Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kuchita Zabwino

Pitirizani Kuchita Zabwino

Pitirizani Kuchita Zabwino

‘Pitirizani kuchita . . . zabwino.’​—LUKA 6:35.

1, 2. N’chifukwa chiyani nthawi zambiri kuchitira ena zabwino kumakhala kovuta?

NTHAWI zambiri kuchitira ena zabwino kumakhala kovuta chifukwa ena amene timawachitira zabwino, sangatichitire zabwino. Ngakhale kuti timayesetsa kuthandiza anthu mwa kuwauza “uthenga wabwino wa ulemerero wa Mulungu wa chisangalalo” ndi Mwana wake, ena salabadira kapena kuyamikira. (1 Tim. 1:11) Enanso amasonyeza kuti ndi “adani a mtengo wozunzikirapo wa Khristu.” (Afil. 3:18) Kodi ife Akhristu tiyenera kuwachitira zotani anthu amenewa?

2 Yesu Khristu anauza ophunzira ake kuti: “Pitirizani kukonda adani anu, [ndi] kuwachitira zabwino.” (Luka 6:35) Tiyeni tikambirane bwinobwino malangizo amenewa. Komanso tiona mfundo zina zimene Yesu ananena zotithandiza kuchitira ena zabwino.

‘Kondani Adani Anu’

3. (a) Fotokozani mwachidule zimene Yesu ananena pa Mateyo 5:43-45. (b) Kodi atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda anali ndi maganizo otani okhudza Ayuda ndi anthu omwe sanali Ayuda?

3 Muulaliki wake wotchuka wapaphiri, Yesu anauza omvera ake kuti azikonda adani awo ndi kupempherera amene akuwazunza. (Werengani Mateyo 5:43-45.) Anthu amene analipo panthawi imeneyi anali Ayuda, omwe anadziwa bwino lamulo la Mulungu lakuti: “Usamabwezera chilango, kapena kusunga kanthu kukhosi pa ana a anthu a mtundu wako; koma uzikonda mnansi wako monga udzikonda wekha.” (Lev. 19:18) Atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda ankaganiza kuti mawu akuti “ana a anthu a mtundu wako” ndiponso “mnansi,” anali kunena za Ayuda okha basi. Chilamulo cha Mose chinangofuna kuti Aisiraeli azidzipatula ku mitundu ina, koma kenako iwowo anayamba kuganiza kuti anthu omwe si Ayuda ndi adani awo.

4. Kodi ophunzira a Yesu anafunika kuchitira adani awo zotani?

4 Mosiyana ndi anthu amenewa, Yesu anati: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mat. 5:44) Ophunzira ake anafunika kukonda anthu onse amene anali adani awo. Malinga ndi zimene Luka analemba mu uthenga wake wabwino, Yesu anati: “Ndikukuuzani inu amene mukumvetseranu, Pitirizani kukonda adani anu, kuchita zabwino kwa amene akudana nanu, kudalitsa okutembererani, kupempherera amene akukunyozani.” (Luka 6:27, 28) Mofanana ndi anthu a m’nthawi ya Yesu amene anamvera malangizo ake, nafenso ‘timachitira zabwino amene akudana nafe’ mwa kuchita zinthu zowathandiza. ‘Timadalitsa anthu amene akutitemberera’ mwa kulankhula nawo mokoma mtima. Ndiponso ‘timapempherera amene akutizunza’ potimenya kapena ‘kutinyoza’ mwa njira zina. Timawapempherera otizunzawo n’cholinga chakuti asinthe mtima wawo ndi kuchita zinthu zomwe zingachititse Yehova kuwayanja.

5, 6. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu?

5 Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kukonda adani athu? Yesu anapereka chifukwa chake. Iye anati: “Kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba.” (Mat. 5:45) Tikamamvera malangizo amenewa, timakhala “ana” a Mulungu chifukwa chakuti timatsanzira Yehova, amene “amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.” Malinga ndi zimene analemba Luka, Mulungu “ndi wachifundo kwa osayamika ndi kwa oipa.”​—Luka 6:35.

6 Potsindika kwa ophunzira ake kufunika koti ‘apitirize kukonda adani awo,’ Yesu anati: “Mukamakonda okhawo amene amakukondani, mudzalandira mphoto yotani? Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu nawonso sachita zimenezo?” (Mat. 5:46, 47) Ngati timakonda anthu okhawo amene amatikonda, sitingalandire “mphoto” kapena kuyanjidwa ndi Mulungu. Ngakhale okhometsa msonkho, amene anthu ambiri anali kudana nawo, ankasonyeza chikondi kwa anthu amene ankawakonda.​—Luka 5:30; 7:34.

7. Kodi n’chifukwa chiyani palibe chachilendo chimene timachita ngati timangopatsa moni “abale” athu okha?

7 Ayuda popatsana moni anali kutchula mawu akuti “mtendere.” (Ower. 19:20; Yoh. 20:19) Amenewa anali mawu ofunira munthu wopatsidwa moniyo thanzi ndi moyo wabwino. Ngati timangopatsa moni “abale” athu okha, ndiye kuti ‘palibe chachilendo chimene tikuchita.’ Yesu ananena kuti “anthu amitundu” anali kuchitanso zimenezi.

8. Kodi Yesu anali kuwalimbikitsa kuchita chiyani omvera ake pamene anati: “Khalani angwiro”?

8 Chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, ophunzira a Khristu anali opanda ungwiro ndipo ankaphonyetsa zinthu zina. (Aroma 5:12) Komabe, Yesu anamaliza ulaliki wake ndi mawu akuti: “Khalani angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.” (Mat. 5:48) Apa Yesu analimbikitsa omvera ake kutsanzira ‘Atate wawo wa kumwamba,’ Yehova, mwa kukhala ndi chikondi changwiro, kapena kuti chokwanira, mpaka kufika pokonda adani awo. Nafenso tiyenera kuchita zimenezi.

Tizikhululuka

9. Malinga ndi zimene Yesu anasonyeza m’pemphero lachitsanzo, kodi kupitiriza kuchita zabwino kumaphatikizapo chiyani?

9 Ngati timakhululuka munthu wina akatilakwira, ndiye kuti tikupitiriza kuchita zabwino. Ndipotu, mawu ena a pemphero la Yesu lachitsanzo amati: “Mutikhululukire zolakwa zathu, pakuti ifenso takhululukira amene atilakwira.”​—Mat. 6:12.

10. Pankhani ya kukhululuka, kodi tingatsanzire bwanji Mulungu?

10 Tiyenera kutsanzira Mulungu chifukwa amakhululukira ndi mtima wonse ochimwa amene alapa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Khalani okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso anakukhululukirani Mulungu ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.” (Aef. 4:32) Wamasalmo Davide anaimba kuti: “Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. . . . Sanatichitira monga mwa zolakwa zathu, kapena kutibwezera monga mwa mphulupulu zathu. . . . Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”​—Sal. 103:8-14.

11. Kodi Mulungu amakhululukira anthu otani?

11 Anthu amakhululukidwa ndi Mulungu ngati nawonso akhululukira ena zolakwa zawo. (Maliko 11:25) Potsindika mfundo imeneyi, Yesu ananenanso kuti: “Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu wa kumwamba adzakhululukiranso inu; koma ngati simumakhululukira anthu zolakwa zawo, Atate wanu sadzakukhululukirani zolakwa zanu.” (Mat. 6:14, 15) Inde, Mulungu amakhululukira anthu amene amakhululukiranso anzawo ndi mtima wonse. Ndipo njira imodzi yopitirizira kuchita zabwino ndi kutsatira malangizo a Paulo akuti: “Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso.”​—Akol. 3:13.

“Lekani Kuweruza Ena”

12. Kodi Yesu anapereka malangizo otani pankhani yoweruza ena?

12 Njira inanso yochitira ena zabwino inanenedwa ndi Yesu muulaliki wapaphiri, pamene anauza omvera ake kuti aleke kuweruza ena. Kuti atsindike mfundo imeneyi, Yesu anagwiritsa ntchito fanizo labwino kwambiri. (Werengani Mateyo 7:1-5.) Tiyeni tikambirane zimene Yesu anatanthauza pamene anati: “Lekani kuweruza ena.”

13. Kodi anthu amene anali kumvetsera Yesu anafunika kuchita chiyani?

13 Mu Uthenga Wabwino wa Mateyo, mawu a Yesu amenewa analembedwa kuti: “Lekani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mat. 7:1) Luka analemba mawu a Yesu omwewa kuti: “Lekani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa; muleke kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira, inunso mudzakhululukidwa.” (Luka 6:37) Potsatira miyambo yosagwirizana ndi Malemba, Afarisi anali kuweruza ena mwankhanza. Ngati panali aliyense mwa omverawo amene ankachita zimenezi, anafunika ‘kuleka kuweruza ena.’ M’malo mwake anafunika ‘kupitiriza kukhululukira ena.’ Nayenso mtumwi Paulo anapereka malangizo ngati amenewa pankhani ya kukhululuka monga taonera kale.

14. Mwa kukhululukira ena, kodi ophunzira a Yesu akanalimbikitsa anthu kuchita chiyani?

14 Mwa kukhululukira ena, ophunzira a Yesu akanalimbikitsa anthu ena kukhala ndi mtima wokhululuka. Yesu anati: “Pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho; ndipo muyeso umene mukupimira ena, iwonso adzakupimirani womwewo.” (Mat. 7:2) Pankhani ya zinthu zimene timachitira ena, timakolola zimene timafesa.​—Agal. 6:7.

15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti kumangodzudzula ena n’kulakwa?

15 Pofuna kusonyeza kuti kumangodzudzula ena n’kulakwa, Yesu anafunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga umene uli m’diso lako? Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako’; pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga?” (Mat. 7:3, 4) Munthu amene amakonda kudzudzula ena amaona ngakhale kanthu kakang’ono “m’diso” la m’bale wake. Munthu wokonda kudzudzula mnzakeyo amaonetsa ngati m’bale wakeyo saona bwino zinthu. Ngakhale kuti vutolo lingakhale laling’ono ngati kachitsotso, wodzudzulayo amafunabe kuti alichotse basi. Pochotsapo iye amanamizira kuti akufuna kuthandiza m’bale wakeyo kuyamba kuona bwino zinthu.

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Afarisi anali ndi “mtanda wa denga” m’diso lawo?

16 Atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda ndi amene ankakonda kwambiri kudzudzula ena. Mwachitsanzo, munthu wina wakhungu atachiritsidwa ndi Khristu, ananena kuti Yesuyo anachokera kwa Mulungu. Koma Afarisi anam’dzudzula kwambiri ponena kuti: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe, ukufuna kuphunzitsa ife kodi?” (Yoh. 9:30-34) Pankhani yoona zinthu mwauzimu ndiponso kuweruza bwino, Afarisi ndiwo anali ndi “mtanda wa denga” m’maso mwawo ndiponso anali akhungu. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino lomwe mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mat. 7:5; Luka 6:42) Ngati tikufuna kukhala bwino ndi anzathu ndi kuwachitira zabwino, sitifunika kumangodzudzula ena, kapena kumangofufuza kachitsotso m’maso mwa m’bale wathu. M’malo mwake, tiyenera kukumbukira kuti ndife opanda ungwiro ndi kupewa kuweruza ndi kudzudzula okhulupirira anzathu.

Zimene Tiyenera Kuchitira Ena

17. Malinga ndi Mateyo 7:12, kodi tiyenera kuchitira ena zotani?

17 Muulaliki wapaphiri, Yesu anati Mulungu amaona atumiki ake kuti ndi ana ake ndipo amayankha mapemphero awo. (Werengani Mateyo 7:7-12.) N’zochititsa chidwi kuti Yesu ananena mfundo iyi: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.” (Mat. 7:12) Sitinganene kuti ndife otsatira enieni a Yesu Khristu ngati sitichita zimene iye ananenazi.

18. Kodi “Chilamulo” chinasonyeza bwanji kuti tiyenera kuchitira ena zimene tikufuna kuti iwo atichitire?

18 Yesu atanena kuti tiyenera kuchitira ena zimene timafuna kuti iwo atichitire, anawonjezera kuti: “Pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.” Tikamachitira ena zabwino monga mmene Yesu ananenera, timakhala tikutsatira mfundo za “Chilamulo,” zopezeka m’Baibulo m’mabuku a Genesis mpaka Deuteronomo. Kuwonjezera pa kuvumbula cholinga cha Yehova chotulutsa mbewu imene idzathetse zinthu zoipa, mabuku amenewa amanena za Chilamulo chimene Mulungu anapatsa mtundu wa Isiraeli kudzera mwa Mose mu 1513 B.C.E. (Gen. 3:15) Mwa zina, Chilamulo chinanena momveka bwino kuti Aisiraeli ayenera kuchita chilungamo, sayenera kukondera, ndi kutinso ayenera kuchitira zabwino anthu ovutika ndiponso alendo.​—Lev. 19:9, 10, 15, 34.

19. Kodi “Zolemba za aneneri” zimasonyeza bwanji kuti tiyenera kuchita zabwino?

19 Potchula “Zolemba za aneneri,” Yesu ankanena za mabuku aulosi a m’Malemba Achiheberi. Mabuku amenewa ali ndi ulosi wonena za Mesiya umene unakwaniritsidwa mwa Khristu. Mabuku amenewa amasonyezanso kuti Mulungu amadalitsa anthu ake iwo akamachita zimene iye amafuna ndi kuchitira ena zabwino. Mwachitsanzo, ulosi wa Yesaya unalangiza Aisiraeli kuti: “Atero Yehova, Sungani inu chiweruziro, ndi kuchita chilungamo . . . Wodala munthu amene achita ichi, ndi mwana wa munthu amene agwira zolimba ichi, . . . nasunga dzanja lake osachita nalo choipa chilichonse.” (Yes. 56:1, 2) Inde, Mulungu amafuna kuti anthu ake apitirize kuchita zabwino.

Nthawi Zonse Tizichitira Ena Zabwino

20, 21. Kodi anthu anamva bwanji atamvetsera ulaliki wapaphiri wa Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani muyenera kusinkhasinkha za ulalikiwu?

20 Taona mfundo zochepa chabe pa mfundo zofunika kwambiri zimene Yesu ananena pa ulaliki wake wapaphiri. Ngakhale zili choncho, n’zosavuta kudziwa zimene omvera ake anachita atamvetsera ulaliki wapadera umenewu. Baibulo limati: “Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake; chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro, osati monga alembi awo.”​—Mat. 7:28, 29.

21 Mosakayikira, Yesu Khristu analidi ‘Phungu Wodabwitsa.’ (Yes. 9:6) Ulaliki wapaphiri ndi chitsanzo chabwino kwambiri chosonyeza kuti Yesu amaona zinthu mmene Atate wake wakumwamba amazionera. Kuwonjezera pa mfundo zimene takambiranazi, muulalikiwu Yesu anatchulanso za mmene tingakhalire ndi moyo wosangalala, mmene tingapewere chiwerewere, mmene tingachitire chilungamo, zimene tingachite kuti tikhale ndi tsogolo labwino, ndi zina zotero. Mungachite bwino kupemphera ndipo kenako kuwerenganso mofatsa Mateyo chaputala 5 mpaka 7. Sinkhasinkhani za uphungu wodabwitsa wa Yesu. Yesetsani kugwiritsa ntchito pamoyo wanu zimene Khristu ananena pa ulaliki umenewu. Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kukondweretsa Yehova, kukhala bwino ndi ena, ndi kupitiriza kuchita zabwino.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi adani athu tiziwachitira zinthu zotani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kumakhululukira ena?

• Kodi Yesu anati chiyani pankhani yoweruza ena?

• Malinga ndi Mateyo 7:12, kodi tiyenera kuchitira ena zotani?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Kodi mumadziwa chifukwa chake Yesu anati: “Lekani kuweruza ena”?

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera otizunza?

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi mumachitira ena zimene mumafuna kuti iwo azikuchitirani?