Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu?

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu?

Kodi Mumakhala Patsogolo Posonyeza Ulemu?

“Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.”​—AROMA 12:10.

1. Kodi masiku ano anthu m’mayiko ambiri sachita chiyani?

M’MAYIKO ena, ndi mwambo kuti ana akakhala ndi anthu achikulire azigwada posonyeza ulemu. Mwakuchita zimenezi, saoneka aatali kuposa anthu akuluakulu. M’madera amenewa, si ulemu mwana kufulatira munthu wachikulire. Anthu azikhalidwe zosiyanasiyana ali ndi njira zawo zosonyezera ulemu, ndipo zimenezi zimatikumbutsa Chilamulo cha Mose. Mu Chilamulochi muli lamulo lakuti: “Pali aimvi uziwagwadira [posonyeza ulemu], nuchitire ulemu munthu wokalamba.” (Lev. 19:32) N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano, anthu m’mayiko ambiri salemekezana.

2. Kodi Mawu a Mulungu amatiuza kuti tizilemekeza ndani?

2 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti kulemekeza ena n’kofunika kwambiri. Amatiuza kuti tiyenera kulemekeza Yehova ndi Yesu. (Yoh. 5:23) Timalamulidwanso kulemekeza anthu am’banja mwathu, okhulupirira anzathu komanso anthu ena. (Aroma 12:10; Aef. 6:1, 2; 1 Pet. 2:17) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza Yehova? Kodi tingawalemekeze bwanji abale ndi alongo athu achikhristu? Tiyeni tikambirane mafunso amenewa ndi ena otero.

Lemekezani Yehova ndi Dzina Lake

3. Kodi njira imodzi yofunika yolemekezera Yehova ndi iti?

3 Njira imodzi yofunika kwambiri yomwe tingasonyezere Yehova ulemu ndiyo kulemekeza dzina lake. Ndipotu, ndife “anthu a dzina lake.” (Mac. 15:14) Ndithudi, ndi mwayi waukulu kudziwika ndi dzina la Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova. Mneneri Mika anati: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthawi yomka muyaya.” (Mika 4:5) ‘Timayenda m’dzina la Yehova’ ngati timayesetsa tsiku lililonse kuchita zinthu zimene zingalemekezetse dzina limene timadziwika nalo. Monga mmene Paulo anakumbutsira Akhristu ku Roma, ngati tichita zinthu zosemphana ndi uthenga wabwino umene timalalikira, dzina la Mulungu ‘limanyozedwa,’ kapena kuchitiridwa mwano.​—Aroma 2:21-24.

4. Kodi mumauona bwanji mwayi wathu wolalikira za Yehova?

4 Timalemekezanso Yehova mwa ntchito yathu yolalikira. Kale, Yehova anaitana mtundu wa Isiraeli kuti ukhale mboni zake, koma iwo analephera ntchito imeneyi. (Yes. 43:1-12) Nthawi zambiri anam’pandukira Yehova “nachepsa [“nam’psetsa mtima,” NW] Woyerayo wa Israyeli.” (Sal. 78:40, 41) Mapeto ake, Yehova anasiyiratu kukonda mtundu umenewu. Koma ife masiku ano timayamikira mwayi umene tili nawo wolalikira za Yehova ndi wolengeza dzina lake. Timayamikira mwayi umenewu chifukwa timamukonda komanso timafuna dzina lake litayeretsedwa. Ndipo sitingasiye kulalikira chifukwa timadziwa choonadi cha Atate wathu wakumwamba ndi zolinga zake. Timamva mofanana ndi mtumwi Paulo amene anati: “Ndinalamulidwa kutero. Ndithudi, tsoka kwa ine ngati sindilengeza uthenga wabwino!”​—1 Akor. 9:16.

5. Kodi kukhulupirira Yehova n’kogwirizana bwanji ndi kumulemekeza?

5 Wamasalmo Davide anati: “Iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira Inu; pakuti, Inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna Inu.” (Sal. 9:10) Ngati timamudziwadi Yehova ndi kulemekeza dzina lake tidzamukhulupirira monga anachitira atumiki ake okhulupirika akale. Kukhulupirira Yehova ndi njira inanso yosonyezera kuti timamulemekeza. Onani kuti Mawu a Mulungu amasonyeza kuti kukhulupirira Yehova n’kogwirizana ndi kumulemekeza. Aisiraeli akale atalephera kumukhulupirira, Yehova anafunsa Mose kuti: “Anthu awa adzaleka liti kundinyoza? ndipo adzayamba liti kundikhulupirira, chinkana zizindikiro zonse ndinazichita pakati pawo?” (Num. 14:11) Choncho amene amalemekeza Mulungu amamukhulupirira. Timasonyeza kuti timalemekeza Yehova ngati timakhulupirira kuti adzatiteteza ndi kutithandiza kupirira tikamayesedwa.

6. Kodi n’chiyani chimatipangitsa kulemekeza kwambiri Yehova?

6 Yesu ananena kuti kulemekeza Yehova kuyenera kuchokera mu mtima. Polankhula ndi anthu amene ankalambira Mulungu mwachinyengo, Yesu anagwira mawu a Yehova akuti: “Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mtima wawo uli kutali ndi ine.” (Mat. 15:8) Choncho timalemekezadi Yehova ngati timamukonda ndi mtima wonse. (1 Yoh. 5:3) Ndipo timakumbukiranso zimene Yehova analonjeza zakuti: “Amene andilemekeza ine, inenso ndidzawalemekeza.”​—1 Sam. 2:30.

Oyang’anira mu Mpingo Ayenera Kulemekeza Ena

7. (a) Kodi n’chifukwa chiyani abale audindo ayenera kulemekeza anthu amene akuwayang’anira? (b) Kodi Paulo analemekeza bwanji okhulupirira anzake?

7 Mtumwi Paulo analangiza okhulupirira anzake kuti: “Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Abale amene ali ndi udindo mumpingo, ayenera kupereka chitsanzo kapena kuti ‘azikhala patsogolo’ posonyeza ulemu anthu amene akuwang’anira. Pankhani imeneyi, anthu amene ali ndi udindo waukulu angachite bwino kutsatira chitsanzo cha Paulo. (Werengani 1 Atesalonika 2:7, 8.) Abale m’mipingo imene Paulo anachezera ankadziwa kuti iye sangawapemphe kuchita zinthu zimene iye sangachite. Paulo analemekeza okhulupirira anzake, ndipo iwonso anamulemekeza. N’zoonekeratu kuti pamene Paulo ananena kuti, “chotero ndikukuchondererani, khalani onditsanzira ine,” anthu ambiri anachitadi zimenezi chifukwa iye anali chitsanzo chabwino.​—1 Akor. 4:16.

8. (a) Kodi ndi njira yofunika kwambiri iti imene Yesu analemekezera ophunzira ake? (b) Kodi oyang’anira masiku ano angatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu?

8 Njira inanso imene abale amene ali ndi udindo amalemekezera anthu amene akuwayang’anira ndi mwa kuwauza zifukwa zimene akuwapemphera ndi kuwalangizira kuchita zinthu zinazake. Akamachita zimenezi amatsanzira Yesu. Mwachitsanzo, pouza ophunzira ake kupempha kuti apatsidwe antchito ambiri kuntchito yokolola, Yesu anawauza chifukwa chake. Iye anati: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” (Mat. 9:37, 38) Komanso, pouza ophunzira ake kuti ‘akhalebe maso,’ anawauzanso chifukwa chake. Iye anati: “Chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwera.” (Mat. 24:42) Nthawi zambiri, Yesu ankauza ophunzira ake zoyenera kuchita komanso chifukwa chake ayenera kuchita zimenezo. Mwakuchita zimenezi, iye anasonyeza kuti ankawalemekeza. Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa oyang’anira achikhristu.

Lemekezani Mpingo wa Yehova ndi Malangizo Ake

9. Kodi tikamalemekeza mpingo wachikhristu wapadziko lonse ndi anthu amene amauyang’anira timakhala tikulemekezanso ndani? Fotokozani.

9 Kuti tilemekeze Yehova, tifunikanso kulemekeza mpingo wachikhristu wapadziko lonse, pamodzi ndi anthu amene amauyang’anira. Tikamamvera malangizo a m’Malemba ochokera kwa gulu la kapolo wokhulupirika, timasonyeza kuti tikulemekeza gulu la Yehova. Mu mpingo wachikhristu wa m’nthawi ya atumwi, Yohane anadzudzula anthu amene sankalemekeza anthu amene anali ndi udindo. (Werengani 3 Yohane 9-11.) Mawu a Yohane akusonyeza kuti anthu ena sankalemekeza oyang’anira komanso zimene ankawaphunzitsa ndi kuwalangiza. Ubwino wake ndi wakuti Akhristu ambiri sankachita nawo zimenezi. Zikuoneka kuti atumwi ali moyo, abale onse monga gulu ankalemekeza kwambiri oyang’anira.​—Afil. 2:12.

10, 11. Fotokozani kuchokera m’Malemba chifukwa chake n’koyenera kuti anthu ena mumpingo wachikhristu azikhala ndi udindo.

10 Popeza Yesu anauza ophunzira ake kuti “nonsenu ndinu abale,” anthu ena amaganiza kuti mumpingo wachikhristu simuyenera kukhala maudindo. (Mat. 23:8) Koma m’Malemba a Chiheberi ndi Chigiriki muli zitsanzo zambiri za amuna amene anapatsidwa udindo ndi Mulungu. Mbiri ya makolo akale, oweruza ndi mafumu achiheberi, ndi umboni wokwanira wakuti Yehova amapereka malangizo kudzera mwa anthu omuimira. Anthu akapanda kulemekeza anthu audindo amenewa, Yehova ankawalanga.​—2 Maf. 1:2-17; 2:19, 23, 24.

11 Akhristu a m’nthawi ya Atumwi nawonso ankalemekeza anthu amene anali ndi udindo. (Mac. 2:42) Mwachitsanzo, Paulo ankalangiza abale ake. (1 Akor. 16:1; 1 Ates. 4:2) Komabe, iyenso ankagonjera anthu amene anali kumuyang’anira. (Mac. 15:22; Agal. 2:9, 10) Ndithudi, Paulo ankawaona moyenera maudindo a mumpingo wachikhristu.

12. Kodi zitsanzo za m’Baibulo zikutiphunzitsa mfundo ziwiri ziti pankhani ya udindo?

12 Tikuphunzirapo mfundo ziwiri pamenepa. Choyamba, ndi zochokera m’Malemba kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kudzera m’Bungwe Lolamulira aziika amuna paudindo. Ndipo amuna ena amapatsidwa udindo woyang’anira anthu amene alinso ndi udindo. (Mat. 24:45-47; 1 Pet. 5:1-3) Chachiwiri, tonsefe, limodzi ndi amuna amene ali ndi udindo omwe, tiyenera kulemekeza anthu amene amatiyang’anira. Nangano kodi tingalemekeze bwanji anthu amene ali ndi udindo woyang’anira mumpingo wachikhristu wapadziko lonse?

Lemekezani Oyang’anira Oyendayenda

13. Kodi tingawalemekeze bwanji oyang’anira mpingo wachikhristu masiku ano?

13 Paulo anati: “Tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza aja amene akugwira ntchito zolimba pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye ndi kukulangizani. Muwapatse ulemu wowirikiza mwa chikondi, chifukwa cha ntchito yawo. Khalani a mtendere kwa wina ndi mnzake.” (1 Ates. 5:12, 13) Ndithudi, oyang’anira oyendayenda ali m’gulu la anthu amene “akugwira ntchito zolimba.” Choncho, tiyeni tiwapatse “ulemu wowirikiza.” Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kutsatira malangizo awo ndi mtima wonse. Oyang’anira amenewa akatipatsa malangizo ochokera ku gulu la kapolo wokhulupirika, “nzeru yochokera kumwamba” idzatithandiza kukhala ‘okonzeka kumvera.’​—Yak. 3:17.

14. Kodi mpingo umasonyeza bwanji kuti umalemekeza ndi mtima wonse oyang’anira oyendayenda, ndipo padzakhala zotsatira zotani?

14 Nanga bwanji akatiuza kuti tichite zinthu mosiyana ndi mmene timachitira nthawi zonse? Ngati timawalemekeza sitidzakana malangizowo, mwina n’kumanena kuti, “Kuno sitichita zinthu choncho” kapena kuti, “Zimenezi zingagwire ntchito m’madera ena osati mumpingo wathu uno.” Koma tidzayesetsa kutsatira malangizo awo. Chingatithandize kuchita zimenezi ndi kukumbukira nthawi zonse kuti mpingo ndi wa Yehova komanso kuti Yesu ndiye Mutu wake. Mpingo umasonyeza kuti umalemekezadi oyang’anira oyendayenda, ngati umatsatira mosangalala malangizo amene iwo amapereka. Mtumwi Paulo anayamikira abale a ku Korinto chifukwa cholemekeza ndiponso kumvera malangizo amene anapatsidwa ndi Tito, mkulu amene anayendera mpingo wawo. (2 Akor. 7:13-16) Masiku ano, ifenso ngati tigwiritsira ntchito ndi mtima wonse malangizo a oyang’anira oyendayenda, tidzakhala osangalala pochita ntchito yolalikira.​—Werengani 2 Akorinto 13:11.

“Lemekezani Anthu, Kaya Akhale a Mtundu Wotani”

15. Kodi ndi njira zina ziti zimene tingalemekezere okhulupirira anzathu?

15 Paulo analemba kuti: “Usadzudzule mwamuna wachikulire mokalipa. Koma um’dandaulire monga bambo wako, amuna achinyamata monga abale ako, akazi achikulire monga amayi wako, akazi achitsikana monga alongo ako, ndi chiyero chonse. Lemekeza akazi amasiye amene alidi amasiye.” (1 Tim. 5:1-3) Inde, Mawu a Mulungu amatilangiza kuti tizilemekeza anthu onse mumpingo wachikhristu. Bwanji ngati simukugwirizana ndi m’bale kapena mlongo winawake? Kodi zimenezi ziyenera kukulepheretsani kumulemekeza? Kapena kodi mungasinthe maganizo anuwo mwa kuona makhalidwe abwino achikhristu amene mtumiki wa Mulungu ameneyo ali nawo? Makamaka anthu amene ali ndi udindo mumpingo, nthawi zonse ayenera kulemekeza abale awo osati ‘kuchita ufumu . . . kwa gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:3) Ndithudi, mumpingo wachikhristu wapadziko lonse, umene umadziwika kuti anthu ake amakondana zenizeni, tili ndi zifukwa zambiri zolemekezerana.​—Werengani Yohane 13:34, 35.

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kulemekeza anthu amene timawalalikira komanso anthu amene amatitsutsa? (b) Kodi ‘tingalemekeze bwanji anthu, kaya akhale a mtundu wotani’?

16 Komabe, sitiyenera kulemekeza anthu a mumpingo wachikhristu okha. Paulo analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Ngati mpata tili nawo, tiyeni tichitire onse zabwino.” (Agal. 6:10) N’zoona kuti kutsatira malangizo amenewa kungakhale kovuta ngati mnzathu wakuntchito kapena kusukulu watichitira chipongwe. Zinthu zikakhala choncho, tifunika kukumbukira mawu akuti: “Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa.” (Sal. 37:1) Kutsatira malangizo amenewa kungatithandize kuchitira ulemu ngakhale anthu otitsutsa. Mofananamo, tikamalalikira, kudzichepetsa kungatithandize kuyankha anthu onse “ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.” (1 Pet. 3:15) Ngakhalenso maonekedwe ndi mavalidwe athu angasonyeze kuti timalemekeza anthu amene timawalalikira.

17 Ndithudi, kaya tikuchita zinthu ndi okhulupirira anzathu kapena ndi anthu ena, tifunika kuyesetsa kutsatira malangizo akuti: “Lemekezani anthu, kaya akhale a mtundu wotani, kondani gulu lonse la abale, opani Mulungu, lemekezani mfumu.”​—1 Pet. 2:17.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi tingasonyeze bwanji kuti timalemekeza:

• Yehova?

• Akulu mumpingo ndiponso oyang’anira oyendayenda?

• Anthu onse mumpingo?

• Anthu amene timawalalikira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankalemekeza bungwe lolamulira

[Chithunzi patsamba 24]

Akulu m’mayiko onse amalemekeza oyang’anira oyendayenda amene amaikidwa ndi Bungwe Lolamulira