa kwambiri tikamaganizira za m’tsogolo? (b) Kodi ndi chiyani chingatithandize kuiona bwino nkhani ya kukwatira ndi kukhala ndi ana?

17 Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti tizikhala ndi nkhawa kwambiri tikamaganizira za m’tsogolo. Makolo okhulupirika kwa Yehova angayembekeze kudzatetezedwa limodzi ndi ana awo aang’ono. (Werengani Yesaya 26:20, 21; Zef. 2:2, 3; 1 Akor. 7:14) Koma pakali pano, tiyeni tiziiona bwino nkhani ya kukwatira ndi kukhala ndi ana, podziwa kuti masiku athu ndi ovuta ndiponso kuti tili m’nthawi ya mapeto. (2 Pet. 3:10-13) Tikatero, kaya ndife okwatira kapena ayi, kaya tili ndi ana kapena tilibe, moyo wathu udzalemekeza ndi kutamanda Yehova ndi mpingo wachikhristu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani buku lachingelezi lakuti Live With Jehovah’s Day in Mind pakamutu kakuti “He Has Hated a Divorcing (Amadana ndi Kusudzulana),” patsamba 125.

^ ndime 5 Anthu amene akukumana ndi mavuto a m’banja angathandizidwe atawerenga nkhani zokhudza ukwati monga zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 2003 ndi mu Galamukani! ya January 8, 2001.

^ ndime 6 Onani mutu 30, wakuti: “Kodi Ndili Wokonzekera Ukwati?” m’buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandiza.

Tibwereze

• Kodi ndi chifukwa chiyani Akhristu achinyamata safunika kuthamangira kukwatira?

• Kodi kulera mwana kumafuna chiyani?

• Kodi ndi chifukwa chiyani Akhristu ambiri amasankha kusakwatira kapena ngati akwatira, kukhala opanda ana?

• Kodi ndi “nsautso” yotani imene makolo achikhristu angakumane nayo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

N’chifukwa chiyani ndi bwino kuti Akhristu achinyamata asamathamangire kukwatira?

[Chithunzi patsamba 18]

Mwamuna angachite zambiri kuti athandize mkazi wake kukhala ndi mpata wochita zinthu zauzimu

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi ndi chifukwa chiyani mabanja ena achikhristu asankha kukhala opanda ana?