Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tisawaiwale Ngakhale Amakhala Kwaokha

Tisawaiwale Ngakhale Amakhala Kwaokha

Tisawaiwale Ngakhale Amakhala Kwaokha

MTUMWI Paulo analangiza Akhristu anzake kuti: “Tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka achibale athu m’chikhulupiriro.” (Agal. 6:10) Masiku ano timatsatirabe malangizo a m’Malemba amenewa, ndipo timayesetsa kupeza njira zochitira zabwino okhulupirira anzathu. Ena amene tiyenera kuwasonyeza chikondi mu mpingo wachikhristu ndi abale ndi alongo athu amene amakhala ku malo osungirako anthu okalamba.

Kumayiko ena, anthu okalamba amakhala pamodzi ndi achibale awo. Koma m’mayiko ena, anthu ambiri okalamba amakhala ku malo osungirako anthu okalamba. Akhristu ena okalamba amasungidwanso kumalo amenewa. Ndiyeno kodi amakumana ndi mavuto otani? Kodi angathane bwanji ndi mavuto awo ngati alibe achibale owasamalira? Kodi mpingo ungawathandize motani? Ndipo kodi ifeyo timapindula bwanji tikamakawaona pafupipafupi?

Mavuto a ku Malo Osungirako Okalamba

Akhristu okalamba akasamukira ku malo amenewa, angapezeke kuti ali m’gawo la mpingo wachilendo. Zimenezi zingachititse kuti Mboni za kumeneko zisamapite kukawaona pafupipafupi. Nthawi zambiri, okalambawa amakhala ndi anthu ambiri azikhulupiriro zina kumalo amenewa. Choncho, Akhristuwa angakumane ndi mavuto ambiri.

Mwachitsanzo, kumalo ena osungirako okalamba kumabwera anthu a zipembedzo zosiyanasiyana kudzachita mapemphero. Munthu wina wosamalira anthu okalamba ananena kuti: “Okalamba ena a Mboni amene satha kulankhula bwinobwino amatengeredwa ku mapemphero popanda kumva maganizo awo.” Nthawi zinanso, anthu ogwira ntchito kumalowa, amachita zinthu zambiri zothandiza okalamba koma amachita zimenezi pa tsiku lobadwa, pa Khirisimasi ndiponso pa Isitala. Mboni zinanso zapatsidwapo chakudya kumalo amenewa chimene chikumbumtima chawo sichiwalola kudya. (Mac. 15:29) Ngati titamawayendera abale ndi alongo athu okalambawa, tingawathandize kulimbana ndi mavuto amenewa.

Mmene Mpingo Ungathandizire

Akhristu oyambirira ankaona kuti ali ndi udindo wothandiza Akhristu okalamba amene analibe achibale oti awathandize. (1 Tim. 5:9) Chimodzimodzinso masiku ano, akulu amaonetsetsa kuti Akhristu okalamba amene akukhala ku malo osungirako okalamba a m’gawo lawo sakunyalanyazidwa. * Robert, yemwe ndi mkulu, anati: “Zingakhale bwino ngati oyang’anira achikhristu atamayendera Akhristu okalamba kuti azikaona mmene akukhalira ndi kumakapemphera nawo. Mpingonso ungachite zambiri kuti uwathandize.” Ngati timapeza nthawi yoyendera okalamba, timasonyeza kuti timadziwa mmene Yehova amaonera kufunika kosamalira anthu osowa thandizo.​—Yak. 1:27.

Ngati pangafunikire, akulu ayenera kukonza zomapereka thandizo kwa abale kapena alongo amene ali ku malo osungirako okalamba a m’gawo lawo. Robert ananenanso kuti thandizo lina limene lingakhale lofunika ndi “kuwalimbikitsa kupita ku misonkhano yathu yachikhristu ngati angakwanitse kutero.” Koma kwa amene sangathe kupita ku Nyumba ya Ufumu, akulu ayenera kupeza njira zina. Jacqueline, yemwe ali ndi zaka za m’ma 80 ndipo amadwala nyamakazi, amamvetsera misonkhano patelefoni. Iye anati: “Zimandithandiza kwambiri kumvetsera misonkhano panthawi yomwe ikuchitika. Sindifuna kuphonya kumvetsera misonkhano imeneyi zivute zitani.”

Ngati Mkhristu wokalamba sangakwanitse kumvetsera misonkhano patelefoni, akulu angakonze zomajambula misonkhanoyo patepi. M’bale amene angamapititse matepiwo, angagwiritse ntchito mwayi umenewu kulimbikitsa wokalambayo. Mkulu wina anati: “Kucheza ndi okalambawo nkhani zina ndi zina zimene zikuchitika mu mpingo, zimathandiza kudzimva kuti akuwerengeredwabe mu mpingowo.”

Musaleke Kulankhula Nawo

Okalamba ambiri amene amasamutsidwira ku malo osungirako okalamba amakhumudwa ndipo zimenezi n’zomveka. Zikatero iwo safuna kuchezanso ndi anthu. Komabe, ngati tiyendera abale ndi alongo athu okalamba panthawi imene angosamuka kumene ndi kuwatsimikizira kuti tipitiriza kuwasamalira, timawathandiza kwambiri kuti akhalebe osangalala ndi achimwemwe.​—Miy. 17:22.

Nthawi zina okalamba angafike posiya kuganiza bwino kapena kumva kumene, ndipo zikatero anthu ena amaona kuti kuwayendera ndi kungotaya nthawi. Komabe, ngati timayesetsa kuwayendera, ngakhale kuti sitingathe kulankhula nawo, timasonyeza kuti tikupitirizabe ‘kukhala patsogolo posonyeza ulemu Akhristu anzathu.’ (Aroma 12:10) Ngati m’bale wokalambayo wayamba kuiwalaiwala, tingamulimbikitse kuti atifotokozere nkhani zakale, ngakhale za paubwana wake, kapena kutifotokozera mmene anaphunzirira choonadi. Nanga tingachite chiyani ngati sakutha kukumbukira mawu ena ndi ena? Tiyenera kupitiriza kumvetsera modekha ndipo ngati n’koyenera, titchule mawu awiri kapena atatu amene akufuna kutchula. Kenako tibwereze mwachidule zimene wanena ndi kumulimbikitsa kupitirizabe. Ngati sakutha kuganiza kapena kulankhula bwino moti n’zovuta kumva, tingayesetse kumva zimene akunena mwa kumvetsera kwambiri mmene mawu ake akumvekera.

Ngati kulankhulana n’kosatheka, tingagwiritse ntchito njira zina. Mpainiya wina dzina lake Laurence, amakonda kuyendera Madeleine, yemwe ndi mlongo wa zaka 80, ndipo satha kulankhula. Laurence akufotokoza mmene amalankhulira naye kuti: “Ndimagwira dzanja la Madeleine pamene ndikupemphera naye. Popempherapo nayenso amagwiritsitsa dzanja langa ndi kumaphethira kusonyeza kuyamikira.” Kugwira dzanja kapena kukumbatira mwachikondi anzathu okalamba kumawalimbikitsa kwambiri.

Muziwayendera

Kuyendera okalambawo pafupipafupi kungachititse kuti anthu owayang’anira aziwasamalira bwino. Danièle, yemwe kwa zaka 20 wakhala akuyendera Mboni zimene zikukhala ku malo osungirako okalamba, anati: “Ogwira ntchito ku malo osungirako okalamba akaona kuti wokalamba amayenderedwa pafupipafupi, amamusamalira bwino.” Robert, yemwe tamutchula kale uja, anati: “Anthu ogwira ntchito ku malo osungira okalamba, savuta kumvera maganizo a munthu amene amabwera pafupipafupi kudzaona okalamba. Koma iwo satero ndi munthu amene amangobwera mwa apo ndi apo.” Chifukwa chakuti achibale ambiri a anthu okalamba amavuta, ogwira ntchito m’malo amenewa amayamikira ngati alendo akuwathokoza pa zimene akuchita. Komanso, ngati titamacheza bwino ndi anthu amenewa, iwo angamalemekeze kwambiri zinthu zimene m’bale wokalamba amene akumusamalirayo amakhulupirira.

Tingakhalenso paubale ndi anthu amenewa ngati titadzipereka kuti tiwathandize ntchito zina ndi zina. Kumadera ena, okalamba salandira chisamaliro chokwanira chifukwa chakuti kuli anthu ochepa owasamalira omwe amadziwa bwino ntchito yawo. Rébecca, yemwe amasamalira okalamba anati: “Panthawi ya chakudya pamakhala ntchito yambiri. Choncho imeneyi ingakhale nthawi yabwino yoyendera okalamba ndi kuwathandiza kuti adye.” Tisazengereze kufunsa anthu ogwira ntchito kumalo amenewa ngati angafune thandizo lathu.

Tikamapita pafupipafupi ku malo osungira anthu okalamba, tidzatha kudziwa zimene abale ndi alongo athu akufunikira, ndipo tingawathandize moyenerera titapempha chilolezo kwa ogwira ntchito kumeneko. Mwachitsanzo, tingathe kukongoletsa chipinda chawo ndi zithunzi za achibale awo kapena zithunzi zojambulidwa ndi ana. Poganizira zosowa za okalambawo, tingathe kuwabweretsera zovala kapena sopo ndi zinthu zina zotero. Ngati panja pali malo abwino, tikhoza kupita nawo panjapo kukapitidwa mphepo. Laurence, yemwe tinamutchula kale uja, anati: “Madeleine amayembekezera mwachidwi kumuyendera mlungu uliwonse. Iye amasangalala kwambiri ndikapitako ndi ana.” Kuchita zinthu zotere kungathandize kwambiri anthu amene akukhala ku malo osungirako okalamba.​—Miy. 3:27.

Tonse Timapindula

Kuyendera okalamba pafupipafupi kungasonyeze ngati ‘chikondi chathu chilidi chenicheni.’ (2 Akor. 8:8) Motani? Zimakhala zopweteka kuona munthu amene timakondana naye akutha mphamvu pang’onopang’ono. Laurence ananenanso mfundo imeneyi kuti: “Poyamba, ndinakhudzidwa kwambiri nditaona Madeleine akutha mphamvu moti nthawi iliyonse ndinkalira ndikakamuona. Koma ndinaona kuti kupemphera mochokera pansi pa mtima kungatithandize kukhala olimba mtima ndiponso olimbikitsa.” Kwa zaka zambiri, Robert wakhala akukaona m’bale Larry, amene akudwala nthenda yamanjenje. Robert anati: “Larry akudwala kwambiri moti sinditha kumva chilichonse chimene amalankhula. Koma tikapemphera limodzi, ndimatha kuonabe kuti ali ndi chikhulupiriro.”

Tikamayendera okhulupirira anzathu okalamba, iwo ndi ife tomwe timapindula. Kuyesetsa kwawo kusasiya kulambira Yehova ngakhale kuti akukhala ndi anthu a zikhulupiriro zosiyanasiyana, kumatithandiza kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kulimba mtima. Ndiponso kuyesetsa kwawo kulandira chakudya chauzimu ngakhale kuti amamva ndi kuona movutikira, kumasonyeza mfundo yakuti: ‘Munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’ (Mat. 4:4) Tikaona okalamba akukondwera ndi zinthu zing’onozing’ono monga kumwetulira kwa mwana kapena kudyera limodzi chakudya, zimatikumbutsa kuti tiyenera kukhutira ndi zinthu zimene tili nazo. Kukonda kwawo zinthu zauzimu kumatithandiza kuchita zinthu mwanzeru.

Kunena zoona, mpingo wonse umapindula ndi thandizo limene timapereka kwa okalamba. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti anthu amene ali ndi thupi lofooka amadalira kwambiri abale achikhristu, mpingo umakhala ndi mwayi wowachitira chifundo. Choncho, tonsefe tiziona kuti kusamalira okalamba, ngakhale kwa nthawi yaitali, ndi udindo wathu wotumikira anzathu. (1 Pet. 4:10, 11) Ngati akulu akutsogolera pankhani imeneyi, adzathandiza anthu ena mumpingo kuona kuti kusamalira okalamba ndi udindo wa Mkhristu aliyense, womwe suyenera kunyalanyazidwa. (Ezek. 34:15, 16) Tikamakonda ndi kusamalira Akhristu anzathu okalamba, timawatsimikizira kuti sitinawaiwale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Mlembi wa mpingo akangodziwa kuti m’bale kapena mlongo wina mumpingo wawo wasamukira ku malo osungirako okalamba m’dera lina, angachite bwino kudziwitsa akulu a m’dera limenelo mwamsanga.

[Mawu Otsindika patsamba 28]

“Ogwira ntchito ku malo osungirako okalamba akaona kuti wokalamba amayenderedwa pafupipafupi, amamusamalira bwino”

[Chithunzi patsamba 26]

Mapemphero ochokera pansi pa mtima angathandize Mkhristu mnzathu wokalamba kukhalabe wosangalala

[Chithunzi patsamba 26]

Tikamasonyeza chikondi Akhristu anzathu okalamba, timawalimbikitsa