Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake

Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake

Mmene Bungwe Lolamulira Limayendetsera Ntchito Zake

BUNGWE Lolamulira la Mboni za Yehova lapangidwa ndi amuna odzipereka amene ndi atumiki odzozedwa a Mulungu. Iwo amaimira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene ali ndi udindo wopereka chakudya chauzimu, malangizo oyendetsera ntchito yolalikira Ufumu ndi kuonetsetsa kuti ntchitoyo ikugwirika bwinobwino padziko lonse.​—Mat. 24:14, 45-47.

Bungwe Lolamulira limakhala ndi msonkhano mlungu uliwonse, makamaka Lachitatu. Zimenezi zimathandiza abalewa kuti azigwira ntchito mogwirizana. (Sal. 133:1) Abale a m’Bungwe Lolamulirawa alinso m’makomiti osiyanasiyana. Posamalira zinthu za Ufumu, komiti iliyonse ili ndi ntchito imene imayang’anira ndipo zimenezi zafotokozedwa mwachidule m’munsimu.

▪ KOMITI YA OYANG’ANIRA: Komiti imeneyi yapangidwa ndi oyang’anira onse a makomiti a Bungwe Lolamulira ndiponso mlembi amenenso ali m’Bungwe Lolamulira. Komitiyi imaonetsetsa kuti makomiti onse akugwira ntchito yawo bwinobwino. Imaonanso za mavuto aakulu amene angabuke, chizunzo, masoka ndi zinthu zina zamwadzidzidzi zokhudza Mboni za Yehova padziko lonse.

▪ KOMITI YOONA ZA ATUMIKI A PA BETELI: Abale a m’komiti imeneyi ali ndi udindo woyang’anira mabanja a Beteli padziko lonse. Amasamalira anthu a pa Beteli mwakuthupi ndi mwauzimu. Komiti imeneyi imayang’anira ntchito yosankha ndi kuitana anthu atsopano pa Beteli ndipo imayankha mafunso okhudza utumiki wawo.

▪ KOMITI YOONA ZA NTCHITO YOFALITSA MABUKU: Komiti imeneyi imayang’anira ntchito yosindikiza, kufalitsa ndi kutumiza mabuku ofotokoza Baibulo padziko lonse. Imayang’anira nyumba zosindikizira mabuku ndi zinthu zonse za mabungwe osiyanasiyana alamulo amene Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito. Komiti imeneyi imapeza njira zabwino zogwiritsira ntchito ndalama zoperekedwa kuti zithandize pa ntchito ya Ufumu padziko lonse.

▪ KOMITI YA UTUMIKI: Komiti imeneyi imayang’anira ntchito yolalikira ndiponso nkhani zokhudza mipingo, apainiya, akulu ndi oyang’anira oyendayenda. Imayang’anira ntchito yokonza Utumiki Wathu wa Ufumu ndipo imaitana ophunzira a Sukulu ya Gileadi ndi a Sukulu Yophunzitsa Utumiki ndi kuwatumiza kumadera osiyanasiyana akamaliza maphunziro.

▪ KOMITI YOONA ZA NTCHITO YOPHUNZITSA: Komiti imeneyi imayang’anira ntchito yokonza nkhani za misonkhano yadera, yachigawo ndi ya mpingo. Imakonza mapulogalamu auzimu a pa Beteli ndipo imayang’anira sukulu zosiyanasiyana, monga Sukulu ya Gileadi ndi Sukulu ya Utumiki Waupainiya ndiponso ntchito yokonza matepi, ma CD ndi mavidiyo.

▪ KOMITI YOONA ZA NTCHITO YOLEMBA MABUKU: Udindo wa komiti imeneyi ndi kuyang’anira ntchito yolemba mabuku a chakudya chauzimu amene amafalitsidwa kwa abale ndi alongo komanso anthu ena onse. Komiti imeneyi imayankha mafunso a m’Baibulo ndipo imavomereza kutulutsidwa kwa zinthu monga masewero ndi maautilaini a nkhani. Imayang’aniranso ntchito yomasulira mabuku padziko lonse.

Mtumwi Paulo anayerekezera mpingo wa odzozedwa ndi thupi la munthu, ndipo anatsindika kufunika kwa munthu wina aliyense, kudalirana kwawo, chikondi ndi kugwirizana kwawo pogwira ntchito imene Mulungu wawapatsa. (Aroma 12:4, 5; 1 Akor. 12:12-31) Yesu Khristu monga Mutu wawo, amawapatsa zonse zofunika kuti azigwira ntchito mogwirizana ndi momvana, ndiponso kuti akhale athanzi mwauzimu. (Aef. 4:15, 16; Akol. 2:19) Mwa njira imeneyi, Bungwe Lolamulira limayendetsa ntchito zake motsogoleredwa ndi Yehova kudzera mwa mzimu woyera.