Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

Khalani Okhulupirika ndi Mtima Wonse

“Ndidzayenda m’choonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”​—SAL. 86:11.

1, 2. Malinga ndi Salmo 86:2, 11, n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova tikamayesedwa? (b) Kodi tiyenera kuyamba liti kukhala okhulupirika ndi mtima wonse?

N’CHIFUKWA chiyani Akhristu ena amene akhala okhulupirika kwa zaka zambiri, mwinanso amangidwapo ndi kuzunzidwa, amapezeka kuti agwa mu msampha wokonda chuma? Chimachititsa ndi mtima wathu kapena kuti umunthu wathu wamkati. Lemba la Salmo 86 limanena kuti munthu afunika kukhala ndi mtima umodzi kuti akhale wokhulupirika. Ndipo zimenezi zimatanthauza kuchita zinthu ndi mtima wonse osati ndi mitima iwiri. N’chifukwa chake wamasalmo Davide anapemphera kuti: “Sungani moyo wanga pakuti ine ndine wokondedwa wanu; inu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu wokhulupirira Inu.” Ndipo anatinso: “Mundionetse njira yanu, Yehova ndidzayenda m’choonadi chanu: Muumbe mtima wanga ukhale umodzi kuti uliope dzina lanu.”​—Sal. 86:2, 11.

2 Ngati timakhulupirira Yehova ndi mtima wathu wonse, sitingasiye kukhala okhulupirika kwa Mulungu woona chifukwa cha nkhawa ndi zinthu zina. Mtima wadyera uli ngati mabomba omwe akwiriridwa m’msewu umene timayendamo. Ngakhale titakhala okhulupirika kwa Yehova panthawi zovuta, n’zotheka kugwa m’misampha ya Satana. N’chifukwa chake n’kofunika kukhala okhulupirika kwa Yehova panopa tisanakumane ndi mayesero. Baibulo limati: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga.” (Miy. 4:23) Tingaphunzire zambiri pa mfundo imeneyi poona zimene zinachitikira mneneri wa ku Yuda amene anatumidwa ndi Yehova kupita kwa Mfumu Yerobiamu ya ku Isiraeli.

“Ndikupatse Mphatso”

3. Kodi Yerobiamu anatani mneneri wa Mulungu atamuuza uthenga wachiweruzo?

3 Taganizirani izi: Munthu wa Mulungu anali atangopereka uthenga wamphamvu kwa Mfumu Yerobiamu, yemwe anayambitsa kulambira mafano a ana a ng’ombe mu ufumu wakumpoto wa mafuko khumi a Isiraeli. Mfumuyo inakwiya ndipo inauza anyamata ake kugwira mtumikiyo. Koma Yehova anali ndi mtumiki wakeyo. Nthawi yomweyo, dzanja la mfumuyo limene inalozera nalo mtumikiyo chifukwa chokwiya, linauma mozizwitsa. Ndipo guwa lomwe amagwiritsa ntchito polambira mafano linang’ambika pakati. Mwadzidzidzi, Yerobiamu anasintha maganizo ake. Ndipo anapempha munthu wa Mulungu kuti: “Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine.” Mneneriyo anam’pemphereradi ndipo dzanja la mfumuyo linachira.​—1 Maf. 13:1-6.

4. (a) Kodi zimene mfumuyo inalonjeza kupatsa mneneri zinayesa bwanji kukhulupirika kwa mneneriyo? (b) Kodi mneneriyo anayankha chiyani?

4 Ndiyeno Yerobiamu anauza munthu wa Mulunguyo kuti: “Tiye kwathu, ukapumule, ndikupatse mphatso.” (1 Maf. 13:7) Kodi pamenepa mneneriyo akanatani tsopano? Kodi akanavomera kupita ku nyumba kwa mfumuyo atapereka uthengawo? (Sal. 119:113) Kapena kodi akanakana kupita ku nyumba kwa mfumu ngakhale kuti mfumuyo inali itazindikira kulakwa kwake? Yerobiamu anali wolemera moti akanatha kupatsa anthu mphatso zamtengo wapatali. Ngati mneneri wa Mulungu anali ndi kamtima kokonda chuma, mphatso zimene mfumuyo imafuna kum’patsa zikanakhala chiyeso chachikulu. Koma Yehova anali atauza mneneriyo kuti: “Usakadye mkate, kapena kumwa madzi, kapena kubwerera njira yomweyo unadzerayo.” Choncho, mneneriyo anayankha mfumuyo mwamphamvu kuti: “Mungakhale mundigawira pakati ndi pakati nyumba yanu, sindilowa kwa inu, kapena kudya mkate, kapena kumwa madzi kuno.” Ndipo mneneriyo atachoka ku Beteli anadzera njira ina. (1 Maf. 13:8-10) Kodi zimene mneneriyu anachita zikutiphunzitsa chiyani pankhani yokhulupirika ndi mtima wonse.​—Aroma 15:4.

‘Khalani Okhutira’

5. Kodi kukonda chuma kumakhudza bwanji kukhulupirika kwathu?

5 Kukonda chuma kungaoneke ngati ndi nkhani yaing’ono, koma kumakhudza kukhulupirika kwathu. Kodi timakhulupirira zimene Yehova watilonjeza kuti adzatipatsa zofuna zathu? (Mat. 6:33; Aheb. 13:5) Kodi tingakhale opanda zinthu zina zimene mwinanso sitingathe kuzipeza panopo, m’malo moyesetsa mmene tingathere kuti tizipeze? (Werengani Afilipi 4:11-13.) Kodi timalephera kuchita zambiri muutumiki chifukwa chofuna kupeza zinthu? Kodi kutumikira Yehova mokhulupirika n’kofunika kwambiri kuposa china chilichonse pamoyo wathu? Zimene tingayankhe pa mafunso amenewa zingasonyeze kuti tikutumikira Mulungu ndi mtima wonse kapena ayi. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kudzipereka kwa Mulungu kumeneko pamodzi ndi kukhutira ndi zimene tili nazo, ndi njiradi yopezera phindu lalikulu. Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndiponso sitingatulukemo ndi kanthu. Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi nyumba, tidzakhala okhutira ndi zinthu zimenezi.”​—1 Tim. 6:6-8.

6. Kodi tingapatsidwe “mphatso” zotani, nanga n’chiyani chingatithandize kudziwa ngati n’zofunika kuzilandira kapena ayi?

6 Mwachitsanzo, bwana wathu angatikweze pantchito n’kutilonjeza kuti tizilandira ndalama zambiri komanso azitipangira zinthu zambiri. Kapena tingaganize kuti tingalemere ngati tipita ku dziko lina kapenanso dera lina kukafuna ntchito. Zinthu zimenezi poyamba tingadzione ngati ndi Yehova amene akutidalitsa. Koma tisanachite zimenezi, tizidzifunsa kuti, kodi cholinga changa n’chiyani? Chinthu chofunika kuchiganizira n’chakuti, “Kodi zimene ndikufuna kuchitazi zikhudza bwanji ubwenzi wanga ndi Yehova?”

7. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuthetseratu mtima wokonda chuma?

7 Dziko la Satanali nthawi zonse limalimbikitsa kukonda chuma. (Werengani 1 Yohane 2:15, 16.) Ndipo cholinga cha Mdyerekezi ndicho kuwononga mitima yathu. Choncho tifunika kukhala tcheru kuti tizindikire ngati tili ndi mtima wokonda chuma n’kuuchotseratu. (Chiv. 3:15-17) Yesu sanavutike kukana maufumu onse a dziko amene Satana anam’lonjeza. (Mat. 4:8-10) Choncho, iye anachenjeza kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwa mtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Motero kukhulupirika kumatithandiza kudalira Yehova m’malo modzidalira.

‘Ananamizidwa’ ndi Mneneri Wokalamba

8. Kodi kukhulupirika kwa mneneri wa Mulungu kunayesedwa bwanji?

8 Zinthu zikanamuyendera bwino mneneri wa Mulungu uja akanangopitiriza ulendo wake wobwerera kwawo. Koma nthawi yomweyo anayesedwanso. Baibulo limati: “Ku Beteli kunakhala mneneri wokalamba, ndipo mwana wake wina anadzam’fotokozera” zinthu zonse zimene zinachitika tsiku limenelo. Atamva zimenezo, munthu wokalambayo anamuuza mwanayo kuti amangirire mbereko pabulu kuti am’thamangire mneneri wa Mulunguyo. Atayenda pang’ono anam’peza mneneriyo akupuma pamtengo winawake waukulu ndipo anati: “Tiye kwathu, ukadye mkate.” Mneneri wa mulunguyo atakana, munthu wokalambayo anati: “Inenso ndine mneneri wonga iwe, ndipo mthenga analankhula ndi ine mwa mawu a Yehova, nati, Kam’bwezere kwanu, kuti akadye mkate, namwe madzi.” Koma Malemba amati “anam’namiza.”​—1 Maf. 13:11-18.

9. Kodi Malemba amanena chiyani za anthu achinyengo, ndipo amavulaza ndani?

9 Kaya mneneri wokalambayu cholinga chake chinali chotani, komabe ananama. N’kutheka kuti nthawi ina iye anali mneneri wa Yehova wokhulupirika. Komabe apa iye anachita chinyengo ndipo Malemba amaletseratu khalidwe limeneli. (Werengani Miyambo 3:32.) Nthawi zambiri anthu achinyengo amadzivulaza okha mwauzimu komanso amavulaza ena.

“Anabwerera” ndi Munthu Wokalamba

10. Kodi mneneri wa Mulungu anatani munthu wokalamba atamuitanira kwawo, nanga chinachitika n’chiyani?

10 Mneneri wa ku Yuda akanatha kudziwa kuti mneneri wokalambayu amamunamiza. Iye akanadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova watumiza mngelo kuuza munthu wina malangizo osiyana ndi amene anandiuza?’ Mneneriyu akanatha kupempha Yehova kuti am’fotokozere bwinobwino nkhaniyo, koma Malemba sasonyeza kuti iye anachita zimenezi. Komano, “anabwerera naye [munthu wokalambayo], nakadya kwawo, namwa madzi.” Koma Yehova sanasangalale ndi zimenezi. Mneneri amene ananamizidwayo akubwerera kwawo ku Yuda, anapezana ndi mkango panjira ndipo unamupha. Ntchito yake ya uneneriyo inathera pomwepo.​—1 Maf. 13:19-25. *

11. Kodi Ahiya anasonyeza chitsanzo chabwino chotani?

11 Komano mneneri Ahiya, amene anatumidwa kukadzoza Yerobiamu kukhala mfumu, anakhalabe wokhulupirika mpaka kukalamba. Ahiya atakalamba komanso atachita khungu, Yerobiamu anatuma mkazi wake kukafunsa Ahiya ngati mwana wake amene amadwala achire. Iye ananena molimba mtima kuti mwanayo amwalira. (1 Maf. 14:1-18) Ahiya anadalitsidwa kwambiri pamoyo wake. Mwachitsanzo zimene ananena zinathandiza polemba Mawu a Mulungu. Kodi zinathandiza bwanji? Polemba Baibulo, wansembe Ezara anagwiritsa ntchito zimene Ahiya analemba.​—2 Mbiri 9:29.

12-14. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira mneneri wachinyamata uja? (b) Fotokozani chifukwa chake tifunika kuganizira mofatsa malangizo a m’Baibulo amene akulu amapereka.

12 Baibulo silinena chifukwa chake mneneri wachinyamata uja sanafunse Yehova asanapite kukadya kwa munthu wokalamba uja. Kodi mwina zimene munthu wokalambayo anauza mneneriyu n’zimene amayembekezera? Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tifunika kukhulupirira ndi mtima wonse kuti malamulo a Yehova ndi olondola. Ndipo tiziyesetsa kuwatsatira, zivute zitani.

13 Ena akamalangizidwa amangotolapo mfundo zokhazo zimene iwo akufuna. Mwachitsanzo, wofalitsa angapatsidwe mwayi wa ntchito imene siizim’patsa mpata wocheza ndi banja lake komanso wochita zinthu zauzimu. Iye angafunsire nzeru kwa mkulu. Mkuluyo angayambe ndi kumulangiza m’baleyo kuti ndi udindo wake kuona zochita pothandiza banja lake. Ndiyeno mkuluyo angaonere limodzi ndi m’baleyo mavuto amene angabwere pamoyo wake wauzimu akalowa ntchitoyo. Kodi m’baleyo ayenera kungogwira mawu oyamba okha a mkuluyo, kapena ayenera kuganizira mofatsa malangizo enawo? Apa m’baleyo angafunike kuona zimene zingamuthandize mwauzimu.

14 Ganizirani chitsanzo china. Mlongo angafunse mkulu ngati n’koyenera kusiyana ndi mwamuna wake wosakhulupirira. Mkuluyo angam’fotokozere kuti zili ndi iye kusiyana ndi mwamuna wakeyo kapena ayi. Ndiyeno angakambirane malangizo a m’Baibulo pankhaniyi. (1 Akor. 7:10-16) Kodi mlongoyo adzamvera zonena za mkuluyo? Kapena waganiza kale zosiyana ndi mwamuna wake? Poganizira zochita pankhaniyi, ndi nzeru kupemphera ndiponso kuganizira mofatsa malangizo a m’Baibulo.

Khalani Odzichepetsa

15. Kodi zimene mneneri wa Mulungu analakwitsa zimatiphunzitsa chiyani?

15 Kodi zimene mneneri wa ku Yuda analakwitsa zikutiphunzitsanso chiyani? Lemba la Miyambo 3:5 limati: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako.” M’malo moti mneneriyu akhulupirirebe Yehova monga amachitira kale, iye anayendera maganizo ake. Zimenezi zinam’phetsa komanso zinachititsa kuti asakhale ndi dzina labwino ndi Mulungu. Izi zikusonyezeratu kuti tifunika kukhala odzichepetsa ndiponso okhulupirika potumikira Yehova.

16, 17. Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe okhulupirika kwa Yehova?

16 Mtima wodzikonda umene anthufe timakhala nawo ungatisocheretse. Baibulo limati: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?” (Yer. 17:9) Kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova, tifunika kuyesetsa kuvula umunthu wakale ndi makhalidwe ake monga kudzikuza ndi kudzidalira. Ndipo tifunika kuvala umunthu watsopano, “umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo choona ndi kukhulupirika.”​—Werengani Aefeso 4:22-24.

17 Lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” Kudzichepetsa ndiponso kudalira Yehova kumatithandiza kuti tisalakwitse zinthu kwambiri. Mwachitsanzo, chifukwa cholefuka tingalephere kuganiza bwino. (Miy. 24:10) Tingatope ndi mbali zina za utumiki wopatulika ndipo tingayambe kuganiza kuti tachita zokwanira m’mbuyomu tsopano ndi nthawi yoti ena apitirize. Kapena tingayambe kufuna kukhala ndi moyo umene anthu amati ndi wabwino. Komabe, ‘kuyesetsa mwamphamvu’ ndiponso ‘kukhala ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye,’ kudzateteza mitima yathu.​—Luka 13:24; 1 Akor. 15:58.

18. Kodi tizitani ngati sitikudziwa chochita pankhani inayake?

18 Nthawi zina tingafunike kuganiza mofatsa posankha zochita pankhani zikuluzikulu, ndipo mwina tingasowe pogwira. Kodi zikatero timayendera nzeru zathu? Ndi nzeru kupempha Yehova kuti atithandize chifukwa lemba la Yakobe 1:5 limati: “Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu . . . popeza iye amapereka mowolowa manja kwa onse.” Atate wathu wa kumwamba angatipatse mzimu woyera kuti utithandize kusankha bwino zochita.​—Werengani Luka 11:9, 13.

Tsimikizani Kukhalabe Okhulupirika

19, 20. Kodi tiyenera kutsimikiza kuchita chiyani?

19 Solomo atasiya kulambira koona, anthu okhulupirika a Mulungu anayesedwa kwambiri. Komabe ena anakhalabe okhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti ambiri anagonja m’njira zosiyanasiyana.

20 Tsiku lililonse timakumana ndi zinthu zimene zimayesa kukhulupirika kwathu. Koma ifenso tikhoza kukhala okhulupirika. Tiyeni nthawi zonse tikhalebe okhulupirika kwa Yehova ndi mtima wonse, chifukwa kwa ‘munthu wokhulupirika, Yehova adzamuchitira mokhulupirika.’​—2 Sam. 22:26, NW.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Baibulo silimanena ngati Yehova anapha mneneri wokalamba.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kuyesetsa kuthetseratu mtima wokonda chuma?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kukhala okhulupirika kwa Yehova?

• Kodi kudzichepetsa kungatithandize bwanji kukhala okhulupirika kwa Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Kodi zimakuvutani kukana mayesero?

[Zithunzi patsamba 10]

Kodi mumapemphera ndi kuganiza mofatsa mukapatsidwa malangizo a m’Baibulo?