Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sitinachite Mantha, Yehova Anali Nafe

Sitinachite Mantha, Yehova Anali Nafe

Sitinachite Mantha, Yehova Anali Nafe

Yosimbidwa ndi egyptia petridou

Mu 1972, Mboni zonse ku Cyprus zinasonkhana ku Nicosia kudzamvera nkhani yapadera ya Nathan H. Knorr, yemwe kwa nthawi yaitali anatsogolera ntchito ya Mboni za Yehova. Atangondiona anandizindikira, ndipo ndisanamuuze n’komwe dzina langa, iye anandifunsa kuti: “Utiuza chiyani za ku Egypt?” Ndinali nditakumanapo ndi M’bale Knorr zaka 20 m’mbuyomo kwathu ku Alexandria, Egypt.

N DINABADWIRA ku Alexandria pa January 23, 1914, ndipo ndine mwana woyamba m’banja la ana anayi. Tinakulira m’khonde mwenimweni mwa nyanja. Nthawi imeneyo, mzinda wa Alexandria unali wokongola kwambiri, ndipo unali ndi anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana. Mzindawu unali wodziwika kwambiri ndi zomangamanga ndiponso mbiri yake. Popeza kuti Azungu ankakhalira limodzi ndi Aluya, anafe tinaphunzira kulankhula Chiarabu, Chingelezi, Chifulenchi ndi Chitaliyana, kuwonjezera pa chinenero chathu, Chigiriki.

Nditamaliza sukulu, ndinayamba ntchito pashopu yosoka zovala yomwe eni ake anali a ku France. Kumeneku ndinkasangalala kukonza masitayelo ndi kusoka zovala zapamwamba za akazi olemera. Ndinalinso wokonda kupembedza ndi kuwerenga Baibulo, ngakhale kuti sindinkamvetsa zomwe ndinali kuwerengazo.

Panthawi imeneyo, cha mu 1935, ndinakumana ndi mnyamata winawake wokongola wa ku Cyprus, dzina lake Theodotos Petrides. Iye anali katswiri wa masewera ogwetsana pansi, komanso anali ataphunzira luso lopanga maswiti ndi makeke ndipo ankagwira ntchito pashopu ina yotchuka yopanga makeke. Theodotos anandikonda kwambiri, ngakhale kuti ndine mkazi wochepa thupi wa tsitsi lakuda. Nthawi zambiri ankandiimbira nyimbo zachikondi za Chigiriki ataima pawindo la nyumba yanga. Tinakwatirana pa June 30, 1940. Masiku amenewo anali osangalatsa kwambiri. Tinkakhala m’nyumba imene inali pansi pa nyumba ya mayi anga. Mwana wathu woyamba John, anabadwa mu 1941.

Kuphunzira Choonadi cha M’Baibulo

Kwa nthawi ndithu, Theodotos sanali kusangalala ndi chipembedzo chathu, ndipo anali ndi mafunso ambiri okhudza Baibulo. Ine ndisakudziwa, iye anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Tsiku lina, ndili panyumba ndi mwana wathu, mayi wina anagogoda pakhomo ndipo anandipatsa khadi lolembedwa uthenga wa m’Baibulo. Mwaulemu, ndinasiya zomwe ndinali kuchita n’kuliwerenga. Kenako anandipatsa mabuku ofotokoza Baibulo. Nditawaona, ndinadabwa kwambiri popeza anali mabuku omwe aja amene Theodotos anabweretsa tsiku lina.

“Aaa! Mabukuwatu ndili nawo, talowani,” ndinatero. Wamboniyu, Eleni Nicolaou atangolowa, ndinam’panikiza ndi mafunso. Modekha, iye anandiyankha pogwiritsa ntchito Baibulo. Zimenezi zinandisangalatsa kwambiri. Ngati kutulo, ndinayamba kumvetsa uthenga wa m’Baibulo. Tili mkati mokambirana, Eleni anaona chithunzi cha mwamuna wanga. Modabwa, iye anati: “Bambowatu ndikuwadziwa!” Chinsinsi cha Theodotos chinaululika ndipo sindinakhulupirire. Theo ankapita yekha ku misonkhano yachikhristu, osandiuza. Atabwera kunyumba tsiku limenelo, ndinamuuza kuti: “Kumene munapita Lamlungu kuja, mlungu uno tipitira limodzi!”

Pamsonkhano woyamba umene ndinapitako, panali gulu la anthu pafupifupi 10, omwe ankakambirana buku la m’Baibulo la Mika. Ndinamwerera mfundo zonse. Kuyambira pamenepo, George ndi Katerini Petraki ankabwera ku nyumba kwathu Lachisanu lililonse madzulo, kudzaphunzira nafe Baibulo. Bambo ndi ang’ono anga ena sanafune kuti tiziphunzira ndi Mboni, koma mng’ono wanga wina sankanditsutsa, ngakhale kuti sanakhale Mboni. Komabe, mayi anga anaphunzira choonadi cha m’Baibulo. Mu 1942, ine, mayi anga ndi Theodotos tinabatizidwa m’nyanja ku Alexandria, posonyeza kudzipereka kwathu kwa Yehova.

Moyo Wathu Usokonekera

Mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba, ndipo posapita nthawi inafalikira. Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1940, mkulu wa asilikali a Germany, dzina lake Erwin Rommel limodzi ndi asilikali ake a pa akasinja anali ku El Alamein, kufupi ndi kwathu. Mzinda wa Alexandria unadzaza ndi asilikali a Britain. Tinasunga zakudya zoyanika. Kenako Theodotos anapemphedwa kuti azikayang’anira shopu yatsopano yopangira makeke ku Port Taufiq, kufupi ndi ku Suez, choncho tinasamuka. Tili kumeneko, Mboni za Chigiriki ziwiri zinayamba kutifunafuna. Ngakhale kuti sizinkadziwa kumene tinali kukhala, zinalalikira nyumba ndi nyumba mpaka kutipeza.

Tili ku Port Taufiq, tinkaphunzira Baibulo ndi Stavros ndi Giula Kypraios limodzi ndi ana awo, Totos ndi Georgia, ndipo iwo anakhala mabwenzi athu apamtima. Stavros ankasangalala kwambiri kuphunzira Baibulo, motero kuti ankabweza mawotchi onse m’nyumba mwawo ndi ola limodzi kuti ife tiphonye sitima yomaliza yopita kwathu n’kukhalabe komweko. Tinkakambirana mpaka usiku.

Titakhala ku Port Taufiq kwa miyezi 18, tinabwerera ku Alexandria mayi atadwala. Iwo anamwalira mu 1947, ali okhulupirika kwa Yehova. Apanso, Yehova anatilimbikitsa kudzera mwa Akhristu anzathu okhwima mwauzimu. Tinalinso ndi mwayi wochereza amishonale opita kukatumikira ku mayiko ena, sitima zawo za pamadzi zikaima padoko la Alexandria.

Madalitso Ndiponso Mavuto

Mu 1952, mwana wathu wachiwiri, James, anabadwa. Makolofe tinazindikira kuti ana athu afunikira kuleredwa bwino mwauzimu, choncho tinapereka nyumba yathu kuti tizichitiramo misonkhano ndipo nthawi zambiri tinkachereza atumiki a nthawi zonse. Motero mwana wathu wamkulu, John, anayamba kukonda choonadi cha m’Baibulo, ndipo adakali wachinyamata, anayamba kuchita upainiya, uku akuphunzira sukulu ya madzulo kuti amalize maphunziro ake.

Posapita nthawi, Theodotos anapezeka ndi matenda oopsa a mtima ndipo analangizidwa kuti asiye ntchito yake. Apa n’kuti mwana wathu James ali ndi zaka zinayi zokha. Kodi tikanatani? Kodi suja Yehova analonjeza kuti: “Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe”? (Yes. 41:10) Simungakhulupirire zimene zinatichitikira. Mu 1956 tinauzidwa kukachita upainiya ku Ismailia, pafupi ndi Suez Canal ndipo tinasangalala kwambiri. Zaka zotsatira zinali zovuta kwambiri, ndipo abale athu achikhristu ku Egypt anafunikira kulimbikitsidwa.

Mu 1960, tinachoka ku Egypt aliyense ndi sutikesi yake basi. Tinapita ku chilumba cha Cyprus, kwawo kwa mwamuna wanga. Panthawi imeneyi, Theodotos anali kudwala kwambiri ndipo sankatha kugwira ntchito. Komabe, m’bale wina wachikhristu ndi mkazi wake anatikomera mtima potipatsa malo okhala panyumba pawo. N’zachisoni kuti patapita zaka ziwiri, mwamuna wanga anamwalira ndipo ndinatsala ndekha ndi mwana wanga wamng’ono James. John, amenenso anali atabwera ku Cyprus, anali atakwatira ndipo anafunikira kusamalira banja lake.

Anatisamalira M’nthawi ya Mavuto

Kenako Stavros ndi Dora Kairis anatipatsa malo okhala m’nyumba mwawo. Ndinagwada pansi ndi kuthokoza Yehova popitiriza kutisamalira. (Sal. 145:16) Stavros ndi Dora atagulitsa nyumba yawo ndi kumanga ina yatsopano yosanja yomwe inali ndi Nyumba ya Ufumu pansi pake, anatikomeranso mtima pomangaponso kanyumba ka zipinda ziwiri kuti ine ndi James tizikhalamo.

M’kupita kwa nthawi, James anakwatira ndipo iye ndi mkazi wake anachita upainiya mpaka pamene mwana wawo woyamba mwa ana awo anayi anabadwa. Mu 1974, patangopita zaka ziwiri kuchokera pa ulendo wosaiwalika wa M’bale Knorr, panali chipwirikiti pandale ku Cyprus. * Anthu ambiri, kuphatikizapo Mboni, anathawira ku madera ena. Mwana wanga John nayenso anathawa. Iye, mkazi wake limodzi ndi ana awo atatu anapita ku Canada. Koma ngakhale zinali choncho, tinali osangalala kuona kuti chiwerengero cha ofalitsa Ufumu ku Cyprus chinawonjezereka.

Nditayamba kulandira ndalama zanga za penshoni, ndinayamba kuthera nthawi yochuluka muutumiki. Koma zaka zingapo zapitazo, ndinadwala sitiroko ndipo ndinapita kukakhala limodzi ndi mwana wanga James ndi banja lake. Pambuyo pake, nditadwala kwambiri, anandigoneka m’chipatala kwa milungu ingapo ndipo kenako anandipititsa ku nyumba yosungirako anthu okalamba ndi odwala. Ngakhale ndimamva kupweteka m’thupi, ndimalalikira kwa ogwira ntchito, odwala, ndi alendo. Komanso ndimathera nthawi yochuluka ndikuwerenga pandekha, ndipo mothandizidwa ndi abale anga auzimu, ndimatha kupita ku Phunziro la Buku la Mpingo lapafupi.

Kutonthozedwa M’zaka za Ukalamba

Zimanditonthoza mtima ndikamva za anthu amene ine ndi Theodotos tinawathandiza. Ana awo ambiri ndi zidzukulu zawo ali mu utumiki wa nthawi zonse. Ena akutumikira ku Australia, Canada, England, Greece, ndi Switzerland. Panopa, mwana wanga John, mkazi wake ndiponso mwana wawo, amakhala ku Canada. Mwana wawo wamkulu wamkazi ndi mwamuna wake ndi apainiya. Mwana wawo wamng’ono ndi mwamuna wake, mayina awo Linda ndi Joshua Snape, anaitanidwa ku Sukulu ya Gileadi, kalasi ya nambala 124.

Mwana wanga James ndi mkazi wake tsopano akukhala ku Germany. Ana awo aamuna awiri akutumikira pa Beteli, wina ku Athens, Greece, wina ku Selters, Germany. Mwana wawo wamng’ono wamwamuna, ndiponso mwana wawo wamkazi ndi mwamuna wake ndi apainiya, ndipo akutumikira ku Germany.

Ndiyetu tidzakhala ndi nkhani zambiri zouza mayi anga ndi wokondedwa wanga Theodotos akadzaukitsidwa kwa akufa. Iwo adzasangalala kwambiri kuona cholowa chabwino chimene anasiyira banja lawo. *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 21 Onani Galamukani! ya Chingelezi ya October 22, 1974, masamba 12-15.

^ ndime 26 Pamene nkhani ino inali kukonzedwa kuti ifalitsidwe, Mlongo Petridou anamwalira ali ndi zaka 93.

[Mawu Otsindika patsamba 24]

Apanso, Yehova anatilimbikitsa kudzera mwa Akhristu anzathu okhwima mwauzimu

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

CYPRUS

NICOSIA

NYANJA YA MEDITERRANEAN

EGYPT

CAIRO

El Alamein

Alexandria

Ismailia

Suez

Port Taufiq

Suez Canal

[Mawu a Chithunzi]

Based on NASA/​Visible Earth imagery

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi Theodotos mu 1938

[Chithunzi patsamba 25]

Mwana wanga John ndi mkazi wake

[Chithunzi patsamba 25]

Mwana wanga James ndi mkazi wake