Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ilitu Ndi Dzina Loyera Ndiponso Lalikulu la Mulungu”

“Ilitu Ndi Dzina Loyera Ndiponso Lalikulu la Mulungu”

“Ilitu Ndi Dzina Loyera Ndiponso Lalikulu la Mulungu”

Mawu amenewa ananena ndi Nicholas wa ku Cusa pa ulaliki wake wa m’chaka cha 1430. * Iye anali ndi chidwi m’zinthu zambiri, mwachitsanzo anaphunzira Chigiriki, Chiheberi, zaumulungu, masamu, za kuthambo ndiponso maphunziro a nzeru za anthu. Ali ndi zaka 22, anakhala katswiri wa malamulo a Tchalitchi cha Katolika. Mu 1448, anasankhidwa kukhala kadinala.

Zaka pafupifupi 550 zapitazo, Nicholas wa ku Cusa anakhazikitsa nyumba yosamaliriramo anthu okalamba ku Kues, komwe panopa kumatchedwa kuti Bernkastel-Kues. Tawuni imeneyi ili pamtunda wa makilomita 130 kum’mwera kwa mzinda wa Bonn, ku Germany. Panopa m’nyumba imeneyi mulinso laibulale ya ku Cusa imene ili ndi mipukutu yoposa 310. Umodzi wa mipukutu imeneyi umatchedwa Codex Cusanus 220 mmene mumapezeka ulaliki wa Nicholas wa ku Cusa wa m’chaka cha 1430. Mu ulaliki umenewo, umene mutu wake unali wakuti In principio erat verbum (Pachiyambi Panali Mawu), Nicholas wa ku Cusa anagwiritsa ntchito dzina lakuti Iehoua, lomwe ndi dzina lakuti Yehova mu Chilatini. * Patsamba 56 la mpukutu umenewu, pali mawu onena za dzina la Mulungu. Mawuwa amati: “Ndi dzina limene Mulungu anadzipatsa. Dzina limeneli lili ndi zilembo zinayi. . . . Ilitu ndi dzina loyera ndiponso lalikulu la Mulungu.” Mawu a Nicholas wa ku Cusa amenewa amagwirizana ndi mfundo yakuti dzina la Mulungu limapezeka m’Malemba oyambirira Achiheberi.​—Eks. 6:3.

Mpukutu umenewu unalembedwa kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1400 ndipo ndi umodzi mwa mipukutu yakale imene ikupezekabe. M’mipukutu imeneyi zilembo zinayi za dzina la Mulungu zimalembedwa kuti “Iehoua.” Zolemba zimenezi ndi umboni winanso wotsimikizira kuti mawu ofanana ndi akuti “Yehova” akhala akugwiritsidwa ntchito kwa zaka zambiri polemba dzina la Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Nicholas wa ku Cusa ankadziwikanso ndi mayina awa: Nikolaus Cryfts (Krebs), Nicolaus Cusanus, ndi Nikolaus von Kues. Dzina lakuti Kues ndi la tawuni ya ku Germany kumene anabadwira.

^ ndime 3 Cholinga cha ulaliki umenewu chinali kulimbikitsa anthu kukhulupirira Utatu.

[Chithunzi patsamba 16]

Laibulale ya ku Cusa