Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinu Wokonzeka Kufotokoza za Chikhulupiriro Chanu?

Kodi Ndinu Wokonzeka Kufotokoza za Chikhulupiriro Chanu?

Kodi Ndinu Wokonzeka Kufotokoza za Chikhulupiriro Chanu?

KODI pali nthawi ina imene munafunika kufotokoza za chikhulupiriro chanu? Izi n’zimene Susana, mlongo wa kusekondale wa zaka 16 ku Paraguay, anafunika kuchita. Tsiku lina ali m’kalasi, paphunziro lokhudza chikhalidwe, mwana wina ananena kuti Mboni za Yehova sizikhulupirira “Chipangano Chakale,” Yesu Khristu komanso Mariya. Winanso ananena kuti Amboni amakana mankhwala ndipo amalolera kufa. Kodi mukanakhala inuyo mukanatani?

Susana anapemphera kwa Yehova ndipo kenako anaimika mkono. Popeza phunzirolo linali likupita kumapeto, iye anapempha aphunzitsi ake kuti amulole kudzafotokoza zimene Mboni za Yehova zimakhulupirira. Aphunzitsiwo sanakane. Susana anakonzekera kwa milungu iwiri zoti akafotokoze ku sukuluko. Anatero pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mboni za Yehova​—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?

Tsikulo litakwana, Susana analongosola chifukwa chake timatchedwa Mboni za Yehova. Analongosolanso za chiyembekezo chathu ndiponso chifukwa chimene timakanira magazi. Kenako anapereka mwayi kuti aliyense m’kalasimo afunse mafunso. Ambiri anaimika mikono. Aphunzitsi aja anachita chidwi kumva mtsikanayu akuyankha mafunso pogwiritsa ntchito Malemba.

Mnyamata wina m’kalasimo anati: “Ine ndinapitapo ku Nyumba ya Ufumu, koma sindinaoneko fano ngakhale limodzi.” Aphunzitsi aja anafuna kudziwa chifukwa chake. Choncho Susana anawerenga Salmo 115:4-8 ndi Eksodo 20:4. Podabwa, aphunzitsiwo anati: “Nanga bwanji matchalitchi athu adzaza ndi mafano pamene Baibulo limaletsa?”

Mafunsowa anatenga mphindi 40. Susana atawafunsa ngati angakonde kuonera vidiyo yakuti No Blood​—Medicine Meets the Challenge, onse anavomera. Chotero aphunzitsi awo anakonza zoti adzaonere vidiyoyi tsiku lotsatira. Atatha kuonera, Susana analongosola kuti pali njira zina zosiyanasiyana zothandizira odwala popanda kuwaika magazi, ndipo Mboni za Yehova zina zimalandira. Atamva zimenezi, aphunzitsiwo anati: “Sindinkadziwa kuti pali njira zosiyanasiyana chonchi zothandizira odwala popanda kuwaika magazi. Ndipo sindinkadziwa ubwino wopewa kuikidwa magazi. Kodi njira zimenezi ndi za Mboni za Yehova zokha?” Atamva kuti si za Amboni okha, aphunzitsiwo anati: “Tsiku limene Mboni za Yehova zidzafike kunyumba kwanga, ndidzacheza nazo.”

Susana anali kuyembekezera kuti akambirana kwa mphindi 20, koma m’malomwake anakambirana kwa maola atatu. Patapita mlungu umodzi, ana ena m’kalasimo anafotokoza zikhulupiriro za matchalitchi awo. Atamaliza anafunsidwa mafunso ambiri okhudza zikhulupiriro zawozo, koma analephera kuyankha. Aphunzitsi awo anawafunsa kuti, “Bwanji mukulephera kufotokoza za chikhulupiriro chanu mmene mnzanu wa Mboni za Yehovayu anachitira?”

Iwo anayankha kuti: “Anzathuwa amaphunziradi Baibulo, koma ife sitiphunzira.”

Kenako aphunzitsiwo anauza Susana kuti: “Zoonadi, inu mumaphunziradi Baibulo ndipo mumayesetsa kuchita zimene limanena. M’pofunika kukuyamikirani kwambiri.”

Susana akanatha kungokhala phee, osayankha. Koma chifukwa choyankhapo, anatsatira chitsanzo chabwino cha kamtsikana kena ka ku Isiraeli kamene kanagwidwa ukapolo ndi Aaramu. Mtsikanayu ankakhala ku nyumba kwa Namani, yemwe anali mkulu wa asilikali a Aaramu. Mkuluyu anadwala nthenda yoopsa ya pakhungu. Mtsikana wa ku Isiraeliyu anauza mkazi wa mbuye wake kuti: “Mbuye wanga akadakhala kwa mneneri ali m’Samariya, akadam’chiritsa khate lake.” Mtsikana ameneyo sanazengereze kuchitira umboni za Mulungu woona. Chifukwa cha zimenezi, mbuye wake Namani anayamba kulambira Yehova.​—2 Maf. 5:3, 17.

Mofanana ndi mtsikanayu, Susana nayenso anachitira umboni za Yehova ndi anthu ake. Mwa kuyankhapo kuti akonze maganizo olakwika okhudza chikhulupiriro chake, Susana anamvera lamulo la m’Malemba lakuti: “Pangani Khristu kukhala woyera m’mitima mwanu, monga Ambuye. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense wofuna kudziwa chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.” (1 Pet. 3:15) Kodi ndinu wokonzeka kufotokoza za chikhulupiriro chanu pakafunika kutero?

[Chithunzi patsamba 17]

Zinthu izi zingakuthandizeni kufotokoza za chikhulupiriro chanu