Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chipulumutso Kudzera mu Ufumu wa Mulungu Chayandikira!

Chipulumutso Kudzera mu Ufumu wa Mulungu Chayandikira!

Chipulumutso Kudzera mu Ufumu wa Mulungu Chayandikira!

“Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”​—MAT. 6:10.

1. Kodi mfundo yaikulu imene Yesu ankaphunzitsa anthu inali yotani?

MUULALIKI wapaphiri, Yesu Khristu anapereka pemphero lachitsanzo limene linali ngati chidule cha mfundo yaikulu imene ankaphunzitsa. Anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mat. 6:9-13) Yesu “anachoka nayendayenda mu mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi, akulalikira ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1) Khristu analimbikitsa otsatira ake kuti: ‘Pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo cha Mulungu.’ (Mat. 6:33) Pamene mukuwerenga nkhani ino, onani njira zimene mungagwiritsire ntchito mfundo zake muutumiki wanu. Mwachitsanzo, ganizirani mmene mungayankhire mafunso awa: Kodi uthenga wa Ufumu ndi wofunikira bwanji? Kodi anthufe tikufunikira kupulumutsidwa ku chiyani? Ndipo kodi Ufumu wa Mulungu udzatipulumutsa bwanji?

2. Kodi uthenga wa Ufumu ndi wofunika bwanji?

2 Yesu analosera kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Anthu akufunikira kwambiri kumva uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Uthenga umenewu ndi wofunikira kwambiri padziko lonse. M’mipingo yoposa 100,000 ya Mboni za Yehova padziko lonse, atumiki a Mulungu okwana pafupifupi 7 miliyoni akugwira ntchito yolalikira yomwe sinachitikeponso, youza ena kuti Ufumu wayamba kulamulira. Kukhazikitsidwa kwa Ufumuwo kulidi uthenga wabwino, chifukwa kukusonyeza kuti Mulungu wapanga boma kumwamba limene lidzalamulire dziko lonse lapansi. Mu Ufumuwu, chifuniro cha Yehova chidzachitika padziko lapansi monga kumwamba.

3, 4. Kodi chidzachitike n’chiyani chifuniro cha Mulungu chikadzachitika padziko lapansi?

3 Kodi kuchitika kwa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi kudzakhudza bwanji anthu? Yehova “adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.” (Chiv. 21:4) Anthu sadzadwala kapena kufa chifukwa cha uchimo ndi kupanda ungwiro. Anthu amene anafa koma Mulungu akuwakumbukira, adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo kosatha chifukwa Baibulo limalonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Sikudzakhalanso nkhondo, matenda, kapena njala, ndipo dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Ngakhale nyama zolusa zidzakhala mwamtendere ndi anthu komanso nyama zinzawo.​—Sal. 46:9; 72:16; Yes. 11:6-9; 33:24; Luka 23:43.

4 Chifukwa cha madalitso onsewa amene Ufumuwo udzabweretsa, n’zosadabwitsa kuti ulosi wa Baibulo umanena mawu olimbikitsa akuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Nanga ndi chiyani chidzachitikire anthu amene amavutitsa anzawo? Malemba amalosera kuti: “Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti.” Koma “iwo akuyembekezera Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.”​—Sal. 37:9-11.

5. Kodi n’chiyani chidzachitikire dongosolo lino la zinthu?

5 Koma kuti zonsezi zichitike, zinthu monga dongosolo lilipoli ndi maboma ake osagwirizana, zipembedzo, ndiponso amalonda, ziyenera kuchotsedwa. Zimenezi ndi zimene boma lakumwamba lidzachite. Mneneri Danieli, anauziridwa kulosera kuti: “Masiku a mafumu aja [amene alipowa] Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu [kumwamba] woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [amene alipowa]. Nudzakhala chikhalire.” (Dan. 2:44) Ndiyeno Ufumu wa Mulungu, womwe ndi boma latsopano lakumwamba, udzalamulira anthu amene adzakhale m’dziko latsopano. Nthawi imeneyo kudzakhala “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano . . . , ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.”​—2 Pet. 3:13.

Tikufunikiradi Kupulumutsidwa

6. Kodi Baibulo limati chiyani za mmene dziko laipira?

6 Satana, komanso Adamu ndi Hava atapandukira Mulungu kuti azidzisankhira okha pankhani ya chabwino ndi choipa, zinthu zinayamba kuvuta padziko lapansi. Patadutsa zaka zoposa 1,600 ndipo Chigumula chitatsala pang’ono kuchitika, “kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso . . . ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” (Gen. 6:5) Patapita zaka zinanso 1,300, Solomo anaona kuti zinthu zaipa kwambiri moti analemba kuti: “Ndinatama akufa atatha kufa kupambana amoyo omwe alipobe; inde yemwe sanabadwe konse aposa onse awiriwo popeza sanaone ntchito yoipa yochitidwa kunja kuno.” (Mlal. 4:2, 3) Zaka zina 3,000 kuchokera panthawi imeneyi, zikutifikitsa m’nthawi yathu pamene zinthu zoipa zikuwonjezereka kwambiri.

7. Kodi n’chifukwa chiyani panopa tikufunikira kwambiri kupulumutsidwa ndi Mulungu?

7 N’zoona kuti zinthu zoipa zakhalapo kwanthawi yaitali, komabe nthawi ino tikufunikira kwambiri kupulumutsidwa ndi Ufumu wa Mulungu kuposa nthawi ina iliyonse m’mbuyomu. Pazaka 100 zapitazi zinthu zaipa kwambiri kuposa kale lonse ndipo zikupitirizabe kuipa. Mwachitsanzo, bungwe lina loona zochitika padziko lonse linati: “Chiwerengero cha anthu omwe anafa pa nkhondo za m’zaka za m’ma [1900] chinawirikiza katatu poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu omwe anafa mu nkhondo zonse zomwe zinachitika kuyambira 1 AD kufika mpaka 1899.” (Worldwatch Institute) Kuyambira 1914, anthu oposa 100 miliyoni afa pa nkhondo. Buku linanso limati, anthu pafupifupi 60 miliyoni anafa pa nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Pakali pano mayiko ena ali ndi zida zoopsa kwambiri moti angathe kupha anthu ambirimbiri nthawi imodzi. Chaka chilichonse ana 5 miliyoni amafa ndi njala, ngakhale kuti sayansi ndi zamankhwala zapita patsogolo.​—Onani mutu 9 m’buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?

8. Kodi zaka zambirimbiri zimene anthu akhala akudzilamulira zatsimikizira chiyani?

8 Anthu ayesetsa kuthetsa mavuto koma alephera. Ndale, mabungwe a zamalonda, ndi zipembedzo, zalephera kubweretsa zinthu zimene anthu amafuna kwambiri monga mtendere, chitukuko, ndi moyo wabwino. Magulu amenewa akungowonjezera mavutowo m’malo mowathetsa. Zaka zambiri zonsezi zimene anthu akhala akudzilamulira okha, zatsimikizira kulondola kwa mawu akuti: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yer. 10:23) Ndi zoona kuti “wina apweteka mnzake pom’lamulira.” (Mlal. 8:9) Ndipo “chilengedwe chonse chikubuula limodzi ndi kumva zopweteka.”​—Aroma 8:22.

9. Kodi Akhristu oona akuyembekezera kuona zinthu zotani “m’masiku otsiriza” ano?

9 Ponena za nthawi yathu, Baibulo linalosera kuti: “M’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta.” Ulosiwu utanena za mmene zinthu zidzakhalire m’masiku otsiriza mu ulamuliro wa anthu, unapitiriza kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe, kusocheretsa ena ndi kusocheretsedwa.” (Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, 13.) Zimenezi ndi zomwe Akhristu akuyembekezera, chifukwa “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo,” Satana. (1 Yoh. 5:19) Komabe, nkhani yabwino ndi yakuti posachedwapa Mulungu adzapulumutsa onse amene amamukonda m’dziko lino limene likuipiraipirabe.

Ndani Angatipulumutse?

10. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova ndiye yekhayo angatipulumutse?

10 Mukamalalikira uthenga wabwino, muzinena mosapita m’mbali kuti Yehova yekha ndiye angatipulumutse. Iye yekha ndiye ali ndi cholinga komanso mphamvu za kutipulumutsa ku mavuto alionse. (Mac. 4:24, 31; Chiv. 4:11) Tisakayike n’komwe kuti Yehova nthawi zonse amapulumutsa anthu ake kuti akwaniritse cholinga chake, chifukwa iye analumbira kuti: “Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa.” Mawu ake ‘sadzabwerera kwa iye chabe.’​—Werengani Yesaya 14:24, 25; 55:10, 11.

11, 12. Kodi Mulungu wawatsimikizira chiyani atumiki ake?

11 Yehova watsimikizira atumiki ake kuti adzawapulumutsa, akamadzaweruza anthu oipa. Pamene anatumiza mneneri Yeremiya kuti akachenjeze ochimwa, Mulungu anati: “Usaope . . . chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikulanditse iwe.” (Yer. 1:8) Nthawi inanso, Yehova atatsala pang’ono kuwononga Sodomu ndi Gomora, anatumiza angelo awiri kuti aperekeze Loti ndi banja lake kuchoka m’deralo. “Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulfure ndi moto.”​—Gen. 19:15, 24, 25.

12 Yehova angapulumutsenso anthu onse padziko lapansi amene amachita chifuniro chake. Pamene Yehova anawononga dziko lakale loipa pa Chigumula, “anasunga Nowa, mlaliki wa chilungamo, pom’pulumutsa pamodzi ndi ena asanu ndi awiri.” (2 Pet. 2:5) Yehova adzapulumutsanso olungama akamadzawononga dziko loipali. Mawu ake amati: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, . . . funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Zef. 2:3) Dziko lapansi likamadzawonongedwa, ‘oongoka mtima adzakhala m’dziko. Koma oipa adzalikhidwamo.’​—Miy. 2:21, 22.

13. Kodi atumiki a Yehova amene anafa adzapulumutsidwa bwanji?

13 Komabe, panopa atumiki ambiri a Mulungu afa chifukwa cha matenda, chizunzo ndi zinthu zina. (Mat. 24:9) Kodi anthu amenewa adzapulumutsidwa bwanji? Monga tanena kale, “kudzakhala kuuka kwa olungama.” (Mac. 24:15) N’zolimbikitsa kudziwa kuti palibe chilichonse chimene chingamulepheretse Yehova kupulumutsa atumiki ake.

Boma Lachilungamo

14. Kodi n’chiyani chikutitsimikizira kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma lachilungamo?

14 Mukakhala mu utumiki, mungafotokoze kuti Ufumu wakumwamba wa Yehova ndi boma lachilungamo. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti bomali limayendera mfundo za Mulungu monga chiweruzo, chilungamo ndi chikondi. (Deut. 32:4; 1 Yoh. 4:8, 16) Mulungu wapereka Ufumuwo kwa Yesu Khristu, yemwe ndi woyenera kulamulira dziko. Yehova wakonzanso zoti Akhristu odzozedwa okwana 144,000 ochokera padziko lapansi aukitsidwe ndi kupita kumwamba. Iwowa adzalamulira dziko lapansi limodzi ndi Khristu.​—Chiv. 14:1-5.

15. Fotokozani kusiyana kwa Ufumu wa Mulungu ndi ulamuliro wa anthu.

15 Ulamuliro wa Yesu ndi a 144,000 udzakhala wosiyana kwambiri ndi ulamuliro wa anthu opanda ungwiro. Olamulira a masiku ano akhala akuchitira nkhanza anthu ndiponso kuyambitsa nkhondo zomwe zaphetsa anthu mamiliyoni ambiri. M’pake kuti Malemba amatilangiza kuti tisamakhulupirire munthu, “amene mulibe chipulumutso mwa iye.” (Sal. 146:3) Koma Khristu adzalamulira anthu mwachikondi. Iye anati: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, pakuti ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzapeza chitsitsimutso cha miyoyo yanu. Pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”​—Mat. 11:28-30.

Masiku Otsiriza Atha Posachedwapa!

16. Kodi masiku otsirizawa adzatha bwanji?

16 Kungoyambira mu 1914, dzikoli lakhala lili m’masiku otsiriza, kapena kuti “mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 24:3) Posachedwapa pachitika zimene Yesu anatchula kuti “chisautso chachikulu.” (Werengani Mateyo 24:21.) Chisautso chimenechi, chomwe sichinachitikepo m’mbuyomu, chidzathetseratu dziko lonse la Satana. Koma kodi chisautso chachikulu chidzayamba bwanji? Ndipo, kodi chidzatha bwanji?

17. Kodi Baibulo limati chisautso chachikulu chidzayamba bwanji?

17 Chisautso chachikulu chidzayamba modzidzimutsa. Inde, “tsiku la Yehova” lidzabwera mosayembekezereka “pamene azidzati: ‘Bata ndi mtendere!’” (Werengani 1 Atesalonika 5:2, 3.) Chisautso chachikuluchi chidzayamba pamene mayiko azidzaganiza kuti atsala pang’ono kuthetsa ena mwa mavuto awo akuluakulu. Kuwonongedwa kodzidzimutsa kwa “Babulo Wamkulu,” womwe ndi ufumu wapadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, kudzakhala kosayembekezereka. Mafumu ndi ena onse adzadabwa kuona Babulo Wamkulu akuwonongedwa.​—Chiv. 17:1-6, 18; 18:9, 10, 15, 16, 19.

18. Kodi Yehova adzatani Satana akadzaukira anthu Ake?

18 Zinthu zikadzafika pachimake, “padzakhala zizindikiro ku dzuwa, ku mwezi ndi ku nyenyezi” ndipo “chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba.” Panthawiyo ‘tidzaimirira chilili ndi kutukula mitu yathu, chifukwa chipulumutso chathu chidzakhala chitayandikira.’ (Luka 21:25-28; Mat. 24:29, 30) Satana, kapena kuti Gogi, ndi anthu ake adzaukira anthu a Mulungu. Koma za anthu olimbana ndi atumiki ake, Yehova akuti: ‘Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso langa.’ (Zek. 2:8) Choncho, Satana sadzapambana pa cholinga chake chowononga atumiki a Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu, sadzachedwa kupulumutsa atumiki ake.​—Ezek. 38:9, 18.

19. Kodi n’chiyani chikutitsimikizira kuti magulu ankhondo a Mulungu adzawononga dongosolo la Satana?

19 Mulungu akamadzaweruza amitundu, iwo ‘adzadziwa kuti iye ndi Yehova.’ (Ezek. 36:23) Iye adzatumiza magulu ake ankhondo, omwe ndi angelo otsogoleredwa ndi Khristu Yesu, kuti awonongeretu dongosolo lonse lotsala la Satana padziko lapansi. (Chiv. 19:11-19) Tikakumbukira kuti tsiku limodzi lokha, mngelo mmodzi ‘anakantha [adani a Mulungu] zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu [185,000],’ tingakhale otsimikiza kuti magulu a nkhondo a kumwamba adzawonongeratu chilichonse cha dongosolo la Satanali pomwe chisautso chachikulu chidzafika pachimake pa Aramagedo. (2 Maf. 19:35; Chiv. 16:14, 16) Satana ndi ziwanda zake adzatsekeredwa ku phompho zaka 1,000, ndipo kenako adzawonongedwa.​—Chiv. 20:1-3.

20. Pogwiritsa ntchito Ufumu wake, kodi Yehova adzakwaniritsa chiyani?

20 Choncho zoipa zidzathetsedwa padziko lapansi, ndipo anthu olungama adzakhala kosatha padzikoli. Apa Yehova adzasonyeza kuti ndi Mpulumutsi Wamkulu. (Sal. 145:20) Pogwiritsa ntchito Ufumu wake, iye adzasonyeza kuti ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse, adzayeretsa dzina lake loyera, ndipo adzakwaniritsa cholinga chake chachikulu chokhudza dziko lapansi. Khalani osangalala pamene mukulalikira uthenga wabwinowu ndiponso pothandiza anthu a “maganizo oyenerera moyo wosatha” kuzindikira kuti chipulumutso kudzera mu Ufumu wa Mulungu chayandikira.​—Mac. 13:48.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yesu anasonyeza bwanji kufunika kwa Ufumu?

• N’chifukwa chiyani tikufunikira kwambiri kupulumutsidwa panopa?

• Kodi ndi zinthu zotani zimene zidzachitike pa chisautso chachikulu?

• Kodi Yehova adzasonyeza bwanji kuti iye ndi Mpulumutsi Wamkulu?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 12, 13]

Mawu a Mulungu analosera kuti m’nthawi yathu kudzachitika ntchito yolalikira yoti sinachitikeponso

[Chithunzi patsamba 15]

Yehova anapulumutsa Nowa ndi banja lake, ndipo angathe kutipulumutsanso ifeyo

[Chithunzi patsamba 16]

Yehova “adzapukuta msozi uliwonse . . . , ndipo imfa sidzakhalaponso.”​—Chiv. 21:4