Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe

Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe

Musadzipanikize, Ndipo Mudzakhala Achimwemwe

“NDALEPHERANSO!” Kodi ndi kangati pamene munanenapo mawu ngati amenewa chifukwa chosakwaniritsa zimene munafuna kuchita? Mayi wachikhristu yemwenso ndi wachitsikana, anganene zimenezi chifukwa chakuti watopa ndi kusamalira mwana wake wakhanda ndipo wakhumudwa chifukwa chakuti sakupeza nthawi yokwanira yochita zinthu zauzimu. Mkhristu wina angaone kuti sangakwanitse kuchita zina ndi zina chifukwa cha mmene analeredwera ndipo angaganize kuti sakuchita zambiri mumpingo. Mboni yokalamba ingakhumudwe chifukwa siitha kuchita zambiri mumpingo wachikhristu monga mmene inkachitira ili ndi mphamvu. Christiane, amene chifukwa cha banja lake sangathe kuchita zambiri potumikira Yehova, anati: “Nthawi zina ndimalira ndikamvetsera nkhani yolimbikitsa kuchita upainiya.”

Kodi tingatani ndi maganizo ngati amenewa? Kodi Akhristu ena atha bwanji kuona zinthu moyenera pamoyo wawo? Kodi kusadzipanikiza kuli ndi ubwino wotani?

Musadzipanikize

Mtumwi Paulo akutiuza chinsinsi chotithandiza kukhalabe achimwemwe. Iye akuti: “Nthawi zonse kondwerani mwa Ambuye. Ndibwerezanso, Kondwerani! Kulolera kwanu kudziwike kwa anthu onse.” (Afil. 4:4, 5) Kuti tikhale achimwemwe komanso okhutira potumikira Mulungu, tifunika kuyesetsa kukhala ololera malinga ndi zimene tingathe kuchita ndiponso mmene zinthu zilili pamoyo wathu. Ngati tidzipanikiza pofuna kuchita zimene sitingathe, tingangodzipweteka. Komabe, tiyenera kusamala kuti tisakhale aulesi n’kubwerera m’mbuyo muutumiki wachikhristu, podzikhululukira n’kumaganiza kuti zimene tikuchitazo ndi zokhazo zimene tingathe.

Yehova amafuna kuti tizichita zonse zimene tingathe, kapena kuti kumutumikira ndi moyo wathu wonse ndi mtima wathu wonse, kaya zinthu zikhale bwanji pamoyo wathu. (Akol. 3:23, 24) Ngati sitichita zonse zimene tingathe, ndiye kuti sitikukwaniritsa kudzipereka kwathu kwa iye. (Aroma 12:1) Komanso ndiye kuti tikutaya mwayi wokhala wokhutira kwambiri, wokhala ndi chimwemwe chenicheni, ndiponso madalitso ena amene amabwera chifukwa chotumikira Mulungu ndi moyo wonse.​—Miy. 10:22.

Mawu omasuliridwa kuti “kulolera” m’Baibulo, amatanthauzanso kudziganizira. (Yak. 3:17) Ndiponso angatanthauze kusadzikhwimitsira zinthu. Chotero ngati ndife ololera, tidzatha kuona zinthu moyenera pamoyo wathu. Kodi kuchita zimenezi n’kovuta? Kwa ena n’zovuta, ngakhale kuti iwo angathe kuganizira anzawo. Mwachitsanzo, ngati mnzathu wapamtima akusonyeza zizindikiro za kutopa chifukwa chodzipanikiza kwambiri, kodi tingangomusiya osamuthandiza kuti aone kufunika kwa kusintha zinthu zina pamoyo wake? Ifenso tifunikira tizitha kuona zizindikiro zakuti tapitirira malire athu.​—Miy. 11:17.

Zingativute kukhala ndi maganizo oyenera pa zinthu zimene sitingakwanitse kuchita ngati tinaleredwa ndi makolo ovuta kwambiri. Ena ali ana, ankaona kuti anafunika kuchita zambiri ndiponso kuchita bwino nthawi zonse kuti makolo awo awakonde. Ngati umu ndi mmene tinakulira, tingakhale ndi maganizo olakwika a mmene Yehova amationera. Yehova amatikonda tikamamutumikira ndi mtima wonse. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti Yehova “adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Sal. 103:14) Amadziwa kuti tili ndi zofooka ndipo amatikonda tikamamutumikira mwachangu ngakhale tili ndi zofooka. Kukumbukira kuti Mulungu wathu sali ngati mbuye wovuta kudzatithandiza kudziwa malire athu ndi kuvomereza kuti zinthu zina sitingazikwanitse.​—Mika 6:8.

Komabe, ena zimawavuta kukhala ndi maganizo oyenera amenewa. Ngati limeneli ndi vuto lanu, bwanji osapempha thandizo kwa mnzanu amene wakhala Mkhristu kwa nthawi yaitali ndipo amakudziwani bwino? (Miy. 27:9) Mwachitsanzo, kodi mukufuna kuchita upainiya wokhazikika? Maganizo amenewo ndi abwino kwambiri. Koma kodi zikukuvutani kuyamba? Mwina mungafunike thandizo kuti musinthe zina ndi zina pamoyo wanu. Kapena Mkhristu mnzanu amene mumamukhulupirira angakambirane nanu, kuona ngati kungakhale kwanzeru kuyamba upainiya wokhazikika pakalipano poganizira udindo wanu wa banja. Iye angakuthandizeni kuona ngati mungakwanitsedi kuchita zimene mukufunazo kapena angakuuzeni zinthu zimene mukufunikira kusintha kuti muchite zochuluka. Mwamuna ndiye angathandize kwambiri mkazi wake kuona zimene angakwanitse malinga ndi mphamvu zake. Mwachitsanzo, angalimbikitse mkazi wake kuti apume kaye asanayambe ntchito yowonjezereka m’miyezi yotsatira. Zimenezi zingamuthandize kupezanso mphamvu ndiponso kukhalabe wachimwemwe muutumiki.

Ganizirani Zinthu Zimene Mungathe Kuchita

Tingakhale ndi malire pa zimene tingachite potumikira Yehova chifukwa cha ukalamba kapena matenda. Ngati ndinu kholo, mungaone ngati simukupindula ndi phunziro laumwini kapena misonkhano yachikhristu chifukwa mumathera nthawi ndi mphamvu zanu mukusamalira ana. Komabe kodi n’kutheka kuti nthawi zina mumalephera kuona zimene mungakwanitse chifukwa chongoganizira kuti ndinu wolephera?

Kale, zaka zikwi zambiri zapitazo, Mlevi wina anakhumba zinthu zomwe sizikanatheka. Iye anali ndi mwayi wotumikira pa kachisi milungu iwiri pachaka. Komabe, anafuna kuti azikhala pafupi ndi guwa la nsembe moyo wake wonse, ndipo zimenezo zinali zotamandika. (Sal. 84:1-3) Kodi n’chiyani chinathandiza munthu wokhulupirikayu kukhutira ndi mwayi umene anali nawo? Anazindikira kuti kukhala m’mabwalo a kachisi ngakhale tsiku limodzi ndi mwayi wapadera kwambiri. (Sal. 84:4, 5, 10) Ifenso, m’malo mongoganizira zimene sitingathe kuchita, tizizindikira ndiponso kuyamikira zinthu zimene tingathe kuchita.

Taganizirani za Nerlande, mlongo wa ku Canada. Iye sachoka panjinga ya olemala, ndipo ankaganiza kuti sangakwanitse kuchita zambiri muutumiki. Komabe, anasintha maganizo ake n’kuyamba kuona sitolo zapafupi ngati gawo lake lolalikiramo. Iye akuti: “Ndimakhala pa njinga yanga pafupi ndi benchi ya m’sitolozo. Ndimasangalala kulalikira anthu amene amabwera kudzapumula kwa kanthawi pabenchipo.” Nerlande amakhala wokhutira kwambiri chifukwa cha kulalikira mwanjira imeneyi.

Sinthani Pakafunika Kusintha

Boti loyendera matanga lingamayende mothamanga kwambiri, mphepo ikumawomba matangawo. Komabe, likakumana ndi chimphepo choopsa, mmalinyero amakakamizika kusintha matangawo. Iye sangathe kuletsa chimphepocho, koma mwa kusintha matangawo, amapitirizabe kuyendetsa botilo bwinobwino. Mofanana ndi zimenezi, ife nthawi zambiri sitingathe kuletsa mavuto onga chimphepo amene timakumana nawo pamoyo wathu. Koma tingathe kulamulira moyo wathu mmene tingathere, mwa kusintha mmene timagwiritsira ntchito mphamvu, nzeru ndiponso maganizo athu. Kuganizira mofatsa zinthu zimene zasintha pa moyo wathu kungatithandize kukhalabe okhutira ndiponso achimwemwe potumikira Mulungu.​—Miy. 11:2.

Ngati tili ndi mphamvu zochepa, ifenso tingachite bwino kupewa kuchita zinthu zimene zingatitopetse tisanapite ku msonkhano wachikhristu kuti tikhale ndi mphamvu zopitira ku msonkhanowo. Zimenezi zingatipatse mpata wokwanira wocheza ndi Akhristu anzathu. Kapena ngati mayi akulephera kuchita nawo utumiki wa ku nyumba ndi nyumba chifukwa chakuti mwana wake akudwala, angapemphe mlongo mnzake kubwera ndi ophunzira ake kuti adzaphunzirire panyumba pake, mwanayo ali m’tulo.

Nanga bwanji ngati simupeza mpata wokonzekera zonse zomwe zikakambidwe ku misonkhano? Mungathe kuona kuti mungakwanitse ziti, n’kukonzekera bwino zimenezo. Mwa kusintha zinthu mwanjira imeneyi, tingakhalebe okangalika ndiponso achimwemwe.

Kuti tisinthe zina ndi zina pa zimene tikufuna kuchita, pamafunika khama. Serge ndi mkazi wake Agnès, ku France, anafunika kusintha kwambiri. Serge anati: “Tinkafuna kukhala amishonale, koma titadziwa kuti Agnès ndi woyembekezera, zonsezi zinalowa pansi.” Panopa Serge ali ndi ana aakazi awiri athanzi, ndipo akufotokoza zimene kenako iye ndi mkazi wake anasankha kuchita. Iye akuti: “Popeza kuti sitinathe kukatumikira ku dziko lina, tinasankha kukhala ‘amishonale’ m’dziko lathu lomwe. Tinayamba kusonkhana ndi gulu la chinenero chakunja.” Kodi iwo anapindula posankha zimenezi? Serge akuti: “Tikuona kuti tikuuthandiza kwambiri mpingo.”

Odile, mlongo wa ku France wazaka za m’ma 70, satha kuimirira nthawi yaitali chifukwa amadwala nyamakazi ya m’mawondo. Anagwa ulesi poona kuti matenda akewo akumulepheretsa kulalikira mokwanira ku nyumba ndi nyumba. Komabe, sanabwerere m’mbuyo. Anasintha n’kuyamba ulaliki wa pa telefoni. Iye akuti: “Ulalikiwu ndi wosavuta ndiponso umasangalatsa kwambiri kusiyana ndi mmene ndinkaganizira!” Kulalikira mwanjira yatsopano imeneyi kunam’thandiza kukhalanso wachangu muutumiki.

Kusadzipanikiza Kuli ndi Madalitso Ake

Kukhala ndi maganizo oyenera pa zimene tingathe kuchita kungatipulumutse ku zokhumudwitsa zambiri. Tikamakhala ndi zolinga zomwe timakwanitsa, timaona kuti sindife olephera ngakhale kuti tili ndi zofooka zina ndi zina. Timasangalala tikaona zimene takwanitsa kuchita, ngakhale zitakhala zochepa bwanji.​—Agal. 6:4.

Ngati tikhala ndi maganizo oyenera pa zimene timafuna kuchita, tingakhalenso oganizira Akhristu anzathu. Podziwa kuti iwonso ali ndi zimene sangakwanitse kuchita, tidzayamikira kwambiri zimene amatichitira. Tikamasonyeza kuyamikira thandizo lililonse limene apereka, timalimbikitsa mgwirizano ndi kumvana. (1 Pet. 3:8) Kumbukirani kuti, Yehova, Atate wathu wachikondi, sayembekeza kuti tichite zimene sitingakwanitse. Ndipo ngati tikhala ndi zolinga zotheka kuzikwaniritsa ndiponso tikamapewa kudzipanikiza, tidzakhala okhutira komanso achimwemwe potumikira Mulungu.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

Kuti tikhale achimwemwe komanso okhutira potumikira Mulungu, tifunika kuyesetsa kukhala ololera malinga ndi zimene tingathe kuchita ndiponso mmene zinthu zilili pamoyo wathu

[Chithunzi patsamba 30]

Nerlande amasangalala pochita zimene angathe muutumiki

[Chithunzi patsamba 31]

Dziwani “kusintha matanga”

[Mawu a Chithunzi]

© Wave Royalty Free/​age fotostock

[Chithunzi patsamba 32]

Serge ndi Agnès anapindula posintha zolinga zawo