Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Makhalidwe Amene Tiyenera Kutsatira

Makhalidwe Amene Tiyenera Kutsatira

Makhalidwe Amene Tiyenera Kutsatira

‘Tsatirani chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa mtima.’​—1 TIM. 6:11.

1. Perekani zitsanzo zosonyeza tanthauzo la mawu akuti “tsatirani.”

KODI mukamva mawu akuti “tsatirani” kapena kuti “londolani,” mumaganiza chiyani? N’kutheka kuti mumaganiza za nthawi ya Mose pamene asilikali a ku Iguputo ‘analondola’ Aisiraeli, n’kungofikira kuwonongedwa m’Nyanja Yofiira. (Eks. 14:23) Kapena mungakumbukire zimene zinkachitika munthu akapha mnzake mwangozi ku Isiraeli. Pofuna kupulumutsa moyo wake, anafunika kuthawira ku wina mwa midzi 6 yopulumukirako. Kulephera kuchita zimenezi mwamsanga kunali koopsa kwambiri chifukwa ‘wolipsa mwazi akanam’londola . . . pokhala mtima wake utatentha, n’kum’peza, . . . n’kumukantha kuti afe.’​—Deut. 19:6.

2. (a) Kodi Akhristu ena ayenera kuyesetsa kupeza mphoto yotani imene Mulungu wawaikira? (b) Kodi Yehova adzapatsa Akhristu ambiri mphoto yotani?

2 Mosiyana ndi zitsanzo za m’Baibulo zomwe tatchulazi, ganizirani mawu amene mtumwi Paulo analemba, akuti: “Ndikuyesetsa mpaka ndikapate mphoto ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba, chodzera mwa Khristu Yesu.” (Afil. 3:14) Baibulo limasonyeza kuti Akhristu odzozedwa okwana 144,000, kuphatikizapo Paulo, amalandira mphoto ya moyo wakumwamba imeneyi. Iwowa adzalamulira dziko lapansi limodzi ndi Yesu Khristu mu ulamuliro wake wa zaka 1,000. Imeneyi ndi mphoto yabwino kwambiri imene Mulungu wawaikira ndipo ayenera kuyesetsa kuitsatira mpaka ataipeza. Koma Akhristu oona ambiri akuyembekezera mphoto yosiyana ndi imeneyi. Yehova mwachikondi adzawapatsa moyo wopanda mavuto m’paradaiso padziko lapansi, umene Adamu ndi Hava anataya.​—Chiv. 7:4, 9; 21:1-4.

3. Kodi tingachite chiyani kuti tisonyeze kuyamikira kwathu kukoma mtima kwa m’chisomo kwa Mulungu?

3 Anthu ochimwafe, pokhala opanda ungwiro, sitingapeze moyo wosatha mwa kuyesetsa kwathu kuchita zinthu zolungama. (Yes. 64:6) Koma tingathe kupeza moyo wosatha kokha ngati tikhulupirira dongosolo lopulumutsira anthu limene Mulungu mwachikondi chake wakonza kudzera mwa Yesu Khristu. Kodi ifeyo tingachite chiyani kuti tisonyeze kuyamikira kwathu kukoma mtima kwa m’chisomo kwa Mulungu kumeneku? China chimene tingachite ndi kumvera lamulo ili lakuti: ‘Tsatirani chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa mtima.’ (1 Tim. 6:11) Kuganizira makhalidwe amenewa kungatithandize tonsefe kuyesetsa kuwatsatira “mowonjezereka.”​—1 Ates. 4:1.

‘Tsatirani Chilungamo’

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutsatira “chilungamo” n’kofunika, ndipo n’chiyani chimene munthu ayenera kuchita choyamba kuti atsatire chilungamo?

4 M’kalata zake zonse ziwiri zopita kwa Timoteyo, mtumwi Paulo anatchula makhalidwe ofunika kuwatsatira, ndipo m’kalata zonsezi, khalidwe loyambirira kulitchula ndi “chilungamo.” (1 Tim. 6:11; 2 Tim. 2:22) Kuwonjezera pamenepa, Baibulo m’mavesi ena limatilimbikitsa mobwerezabwereza kutsatira chilungamo. (Miy. 15:9; 21:21; Yes. 51:1) Chinthu choyamba chimene tingachite potsatira chilungamo ndicho ‘kuphunzira ndi kudziwa za . . . Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene [iye] anam’tuma.’ (Yoh. 17:3) Pofuna kutsatira chilungamo, munthu amalapa machimo amene anachita ndi “kutembenuka” kuti achite chifuniro cha Mulungu.​—Mac. 3:19.

5. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale olungama pamaso pa Mulungu ndiponso kuti tipitirizebe kutero?

5 Anthu ambiri amene akutsatiradi chilungamo apereka moyo wawo kwa Yehova ndipo asonyeza zimenezi mwa kubatizidwa. Ngati ndinu Mkhristu wobatizidwa, kodi mwaganizirapo mfundo yakuti zimene mumachita pa moyo wanu ziyenera, ndipo tikhulupirira kuti zimasonyeza kumene, kuti mukupitiriza kutsatira chilungamo? Njira imodzi yosonyeza kuti mukutsatira chilungamo ndiyo kugwiritsa ntchito Baibulo posiyanitsa “choyenera ndi cholakwika” pamene mukupanga zosankha zazikulu zokhudza moyo wanu. (Werengani Aheberi 5:14.) Mwachitsanzo, ngati ndinu Mkhristu wamsinkhu wokwatira kapena kukwatiwa, kodi ndinu wotsimikiza mtima kuti zivute zitani, mudzapeweratu kukhala pa chibwenzi ndi Mkhristu wosabatizidwa? Ngati mukutsatira chilungamo, ndiye kuti ndinu wotsimikizadi.​—1 Akor. 7:39.

6. Kodi kutsatiradi chilungamo kumafuna chiyani?

6 Kukhala wolungama n’kosiyana ndi kudzilungamitsa kapena ‘kukhala wolungama mopambanitsa.’ (Mlal. 7:16) Yesu anachenjeza kuti tisamadzionetse kukhala olungama kuti tioneke abwino kuposa ena. (Mat. 6:1) Kutsatiradi chilungamo kumafuna kuti tikonze mtima wathu, kuchotsamo maganizo, zolinga, ndi zilakolako zoipa. Tikamayesetsa kukonza mtima wathu, tidzapewa kuchita machimo akuluakulu. (Werengani Miyambo 4:23; yerekezerani ndi Yakobe 1:14, 15.) Ndiponso Yehova adzatidalitsa ndi kutithandiza pamene tikutsatira makhalidwe ena ofunika achikhristu.

‘Tsatirani Kudzipereka kwa Mulungu’

7. Kodi “kudzipereka kwa Mulungu” n’kutani?

7 Kudzipereka kumaphatikizapo kudzikhuthula ndi mtima wonse ndiponso kukhala wokhulupirika. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limanena kuti mawu a Chigiriki omasuliridwa kuti “kudzipereka kwa Mulungu” amafotokoza za “mtima wofuna kupitirizabe kuopa Mulungu.” Aisiraeli ankachita zinthu zosonyeza kusamvera ngakhale pambuyo poti Mulungu wawamasula ku ukapolo ku Iguputo. Zimenezi ndi umboni wakuti nthawi zambiri ankalephera kusonyeza kudzipereka kotereku.

8. (a) Kodi tchimo la Adamu linayambitsa funso lotani? (b) Kodi yankho la “chinsinsi chopatulika” chimenechi linaululidwa motani?

8 Kuchimwa kwa Adamu kunayambitsa funso limene linatenga zaka zambiri osayankhidwa. Funso lake linali lakuti, “Kodi pangapezeke munthu wodzipereka kwa Mulungu popanda kulakwitsako chilichonse?” Nthawi yonseyo, panalibe munthu wopanda ungwiro aliyense amene anakwanitsa kukhala wodzipereka kwa Mulungu popanda kulakwitsako chilichonse. Koma panthawi yake yoyenera, Yehova anaulula yankho la “chinsinsi chopatulika” chimenechi. Iye anasamutsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya kuti abadwe monga munthu wangwiro. M’moyo wake wonse wa padziko lapansi, kuphatikizapo imfa yake yochititsa manyazi, Yesu anasonyeza zimene kudzikhuthula ndi mtima wonse komanso kukhala wokhulupirika kotheratu kwa Mulungu woona, kumatanthauza. Mapemphero ake anasonyeza kuti iye ankalemekeza kwambiri Atate wake wakumwamba, yemwe ndi wachikondi. (Mat. 11:25; Yoh. 12:27, 28) Motero, Yehova anauzira Paulo kutchula za ‘kudzipereka kwa Mulungu’ pofotokoza za chitsanzo chabwino cha moyo wa Yesu.​—Werengani 1 Timoteyo 3:16.

9. Kodi kudzipereka kwa Mulungu tingakutsatire motani?

9 Popeza kuti ndife anthu ochimwa, sitingathe kukhala odzipereka kwa Mulungu popanda kulakwitsako chilichonse. Komabe tingathe kutsatira kudzipereka kwa Mulungu. Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tifunika kutsatira chitsanzo cha Khristu mosamalitsa. (1 Pet. 2:21) Tikatero, sitidzafanana ndi anthu onyenga amene ‘amaoneka ngati odzipereka kwa Mulungu’ koma zochita zawo sizigwirizana ndi kudziperekako. (2 Tim. 3:5) Kodi izi zikutanthauza kuti kudzipereka kwenikweni kwa Mulungu sikukhudza maonekedwe athu? Ayi. Mwachitsanzo, kaya tikusankha diresi la ukwati kapena zimene tiyenera kuvala pokagula zinthu, maonekedwe athu ayenera kugwirizana ndi zimene timanena kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ (1 Tim. 2:9, 10) Inde, kutsatira kudzipereka kwa Mulungu kumafuna kuti pamoyo wathu, tiziganizira mfundo zake zolungama.

‘Tsatirani Chikhulupiriro’

10. Kodi tingatani kuti tikhalebe ndi chikhulupiriro cholimba?

10 Werengani Aroma 10:17. Kuti Mkhristu akhale ndi chikhulupiriro cholimba ndi kupitirizabe kukhala nacho, sayenera kusiya kusinkhasinkha mfundo za choonadi zapamwamba zopezeka m’Mawu a Mulungu. Pofuna kutithandiza, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” watipatsa mabuku abwino ambiri. Ena mwa mabukuwa ndi Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako, Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso ndi “Come Be My Follower.” Mabuku atatu apaderawa anakonzedwa kuti atithandize kum’dziwa bwino Khristu, kuti tithe kumutsanzira. (Mat. 24:45-47) Gulu la kapolo limakonzanso misonkhano yampingo, yadera ndi yachigawo. Ndipo misonkhano yambiri imafotokoza “mawu onena za Khristu.” Kodi mwaganizirapo mmene mungapindulire kwambiri ndi misonkhanoyi ngati ‘musamalira mwapadera, koposa mwa nthawi zonse’ zimene Mulungu akupereka?​—Aheb. 2:1.

11. Kodi pemphero ndi kumvera, n’zofunika bwanji kuti titsatire chikhulupiriro?

11 Pemphero lingatithandizenso kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Panthawi ina, otsatira a Yesu anam’pempha kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.” Nafenso tingam’pemphe Mulungu modzichepetsa kuti atiwonjezere chikhulupiriro. (Luka 17:5) Ndiyetu m’pofunika kupempherera thandizo la Mulungu la mzimu woyera, popeza “chikhulupiriro” ndi mbali ya chipatso cha mzimu. (Agal. 5:22) Komanso, kumvera malamulo a Mulungu kumalimbitsa chikhulupiriro chathu. Mwachitsanzo, tingadzipereke kuti tichite zambiri m’ntchito yathu yolalikira. Kuchita zimenezi kungatithandize kukhala ndi chimwemwe chachikulu. Ndiponso kuganizira madalitso amene amabwera chifukwa cha “kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu],” kudzakulitsa chikhulupiriro chathu.​—Mat. 6:33.

‘Tsatirani Chikondi’

12, 13. (a) Kodi lamulo latsopano la Yesu ndi lotani? (b) Kodi tiyenera kutsatira chikondi cha Khristu m’njira zofunika ziti?

12 Werengani 1 Timoteyo 5:1, 2Paulo anapereka malangizo abwino a mmene Akhristu angasonyezerane chikondi. Kudzipereka kwathu kwa Mulungu kumaphatikizapo kumvera lamulo latsopano la Yesu lakuti ‘tizikondana wina ndi mnzake’ mmene iye anatikondera. (Yoh. 13:34) Mtumwi Yohane anafunsa mosapita m’mbali kuti: “Aliyense amene ali ndi zofunika pa moyo m’dziko lino, n’kuona m’bale wake zikum’sowa, koma n’kumutsekereza chifundo chake chachikulu, kodi munthu ameneyu amakonda Mulungu?” (1 Yoh. 3:17) Kodi mukukumbukira nthawi imene munasonyeza chikondi mwa kuthandiza munthu wina?

13 Njira ina imene timasonyezera kuti tikutsatira chikondi ndiyo kukhululukira abale athu, osati kusungirana zakukhosi. (Werengani 1 Yohane 4:20.) Tifunika kutsatira uphungu wouziridwa uwu: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso.” (Akol. 3:13) Kodi pali wina mumpingo amene mukufunika kumukhululukira? Kodi mum’khululukira?

‘Tsatirani Chipiriro’

14. Kodi tingaphunzire chiyani ku mpingo wa ku Filadefiya?

14 N’zosavuta anthufe kuchita khama ngati chinthu chimene tikufuna tichipeza msanga, koma n’zovuta kuchita khama ngati chinthu chimene tikufuna sitichipeza msanga. N’chifukwa chake tifunika kupirira kuti tidzapeze moyo wosatha. Ambuye Yesu anauza mpingo wa ku Filadefiya kuti: “Pakuti unasunga mawu onena za chipiriro changa, inenso ndidzakusunga pa ola la kuyesedwa.” (Chiv. 3:10) Indedi, Yesu anaphunzitsa kufunika kwa kupirira, khalidwe lomwe limatithandiza kuti tisagonje tikakumana ndi ziyeso. Abale a mumpingo wa ku Filadefiya ayenera kuti anasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri cha kupirira pamene chikhulupiro chawo chinayesedwa. N’chifukwa chake Yesu anawatsimikizira kuti adzawathandizanso pa chiyeso chachikulu chimene anali kudzakumana nacho.​—Luka 16:10.

15. Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani za kupirira?

15 Yesu anadziwa kuti otsatira ake adzadedwa ndi achibale osakhulupirira komanso ndi dziko. N’chifukwa chake kawiri konse anawalimbikitsa kuti: “Yekhayo amene adzapirira mpaka mapeto ndi amene adzapulumuka.” (Mat. 10:22; 24:13) Yesu anasonyezanso mmene ophunzira ake akanapezera mphamvu zowathandiza kupirira panthawiyo. M’fanizo lake lina, iye anayerekezera ndi nthaka yamiyala anthu “amene akangomva [mawu a Mulungu], amawalandira ndi chimwemwe,” koma nthawi ya kuyesedwa ikafika amagwa. Koma iye anayerekezera otsatira ake okhulupirika ndi nthaka yabwino chifukwa ‘amasunga’ mawu a Mulungu ndi “kubereka zipatso mwa kupirira.”​—Luka 8:13, 15.

16. Kodi n’chiyani chathandiza anthu ambiri kupirira?

16 Kodi mwaona chinsinsi cha kupirira? Tifunika ‘kusunga’ mawu a Mulungu, kutanthauza kuti mawuwo azikhala amoyo mumtima ndi m’maganizo mwathu. N’zotheka kuchita zimenezi popeza tili ndi Baibulo la Dziko Latsopano, lomwe ndi lolondola ndiponso losavuta kuwerenga, komanso likumasuliridwa m’zinenero zambiri. Tikamawerenga tsiku ndi tsiku kachigawo ka Mawu a Mulungu ndi kusinkhasinkha, timapeza mphamvu zofunika kuti tipitirize kubereka zipatso “mwa kupirira.”​—Sal. 1:1, 2.

‘Tsatirani Kufatsa Mtima’ ndi Mtendere

17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani “kufatsa mtima” kuli kofunika kwambiri? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali wofatsa mtima?

17 Palibe amene amasangalala akamaimbidwa mlandu pa zinthu zimene sananene kapena kuchita. Anthu ambiri amayankha mwaukali ena akawanamizira chinachake. Koma zimakhala bwino “kufatsa mtima.” (Werengani Miyambo 15:1.) Kuti munthu akhale wofatsa akanamiziridwa, amafunika kudziletsa kwambiri. Yesu Khristu ndi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi. “Pamene anali kunenedwa zachipongwe, sanabwezere zachipongwe. Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa iye amene amaweruza molungama.” (1 Pet. 2:23) Ngakhale kuti ifeyo sitingathe kutsatira Yesu ndendende pankhani imeneyi, kodi sitingayesetse kukhala ofatsa mtima?

18. (a) Kodi kufatsa mtima kuli ndi ubwino wotani? (b) Kodi ndi khalidwe linanso liti limene tikulimbikitsidwa kulitsatira?

18 Potsanzira Yesu, tiyeni tikhale “okonzeka nthawi zonse kuyankha” mafunso okhudza zimene timakhulupirira, koma tiziyankha ndi ‘mtima wofatsa ndi ulemu waukulu.’ (1 Pet. 3:15) Tikasemphana maganizo ndi anthu amene takumana nawo muutumiki kapena ndi okhulupirira anzathu, kufatsa mtima kumatithandiza kusakwiya msanga ndi kupewa kuyambitsa mikangano. (2 Tim. 2:24, 25) Kufatsa kumatithandiza kukhala pamtendere. Mwina n’chifukwa chake Paulo, m’kalata yake yachiwiri yopita kwa Timoteyo, anatchulanso “mtendere” pamakhalidwe ofunika kuwatsatira. (2 Tim. 2:22; yerekezerani ndi 1 Timoteyo 6:11.) Zoonadi, “mtendere” ndi khalidwe lina limene Malemba amatilimbikitsa kutsatira.​—Sal. 34:14; Aheb. 12:14.

19. Pambuyo pokambirana makhalidwe 7 achikhristu, kodi inuyo muyesetsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?

19 Takambirana makhalidwe 7 achikhristu amene tikulimbikitsidwa kuwatsatira. Makhalidwewa ndi chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, kufatsa mtima ndi mtendere. Zimasangalatsa kwambiri ngati abale ndi alongo mumpingo akuyesetsa kukhala ndi makhalidwe apamwamba amenewa. Zimenezi zimalemekeza Yehova ndipo zimathandiza kuti aumbe aliyense wa ife kuti iyeyo atamandike.

Mfundo Zoti Musinkhesinkhe

• Kodi kutsatira chilungamo ndi kudzipereka kwa Mulungu kumaphatikizapo chiyani?

• Kodi chingatithandize n’chiyani kuti titsatire chikhulupiriro ndi chipiriro?

• Kodi chikondi chimakhudza bwanji zochita zathu ndi ena?

• Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kutsatira kufatsa ndi mtendere?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 12]

Yesu anachenjeza kuti si bwino kudzionetsera kuti ndife olungama

[Chithunzi patsamba 13]

Tingatsatire chikhulupiriro tikamasinkhasinkha choonadi cha m’Mawu a Mulungu

[Chithunzi patsamba 15]

Tiyenera kutsatira chikondi ndi kufatsa mtima