Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani ‘Oyera Poopa Mulungu’

Khalani ‘Oyera Poopa Mulungu’

Khalani ‘Oyera Poopa Mulungu’

POFUNA kutsindika kuti Yehova Mulungu ndi woyera kuposa wina aliyense, Baibulo limati: “Woyera, Woyera, Woyera, Yehova.” (Yes. 6:3; Chiv. 4:8) Mawu a Chiheberi ndi a Chigiriki omasuliridwa kuti “kuyera,” amanena za kusaipitsidwa kapena kusadetsedwa pa chipembedzo, kukhala wopatulika. Tikamanena kuti Mulungu ndi woyera, timatanthauza kuti makhalidwe ake onse ndi angwiro.

Popeza kuti Yehova ndi Mulungu woyera, kodi amafunanso kuti anthu amene akumulambira akhale oyera mwakuthupi, mwamakhalidwe ndiponso mwauzimu? Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti Yehova amafuna kuti anthu ake akhale oyera. Lemba la 1 Petulo 1:16 limati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.” Kodi ndi zotheka kuti anthu opanda ungwiro akhaledi oyera ngati Yehova? Inde, koma osati ndendende. Mulungu angatiyese oyera ngati pomulambira tili osadetsedwa mwauzimu ndiponso ngati ubale wathu ndi iye uli bwino.

Nanga kodi tingatani kuti tikhalebe oyera m’dziko la makhalidwe oipali? Kodi tiyenera kupewa kuchita zinthu ziti? Kodi tiyenera kusiya kalankhulidwe ndi makhalidwe ati? Tiyeni tione zimene tingaphunzire pa nkhani ya kukhala oyera imeneyi, malinga ndi zimene Mulungu anafuna kwa Ayuda obwerera kwawo kuchokera ku Babulo mu 537 B.C.E.

‘Kudzakhala Njira Yopatulika’

Yehova analosera kuti anthu ake amene anali ku ukapolo ku Babulo adzabwerera kwawo. Malinga ndi ulosi umenewu, Mulungu analonjeza kuti: “Kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika.” (Yes. 35:8a) Mawu amenewa akusonyeza kuti Yehova anatsegulira Ayuda njira yobwerera kwawo ndiponso anawalonjeza kuti adzawateteza pa ulendo wawo.

Masiku anonso, Yehova watsegulira atumiki ake “Njira Yopatulika” kuchoka m’Babulo Wamkulu, ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Mu 1919 iye mwauzimu anamasula Akhristu odzozedwa ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga, ndipo iwo m’kupita kwa nthawi anayeretsa kulambira kwawo mwa kusiya ziphunzitso zonse zonyenga. Lero gulu la Yehova ndi loyera ndiponso ndi lamtendere. M’gululi timalambira Yehova, ndipo ubale wathu ndi iye komanso ndi anzathu, ndi wamtendere.

Akhristu odzozedwa a “kagulu ka nkhosa” ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” limene likuwonjezeka, asankha kuyenda pa njira yoyera ndipo akupempha anthu ena kuti ayendere limodzi. (Luka 12:32; Chiv. 7:9; Yoh. 10:16) Onse amene akufuna ‘kuti apereke matupi awo nsembe yamoyo, yoyera, yovomerezeka kwa Mulungu,’ angathe kulowa pa “Njira Yopatulika.”​—Aroma 12:1.

“Wodetsedwa Sadzapita Mmenemo”

Mu 537 B.C.E., Ayuda obwerera kwawo anayenera kukwanitsa mfundo yofunika kwambiri. Pofotokoza za anthu oyenera kuyenda mu “Njira Yopatulika,” lemba la Yesaya 35:8b limati: “Audyo [“wodetsedwa,” NW] sadzapita mmenemo; koma iye adzakhala nawo oyenda m’njira, ngakhale opusa, sadzasochera m’menemo.” Popeza kuti cholinga cha Ayuda obwerera ku Yerusalemu chinali chakuti akakhazikitsenso kulambira koyera, kumeneko sikunafunikire anthu adyera, osalemekeza zinthu zopatulika, kapena odetsedwa mwauzimu. Anthu obwerera kumeneko anafunika kusunga mfundo zapamwamba za Yehova za makhalidwe abwino. Masiku anonso, anthu amene akufuna kuti Mulungu awayanje ayenera kuchita zimenezi. Ayenera kukhala ‘oyera poopa Mulungu.’ (2 Akor. 7:1) Nanga kodi ndi makhalidwe onyansa ati amene tiyenera kupewa?

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ntchito za thupi zimaonekera, ndizo dama, chonyansa, khalidwe lotayirira.” (Agal. 5:19) Dama ndi pamene anthu osakwatirana agwiritsa ntchito ziwalo zawo zoberekera kuchita zachiwerewere zamtundu uliwonse. Khalidwe lotayirira limatanthauza “kutayirira; kufuna chisangalalo chogonana nthawi zonse; khalidwe lopanda manyazi; khalidwe lonyansa.” Zonse ziwiri, dama ndi khalidwe lotayirira, ndi zosemphana ndi chiyero cha Yehova. N’chifukwa chake anthu amene sasiya kuchita zinthu zimenezi saloledwa kulowa mu mpingo wachikhristu kapena amachotsedwa mu mpingo. Ndi mmenenso zimakhalira ndi anthu amene mwachizolowezi amachita chonyansa choipitsitsa, kutanthauza kuchita chonyansa chamtundu uliwonse mwadyera.​—Aef. 4:19.

Mawu akuti “chonyansa” amanena za machimo osiyanasiyana. Mawu a Chigiriki omasuliridwa kuti “chonyansa” amatanthauza kuipitsidwa kapena kudetsedwa kulikonse pa makhalidwe, kalankhulidwe ndiponso pa kupembedza. Mawuwa amaphatikizanso zinthu zina zimene ndi zonyansa ndithu koma zimene sizingafunikire komiti ya chiweruzo. * Koma kodi tinganene kuti anthu amene amachita zinthu zoterezi akuyesetsa kukhala oyera?

Bwanji ngati Mkhristu wayamba kuonera zinthu zolaula mwamseri? Pang’ono ndi pang’ono zikhumbo zonyansazo zikamakula, munthuyo salimbanso ndipo zimavuta kuti akhalebe woyera kwa Yehova. Zikatero, sikuti munthuyo wachita chonyansa choipitsitsa, komabe amakhala kuti wasiya kuganizira zinthu ‘zilizonse zoyera, zilizonse za chikondi ndi zilizonse zoneneredwa zabwino.’ (Afil. 4:8) Zinthu zolaula n’zonyansa ndipo zimawononga ubale wathu ndi Mulungu. Chonyansa cha mtundu uliwonse sichiyenera kutchulidwa n’komwe pakati pathu.​—Aef. 5:3.

Nanga bwanji ngati Mkhristu ali ndi chizolowezi chochita psotopsoto kapena kuti kukesya, kutanthauza kuseweretsa chiwalo choberekera pofuna kukhutiritsa chilakolako chogonana, uku akuonerera zinthu zolaula kapena ayi? Ngakhale kuti mawu akuti “psotopsoto” satchulidwa m’Baibulo, ndi zosakayikitsa kuti khalidweli limaipitsa maganizo ndi mtima wa munthu. Ngati munthu atapitirizabe khalidwe lodetsa limeneli, kodi sangawononge ubale wake ndi Yehova ndi kukhala wodetsedwa pamaso pa Mulungu? Tiyeni tilabadire malangizo a mtumwi Paulo akuti “tidziyeretse kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu” ndi ‘kuchititsa ziwalo za thupi lathu pa dziko lapansi kukhala zakufa ku dama, chonyansa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje.’​—2 Akor. 7:1; Akol. 3:5.

Dziko la Satanali limalekerera ngakhalenso kulimbikitsa kumene khalidwe lonyansa. Kupewa khalidwe limeneli ndi kovuta kwambiri. Koma Akhristu oona sayenera ‘kuyendanso monga amitundu amayendera, potsatira maganizo awo opanda pake.’ (Aef. 4:17) Yehova sangatilole kupitirizabe mu “Njira Yopatulika,” pokhapokha ngati titapewa khalidwe lonyansa mseri kapena pagulu.

“Sikudzakhala Mkango Kumeneko”

Kuti ayanjidwe ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu woyera, ena angafunike kusintha kwambiri khalidwe ndi kalankhulidwe kawo. Lemba la Yesaya 35:9 limati: “Sikudzakhala mkango kumeneko, ngakhale chilombo cholusa sichidzapondapo,” kutanthauza pa “Njira Yopatulika.” Anthu amene ndi achiwawa ndiponso aukali m’zochita ndi m’zolankhula zawo amafanana ndi zilombo. Anthu oterewa sadzapeza malo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. (Yes. 11:6; 65:25) Choncho ndi zofunika kwambiri kuti anthu amene akufuna kuyanjidwa ndi Mulungu asiye makhalidwe a zilombo ndi kukhala ndi makhalidwe oyera.

Malemba amatilangiza kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aef. 4:31) Pa Akolose 3:8, timawerenganso kuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu, mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe; ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” “Mawu achipongwe” omwe atchulidwa m’mavesi awiriwa amanena za mawu opweteka, onyoza kapena amwano.

Masiku ano anthu ambiri amakonda kulankhula mawu opweteka ndi otukwana, ngakhale panyumba. Anthu okwatirana amanena mawu okhadzula ndi onyoza kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa ana awo. Nkhanza ya mawu yotereyi siyenera kupezeka m’mabanja achikhristu.​—1 Akor. 5:11.

Tikakhala ‘Oyera Poopa Mulungu’ Timadalitsidwa

Kutumikira Yehova, Mulungu woyera, ndi mwayi waukulu. (Yos. 24:19) Paradaiso wauzimu amene Yehova watipatsa ndi wamtengo wapatali. Palibe moyo winanso wabwino umene tingakhale nawo kuposa kukhala ndi khalidwe loyera pamaso pa Yehova.

Posachedwapa Mulungu adzakwaniritsa lonjezo lake ndipo dziko lapansi lidzakhala Paradaiso. (Yes. 35:1, 2, 5-7) Anthu amene akuyembekezera dzikoli ndipo akuyesetsa kukhala ndi khalidwe labwino adzapeza malo m’dziko limenelo. (Yes. 65:17, 21) Ndiyetu tiyeni tipitirize kulambira Mulungu tili oyera mwauzimu ndi kukhala pa ubale wabwino ndi iyeyo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006, masamba 29-31, kuti mumvetse kusiyana kwa kuchita “chonyansa chamtundu uliwonse mwadyera [chidetso . . . mu umbombo]” ndi “chonyansa [chidetso].”

[Chithunzi patsamba 26]

Kodi Ayuda anafunika kuchita chiyani kuti ayende mu “Njira Yopatulika”?

[Chithunzi patsamba 27]

Zolaula zimawononga ubale wathu ndi Yehova

[Chithunzi patsamba 28]

“Kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu”