Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Pewani “Mzimu wa Dziko”

Pewani “Mzimu wa Dziko”

Pewani “Mzimu wa Dziko”

“Sitinalandire mzimu wa dziko, koma mzimu wochokera kwa Mulungu.”​—1 AKOR. 2:12.

1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kale ku Britain ankaika mbalame m’migodi? (b) Kodi Akhristu ali pavuto lotani?

MU 1911, boma la Britain linakhazikitsa lamulo loteteza anthu ogwira ntchito m’migodi ya malasha. Lamuloli linanena kuti mu mgodi uliwonse muzikhala mbalame ziwiri. Kodi cholinga chake chinali chiyani? Chinali chakuti, ngati mu mgodi mwabuka moto, opulumutsa anthu adziwe msanga. Mbalamezi zimafooka kapena kugwa kumene zikangopuma mpweya woipa. Zizindikiro zimenezi zinali zofunika kwambiri chifukwa mpweya wina woipa suoneka ndipo sununkha. Mpweya umenewu umapha chifukwa umalepheretsa mpweya wabwino kuyenda bwino m’thupi. Popanda kuona zizindikiro za mbalamezi, anthuwo amatha kukomoka kapena kufa kumene asakudziwa kuti apuma mpweya woipa.

2 Mwauzimu, Akhristu amafanana ndi anthu ogwira ntchito mu mgodi. Motani? Pamene Yesu amapatsa ophunzira ake ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse, ankadziwa kuti akuwatumiza m’dziko loopsa, lotsogoleredwa ndi Satana ndiponso mzimu wa dziko. (Mat. 10:16; 1 Yoh. 5:19) Yesu anali kudera nkhawa ophunzira ake moti usiku woti afa mawa anapemphera kwa Atate ake kuti: “Sindikupempha kuti muwachotse m’dziko, koma kuti muwayang’anire kuopera woipayo.”​—Yoh. 17:15.

3, 4. Kodi Yesu anachenjeza ophunzira ake za chiyani, ndipo zimenezi zikutikhudza bwanji?

3 Yesu anachenjeza otsatira ake za vuto limene lingawaphetse mwauzimu. Mawu ake ndi ofunika kwambiri kwa ife amene tikukhala ku mapeto a dongosolo lino la zinthu. Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti: “Khalani maso . . . kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika. Kutinso mudzathe kuima pamaso pa Mwana wa munthu.” (Luka 21:34-36) N’zosangalatsa kuti Yesu analonjezanso kuti Atate ake adzawapatsa mzimu woyera umene udzawakumbutse zimene anaphunzira ndi kuwathandiza kukhala maso komanso olimba mtima.​—Yoh. 14:26.

4 Nanga bwanji masiku ano? Kodi nafenso mzimu woyera ungatithandize? Ngati ungatithandize, kodi tingachite chiyani kuti tipatsidwe mzimuwo? Nanga kodi mzimu wa dziko n’chiyani, ndipo umagwira ntchito bwanji? Nanga tingaupewe bwanji?​—Werengani 1 Akorinto 2:12.

Kodi Mumatsogoleredwa ndi Mzimu Woyera Kapena Mzimu wa Dziko?

5, 6. Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji, ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tipatsidwe mzimuwo?

5 Si Akhristu a m’nthawi ya atumwi okha amene anali ndi mwayi wolandira mzimu woyera. Ifenso tingaulandire ndipo mzimu wa Mulungu ungatipatse mphamvu kuti tizichita zinthu zabwino komanso kuti tizitumikira Mulungu. (Aroma 12:11; Afil. 4:13) Mzimu woyera ungatithandizenso kukhala ndi “zipatso za mzimu” monga chikondi, kukoma mtima, ndi ubwino. (Agal. 5:22, 23) Komabe, Yehova Mulungu sapatsa anthu mzimu woyera mokakamiza.

6 Ndiye ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndingatani kuti ndilandire mzimu woyera?’ Baibulo limasonyeza kuti pali zinthu zambiri zimene tingachite. Chinthu chofunika kwambiri komanso chosavuta ndi kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake woyera. (Werengani Luka 11:13.) Chinthu china chofunika ndicho kuphunzira ndiponso kugwiritsa ntchito malangizo ouziridwa ndi mzimu opezeka m’Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16) Sikuti aliyense amene amawerenga Baibulo amalandira mzimu wa Mulungu. Koma Mkhristu woona akamaphunzira Mawu a Mulungu angamachite zinthu mogwirizana ndi Mawu ouziridwa. Tifunikiranso kuzindikira kuti Yehova anasankha Yesu kukhala womuimira komanso njira imene Mulungu akuperekera mzimu wake. (Akol. 2:6) Choncho, tifunika kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi zimene iye anaphunzitsa. (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kutsatira Khristu, m’pamene timalandiranso mzimu woyera.

7. Kodi mzimu wa dziko umatsogolera bwanji anthu?

7 Koma mzimu wa dziko umachititsa anthu kusonyeza makhalidwe a Satana. (Werengani Aefeso 2:1-3.) Mzimu wa dziko umagwira ntchito m’njira zambiri. Monga mmene timaonera masiku ano, mzimu wa dziko umalimbikitsa anthu kusamvera malamulo a Mulungu. Umalimbikitsanso “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yoh. 2:16) Umachititsa anthu kuchita ntchito zathupi monga dama, kupembedza mafano, kukhulupirira mizimu, nsanje, kupsa mtima, ndiponso kumwa mwauchidakwa. (Agal. 5:19-21) Umalimbikitsanso nkhani zampatuko zimene zimaipitsa zinthu zoyera. (2 Tim. 2:14-18) Ngati munthu amatsatira kwambiri mzimu wa dziko, amasonyeza kwambiri makhalidwe a Satana.

8. Kodi tonse tifunika kusankha chiyani?

8 N’zosatheka kuti munthu akhale wosatsogoleredwa ndi mzimu uliwonse. Munthu aliyense ayenera kusankha, kaya kutsogoleredwa ndi mzimu woyera kapena mzimu wa dziko. Anthu amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa dziko angasinthe n’kumatsogoleredwa ndi mzimu woyera. Koma n’zothekanso kuti anthu amene akutsogoleredwa ndi mzimu woyera ayambe kutsogoleredwa ndi mzimu wa dziko. (Afil. 3:18, 19) Tsopano tiyeni tikambirane zimene tingachite kuti tipewe mzimu wa dziko.

Kodi Tingadziwe Bwanji Kuti Tayamba Kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Dziko?

9-11. Kodi tingadziwe bwanji kuti tayamba kutsogoleredwa ndi mzimu wa dziko?

9 Anthu ogwira ntchito m’migodi amene tawatchula kumayambiriro kwa nkhani ino, ankagwiritsa ntchito mbalame kuti adziwe ngati mu mgodi muli mpweya woipa. Ngati wogwira ntchito mu mgodi waona mbalame itagwa, amadziwa kuti afunika kuthawa kuti apulumuke. Nanga pamoyo wathu wauzimu, kodi tingadziwe bwanji kuti mzimu wa dziko wayamba kutitsogolera?

10 Titangophunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu n’kudzipereka kwa Yehova, mwina tinkakonda kuwerenga kwambiri Baibulo. Mosakayikira nthawi zambiri tinkapemphera mochokera pansi pamtima. Ndipo tinkasangalala kupezeka pa misonkhano ya mpingo komanso tinkaona msonkhano uliwonse kuti ndi njira yotitsitsimutsira mwauzimu monga amachitira madzi kwa munthu wa ludzu. Zimenezi zinatithandiza kuti tisiyane ndi mzimu wa dziko.

11 Kodi timayesetsabe kuwerenga Baibulo tsiku ndi tsiku? (Sal. 1:2) Kodi timapemphera kawirikawiri ndiponso mochokera pansi pamtima? Kodi timapezeka pa misonkhano yonse ya mpingo mlungu uliwonse? (Sal. 84:10) Kapena kodi tinaleka kuchita zina mwa zinthu zimenezi? N’zoona kuti tingakhale ndi zochita zambiri zofuna nthawi ndi mphamvu zathu ndipo zingakhale zovuta kuti tipitirize kuchita zinthu zonse zauzimu. Koma ngati tinasiya kuchita zina mwa zinthu zimenezi, kodi chingakhale chifukwa chakuti tayamba kutsogoleredwa ndi mzimu wa dziko? Kodi tsopano tingayesetse kuyambiranso kuchita zinthu zabwino zimene tinkachita kale?

‘Musalemedwe’

12. Kodi Yesu anachenjeza chiyani ophunzira ake, ndipo n’chifukwa chiyani?

12 Kodi n’chiyaninso chimene tingachite kuti tipewe mzimu wa dziko? Pamene Yesu amalangiza ophunzira ake kuti ‘akhale maso’ anali atangowachenjeza zinthu zofunika kupewa. Iye anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo, kuti tsikulo lingadzakufikireni modzidzimutsa ngati msampha.”​—Luka 21:34, 35.

13, 14. Pankhani ya kudya ndi kumwa, kodi ndi bwino kudzifunsa mafunso ati?

13 Taganizirani za chenjezo limeneli. Kodi Yesu amatanthauza kuti sitiyenera kudya ndi kumwa? Ayi, chifukwa iye ankadziwa zimene Solomo ananena kuti: “Ndidziwa kuti [ana a anthu] alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlal. 3:12, 13) Komabe, Yesu anadziwa kuti mzimu wa dziko umachititsa kuti anthu asamadziletse pa zinthu zimenezi.

14 Kodi tingadziwe bwanji kuti sitikutengera mzimu wa dziko pankhani ya kudya ndi kumwa kwambiri? Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimamva bwanji ndikawerenga malangizo m’Baibulo kapena m’mabuku athu onena za kususuka? Kodi ndimaona kuti palibe cholakwika ndi zimene ndimachita kapena ndimaona kuti malangizo amenewa si ofunika komanso ndi onyanyira? * Kodi ndimawaona motani malangizo okhudza kumwa mowa mosapitirira muyezo ndi kupewa “maphwando a phokoso”? Kodi ndimanyalanyaza malangizo amenewa, n’kumaganiza kuti sakundikhudza? Ngati ena sakusangalala ndi mmene ndimamwera, kodi ndimadziikira kumbuyo kapena kukwiya kumene? Kodi ndimalimbikitsa ena kunyalanyaza malangizo a m’Baibulo amenewa?’ Indedi, tingadziwe kuti munthu akutsogoleredwa ndi mzimu wa dziko, mwa kuona mmene amaonera nkhani imeneyi.​—Yerekezerani ndi Aroma 13:11-14.

Pewani Kutsamwitsidwa ndi Nkhawa

15. Kodi Yesu anachenjeza anthu kupewa chizolowezi chotani?

15 Chinanso chimene tingachite kuti tipewe mzimu wa dziko ndi kuchepetsa nkhawa. Yesu anadziwa kuti anthu opanda ungwirofe timakonda kuda nkhawa ndi zinthu za tsiku ndi tsiku. Anauza ophunzira ake mwachikondi kuti: “Lekani kudera nkhawa.” (Mat. 6:25) Komabe, n’zomveka kudera nkhawa zinthu zofunika monga kukondweretsa Mulungu, kusamalira udindo wathu wachikhristu, ndi kupezera banja lathu zinthu zofunika pamoyo. (1 Akor. 7:32-34) Nanga kodi tikuphunzira chiyani pa chenjezo la Yesu limeneli?

16. Kodi mzimu wa dziko ukusocheretsa bwanji anthu ambiri?

16 Mzimu wa dziko umene umalimbikitsa kwambiri anthu kukhala ndi mtima wodziwonetsera, wachititsa anthu ambiri kukhala ndi nkhawa pa zinthu zosafunikira. Dziko limafuna kuti tizikhulupirira kuti munthu akakhala ndi ndalama ndiye kuti ali ndi moyo wabwino. Limafunanso kuti tizikhulupirira kuti munthu amakhala wofunika chifukwa cha zinthu zimene ali nazo osati chifukwa cha makhalidwe achikhristu. Anthu amene amatengeka ndi maganizo amenewa amakhala akapolo a chuma ndipo nthawi zonse amakhala ndi nkhawa yoti apeze zinthu zatsopano, zazikulu komanso zotsogola. (Miy. 18:11) Maganizo olakwika amenewa amayambitsa nkhawa imene imalepheretsa anthu kukula mwauzimu.​—Werengani Mateyo 13:18, 22.

17. Kodi tingapewe bwanji kutsamwitsidwa ndi nkhawa?

17 Tingapewe kutsamwitsidwa ndi nkhawa ngati titsatira malangizo a Yesu akuti: “Chotero pitirizani kufuna ufumu choyamba ndi chilungamo [cha Mulungu].” Yesu akutitsimikizira kuti tikachita zimenezi, tidzapatsidwa zinthu zonse zimene timafunikira pamoyo wathu. (Mat. 6:33) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira lonjezo limeneli? Njira imodzi ndi mwa kufuna choyamba chilungamo cha Mulungu, kapena kuti kumvera malamulo a Mulungu pankhani za ndalama. Mwachitsanzo, timapewa kuchita chinyengo pankhani yolipira msonkho kapena kunama pankhani zimene tingazione ngati zazing’ono zokhudza malonda. Tiziyesetsa kulipira ngongole, ndipo ‘Inde wathu azikhaladi Inde’ pankhani imeneyi. (Mat. 5:37; Sal. 37:21) Kuona mtima kotere sikungachititse munthu kukhala wolemera, koma kumasangalatsa Mulungu, ndipo munthu amakhala ndi chikumbumtima chabwino, komanso sakhala ndi nkhawa zambiri.

18. Kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani, ndipo timapindula bwanji tikamamutsanzira?

18 Kuti tifune Ufumu choyamba, tiyenera kudziwa zinthu zofunika kwambiri pamoyo wathu. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Nthawi zina, Yesu ankavala chovala cha mtengo wapatali. (Yoh. 19:23) Ankadya chakudya ndi kumwa vinyo pamodzi ndi anzake abwino. (Mat. 11:18, 19) Komabe, katundu ndi kusangalala zinali zinthu zongowonjezera pamoyo wake osati zofunika kwambiri. Chinthu chofunika kwambiri kwa Yesu chinali kuchita chifuniro cha Mulungu. (Yoh. 4:34-36) Moyo umasangalatsa kwambiri tikamatsanzira Yesu. Timasangalala tikamathandiza anthu oponderezedwa mwa kuwalimbikitsa ndi Malemba. Ndipo anthu a mu mpingo amatikonda komanso amatilimbikitsa. Ndiponso timasangalatsa Yehova. Tikaika zinthu zofunika pamalo oyenera, katundu ndi zinthu zosangalatsa sizingatilamulire. M’malo mwake zinthu zimenezi zimatithandiza polambira Yehova. Ndipo tikamachita khama pantchito ya Ufumu wa Mulungu, mzimu wa dziko sungatitsogolere.

Pitirizani ‘Kuika Maganizo pa Zinthu za Mzimu’

19-21. Kodi tingapitirize bwanji “kuika maganizo pa zinthu za mzimu,” nanga n’chifukwa chiyani tifunika kuchita zimenezi?

19 Tisanachite chinthu china chilichonse, timayamba taganiza kaye. Zinthu zimene anthu amati munthu wachita mosaganizira, nthawi zambiri amazichita chifukwa choganiza mwakuthupi. N’chifukwa chake mtumwi Paulo anatikumbutsa kuti tifunika kusamala ndi zinthu zimene tikuganiza. Iye analemba kuti: “Otsatira zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatira za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.”​—Aroma 8:5.

20 Kodi tingateteze bwanji maganizo athu ndi zochita zathu kuti tisatsogoleredwe ndi mzimu wa dziko? Tiyenera kuyesetsa kwambiri kuteteza maganizo athu kuti musalowe mfundo za dziko. Mwachitsanzo, posankha zosangalatsa, tisalole maganizo athu kuipitsidwa ndi zinthu zimene zimalimbikitsa chiwerewere ndi chiwawa. Tifunika kuzindikira kuti mzimu woyera wa Mulungu sugwira ntchito kwa munthu amene ali ndi maganizo oipa. (Sal. 11:5; 2 Akor. 6:15-18) Ndipo mzimu wa Mulungu umagwira ntchito m’maganizo mwathu ngati timawerenga Baibulo nthawi zonse, kupemphera, kusinkhasinkha ndi kupezeka pamisonkhano. Komanso tikamalalikira, timakhala tikugwira ntchito ndi mzimu umenewu.

21 Ndithudi, tiyenera kupewa mzimu wa dziko ndiponso kukonda chuma kumene mzimuwu umalimbikitsa. Kuchita zimenezi n’kofunika kwambiri, monga mmene Paulo ananenera kuti: “Kuika maganizo pa zinthu za thupi ndiko imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu ndiko moyo ndi mtendere.”​—Aroma 8:6.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Munthu wosusuka amakhala ndi maganizo aumbombo ndipo amadya mosadziletsa. Choncho, amaonekera osati ndi kunenepa kwa munthu koma ndi mmene munthuyo amaonera chakudya. Munthu atha kukhala wochepa thupi kapena wowonda koma ali wosusuka. Nthawi zina munthu amatha kukhala wonenepa chifukwa cha matenda kapena chibadwa chake. Komabe, kaya munthu ndi wonenepa kapena wowonda, nkhani yagona pa dyera la munthuyo pankhani ya chakudya.​—Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2004.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi tifunika kuchita chiyani kuti tilandire mzimu woyera?

• Kodi mzimu wa dziko ungatikhudze m’njira zotani?

• Kodi tingapewe bwanji mzimu wa dziko?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Pemphani mzimu woyera musanapite ku ntchito kapena kusukulu

[Zithunzi patsamba 23]

Tiyenera kukhala oyera m’maganizo, kukhala oona mtima pankhani zamalonda, komanso tisamadye ndi kumwa mopitirira muyezo