Pitani Patsogolo Mwauzimu Potsanzira Paulo
Pitani Patsogolo Mwauzimu Potsanzira Paulo
“Ndamenya nkhondo yabwino, ndathamanga panjirayo mpaka pomalizira pake, ndasunga chikhulupiriro.”—2 TIM. 4:7.
1, 2. Kodi Saulo wa ku Tariso anasintha bwanji, ndipo anayamba ntchito yofunika yotani?
SAULO wa ku Tariso anali munthu wanzeru ndi wosazengereza pochita zinthu. Koma iye ‘anatsatira zilakolako za thupi lake.’ (Aef. 2:3) Ndipo kenako ananena kuti iye anali “wonyoza ndi wozunza ndiponso wachipongwe.”—1 Tim. 1:13.
2 Patapita nthawi, Saulo anasintha kwambiri. Anasiya moyo wake wakale ndipo anayesetsa kuti ‘asamangofuna zopindulitsa iye yekha ayi, koma zopindulitsa anthu ambiri.’ (1 Akor. 10:33) Anakhala wodekha ndipo anayamba kukonda kwambiri anthu omwe kale anali adani ake. (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Iye analemba kuti: “Ndinakhala mtumiki . . . Kukoma mtima kwa m’chisomo kumeneku kunapatsidwa kwa ine, munthu wochepa pondiyerekeza ndi wochepetsetsa wa oyera onse. Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndilengeze kwa mitundu uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu.”—Aef. 3:7, 8.
3. Kodi kuwerenga kalata za Paulo ndi nkhani za utumiki wake kungatithandize kuchita chiyani?
3 Saulo, yemwe ankadziwikanso kuti Paulo, anapita patsogolo kwambiri mwauzimu. Mac. 13:9) Chotero, njira ina yabwino imene ingatithandize kupita patsogolo m’choonadi ndiyo kuwerenga kalata za Paulo ndi nkhani za utumiki wake ndipo kenako kutsanzira chikhulupiriro chake. (Werengani 1 Akorinto 11:1; Aheberi 13:7.) Tiyeni tione mmene kuchita zimenezi kungatithandizire kukhala ndi phunziro laumwini lokhazikika, kuyamba kukonda anthu ndi kudziona moyenera.
(Paulo Ankaphunzira Malemba Mokhazikika
4, 5. Kodi phunziro laumwini linamuthandiza bwanji Paulo?
4 Paulo ankadziwako Malemba chifukwa chakuti anali Mfarisi wophunzitsidwa ‘pamapazi a Gamaliyeli. Anaphunzitsidwa kutsatira Chilamulo cha makolo ake akale mokhwimitsa zinthu kwambiri.’ (Mac. 22:1-3; Afil. 3:4-6) Atangobatizidwa, ‘anapita ku Arabiya,’ mwina kuchipululu cha Suriya kapena kumalo ena aphee m’chigawo cha Arabiya kukasinkhasinkha. (Agal. 1:17) Paulo ayenera kuti anafuna kukaganizira malemba osonyeza kuti Yesu ndi Mesiya. Chinanso, Paulo anafuna kukakonzekera ntchito yomwe inali m’tsogolo mwake. (Werengani Machitidwe 9:15, 16, 20, 22.) Iye anali ndi khama posinkhasinkha zinthu zauzimu.
5 Paulo anadziwa bwino Malemba chifukwa chokhala ndi phunziro laumwini ndipo zimenezi zinamuthandiza kuphunzitsa choonadi mogwira mtima. Mwachitsanzo, ali kusunagoge wa ku Antiokeya ku Pisidiya, Paulo anagwira mawu m’Malemba Achiheberi kasanu konse kuti asonyeze kuti Yesu ndi Mesiya. Paulo anatchulanso malemba kambirimbiri popanda kuwagwira mawu. Mfundo zake za m’Baibulo zinali zokopa kwambiri motero kuti “Ayuda ndi otembenukira ku Chiyuda ambiri amene anali kulambira Mulungu anatsatira Paulo ndi Baranaba” kuti akaphunzire zochuluka. (Mac. 13:14-44) Patapita zaka zingapo, Ayuda a ku Roma anapita kumene Paulo anali kukhala, ndipo iye anawafotokozera nkhani yonse “pochitira umboni bwino lomwe ufumu wa Mulungu. Anateronso mwa kugwiritsa ntchito mfundo zokopa ponena za Yesu, kuchokera m’chilamulo cha Mose ndi mu Zolemba za aneneri.”—Mac. 28:17, 22, 23.
6. Kodi n’chiyani chinathandiza Paulo kukhalabe wolimba mwauzimu pokumana ndi mayesero?
6 Atakumana ndi mayesero, Paulo anapitirizabe kuwerenga mozama Malemba ndipo uthenga wake unamupatsa mphamvu. (Aheb. 4:12) Ali m’ndende ku Roma asanaphedwe, Paulo anapempha Timoteyo kuti amupititsire “mipukutu” ndi “zikopa.” (2 Tim. 4:13) Zinthu zimenezi ziyenera kuti zinali Malemba Achiheberi amene Paulo anagwiritsa ntchito pophunzira. Kudziwa Malemba mwa kukhala ndi phunziro la Baibulo lokhazikika, kunali kofunika kwambiri kwa Paulo kuti iye akhalebe wolimba.
7. Kodi kuphunzira Baibulo mokhazikika kungatithandize bwanji?
7 Kuphunzira Baibulo nthawi zonse komanso kusinkhasinkha mwatanthauzo, kungatithandize kupita patsogolo mwauzimu. (Aheb. 5:12-14) Pofotokoza ubwino wa Mawu a Mulungu, wamasalmo anaimba kuti: “Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwizikwi. Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga; pakuti akhala nane chikhalire. Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yoipa, kuti ndisamalire mawu anu.” (Sal. 119:72, 98, 101) Kodi mumaphunzira Baibulo mokhazikika panokha? Kodi mukukonzekera kudzagwira ntchito zosiyanasiyana muutumiki wa Mulungu mwa kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku ndi kusinkhasinkha zimene mukuwerenga?
Saulo Anaphunzira Kukonda Anthu
8. Kodi Saulo anali kuchitira zotani anthu amene sanali m’chipembedzo cha Chiyuda?
8 Saulo asanakhale Mkhristu, anali wachangu pachipembedzo chake cha Chiyuda koma sanali kuwerengera m’pang’ono pomwe anthu amene sanali m’chipembedzocho. (Mac. 26:4, 5) Iye anaonerera Ayuda akuponya miyala Sitefano ndipo anagwirizana nazo. Saulo ayenera kuti analimba mtima ataona zimenezi, ndipo mwina anaona kuphedwa kwa Sitefano ngati chilango choyenerera. (Mac. 6:8-14; 7:54–8:1) Malemba amati: “Saulo anayamba kusakaza mpingo mwa nkhanza. Anali kulowa nyumba ndi nyumba, nakokera panja amuna ndi akazi omwe, n’kukawaponya m’ndende.” (Mac. 8:3) Iye ‘anafika pa kuwazunza ngakhale m’mizinda yakunja.’—Mac. 26:11.
9. Kodi zinatani kuti Saulo asinthe n’kuyamba kukhala bwino ndi anthu?
9 Saulo ali pa ulendo wa ku Damasiko kukazunza ophunzira a Khristu, Ambuye Yesu anamuonekera. Saulo ataona kuwala kothobwa m’maso kwa Mwana wa Mulungu, anachita khungu ndipo anadalira ena kumuthandiza. Nthawi imene Yehova anagwiritsa ntchito Ananiya kutsegula maso ake, mtima wa Saulo unali utasinthiratu. (Mac. 9:1-30) Atakhala wotsatira wa Khristu, iye anayesetsa kwambiri kukhala ndi anthu ngati mmene Yesu anali kuchitira. Anasiya chiwawa chake chija ndipo anayamba kukhala “mwa mtendere ndi anthu onse.”—Werengani Aroma 12:17-21.
10, 11. Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali kukonda kwambiri anthu?
10 Kukhala mwamtendere ndi anthu sikunali kokwanira kwa Paulo. Iye anafuna kuwakonda kwambiri, ndipo utumiki wachikhristu unamupatsa mpata wochita zimenezi. Paulendo wake woyamba waumishonale, Paulo analalikira uthenga wabwino ku Asia Minor. Ngakhale kuti anatsutsidwa kwambiri, Paulo ndi anzake analimbikira kuthandiza anthu ofatsa kukhala Akhristu. Paulo ndi anzakewo anabwereranso ku Lusitara ndi Ikoniyo, ngakhale kuti anthu otsutsa kumeneko anafuna kupha Paulo.—Mac. 13:1-3; 14:1-7, 19-23.
11 Kenako, Paulo ndi anzake anayamba kufufuza anthu a mtima wabwino mumzinda wa Filipi ku Makedoniya. Lidiya amene anali atalowa Chiyuda, anamvetsera uthenga wabwino ndipo anakhala Mkhristu. Akuluakulu a boma anakwapula ndi ndodo Paulo ndi Sila, ndipo kenako anawaponya m’ndende. Mmenemo, Paulo analalikira woyang’anira ndende ndipo iye ndi banja lake lonse anabatizidwa ndi kuyamba kulambira Yehova.—Mac. 16:11-34.
12. Kodi ndi chiyani chinachititsa kuti Saulo wachipongwe uja akhale mtumwi wachikondi wa Yesu Khristu?
12 Kodi zinatheka bwanji kuti Saulo, yemwe kale anali wozunza, alowe chipembedzo cha anthu omwe anali kuwazunzawo? Kodi ndi chiyani chinachititsa wachipongwe uja kukhala mtumwi wokoma mtima ndi wachikondi, komanso wokonzeka kuika moyo wake pachiswe kuti ena aphunzire choonadi cha Mulungu ndi Khristu? Paulo mwiniwakeyo anati: ‘Mulungu, amene . . . anandiitana mwa kukoma mtima kwa m’chisomo chake, kunamukomera kuvumbula Mwana wake kudzera mwa ine.’ (Agal. 1:15, 16) Polembera Timoteyo, Paulo anati: “Anandichitira chifundo kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa koposa, monga chitsanzo kwa amene adzam’khulupirira iye kuti akapeze moyo wosatha.” (1 Tim. 1:16) Yehova anakhululukira Paulo, ndipo chifukwa cholandira kukoma mtima kwa m’chisomo ndi chifundo, anayamba kukonda ena ndipo anali kuwalalikira uthenga wabwino.
13. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukonda ena, ndipo tingachite bwanji zimenezi?
13 Nafenso Yehova amatikhululukira machimo ndi zolakwa zathu. (Sal. 103:8-14) Wamasalmo anafunsa kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye?” (Sal. 130:3) Popanda Mulungu kutichitira chifundo, ife tonse sitikanakhala ndi mwayi wochita utumiki wopatulika kapena mwayi wodzakhala ndi moyo wosatha. Mulungu watichitira zazikulu kaamba ka kukoma mtima kwa m’chisomo chake. Choncho, mofanana ndi Paulo, tiyenera kuyesetsa kukonda ena powalalikira ndi kuwaphunzitsa choonadi ndiponso polimbikitsa okhulupirira anzathu.—Werengani Machitidwe 14:21-23.
14. Kodi tingachite chiyani kuti tiwonjezere utumiki wathu?
14 Popeza anali mtumiki wa uthenga wabwino, Paulo anafuna kupita patsogolo ndipo chitsanzo cha Yesu chinamugwira mtima. Mwana wa Mulungu anasonyeza chikondi chosayerekezeka kwa anthu m’njira zosiyanasiyana ndipo njira ina inali mwa kuwalalikira. Yesu anati: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:35-38) Paulo ayenera kuti anapempha kuti antchito awonjezereke ndipo anachita mogwirizana ndi zimene anapemphazo mwa kukhala wachangu pantchito yake. Nanga bwanji inuyo? Kodi mukuwonjezera luso lanu la kulalikira? Kapena kodi mungawonjezere nthawi imene mumathera pa ntchito yolalikira Ufumu, mwina kuyamba upainiya? Tiyeni tizikonda kwambiri anthu mwa kuwathandiza ‘kugwira molimbika mawu a moyo.’—Afil. 2:16.
Kodi Paulo Anali Kudziona Bwanji?
15. Kodi Paulo anali kudziona bwanji pakati pa Akhristu anzake?
15 Monga mtumiki wachikhristu, Paulo anatisiyira chitsanzo chabwino kwambiri m’njira inanso. Ngakhale kuti anachita zazikulu mumpingo wachikhristu, Paulo anali kudziwa bwino kuti zimene anachitazo sizinali chifukwa cha khama lake kapena luso lake ayi. Iye anadziwa kuti zimenezo zinatheka chifukwa cha kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu. Paulo anadziwanso kuti Akhristu anzake analinso atumiki ogwira mtima a uthenga wabwino. Iye anali ndi udindo waukulu pakati pa anthu a Mulungu koma anakhalabe wodzichepetsa.—Werengani 1 Akorinto 15:9-11.
16. Pankhani ya mdulidwe, kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti anali wodzichepetsa ndiponso kuti anali kudziwa malire ake?
16 Tiyeni tione mmene Paulo anasamalira vuto limene linabuka mu mzinda wa Antiokeya ku Suriya. Mpingo wachikhristu kumeneko unagawanika chifukwa cha nkhani ya mdulidwe. (Mac. 14:26–15:2) Popeza kuti Paulo anali atasankhidwa kutsogolera ntchito yolalikira anthu omwe sanali Ayuda, akanatha kudziona ngati katswiri pankhani zokhudza anthu amenewa, ndipo woyenerera kuthetsa vuto linabukalo. (Werengani Agalatiya 2:8, 9.) Koma atalephera kuthetsa vutolo, iye anadziwa malire ake ndipo modzichepetsa anagwirizana ndi dongosolo lakuti apereke nkhaniyo ku bungwe lolamulira ku Yerusalemu. Paulo anagwirizana ndi zonse zimene bungwe lolamulira linagamula litamva nkhaniyo, ndipo bungwelo linatumiza iyeyo ndi ena monga nthumwi. (Mac. 15:22-31) Motero Paulo ‘anakhala patsogolo posonyeza ulemu’ kwa atumiki anzake.—Aroma 12:10b.
17, 18. (a) Kodi Paulo anasonyeza mtima wotani kwa anthu m’mipingo? (b) Kodi zimene akulu a ku Efeso anachita posiyana ndi Paulo zikutiphunzitsa chiyani za iye?
17 Chifukwa cha kudzichepetsa kwake, Paulo sanadzipatule kwa abale ndi alongo ake m’mipingo. M’malo mwake, anali kuwakonda kwambiri. M’kalata yake yopita kwa Aroma, anapereka moni kwa anthu oposa 20 ndipo anawatchula Aroma 16:1-16.
mayina awo. Ambiri a iwo satchulidwa kwina kulikonse m’Malemba kupatulapo m’kalata yakeyi basi, ndipo ndi ochepa amene anali ndi udindo pampingo. Koma onsewo anali atumiki okhulupirika a Yehova ndipo Paulo anali kuwakonda kwambiri.—18 Khalidwe la Paulo la kudzichepetsa ndi kukonda anthu linalimbikitsa mipingo. Atakumana ndi akulu a ku Efeso komaliza, iwo “anam’kumbatira Paulo ndi kum’psompsona mwachikondi. Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.” Iwo sakanachita zimenezo ngati Paulo akanakhala wonyada ndi wodzikweza.—Mac. 20:37, 38.
19. Kodi tingasonyeze bwanji ‘kudzichepetsa’ pochita zinthu ndi Akhristu anzathu?
19 Onse amene akufuna kupita patsogolo mwauzimu afunika kukhala ndi mtima wodzichepetsa ngati wa Paulo. Iye analangiza Akhristu anzake kuti ‘asachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, akumaona ena kukhala owaposa.’ (Afil. 2:3) Kodi uphungu umenewu tingautsatire bwanji? Njira ina imene tingachitire zimenezi ndiyo kugwirizana ndi akulu mumpingo mwa kutsatira malangizo awo ndi kuvomereza zimene agamula posamalira machimo aakulu. (Werengani Aheberi 13:17.) Njira inanso ndiyo kulemekeza kwambiri abale ndi alongo mumpingo. Mipingo ya anthu a Yehova yapangidwa ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana, ndiponso osiyana chikhalidwe, fuko ndi khungu. Ndiye pamenepa, kodi sitiyenera kuphunzira kuwakonda onsewo popanda tsankho ngati mmene Paulo anachitira? (Mac. 17:26; Aroma 12:10a) Ndipotu timalimbikitsidwa kuti “landiranani wina ndi mnzake, mmene Khristu anatilandirira, kuti ulemerero upite kwa Mulungu.”—Aroma 15:7.
‘Thamangani Mopirira’ Mpikisano wa Moyo
20, 21. Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tithamange ndi kupambana mpikisano wa moyo?
20 Moyo wa Mkhristu tingauyerekeze ndi mpikisano wothamanga mtunda wautali. Paulo analemba kuti: “Ndathamanga panjirayo mpaka pomalizira pake, ndasunga chikhulupiriro. Kuyambira tsopano kumka mtsogolo, andisungira kolona wa chilungamo. Ambuye, woweruza wolungama, adzandipatsa mphotoyo m’tsikulo. Sadzapatsa ine ndekha ayi, komanso onse okonda kuonekera kwake.”—2 Tim. 4:7, 8.
21 Kutsatira chitsanzo cha Paulo kungatithandize kuti tithamange ndi kupambana mpikisano wa moyo wosatha. (Aheb. 12:1) Choncho, tiyeni tipitebe patsogolo mwauzimu mwa kukhala ndi phunziro laumwini lokhazikika, kukonda kwambiri anthu ndi kukhalabe odzichepetsa.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi kuphunzira Malemba mokhazikika payekha kunamuthandiza bwanji Paulo?
• Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu oona amafunika kukonda kwambiri anthu?
• Kodi ndi makhalidwe ati amene angakuthandizeni kupewa tsankho?
• Kodi chitsanzo cha Paulo chingakuthandizeni bwanji kugwirizana ndi akulu mumpingo wanu?
[Mafunso]
[Chithunzi patsamba 23]
Pezani mphamvu m’Malemba, ngati Paulo
[Chithunzi patsamba 24]
Kondani ena powalalikira uthenga wabwino
[Chithunzi patsamba 25]
Abale anakonda kwambiri Paulo. Kodi mukudziwa chifukwa chake?