Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Yesu Anali Kunena za Moto wa Helo?

Kodi Yesu Anali Kunena za Moto wa Helo?

Kodi Yesu Anali Kunena za Moto wa Helo?

ANTHU ena amene amakhulupirira chiphunzitso cha moto wa helo amagwiritsa ntchito mawu a Yesu a pa Maliko 9:48. Pamenepa iye ananena za mphutsi zimene sizifa komanso za moto umene suzima. Kodi munthu wina atakufunsani za mawu amenewa, mungamuyankhe bwanji?

Malinga ndi Baibulo limene ali nalo, munthu angawerenge vesi 44, 46, kapena 48 chifukwa mavesi amenewa amafanana m’Mabaibulo ena. * Baibulo la Dziko Latsopano limati: “Ngati diso lako limakupunthwitsa, ulitaye; ndi bwino kuti ulowe mu ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana n’kuponyedwa mu Gehena uli ndi maso onse awiri, kumene mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.”​—Maliko 9:47, 48.

Ngakhale zili choncho, ena amanena kuti mawu a Yesu amachirikiza mfundo yakuti anthu oipa akamwalira, mizimu yawo imazunzika kosatha. Mwachitsanzo, ndemanga yopezeka m’Baibulo la Chisipanishi la Sagrada Biblia la ku Yunivesite ya Navarre, imati: “Ambuye wathu anagwiritsa ntchito [mawu amenewa] pofotokoza kuzunzika kwa anthu ku helo. Kawirikawiri ‘mphutsi imene siifa’ imaimira chisoni chosatha chimene anthu ku helo amakhala nacho. Ndipo ‘moto umene suzima’ umaimira kupweteka kumene iwo amamva polangidwa.”

Ndiyeno, tayerekezerani mawu a Yesu ndi mawu amene ali pa vesi lomaliza la ulosi wa Yesaya. * Kodi si zoonekeratu pamenepa kuti Yesu anali kuganiza za mawu a mu Yesaya chaputala 66 amenewa? Malinga ndi nkhaniyo, zikuoneka kuti mneneriyo ananena za kutuluka “mu Yerusalemu kupita ku Chigwa cha Hinomu (Gehena) chimene chinali kunja, kumene ankapereka nsembe za anthu kalelo (Yer. 7:31), ndipo kenako chinadzakhala dzala.” (The Jerome Biblical Commentary) Mwachionekere, mawu ophiphiritsa a pa Yesaya 66:24 sanena za kuzunza anthu. Amanena za mitembo. Ndipo zimene lembali likunena kuti sizifa ndi mphutsi. Silinena za anthu amoyo kapena mizimu yosafa. Nanga kodi mawu a Yesu amatanthauza chiyani?

Taonani mmene buku lina la Chikatolika limafotokozera lemba la Maliko 9:48. Limati: “Mawuwa achokera pa Yesaya (66,24). Pamenepo mneneriyo akufotokoza za njira ziwiri zimene kawirikawiri mitembo inkawonongekera: inali kuwola kapena kupsa ndi moto . . . Kutchulira limodzi mphutsi ndi moto kukutsindika kuopsa kwa chiwonongeko. . . . Zinthu ziwirizo zimene zili ndi mphamvu yowononga zikufotokozedwa kuti ndi zosatha (‘suzima, sizifa’), ndipo ndi zosathawika. Palemba limeneli, mphutsi ndi moto basi n’zimene sizikuwonongeka, osati anthu. Ndipo mphutsi ndi moto zikuwonongeratu chilichonse chimene chagweramo. Choncho, apa sakufotokoza za kuzunzika kosatha, koma za chiwonongeko chotheratu chimene ndi imfa yomaliza, chifukwa owonongedwawo sadzaukitsidwa. Chotero, [moto] ndi chizindikiro cha chiwonongeko chotheratu.”​—El evangelio de Marcos. Análisis lingüístico y comentario exegético, Voliyumu II.

Aliyense amene amadziwa kuti Mulungu woona ndi wachikondi komanso wachilungamo, atha kuona kuti m’pomveka kufotokoza tanthauzo la mawu a Yesu mwanjira imeneyi. Yesu sanali kunena kuti oipa adzazunzidwa kosatha. M’malomwake, oipawo atha kulandira chiwonongeko chotheratu popanda chiyembekezo cha kuukitsidwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 M’mipukutu yodalirika ya Baibulo mulibe vesi 44 ndi 46. Akatswiri amavomereza kuti mavesi awiriwa anangowonjezeredwa pambuyo pake. Pulofesa Archibald T. Robertson analemba kuti: “M’mipukutu yakale kwambiri komanso yodalirika mulibe mavesi awiriwa. Mavesiwa anachokera m’mipukutu ya Kumadzulo ndi ya ku Suriya (Byzantine). Ndipo amangobwereza mawu a m’vesi 48. Choncho, m’mavesi athu [tachotsamo] vesi 44 ndi 46 amene si oona.”

^ ndime 5 “Iwo adzatuluka ndi kuyang’ana mitembo ya anthu amene andilakwira Ine, pakuti mbozi yawo sidzafa, pena moto wawo sudzazimidwa; ndipo iwo adzanyansa anthu onse.”​—Yes. 66:24.