Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tingakhale Amphamvu Ngakhale Tili Ndi Zofooka

Tingakhale Amphamvu Ngakhale Tili Ndi Zofooka

Tingakhale Amphamvu Ngakhale Tili Ndi Zofooka

ZOFOOKA zanu zingakuthetseni nzeru, ndipo zingakumatirireni ngati misundu, osachoka. Mungaganize kuti simungathe kugonjetsa zofookazo kapena mungadzione kuti ndinu wolephera kuyerekeza ndi ena, ndipo mungaone kuti iwo amakuposani. Mwinanso mungakhale mukuvutika ndi matenda ofoola komanso osowetsa mtendere. Mulimonse mmene zilili, inu mungasowe mochitira. Mungaganize mofanana ndi Yobu, yemwe anauza Mulungu kuti: “Ha! mukadandibisa kumanda, mukadandisunga m’seri, mpaka wapita mkwiyo wanu. Mukadandiikira nthawi, ndi kundikumbukira.”​—Yobu 14:13.

Kodi mungamasuke bwanji ku nkhawa zoterezi? Muyenera kuiwala kaye za mavuto anu ngakhale kuti kuchita zimenezi kungakhale kovuta. Mwachitsanzo, mungaganizire mafunso amene Yehova anafunsa mtumiki wake wokhulupirika Yobu kuti: “Unali kuti muja ndinaika maziko a dziko lapansi? Fotokoza ngati udziwa kuzindikira. Analemba malire ake ndani, popeza udziwa? Anayesapo chingwe chake ndani?” (Yobu 38:4, 5) Tikamaganizira mfundo ya mafunso amenewa, tingazindikire kuti Yehova ali ndi nzeru zapamwamba ndiponso mphamvu. Choncho walola mavuto omwe alipo m’dzikoli kupitirirabe pa chifukwa chabwino.

“Munga M’thupi”

Mtumiki wokhulupirika Paulo anapempha Yehova kuti amuchotsere “munga m’thupi,” kutanthauza vuto losatherapo. Mtumwiyu anachonderera Mulungu katatu konse kuti amuchotsere vutoli. Sitikudziwa kuti vutolo linali lotani, komabe mofanana ndi munga womwe umasowetsa mtendere, likanatha kum’landa chimwemwe chake potumikira Yehova. Paulo anayerekezera vutolo ndi kumenyedwa nthawi zonse. Poyankha, Yehova anati: “Kukoma mtima kwa m’chisomo changa kwakukwanira; pakuti mphamvu yanga imakhala yokwanira m’kufooka.” Yehova sanachotse munga m’thupi umenewo. Paulo anapitiriza kulimbana nawo, koma ananena kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndili wamphamvu.” (2 Akor. 12:7-10) Kodi anatanthauza chiyani?

Vuto la Paulo silinathe mozizwitsa. Ngakhale zinali choncho, silinamulepheretse kuchita zazikulu potumikira Yehova. Paulo anadalira Yehova kuti amusamalira ndipo nthawi zonse ankamupempha kuti amuthandize. (Afil. 4:6, 7) Pofika ku mapeto kwa moyo wake wa padziko lapansi, Paulo anatha kunena kuti: “Ndamenya nkhondo yabwino, ndathamanga panjirayo mpaka pomalizira pake, ndasunga chikhulupiriro.”​—2 Tim. 4:7.

Yehova amagwiritsa ntchito anthu kuchita chifuniro chake ngakhale kuti iwo ndi opanda ungwiro ndipo ali ndi mavuto awo. Ndipo m’pake kuti ulemu uzipita kwa iye. Amawatsogolera ndi kuwapatsa nzeru kuti apirire mavuto awo ndi kukhalabe achimwemwe pomutumikira. Zoonadi, iye amagwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuchita zazikulu ngakhale kuti iwo ali ndi zofooka.

Pofotokoza chifukwa chimene Mulungu sanamuchotsere munga m’thupi, Paulo anati: “Kuti ndisadzikweze mopambanitsa.” (2 Akor. 12:7) “Munga” wa Paulo unamukumbutsa kuti ali ndi mbali zimene amaperewera ndipo unamuthandiza kukhala wodzichepetsa. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa kuti: “Aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.” (Mat. 23:12) Mayesero angaphunzitse anthu a Mulungu kudzichepetsa ndi kuwathandiza kuzindikira kuti afunika kudalira Yehova kuti apirire mokhulupirika. Ndipo mofanana ndi mtumwiyo, iwo ‘angadzitame mwa Yehova.’​—1 Akor. 1:31.

Zofooka Zobisika

Ena angakhale ndi zofooka koma sadziwa kuti ali nazo kapena safuna kuvomereza kuti ali nazo. Mwachitsanzo, munthu angamadzidalire mopitirira muyeso, n’kumadalira nzeru zake zokha. (1 Akor. 10:12) Chofooka china chimene anthu opanda ungwirofe tili nacho ndi chakuti timafuna kutchuka.

Yoabu, yemwe anali mkulu wa asilikali a Mfumu Davide, anali munthu wolimba mtima, wosazengereza pochita zinthu ndiponso wanzeru. Komabe, Yoabu anachita zinthu zoipa kwambiri zimene zinasonyeza kuti anali ndi mzimu wodzitukumula komanso wofuna udindo. Anapha mwankhanza akulu awiri a asilikali. Woyamba anali Abineri, yemwe anamupha pofuna kubwezera. Wachiwiri anali Amasa, m’bale wake. Yoabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuchita ngati akufuna kum’psompsona koma kenako anamugwaza m’mimba ndi lupanga lomwe anagwira kumanzere kwake. (2 Sam. 17:25; 20:8-10) Yoabu anali atachotsedwa pa udindo wake monga mkulu wa asilikali n’kulowedwa m’malo ndi Amasa. Apa m’pamene Yoabu anapezerapo mpata wophera m’bale wakeyo, poganiza kuti mwina angapatsidwenso udindo wake uja. Mukhoza kuona kuti Yoabu analephera kulamulira mtima wake ndi maganizo ake ofuna udindo. Zimene anachitazi ndi nkhanza yoopsa, koma anachita zimenezi mtima uli zii. Mfumu Davide itatsala pang’ono kufa, inauza mwana wake Solomo kuti adzaonetsetse kuti Yoabu walandira chilango.​—1 Maf. 2:5, 6, 29-35.

Ifeyo sitiyenera kulekerera maganizo athu olakwika. Tingathe kulimbana ndi zofooka zathu. Choyamba, tiyenera kuzindikira zofookazo ndi kuzivomereza. Kenako tiyenera kuyesetsa kuthana nazo. Tingapemphere kwa Yehova nthawi zonse kuti atithandize kugonjetsa zofookazo, ndi kuphunzira mwakhama Mawu ake kuti tipeze njira zotithandiza kulimbana ndi maganizo athu olakwika. (Aheb. 4:12) Mwina tingafunike kulimbana ndi zofooka zathu kwa nthawi yaitali koma sitiyenera kugwa ulesi. Ndipo mwina nkhondo imeneyi ingakhale ya moyo wathu wonse chifukwa ndife opanda ungwiro. Paulo anazindikira kuti anali ndi vuto limeneli ndipo analemba kuti: “Zimene ndimafuna kuchita, sindichita; koma zimene ndimadana nazo ndi zimene ndimachita.” Komabe, monga mukudziwa, Paulo sanalekerere zofooka zake ngati kuti sakanatha kulimbana nazo. M’malo mwake, iye analimbanabe ndi zofooka zake, akudalira Mulungu kuti amuthandize kudzera mwa Yesu Khristu. (Aroma 7:15-25) Panthawi ina, Paulo anati: “Ndipumphuntha thupi langa ndi kulitsogolera ngati kapolo, kuopera kuti, pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ine ndemwe ndingakhale wosayenera m’njira inayake.”​—1 Akor. 9:27.

Anthufe timakonda kudzikhululukira. Vutoli tingathane nalo mwa kuyesetsa kukhala ndi maganizo a Yehova, monga mmene Paulo analangizira Akhristu kuti: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.” (Aroma 12:9) Kuti tipambane nkhondo yolimbana ndi zofooka zathu, timafunika kuvomereza kuti tili nazo, kuchita khama komanso kudziletsa. Davide anapempha Yehova kuti: “Yeretsani impso zanga ndi mtima wanga.” (Sal. 26:2) Iye anadziwa kuti Mulungu amatha kusanthula za mumtima mwathu ndi kutipatsa thandizo lofunikira. Ngati titsatira malangizo amene Yehova amapereka kudzera m’Mawu ake ndi mzimu wake woyera, tingapite patsogolo pankhondo yathu yolimbana ndi zofooka mpaka kupambana.

Ena angamavutike ndi zinthu zimene akuganiza kuti paokha sangazikwanitse. Apa m’pamene akulu mumpingo angapereke thandizo ndiponso chilimbikitso. (Yes. 32:1, 2) Koma tisayembekezere kuti mavuto athu onse angathe panopa. Pajatu mavuto ena sangatheretu m’dongosolo la zinthu lino. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri aphunzira kupirira, ndipo zimenezi zawathandiza kukhalabe osangalala.

Yehova Adzatisamalira

Kaya tikukumana ndi mavuto otani m’nthawi yovuta ino, tikudziwa kuti Yehova adzatitsogolera ndi kutisamalira. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti m’nthawi yake akakukwezeni. Teroni pamene mukum’tulira nkhawa zanu zonse, pakuti amasamala za inu.”​—1 Pet. 5:6, 7.

Kathy wakhala akutumikira pa Beteli kwa zaka zambiri. Atazindikira kuti mwamuna wake ali ndi matenda oopsa a muubongo, anaganiza kuti sangathe kupirira vuto la mwamuna wakeyo. Tsiku lililonse, Kathy ankachonderera Yehova kuti amupatse nzeru ndi kumulimbikitsa. M’kupita kwa nthawi matenda a mwamuna wake anakula. Koma chifukwa cha chikondi, abale anayesetsa kuphunzira za matendawo kuti adziwe mochitira, ndipo alongo analimbikitsa Kathy ndi mwamuna wake. Akhristu amenewa anali njira ina imene Yehova anaperekera chilimbikitso, ndipo Kathy anatha kusamalira mwamuna wake mpaka imfa yake, patatha zaka 11. Kathy anati: “Ndinalira pothokoza kwambiri Yehova chifukwa cha zonse zimene anandichitira. Iye anandithandiza kupirira. Sindinadziwe kuti ndikanatha kuchita zonse zofunikira kwa zaka zonsezi ngakhale kuti ndinali kufooka kwambiri chifukwa cha kutopa.”

Thandizo Logonjetsera Zofooka Zathu Zobisika

Anthu omwe amadziona kuti ndi osafunikira, amaganiza kuti Yehova sangawamve akam’pempha thandizo panthawi yamavuto. Ndiyetu ndi bwino kukumbukira zimene Davide ananena atadzimvera chisoni chifukwa cha tchimo lalikulu limene anachita ndi Bateseba. Iye anati: “Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Sal. 51:17) Davide analapa kuchokera pansi pa mtima, ndipo anadziwa kuti akhoza kupemphera kwa Mulungu ndi kuchitiridwa chifundo. Mofanana ndi Yehova, Yesu naye ali ndi mtima wachifundo. Mu uthenga wake wabwino, Mateyo anasonyeza kuti Yesu anakwaniritsa mawu a Yesaya awa: “Bango lophwanyika sadzalisansantha, ndi nyale yofuka sadzaizimitsa.” (Mat. 12:20; Yes. 42:3) Ali padziko lapansi, Yesu anachitira chifundo anthu ovutika ndi oponderezedwa. Motero tingati iye sanazimitse lawi lozirala, kapena kuti kumaliziratu anthu amene anali ngati nyale yofuka yomwe yatsala pang’ono kuzima. M’malo mwake, anasamalira mwachikondi anthu ovutika ndi kutsitsimutsa moyo wawo ngati mmene munthu amawonjezerera mafuta mu nyale kuti lawi lisazime. Umu ndi mmene iye anachitira ali padziko pano. Kodi simukukhulupirira kuti Yesu ndi mmenenso alili panopa ndi kuti angakumvereni chisoni pa zofooka zanu? Lemba la Aheberi 4:15 limasonyeza kuti iye ‘angatimvere chisoni pa zofooka zathu.’

Polemba za “munga m’thupi” umene anali nawo, Paulo ananena kuti mphamvu ya Khristu inali “ngati hema” pa iye. (2 Akor. 12:7-9) Iye anadziwa kuti Mulungu akumuteteza kudzera mwa Khristu, monga mmene munthu amene ali m’hema amamvera kuti ndi wotetezeka ku mvula ndi dzuwa. Mofanana ndi Paulo, ifenso sitiyenera kugonja ku zofooka ndiponso ku mavuto athu. Kuti tikhalebe olimba mwauzimu, tiyenera kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova watipatsa kudzera m’mbali ya padziko lapansi ya gulu lake. Tiyenera kuchita zonse zimene anthufe tingathe ndipo kenako kuyang’ana kwa Yehova, tili ndi chikhulupiriro chakuti adzatitsogolera. Tikaona mmene mphamvu ya Mulungu yatithandizira kugonjetsa zofooka zathu, tidzatha kunena zimene Paulo ananena kuti: “Pamene ndili wofooka, m’pamene ndili wamphamvu.”​—2 Akor. 12:10.

[Chithunzi patsamba 3]

Paulo sanasiye kupemphera kwa Yehova kuti amuthandize kukwaniritsa utumiki wake

[Chithunzi patsamba 5]

Mfumu Davide inapatsa Yoabu udindo wotsogolera asilikali

[Chithunzi patsamba 5]

Yoabu anapha Amasa amene anatenga udindo wake

[Chithunzi patsamba 6]

Mwachikondi akulu amapereka malangizo a m’Malemba otithandiza kupirira mavuto athu