Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane

Mawu a Yehova Ndi Amoyo

Mfundo Zazikulu za M’buku la Yohane

YOHANE, “wophunzira amene Yesu anali kum’konda,” ndi munthu womaliza kulemba za moyo ndi utumiki wa Khristu. (Yoh. 21:20) Uthenga Wabwino wa Yohane, wolembedwa cha mu 98 C.E., uli ndi nkhani zambiri zomwe sizipezeka m’mabuku ena atatu a Uthenga Wabwino.

Mtumwi Yohane analemba uthenga wake wabwino ndi cholinga chapadera. Ponena za zomwe analemba, iye anati: “Izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu alidi Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kutinso, mwa kukhulupirira, mukhale ndi moyo m’dzina lake.” (Yoh. 20:31) Uthenga wake ndi wofunikiradi kwa ife.​—Aheb. 4:12.

“TAONANI, MWANA WANKHOSA WA MULUNGU”

(Yoh. 1:1–11:54)

Atangoona Yesu, Yohane Mbatizi anafuula kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!” (Yoh. 1:29) Pamene Yesu amalalikira ndi kuphunzitsa komanso kuchita zozizwitsa zambiri ku Samariya, Galileya, Yudeya ndi kudera la kum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano, ‘anthu ambiri anabwera ndipo anakhulupirira mwa iye.’​—Yoh. 10:41, 42.

Kuukitsidwa kwa Lazaro ndi chimodzi mwa zozizwitsa zodziwika bwino za Yesu. Anthu ambiri anayamba kukhulupirira Yesu ataona kuti munthu amene anali wakufa kwa masiku anayi waukitsidwa. Koma ansembe aakulu ndi Afarisi anakambirana zoti aphe Yesu. N’chifukwa chake Yesu anachoka ndi kupita “kudera lina lapafupi ndi chipululu, mu mzinda wotchedwa Efuraimu.”​—Yoh. 11:53, 54.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

1:35, 40—Kuwonjezera pa Andireya, kodi ndi wophunzira winanso uti amene anaima pamodzi ndi Yohane Mbatizi? Munthu yemwe analemba nkhaniyi nthawi zonse anali kugwiritsa ntchito dzina lakuti “Yohane” ponena za Yohane Mbatizi ndipo sanadzitchule dzina mu uthenga wake wabwino. Choncho, zikuoneka kuti wophunzira amene sanatchulidwe dzinayo ndi Yohane yemwe analemba Uthenga Wabwinowu.

2:20—Kodi kachisi amene “anam’manga zaka 46” ndi uti? Ayuda anali kunena za kachisi wa Zerubabele amene anamangidwanso ndi Mfumu Herode ya Yudeya. Malinga ndi Josephus, katswiri wa mbiri yakale, ntchito imeneyi inayamba m’chaka cha 18 cha ulamuliro wa Herode, mu 18 kapena 17 B. C. E. Kachisiyo ndiponso nyumba zina zikuluzikulu zinamangidwa kwa zaka 8. Komabe ntchito yomanga zinthu zina ndi zina pakachisipo inapitirirabe mpaka atadutsa Pasika wa mu 30 C. E. N’chifukwa chake Ayuda anati kachisiyo anam’manga zaka 46.

5:14—Kodi munthu amadwala chifukwa chakuti wachita tchimo? Osati nthawi zonse. Munthu yemwe Yesu anam’chiritsa anadwala zaka 38 chifukwa cha kupanda ungwiro kobadwa nako. (Yoh. 5:1-9) Apa Yesu anatanthauza kuti popeza munthuyo wachitiridwa chifundo, ayenera kutsatira njira ya chipulumutso ndi kusachimwanso dala kuopera kuti chinthu china choopsa kuposa matenda chingamuchitikire. Munthuyo akanatha kupalamula tchimo losakhululukidwa, lomwe chilango chake ndi imfa yopanda chiukiriro.​—Mat. 12:31, 32; Luka 12:10; Aheb. 10:26, 27.

5:24, 25—Kodi ndani amene ‘amachoka ku imfa kuwolokera ku moyo’? Apa Yesu akunena za anthu amene anali akufa mwauzimu koma atamva mawu ake, anayamba kumukhulupirira ndi kusiya kuyenda m’machimo awo. Iwo ‘amachoka ku imfa kuwolokera ku moyo’ chifukwa chakuti amawachotsera chilango cha imfa, ndipo amapatsidwa chiyembekezo cha moyo wosatha kaamba kokhulupirira Mulungu.​—1 Pet. 4:3-6.

5:26; 6:53—Kodi kukhala ndi ‘moyo mwa ife tokha’ kumatanthauza chiyani? Kwa Yesu Khristu, zimenezi zimatanthauza kupatsidwa ndi Mulungu mphamvu za mitundu iwiri. Yoyamba ndi yothandizira anthu kukhala ndi mbiri yabwino kwa Yehova, ndipo yachiwiri ndi yopereka moyo mwa kuukitsa akufa. Kwa otsatira a Yesu, ‘kukhala ndi moyo mwa iwo okha’ kumatanthauza kukhala ndi moyo wokwanira. Akhristu odzozedwa amalandira moyo umenewu akaukitsidwa ndi kupita kumwamba. Anthu okhulupirika amene akuyembekeza kudzakhala pa dziko lapansi adzakhala ndi moyo wokwanira atapambana chiyeso chomaliza, chomwe chidzachitika utangotha Ulamuliro wa Khristu wa Zaka 1,000.​—1 Akor. 15:52, 53; Chiv. 20:5, 7-10.

6:64—Posankha Yudasi Isikariyoti, kodi Yesu anadziwiratu kuti iye adzamupereka? Zikuoneka kuti sanadziwiretu. Komabe nthawi ina mu 32 C.E., Yesu anauza atumwi ake kuti: “Mmodzi wa inu ndi wodyerekeza.” Mwina panthawi imeneyi Yesu anaona ‘chiyambi’ cha mtima woipa mwa Yudasi Isikariyoti.​—Yoh. 6:66-71.

Zimene Tikuphunzirapo:

2:4. Apa Yesu anasonyeza Mariya kuti iye, monga mwana wobatizidwa ndi wodzozedwa wa Mulungu, ayenera kutsatira malangizo a Atate wake wakumwamba. Ngakhale kuti Yesu anali atangoyamba kumene utumiki wake, iye anali kudziwa bwino nthawi yochita ntchito imene anapatsidwa, kuphatikizapo imfa yake ya nsembe. Palibe wachibale wake aliyense, ngakhale Mariya, amene akanamusokoneza kuchita chifuniro cha Mulungu. Ifenso tikhale ndi mtima womwewo potumikira Yehova Mulungu.

3:1-9. Nkhani ya Nikodemo, wolamulira wa Ayuda, imatiphunzitsa zinthu ziwiri. Choyamba, Nikodemo anali wodzichepetsa, wozindikira zinthu ndiponso anali kudziwa zosowa zake zauzimu, chifukwa iye anazindikira kuti mwana wa wopala matabwa anali mphunzitsi wotumidwa ndi Mulungu. Akhristu oona masiku ano amafunikanso kukhala odzichepetsa. Chachiwiri, Nikodemo anachita mantha kukhala wophunzira pamene Yesu anali padziko lapansi. Mwina sanafune kukhala wophunzira chifukwa choopa anthu, kuganizira udindo wake m’Bungwe Lalikulu la Ayuda kapena chifukwa chokonda kwambiri chuma chake. Apa tikuphunzirapo mfundo yofunika kwambiri yakuti: Zinthu ngati zimenezi zisatilepheretse ‘kunyamula mtengo wathu wozunzikirapo ndi kutsatira Yesu mosalekeza.’​—Luka 9:23.

4:23, 24. Kuti Mulungu avomereze kulambira kwathu, kulambirako kuyenera kugwirizana ndi choonadi cha m’Baibulo ndipo kuyenera kutsogoleredwa ndi mzimu woyera.

6:27. Kugwirira ntchito “chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha” kumatanthauza kuchita khama kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu. Tikachita zimenezi timakhala osangalala.​—Mat. 5:3.

6:44. Yehova amasamala aliyense payekha. Iye amatikokera kwa Mwana wake kudzera mu ntchito yolalikira, ndiponso mwa mzimu wake woyera amatithandiza kumvetsa ndi kugwiritsa ntchito mfundo za choonadi.

11:33-36. Kumva chisoni si chizindikiro chakuti ndife osalimba mtima.

‘PITIRIZANI KUTSATIRA IYE’

(Yoh. 11:55–21:25)

Pasika wa mu 33 C.E. atayandikira, Yesu anabwerera ku Betaniya. Pa Nisani 9, iye analowa mu Yerusalemu atakwera mwana wa bulu. Pa Nisani 10, Yesu anapitanso ku kachisi. Poyankha pemphero lake lakuti dzina la Atate wake lilemekezedwe, mawu ochokera kumwamba anati: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”​—Yoh. 12:28.

Yesu ndi otsatira ake akuchita mwambo wa Pasika, iye anawapatsa malangizo omaliza ndipo anawapempherera. M’kupita kwa nthawi anamugwira, kumuweruza ndi kumupachika, ndipo kenako anaukitsidwa.

Kuyankha Mafunso a M’Malemba:

14:2—Kodi Yesu ‘anakawakonzera motani malo’ kumwamba otsatira ake okhulupirika? Yesu anakaonekera pamaso pa Mulungu ndi kupereka mtengo wa magazi ake. Izi zinachititsa kuti pangano latsopano liyambe kugwira ntchito. Kukonza maloko kunaphatikizapo kulandira kwake mphamvu ya Ufumu, ndipo zitatero otsatira ake odzozedwa anayamba kuukitsidwa ndi kupita kumwamba.​—1 Ates. 4:14-17; Aheb. 9:12, 24-28; 1 Pet. 1:19; Chiv. 11:15.

19:11—Polankhula ndi Pilato za munthu amene anamupereka, kodi Yesu anali kunena za Yudasi Isikariyoti? Yesu sanali kulankhula za Yudasi yekha kapena munthu wina wake, koma zikuoneka kuti anali kulankhula za anthu onse omwe anakhudzidwa ndi tchimo lomupha. Ena mwa anthu amenewa anali Yudasi, “ansembe aakulu ndi Bungwe Lalikulu lonse la Ayuda” ndiponso “anthu” amene ananyengereredwa kuti apemphe kumasulidwa kwa Baraba.​—Mat. 26:59-65; 27:1, 2, 20-22.

20:17—Kodi n’chifukwa chiyani Yesu anauza Mariya Mmagadala kuti asamukangamire? Zikuoneka kuti Mariya anakangamira kapena kuti kukakamira Yesu chifukwa choganiza kuti Yesuyo akwera kumwamba ndipo sadzamuonanso. Pofuna kumutsimikizira kuti nthawi yakuti akwere kumwamba inali isanakwane, Yesu anauza Mariya kuti asamukakamire koma apite kukadziwitsa ophunzira ake kuti wauka.

Zimene Tikuphunzirapo:

12:36. Kuti tikhale ‘ana a kuwala’ kapena kuti oonetsa kuwala, tifunikira kudziwa Mawu a Mulungu Baibulo, molondola. Kenako tiyenera kugwiritsa ntchito zimene tikudziwazo pothandiza anthu kuchoka mu mdima wauzimu kulowa m’kuwala kwa Mulungu.

14:6. Palibe njira ina imene Mulungu angatiyanjire kupatulapo mwa Yesu Khristu yekha basi. Tingakhale mabwenzi a Yehova kokha mwa kukhulupirira Yesu ndi kutsatira chitsanzo chake.​—1 Pet. 2:21.

14:15, 21, 23, 24; 15:10. Kumvera Mulungu kumatithandiza kuti tikhalabe m’chikondi chake ndi cha Mwana wake.​—1 Yoh. 5:3.

14:26; 16:13. Mzimu woyera wa Yehova umagwira ntchito ngati mphunzitsi ndipo umatikumbutsa zinthu. Umavumbulanso choonadi. Motero, ungatithandize kudziwa zambiri, kukhala anzeru, ozindikira ndiponso oganiza bwino. Choncho tizilimbikira kupemphera, makamaka kupempha mzimuwo.​—Luka 11:5-13.

21:15, 19. Petulo anafunsidwa ngati anakonda Yesu kuposa “izi,” kutanthauza nsomba zinali pomwepo. Motero apa Yesu anatsindika kufunika koti Petulo asankhe kutsatira Yesuyo kwa moyo wake wonse, m’malo mwa ntchito yake ya usodzi. Popeza taona nkhani za m’Mauthenga Abwino, tisasiye kukonda Yesu kwambiri kuposa china chilichonse chimene tingakopeke nacho. Inde, tiyeni tipitirize kumutsatira ndi mtima wonse.

[Chithunzi patsamba 31]

Kodi nkhani ya Nikodemo ikutiphunzitsa chiyani?