Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musasiye ‘Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba’

Musasiye ‘Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba’

Musasiye ‘Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba’

‘Gwiranibe zolimba chimene muli nacho.’​—CHIV. 3:11.

1, 2. Kodi munamva bwanji mutakhutira kuti zimene munali kuphunzira zokhudza Yehova ndi zoona?

KODI mukukumbukira nthawi yoyamba imene munaphunzira za chiyembekezo chosangalatsa chimene Yehova amapereka kwa anthu omvera? Ngati munali m’chipembedzo china, kodi munamva bwanji pamene Mboni zinakufotokozerani zolinga za Mulungu kuchokera m’Malemba, kapena pamene zinakufotokozerani bwinobwino ziphunzitso zimene poyamba simunkazimvetsa? Mwina munazindikira kuti kuchipembedzo chanu munali wosochera. Koma tsopano mukusangalala kuti mwadziwa choonadi. Ngati munaleredwa ndi makolo achikhristu, kodi mukukumbukira mmene munamvera mutakhutira kuti zimene munali kuphunzira zokhudza Yehova ndi zoona, kenako kusankha kuzitsatira?​—Aroma 12:2.

2 Abale anu auzimu ambiri angakuuzeni kuti atayamba kuphunzira choonadi, anasangalala kwambiri, anayandikira Yehova ndipo anamuthokoza kuti anawakokera mu mpingo wake. (Yoh. 6:44) Chifukwa chosangalala, iwo anayamba kutenga nawo mbali m’zochitika zachikhristu. Anali ndi chimwemwe chodzadza tsaya motero kuti ankafuna kuuza wina aliyense zimene aphunzira. Kodi ndi zimenenso zinakuchitikirani inuyo?

3. Kodi zinthu zinali bwanji mumpingo wa ku Efeso pamene Yesu anawatumizira uthenga?

3 Polankhula ndi mpingo wachikhristu wa ku Efeso, Yesu ananena za “chikondi chimene unali nacho poyamba.” Abale a ku Efeso anali ndi makhalidwe abwino ambiri, koma chikondi chimene anali nacho poyamba chinali chitazirala. N’chifukwa chake Yesu anawauza kuti: “Ndikudziwa ntchito zako, kulimbika kwako, ndi chipiriro chako, ndi kuti sungalekelere anthu oipa. Unayesanso anthu amene amadzitcha atumwi pamene sali atumwi, ndipo unapeza kuti ndi onama. Umaonetsanso kupirira, ndipo walimbika chifukwa cha dzina langa, sunatope. Komabe, ndakupeza ndi mlandu uwu, unasiya chikondi chimene unali nacho poyamba.”​—Chiv. 2:2-4.

4. N’chifukwa chiyani uthenga umene Yesu anapereka ku mpingo wa ku Efeso uli wofunika masiku ano?

4 Uphungu umene Yesu anapereka ku mpingo wa ku Efeso ndi mipingo ina yotchulidwa m’buku la Chivumbulutso ndi woyenerera, tikaganiza za mmene zinthu zinalili pakati pa Akhristu odzozedwa kwa zaka zingapo kuyambira 1914. (Chiv. 1:10) N’zotheka kuti ngakhale panopa Akhristu ena angasiye “chikondi chimene [anali] nacho poyamba” kwa Yehova ndiponso pa choonadi. Poganizira zimenezi, tiyeni tione mmene kukumbukira ndi kusinkhasinkha zimene zinakuchitikirani, kungakuthandizireni kukhalabe ndiponso kukulitsa chikondi komanso changu chimene munali nacho poyamba, kwa Mulungu ndi pa choonadi.

Kodi N’chiyani Chinakukhutiritsani Kuti Mwapeza Choonadi?

5, 6. (a) Kodi Mkhristu aliyense ayenera kutsimikizira chiyani? (b) Kodi n’chiyani chinakukhutiritsani kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi? (c) Kodi n’chiyani chingathandize munthu kukhalanso ndi chikondi chimene anali nacho poyamba?

5 Munthu aliyense amene akufuna kudzipereka kwa Yehova afunika choyamba ‘kuzindikira,’ kapena kuti kutsimikizira “chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” (Aroma 12:1, 2) Kuchita zimenezi kumaphatikizapo kuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Anthu amakhutiritsidwa kuti Mboni za Yehova zimaphunzitsa choonadi pazifukwa zosiyanasiyana. Ena amakumbukira kuti anasintha maganizo awo atawerenga koyamba dzina la Mulungu m’Baibulo kapena atamvetsa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira. (Sal. 83:18; Mlal. 9:5, 10) Ena anakhudzidwa ataona chikondi chimene anthu a Yehova ali nacho. (Yoh. 13:34, 35) Ndipo enanso anakhutira atadziwa zimene kusakhala mbali ya dziko kumatanthauza. Iwo anafika poona kuti Akhristu oona salowerera mikangano ya ndale kapena nkhondo za dziko lililonse.​—Yes. 2:4; Yoh. 6:15; 17:14-16.

6 Kwa anthu ambiri, mfundo zimenezi ndiponso zina ndi zimene zinawachititsa kuyamba kukonda Mulungu. Inunso muli ndi mfundo zimene zinakukhutiritsani kuti mwapeza choonadi. Choncho, muziganizira mfundo zimenezo. Pajatu inu ndinu munthu panokha ndipo zochitika pamoyo wanu zingasiyane ndi za ena. Motero zifukwa zimene munakondera Yehova ndi kukhulupirira malonjezo ake, zingasiyanenso ndi za ena. Mpaka panopa, zifukwazo ziyenera kuti sizinasinthe, zili mmene zinalili poyamba. Choonadi sichinasinthe. Chotero, kusinkhasinkha mfundo zimenezo ndi mmene zinakukhudzirani, kungakuthandizeni kukhalanso ndi chikondi chanu choyamba pa choonadi.​—Werengani Salmo 119:151, 152; 143:5.

Kulitsani Chikondi Chimene Munali Nacho Poyamba

7. N’chifukwa chiyani tifunika kukulitsa chikondi chathu choyamba pa choonadi, ndipo tingachite bwanji zimenezi?

7 N’kutheka kuti zinthu zambiri zasintha pamoyo wanu kuyambira pamene inuyo munadzipereka kwa Yehova. Chikondi chanu choyamba pa choonadi chinali chofunika, koma m’kupita kwa nthawi, munafunika chikondi chozamirapo kuti mulimbane ndi mavuto oyesa chikhulupiriro chanu. Komabe Yehova anakuthandizani. (1 Akor. 10:13) Choncho, zinthu zimene zachitika pa moyo wanu zaka zonsezi ndi zofunika kwambiri kwa inu. Zakuthandizani kukulitsa chikondi chimene munali nacho poyamba, ndipo ndi njira ina imene mungatsimikizire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka.​—Yos. 23:14; Sal. 34:8.

8. Kodi Yehova anazidziwikitsa bwanji kwa Mose, ndipo kodi Aisiraeli anafika bwanji pa kumudziwa bwinobwino Mulungu?

8 Mwachitsanzo, talingalirani mmene zinthu zinalili kwa Aisiraeli pamene Yehova ananena kuti akufuna kuwamasula ku ukapolo ku Iguputo. Mulungu anazidziwikitsa kwa Mose kuti: “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eks. 3:7, 8, 13, 14) Apa Yehova anatanthauza kuti iye akhoza kukhala aliyense kuti amasule anthu ake. Malinga ndi zimene zinadzachitika pambuyo pake, Aisiraeli anaona Yehova akuvumbula mbali zosiyanasiyana za umunthu wake. Iye anakhala Wamphamvuyonse, Woweruza, Mtsogoleri, Mpulumutsi, Wankhondo ndi Wosamalira.​—Eks. 12:12; 13:21; 14:24-31; 16:4; Neh. 9:9-15.

9, 10. Kodi ndi zochitika zotani zimene zingathandize munthu kumudziwa kwambiri Mulungu, ndipo n’chifukwa chiyani ndi bwino kukumbukira zimenezo?

9 Zinthu pamoyo wanu ndi zosiyana ndi mmene zinalili kwa Aisiraeli. Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zimene zachitika pamoyo wanu zomwe zakukhutiritsani kuti Mulungu amakukondani, ndipo zalimbitsa chikhulupiriro chanu. Mwina Yehova mwa njira inayake anakhala Wokusamalirani, Wokutonthozani kapena Mphunzitsi wanu. (Werengani Yesaya 30:20b, 21.) Mwinanso munaona pemphero lanu likuyankhidwa. N’kutheka kuti munali ndi vuto linalake, koma Mkhristu mnzanu anakuthandizani. Kapena phunziro laumwini linakuthandizani kukumbukira malemba oyenerera.

10 Mutati mufotokozere anthu zimenezi, mwina ena sangachite nazo chidwi. Ndipo m’pomveka, chifukwa sizinali zozizwitsa. Koma kwa inuyo, zili ndi tanthauzo lalikulu. Inde, Yehova anakhala amene anafunika kukhala kuti akuthandizeni inuyo. Taganizirani zaka zomwe mwakhala m’choonadi. Kodi mungakumbukire nthawi zosiyanasiyana pamene munaona Yehova akukusamalirani? Kukumbukira zinthu zimenezi ndi mmene zinakukhudzirani, kungakolezere mu mtima mwanu chikondi chimene munali nacho kwa Yehova panthawi imeneyo. Musamaiwale zochitika zimenezo. Muzizisinkhasinkha. Zimenezo ndi umboni wakuti Yehova amakukondani inuyo panokha, ndipo palibe angakuletseni kukhulupirira mfundo imeneyi.

Dzifufuzeni

11, 12. Ngati chikondi cha Mkhristu pa choonadi chazirala, kodi chingakhale chifukwa chiyani, ndipo kodi Yesu anapereka uphungu wotani?

11 Ngati mukuona kuti simukukonda Mulungu ndiponso choonadi monga mmene munkachitira, sindiye kuti Mulungu wasintha. Yehova sasintha. (Mal. 3:6; Yak. 1:17) Iye ankakukondani masiku amenewo, ndipo akukukondanibe mpaka pano. Koma nanga bwanji ngati penapake ubale wanu ndi Yehova wasintha? Kodi kapena chingakhale chifukwa chakuti mukupanikizika kwambiri ndi nkhawa zamoyo? Mwina kale munkapemphera kwambiri ndi mtima wonse, munkaphunzira mwakhama ndipo munkakonda kusinkhasinkha. Kodi munali achangu muutumiki ndipo munkapezeka pa misonkhano mokhazikika kuposa panopa?​—2 Akor. 13:5.

12 Mwina simungathe kuzindikira kuti muli ndi mavuto amenewa, koma ngati mungawazindikire, kodi anayamba bwanji? Kodi nkhawa zoyenera, monga kudyetsa banja lanu, kusamalira thanzi lanu, ndi zina zotere, zakuiwalitsani kuti tsiku la Yehova layandikira? Yesu anachenjeza atumwi ake kuti: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha. Pakuti lidzafikira onse okhala pa nkhope ya dziko lonse lapansi. Chotero khalani maso, muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika.”​—Luka 21:34-36.

13. Kodi Yakobe anayerekezera Mawu a Mulungu ndi chiyani?

13 Yakobe, amene analemba nawo Baibulo, anapempha okhulupirira anzake kudzifufuza moona mtima, pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Mouziridwa, Iye analemba kuti: “Khalani ochita zimene mawu amanena, osati ongomva chabe, ndi kudzinyenga ndi malingaliro onama. Pakuti ngati munthu ali wongomva mawu, koma wosachita, ali ngati munthu wodziyang’anira nkhope yake yachibadwa pa kalilole. Pakuti amadziyang’ana yekha, koma akachokapo, nthawi yomweyo amaiwala mmene akuonekera. Koma woyang’anitsitsa m’lamulo langwiro laufulu, amene amalimbikira kutero, adzakhala wosangalala polichita chifukwa chakuti sali wongomva n’kuiwala, koma wochita.”​—Yak. 1:22-25.

14, 15. (a) Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji kupita patsogolo mwauzimu? (b) Kodi mungaganizire mafunso ati?

14 Munthu amagwiritsa ntchito kalilole pofuna kuonetsetsa kuti akuoneka bwino. Mwachitsanzo, ngati mwamuna waona kuti taye yake yapindika, amaiwongola. Ngati mkazi waona kuti tsitsi lake silikuoneka bwino, amalikonzanso. Mofanana ndi zimenezi, Malemba amatithandiza kudzifufuza kuti tione mmene tilili. Tikamayerekezera mmene tilili ndi zimene Baibulo limanena, ndiye kuti tikuligwiritsa ntchito ngati kalilole. Koma ngati tingayang’ane m’kalilole n’kuona kuti penapake pakufunika kukonza, ife osakonza, kodi pali phindu lanji? Choncho, ndi nzeru kuchita zimene taona “m’lamulo langwiro” la Mulungu kuti tikhale ‘ochita’ mawu. Ndiyetu munthu akazindikira kuti chikondi chake choyamba kwa Yehova ndi pa choonadi chazirala, angachite bwino kuganizira mafunso awa: ‘Kodi ndikukumana ndi mavuto otani pamoyo wanga, ndipo ndikulimbana nawo bwanji? Kodi kale ndinkalimbana nawo bwanji? Kodi pali chinachake chimene chasintha?’ Ngati podzifufuza mwanjira imeneyi mwapeza kuti muli ndi zofooka, musazinyalanyaze. Ngati mukufunika kusintha, sinthani mwamsangamsanga zivute zitani.​—Aheb. 12:12, 13.

15 Kusinkhasinkha kotereku kungakuthandizeninso kukhala ndi zolinga zoyenerera zomwe zingakuthandizeni kukula mwauzimu. Mtumwi Paulo anapereka uphungu wouziridwa kwa wantchito mnzake Timoteyo, umene ukanamuthandiza kupita patsogolo muutumiki wake. Paulo analimbikitsa wachinyamatayo kuti: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” Ifenso tingachite bwino kumasinkhasinkha Mawu a Mulungu, kuti tione mmene tingapitire patsogolo.​—1 Tim. 4:15.

16. Kodi muyenera kusamala chiyani pamene mukudzifufuza pogwiritsa ntchito Malemba?

16 Tikadzifufuza moona mtima, mosakayikira tidzaona zofooka zina ndi zina. Zofookazo zingatikhumudwitse, koma tisalole zimenezo. Ndipotu cholinga chodzifufuza ndi chakuti tione zinthu zimene tifunika kukonza. Satana amafuna kuti Mkhristu azidziona kuti ndi wosafunika chifukwa cha zofooka zake. Ndipo amanena kuti Mulungu alibe nafe ntchito ngakhale titayesetsa kumutumikira mwakhama. (Yobu 15:15, 16; 22:3) Limeneli ndi bodza ndipo Yesu analitsutsa mwamphamvu. Mulungu amaona kuti aliyense wa ife ndi wofunika kwambiri. (Werengani Mateyo 10:29-31.) Kudziwa zofooka zanu kuyenera kukuthandizani kukhala wodzichepetsa ndi kufunitsitsa kusintha, mothandizidwa ndi Yehova. (2 Akor. 12:7-10) Ngati simungathe kuchita zambiri chifukwa cha matenda kapena ukalamba, khalani ndi zolinga zimene mungazikwanitse, koma musabwerere m’mbuyo kapena kulola chikondi chanu kuzirala.

Pali Zifukwa Zambiri Zokhalira Oyamikira

17, 18. Kodi ubwino wokulitsa chikondi chimene munali nacho poyamba ndi wotani?

17 Mukapitiriza kukulitsa chikondi chimene munali nacho poyamba, mudzapeza madalitso ambiri. Mungathe kumudziwa kwambiri Mulungu ndi kukulitsa mtima woyamikira malangizo ake achikondi. (Werengani Miyambo 2:1-9; 3:5, 6.) Wamasalmo anati: ‘M’kusunga [maweruzo a Yehova] muli mphotho yaikulu.’ Anatinso: “Mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.” Komanso anati: “Odala angwiro m’mayendedwe awo, akuyenda m’chilamulo cha Yehova.”​—Sal. 19:7, 11; 119:1.

18 Ndithudi mungavomereze kuti pali zinthu zambiri zabwino zimene muyenera kuyamikira. Mwachitsanzo, mukudziwa chifukwa chimene dziko lafikira poipa chonchi. Mukulandira chithandizo ndi chisamaliro chauzimu chimene Mulungu akupatsa anthu ake masiku ano. Mosakayikira, mumayamikiranso kuti Yehova wakukokerani mu mpingo wake wa padziko lonse ndipo wakupatsani mwayi wokhala Mboni yake. Muziwerengetsera madalitso amene muli nawo. Mutati muyambe kutchula madalitsowo limodzi ndi limodzi, mudzaona kuti ndi ochuluka. Ngati mungamachite zimenezi nthawi ndi nthawi, zidzakuthandizani kutsatira uphungu uwu wakuti: ‘Gwiranibe zolimba chimene muli nacho.’​—Chiv. 3:11.

19. Kuwonjezera pa kusinkhasinkha za ubale wanu ndi Mulungu, kodi chofunika n’chiyani kuti mukhalebe athanzi mwauzimu?

19 Kusinkhasinkha mmene chikhulupiriro chanu chakulira pa zaka zonsezi, ndi njira imodzi imene ingakuthandizeni kugwirabe zolimba chimene muli nacho. Magazini iyi yakhala ikufotokoza mobwerezabwereza zinthu zinanso zofunikira, zimene zingakuthandizeni kukhalabe athanzi mwauzimu. Zinthuzo ndi monga kupemphera, kupezeka ndiponso kutenga mbali pa misonkhano, komanso kulalikira mwachangu. Zimenezi zingakuthandizeni kukhalanso ndi chikondi chimene munali nacho poyamba ndi kuchikulitsa.​—Aef. 5:10; 1 Pet. 3:15; Yuda 20, 21.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi zifukwa zimene munayambira kukonda Yehova zingakulimbikitseni motani panopa?

• Kodi kusinkhasinkha zomwe zakuchitikirani zaka zonsezi, kungakutsimikizireni za chiyani?

• N’chifukwa chiyani muyenera kufufuza mmene chikondi chanu pa Mulungu chilili?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Kodi ndi mbali iti ya choonadi imene inakukhudzani mtima ndi kukukhutiritsani?

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi mukuona kuti muli ndi mbali zimene mufunika kukonza?