Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maphunziro a Gileadi Amishonale Ali Ngati Dzombe

Maphunziro a Gileadi Amishonale Ali Ngati Dzombe

Kalasi ya Nambala 124 ya Omaliza

Maphunziro a Gileadi Amishonale Ali Ngati Dzombe

MIYEZI 6 iliyonse, Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, imakhala ndi mwambo wa omaliza maphunziro a m’sukuluyi ndipo banja lonse la Beteli la ku United States limaitanidwa pamwambowu. Pa March 8, 2008, alendo ochokera m’mayiko oposa 30 anasonkhana pamodzi ndi banja la Beteli pa mwambo wa omaliza maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya kalasi ya nambala 124. Anthu onse amene anapezeka pa mwambowu analipo 6,411 ndipo anasangalala ndi omaliza maphunzirowa patsiku lawo lapaderali.

M’bale Stephen Lett, wa m’Bungwe Lolamulira ndiye anali tcheyamani. Iye anatsegulira mwambowu ndi nkhani yakuti: “Yendani ndi Dzombe la Yehova Lophiphiritsa.” Lemba la Chivumbulutso 9:1-4 limayerekezera kagulu ka Akhristu odzozedwa, amene anayambanso mwamphamvu ntchito yawo yotumikira Yehova mu 1919, ndi dzombe. Ophunzirawo anakumbutsidwa kuti monga a m’gulu la “nkhosa zina,” azigwira ntchito limodzi ndi dzombe lophiphiritsali.​—Yoh. 10:16.

Kenako, m’bale Lon Schilling, yemwe ali m’Komiti ya Nthambi ya ku United States anakamba nkhani yakuti: “Muzithandizana.” Nkhaniyi inatengedwa pa chitsanzo cha m’Baibulo cha Akula ndi mkazi wake Purisika. (Aroma 16:3, 4) Mabanja 28 a m’kalasili anauzidwa kuti afunikira kukhala ogwirizana kwambiri kuti zinthu zikawayendere bwino paumishonale wawo. Baibulo silitchula Akula popanda kutchulanso mkazi wake Purisika. Ndiye kuti, mtumwi Paulo ndi anthu onse mu mpingo ankaona kuti banja limeneli linali logwirizana. Chimodzimodzinso masiku ano, banja la amishonale liyenera kukhala logwirizana kwambiri ndi kuchitira zinthu pamodzi monga pogwira ntchito, polambira, ndiponso pothana ndi mavuto amene angakumane nawo kudziko lachilendo.​—Gen. 2:18.

Nkhani yotsatira ya mutu wakuti “Tsanzirani Ubwino wa Yehova,” inakambidwa ndi m’bale Guy Pierce, wa m’Bungwe Lolamulira. M’bale Pierce anati, ubwino sumangotanthauza kupewa kuchita zoipa. Munthu wabwino amathandiza ena. Yehova Mulungu ndi wokoma mtima kuposa wina aliyense. (Zek. 9:16, 17) Kutsanzira ubwino ndi chikondi cha Mulungu kungatipangitse kuchitira ena zabwino. Pomaliza nkhani yake, m’bale Pierce anathokoza ophunzirawo mwa kuwauza kuti: “Mwakhala Mukuchita Bwino.” Tikukhulupirira kuti mupitiriza kutsanzira Mulungu pochitira ena zabwino m’ntchito iliyonse imene Yehova Mulungu akupatseni.”

Kenako, m’bale Michael Burnett, yemwe anali m’mishonale koma panopa akuphunzitsa m’sukulu ya Gileadi, anakamba nkhani yakuti “Valani Chapamphumi Pakati pa Maso Anu.” Aisiraeli anafunika kukumbukira mmene Yehova anawapulumutsira mozizwitsa ku Iguputo monga ngati avala “chapamphumi” pakati pa maso awo. (Eks. 13:16) Ophunzirawo analangizidwa kuti afunikira kukumbukira zimene aphunzira m’Sukulu ya Gileadi monga ngati avala chapamphumi pakati pa maso awo. M’bale Burnett, anagogomezera kufunika kokhala odzichepetsa ndipo anawalimbikitsa kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothetsa kusamvana kumene kungakhalepo ndi amishonale anzawo kapena anthu ena.​—Mat. 5:23, 24.

M’bale Mark Noumair, yemwe wakhala akuphunzitsa m’Sukulu ya Gileadi kwa nthawi yaitali, anakamba nkhani yakuti “Kodi Adzakuimbirani Nyimbo Yotani?” Kale anthu akapambana nkhondo ankaimba nyimbo. Nyimbo imodzi yotere inali yotamanda fuko la Zebuloni chifukwa cha kudzipereka kwawo, koma imanena mafuko a Rubeni, Dani, ndi Aseri kuti anali osadzipereka. (Ower. 5:16-18) Monga nyimbo, zochita za Mkhristu wina aliyense zimadziwika kwa ena. Munthu amene amadzipereka ku ntchito ya Mulungu ndiponso amene amamvera malangizo a gulu la Mulungu, amakhala ndi mbiri yabwino kwa Yehova ndipo amakhala chitsanzo chabwino kwa abale. Anthu ena mumpingo akamamvera nyimbo yophiphiritsa ya zochita zathu, amatsanzira chitsanzo chathu.

Pamaphunziro amenewa, ophunzira a m’Sukulu ya Gileadi a kalasi ya nambala 124, anathera maola pafupifupi 3,000 m’ntchito yolalikira. M’nkhani ya mutu wakuti “Kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera,” imene inakambidwa ndi m’bale Sam Roberson wa m’dipatimenti ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ophunzira anafotokoza zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo m’munda ndipo anachita zitsanzo za zinthu zimene anakumana nazo. Kenako m’bale Patrick LaFranca wa m’Komiti ya Nthambi ya ku United States, anafunsa mafunso amishonale ena amene anamaliza maphunziro a Gileadi omwe akutumikira m’mayiko ena. Ophunzirawo anayamikira malangizo amene analandira kuchokera kwa abale amenewa.

M’bale Anthony Morris, wa m’Bungwe Lolamulira, anakamba nkhani yomaliza ya mutu wakuti, “Kumbukirani Kuti Zinthu Zooneka N’zakanthawi.” Malemba amatilimbikitsa kuti tiziganizira kwambiri za madalitso amene Yehova adzatipatse m’tsogolo m’malo mongoganizira za mavuto akanthawi kochepa amene tikukumana nawo. (2 Akor. 4:16-18) Umphawi, kupanda chilungamo, kuponderezana, matenda ndi imfa n’zofala masiku ano. Amishonale angathe kukumana ndi mavuto amenewa. Koma ngati tikumbukira kuti zinthu zimenezi n’zakanthawi, tidzakhalabe ndi chiyembekezo komanso olimba mwauzimu.

Pomaliza, ophunzira onse anakhala pafupi ndi wokamba nkhani, m’bale Lett, amene anawalimbikitsa kuti apitirizebe kukhala okhulupirika. Iye anati: “Kaya tikumane ndi mavuto otani, koma ngati Yehova ali kumbali yathu, tidzapirira ndipo tidzakhalabe okhulupirika.” Analimbikitsa amishonale atsopanowa kuti akhale ngati dzombe mwa kupitirizabe kutumikira Yehova ndi kukhalabe achangu, okhulupirika ndi omvera mpaka mapeto.

[Bokosi patsamba 30]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira achokera: 7

Chiwerengero cha mayiko amene atumizidwa: 16

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Avereji ya zaka za kubadwa: 33.8

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 18.2

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13.8

[Chithunzi patsamba 31]

Kalasi ya Nambala 124 ya Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pa m’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja mumzera uliwonse.

(1) Nicholson, T.; Main, H.; Senge, Y.; Snape, L.; Vanegas, C.; Pou, L. (2) Santana, S.; Oh, K.; Lemaitre, C.; Williams, N.; Alexander, L. (3) Woods, B.; Stainton, L.; Huntley, E.; Alvarez, G.; Cruz, J.; Bennett, J. (4) Williamson, A.; González, N.; Zuroski, J.; Degandt, I.; May, J.; Diemmi, C.; Tavener, L. (5) Lemaitre, W.; Harris, A.; Wells, C.; Rodgers, S.; Durrant, M.; Senge, J. (6) Huntley, T.; Vanegas, A.; Pou, A.; Santana, M.; Bennett, V.; Tavener, D.; Oh, M. (7) Zuroski, M.; Rodgers, G.; Diemmi, D.; Nicholson, L.; Alvarez, C.; Snape, J. (8) Harris, M.; González, P.; Main, S.; Woods, S.; Stainton, B.; Williamson, D.; Durrant, J. (9) Cruz, P.; Degandt, B.; Williams, D.; Wells, S.; Alexander, D.; May, M.

[Chithunzi patsamba 32]

Sukulu ya Gileadi ili ku Likulu la Maphunziro la Watchtower