Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba

Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba

Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba

“Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”​—AHEB. 6:10.

1, 2. (a) Kodi munthu waimvi angakukumbutseni chiyani? (b) Kodi Yehova amawaona bwanji Akhristu okalamba?

Mukaona okalamba aimvi mumpingo, kodi mumakumbukira za masomphenya a Danieli? M’masomphenya amenewa, Yehova Mulungu anaoneka waimvi. Danieli analemba kuti: “Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pa mutu pake ngati ubweya woyera.”​—Dan. 7:9.

2 Mawu akuti “Nkhalamba ya kale lomwe” ndiponso akuti ‘tsitsi ngati ubweya woyera’ akusonyeza kuti Mulungu ali ndi zaka ndiponso nzeru zochuluka, zimene zimachititsa kuti tizimulemekeza kwambiri. Koma kodi Yehova kapena kuti nkhalamba ya kale lomwe, amawaona bwanji anthu okalamba okhulupirika? Mawu a Mulungu amati: ‘Imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’ (Miy. 16:31) Choncho, ngati Mkhristu wokhulupirika ali ndi imvi chifukwa cha ukalamba, iye ndi wokongola kwa Mulungu. Kodi mumaona abale ndi alongo okalamba ngati mmene Yehova amawaonera?

Chifukwa Chake Timawakonda

3. N’chifukwa chiyani atumiki anzathu okalamba timawakonda?

3 Atumiki ena a Mulungu okalamba komanso okondedwa amenewa ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova. Ena anatumikirapo kapena akutumikirabe monga oyang’anira oyendayenda, apainiya achangu, ndi ofalitsa Ufumu amene akutumikira mokhulupirika m’mipingo yosiyanasiyana. Mwinanso mukudziwa ena amene akhala akulalikira uthenga wabwino kwa zaka zambiri ndipo chitsanzo chawo chabwino chalimbikitsa achinyamata ndi kuwathandiza kukhala ndi moyo wabwino. Atumiki ena okalamba akhala ndi maudindo aakulu ndipo apirira chizunzo chifukwa cha uthenga wabwino. Yehova ndiponso “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amayamikira kwambiri zonse zimene achita ndi zimene akuchita pa ntchito ya Ufumu.​—Mat. 24:45.

4. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kulemekeza Akhristu okalamba ndi kuwapempherera?

4 Atumiki onse a Yehova Mulungu afunika kuyamikira ndi kulemekeza Akhristu okalamba ndi okhulupirika amenewa. Ndipotu lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose limasonyeza kuti anthu oopa Yehova amafunika kuganizira ndi kulemekeza okalamba. (Lev. 19:32) Nthawi zonse tiyenera kuwapempherera ndi kuthokoza Mulungu chifukwa cha ntchito yawo yabwino. Mtumwi Paulo anapempherera anzake amene amagwira nawo ntchito, aang’ono ndi aakulu omwe.​—Werengani 1 Atesalonika 1:2, 3.

5. Kodi tikamacheza ndi Akhristu a Yehova okalamba tingapindule bwanji?

5 Komanso, tonse mumpingo tingapindule tikamacheza ndi Akhristu okalamba. Atumiki a Yehova okalamba ndi okhulupirika amenewa amadziwa zinthu zambiri chifukwa awerenga komanso aona zambiri pamoyo wawo. Aphunzira kukhala oleza mtima ndi omvetsa zinthu, ndipo amasangalala kuphunzitsa ena zimene akudziwa. (Sal. 71:18) Achinyamatanu, ngati mukufuna kukhala anzeru, yesetsani kuphunzira zinthu kwa okalamba amenewa monga mmene mungatungire madzi pachitsime chakuya.​—Miy. 20:5.

6. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumawakondadi anthu okalamba?

6 Kodi anthu okalamba mumawakonda monga momwe Yehova amawakondera? Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kuwauza kuti mumawakonda kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwawo ndiponso nzeru zawo. Komanso ngati mumatsatira zimene akukuuzani mumasonyeza kuti mumawalemekeza ndi mtima wonse. Akhristu ambiri okalamba amakumbukira malangizo anzeru amene anapatsidwa ndi okalamba ena okhulupirika ndi mmene kuwagwiritsa ntchito malangizowo kwawathandizira pamoyo wawo. *

Sonyezani Kuti Mumawakonda

7. Kodi Yehova wapatsa ndani kwenikweni udindo wosamalira okalamba?

7 Mulungu anapereka udindo wosamalira okalamba kwenikweni kwa anthu apabanja pawo. (Werengani 1 Timoteyo 5:4, 8.) Yehova amasangalala mabanja akamakwanitsa udindo wawo wosamalira okalamba. Izi zimasonyeza kuti amakonda okalambawo monga mmene Yehova amachitira. Mulungu amathandiza mabanja amenewa ndipo amawadalitsa chifukwa cha khama ndi kudzipereka kwawo. *

8. N’chifukwa chiyani mpingo uyenera kuthandiza Akhristu okalamba?

8 Yehova amasangalalanso mpingo ukamathandiza okalamba okhulupirika koma omwe alibe achibale oti angawathandize. (1 Tim. 5:3, 5, 9, 10) Mpingo ukamachita zimenezi, ndiye kuti ‘umamvera chisoni, umakonda ndi kuchitira chifundo chachikulu’ okalamba. (1 Pet. 3:8) Paulo anasonyeza bwino kwambiri chifukwa chake tiyenera kuchitira chifundo okalamba mumpingo pamene ananena kuti chiwalo chimodzi chikavutika, “ziwalo zina zonse zimavutika limodzi nacho.” (1 Akor. 12:26) Tikamasonyeza chifundo mwa kuthandiza anthu okalamba, ndiye kuti tikutsatira mfundo imene ikupezeka m’malangizo a Paulo akuti: “Musaleke kuthandizana kunyamula mtolo wa wina ndi mnzake, mukatero mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.”​—Agal. 6:2.

9. Kodi munthu akakalamba amakumana ndi mavuto otani?

9 Kodi okalamba amakumana ndi mavuto otani? Ambiri amatopa msanga ndipo amaona kuti sangakwanitse kuchita zinthu zina monga kupita ku chipatala, kuyeretsa m’nyumba ndi kuphika chakudya. Popeza munthu akamakalamba sakonda kudya, ambiri amachita ulesi kuti adye kapena kumwa madzi. Zingakhalenso chimodzimodzi ndi chakudya chauzimu. Munthu wokalamba angavutike kuwerenga ndi kumvetsera misonkhano ndipo ngakhale kukonzekera kupita ku misonkhano yachikhristu kumakhala kovuta kwambiri. Ndiyeno, kodi ena angawathandize bwanji anthu okalambawa?

Mmene Mungawathandizire

10. Kodi akulu angachite chiyani kuti okalamba azilandira thandizo limene akufunikira?

10 M’mipingo yambiri, okalamba amasamalidwa bwino kwambiri. Abale ndi alongo achikondi amawathandiza ntchito monga kukagula zinthu, kuphika ndi kusesa m’nyumba. Amawathandizanso kuwerenga, kukonzekera kupita ku misonkhano ndiponso kuti azilalikira mokhazikika. Mboni zachinyamata zimakawatenga popita ku misonkhano. Anthu okalamba ngati akulephera kupita ku misonkhano, angamvetsere misonkhanoyo pa telefoni kapena angawaikire pa tepi. Ngati n’kotheka akulu azionetsetsa kuti okalamba mumpingo akulandira thandizo limene akufunikira. *

11. Fotokozani mmene banja lina linathandizira m’bale wokalamba?

11 Mkhristu aliyense angathandizenso okalamba mwa kucheza nawo ndi kuwapatsa zinthu. M’bale wina wokalamba mkazi wake atamwalira, iye sanakwanitse kulipira nyumba popanda ndalama za penshoni ya mkazi wake. Iye ndi mkazi wake anaphunzitsa Baibulo banja lina la ana aakazi awiri. Banjali linali ndi nyumba yaikulu ndipo linapatsa m’baleyu zipinda ziwiri kuti azikhalamo. Banjali linakhala limodzi ndi m’baleyu kwa zaka 15 ndipo amacheza ndi kudyera pamodzi. Ana a m’banjali anaphunzira zambiri chifukwa cha chikhulupiriro ndi kudziwa zinthu kwa m’baleyu. Ndipo iyenso anapindula kwambiri chifukwa chokhala ndi banjali. M’baleyu anakhala ndi banja limeneli mpaka nthawi imene anamwalira ali ndi zaka 89. Banjali limathokozabe Mulungu chifukwa cha madalitso ambiri amene analandira chifukwa chosunga m’baleyu. ‘Mphoto yawo sinatayike konse’ chifukwa chothandiza wophunzira wa Yesu Khristu mnzawo.​—Mat. 10:42. *

12. Kodi mungachite chiyani kuti musonyeze chikondi kwa abale ndi alongo okalamba?

12 Mwina simungathe kusamalira munthu wokalamba mmene banjali linachitira koma mungathe kuwathandiza kupita ku misonkhano ndi muutumiki wa kumunda. Mungathe kuwaitaniranso ku nyumba kwanu ndi kupita nawo kokasangalala. Mungawachezere makamaka akadwala kapena ngati satha kuyenda. Ndiponso nthawi zonse mungathe kuwachitira zinthu zina popeza ndi anthu achikulire. Akhristu okalamba ayenera kufunsidwa posankha zochita pankhani zimene zikuwakhudza. Ngakhale amene sangathe kuganiza bwinobwino amadziwa ngati tikuwalemekeza kapena ayi.

Yehova Sadzaiwala Ntchito Yanu

13. N’chifukwa chiyani n’kofunika kuganizira mmene Akhristu okalamba akumvera?

13 Kuganizira mmene okalamba akumvera n’kofunika. Nthawi zambiri okalamba amakhumudwa akamalephera kuchita zinthu zimene ankachita ali achinyamata. Mwachitsanzo, mlongo wina yemwe anatumikira Yehova mwachangu zaka pafupifupi 50 ndipo anali mpainiya wokhazikika anadwala matenda ofoola thupi. Chifukwa cha matendawa zimamuvuta kwambiri kupezeka pa misonkhano. Nthawi ina, iye ataganizira mmene ankachitira mu utumiki ndi mmene akuchitira panopo, anagwetsa misozi. Uku akulira anaweramitsa mutu wake ndipo anati, “Palibe chomwe ndikuchita.”

14. Kodi buku la Masalmo limalimbikitsa bwanji atumiki a Yehova okalamba?

14 Ngati ndinu wokalamba, kodi munayamba mwaganizapo chonchi? Kapena kodi nthawi zina mumaona kuti Yehova wakutayani? Wamasalmo ayenera kuti atakalamba analinso ndi maganizo amenewa chifukwa anapempha Yehova kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga. . . . Pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu.” (Sal. 71:9, 18) Yehova sanataye wolemba salmo ameneyu ndipo inunso sadzakutayani. Mu salmo lina, Davide anasonyeza kuti Mulungu amathandiza kwambiri. (Werengani Salmo 68:19.) Dziwani kuti ngati ndinu Mkhristu wokalamba wokhulupirika, Yehova ali nanu ndipo adzakusamalirani nthawi zonse.

15. Kodi n’chiyani chingathandize okalamba kudziona kuti ndi ofunika?

15 Yehova amakumbukira zinthu zonse zimene okalamba onse a Mboni za Yehova achita ndi zimene akuchita panopo polemekeza Mulungu. Baibulo limati: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Motero, pewani kukhala ndi maganizo olakwika oti ndinu wosafunika kwa Yehova chifukwa chakuti mwakalamba. Yesetsani kuganizira zinthu zolimbikitsa m’malo mwa zofooketsa. Khalani osangalala chifukwa cha madalitso amene muli nawo ndiponso zimene mukuyembekezera kutsogoloku. Tili ndi tsogolo ndi ‘chiyembekezo’ chabwino kwambiri chimene Mlengi wathu watilonjeza. (Yer. 29:11, 12; Mac. 17:31; 1 Tim. 6:19) Ganizirani zimene mukuyembekezera komanso zinthu zolimbikitsa monga amachitira achinyamata ndipo musadzione kuti ndinu wosafunika mu mpingo. *

16. N’chifukwa chiyani m’bale wina wokalamba anaganiza zosiya kutumikira monga mkulu, koma kodi bungwe la akulu linam’limbikitsa bwanji?

16 Ganizirani za a Johan, azaka 80 amene nthawi zonse amasamalira akazi awo okhulupirika a Sannie, amene tsopano satha kuzisamalira okha. * Alongo amasinthana kusamalira a Sannie kuti a Johan azitha kupita ku misonkhano ndi muutumiki. Komabe, posachedwapa m’bale Johan anafika potopa ndipo anayamba kuganiza kuti sakuyeneranso kukhala mkulu mumpingo. Misozi italengeza m’maso mwawo anati: “N’chifukwa chiyani ndili mkulu? Palibe chimene ndikuchita mumpingo.” Akulu anzawo anawalimbikitsa kuti zinthu zambiri zimene akudziwa ndiponso nzeru zawo n’zothandiza kwambiri. Ngakhale kuti sachita zambiri, anawalimbikitsa kuti apitirize kutumikira monga mkulu. Atalimbikitsidwa kwambiri, a Johan akupitiriza kutumikira monga mkulu ndipo akuthandiza kwambiri mumpingomo.

Yehova Amasamaliradi

17. Kodi Baibulo limalimbikitsa motani Akhristu okalamba?

17 Malemba amafotokoza bwino kuti okalamba angapitirizebe kuchita bwino mwauzimu ngakhale kuti amakumana ndi mavuto. Wamasalmo anati: “Iwo ookedwa m’nyumba ya Yehova, . . . atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri.” (Sal. 92:13, 14) Mtumwi Paulo, yemwe ayenera kuti anali ndi matenda amene amamuvutitsa ‘sanabwerere m’mbuyo ngakhale munthu wake wakunja amatha.’​—Werengani 2 Akorinto 4:16-18.

18. Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu anzathu okalamba komanso owasamalira amafunika kuthandizidwa?

18 Zitsanzo zambiri masiku ano zikusonyeza kuti okalamba angapitirize kubala “zipatso” ngakhale akukumana ndi mavuto. Mavuto amene munthu angapeze chifukwa chokalamba ndiponso kudwala angam’topetse kwambiri ngakhale kuti munthuyo ali ndi achibale abwino omusamalira. Anthu osamalira okalamba nawonso angatope kwambiri. Mpingo uli ndi udindo wosonyeza chikondi kwa anthu okalamba ndiponso amene akuwasamalira. (Agal. 6:10) Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timawathandizadi m’malo mongonena chabe kuti “mukhale wofunda ndi wosazizidwa, ndipo mukhale wodya bwino.”​—Yak. 2:15-17.

19. N’chifukwa chiyani Akhristu okhulupirika okalamba ayenera kusangalala pamene akuyembekezera zam’tsogolo?

19 Ukalamba ungalepheretse munthu kuchita zambiri mu utumiki wachikhristu, koma Yehova sasiya kukonda atumiki ake chifukwa chakuti akalamba. Iye amawakonda kwambiri Akhristu okhulupirika amenewa, ndipo sadzawataya. (Sal. 37:28; Yes. 46:4) Yehova adzawasamalira ndi kuwatsogolera panthawi yonse ya ukalamba.​—Sal. 48:14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Onani Galamukani! ya February 8, 1994, masamba 3 mpaka 10.

^ ndime 10 M’mayiko ena, zimenezi zingaphatikizepo kuthandiza okalamba kukalandira thandizo la boma. Onani nkhani yakuti “Mulungu Amasamalira Okalamba,” mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2006.

^ ndime 15 Onani nkhani yakuti “Ulemerero wa Imvi,” mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1993.

^ ndime 16 Tasintha mayina ena.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani Akhristu okhulupirika okalamba mumawakonda?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawakonda Akhristu anzathu okalamba?

• Kodi n’chiyani chingathandize atumiki a Yehova okalamba kudziona kuti ndi ofunika?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 18]

Akhristu amalemekeza kwambiri anzawo okalamba