Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Amatiyang’ana ndi Zolinga Zabwino

Yehova Amatiyang’ana ndi Zolinga Zabwino

Yehova Amatiyang’ana ndi Zolinga Zabwino

“Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”​—2 MBIRI 16:9.

1. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova amatisanthula?

YEHOVA ndi Tate wabwino. Amatidziwa bwino kwambiri moti amadziwa ngakhale “zolingirira zonse za maganizo” athu. (1 Mbiri 28:9) Komabe, iye satiyang’ana n’cholinga choti atipezere zifukwa. (Sal. 11:4; 130:3) Iye amafuna kutiteteza mwachikondi ku zinthu zimene zingawononge ubwenzi wathu ndi iye komanso ku zinthu zimene zingatilepheretse kudzalandira moyo wosatha.​—Sal. 25:8-10, 12, 13.

2. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza ndani?

2 Yehova ndi wamphamvu zonse ndipo amaona zinthu zonse. Chifukwa cha mphamvu zimenezi, iye amathandiza atumiki ake okhulupirika nthawi iliyonse imene am’pempha thandizo ndiponso akamayesedwa. Lemba la 2 Mbiri 16:9 limati: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” Onani kuti Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza anthu amene amamutumikira ndi mtima wangwiro kapena kuti mtima woyera ndiponso wa zolinga zabwino. Iye sasonyeza chikondi chotere kwa anthu achinyengo.​—Yos. 7:1, 20, 21, 25; Miy. 1:23-33.

Yendani ndi Mulungu

3, 4. Kodi ‘kuyenda ndi Mulungu’ kumatanthauza chiyani, ndipo ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zikutithandiza kuona kuti zimenezi n’zotheka?

3 Anthu ambiri amaganiza kuti n’zosatheka kuyenda ndi Mlengi wa chilengedwe chonse. Komabe, zimenezi n’zimene Yehova akufuna kuti tichite. M’nthawi za m’Baibulo, Enoke ndi Nowa ‘anayenda ndi Mulungu.’ (Gen. 5:24; 6:9) Mose “anapitirizabe kukhala wochirimika ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb. 11:27) Mfumu Davide anayenda modzichepetsa ndi Atate wake wakumwamba. Iye anati: “Popeza [Yehova] ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.”​—Sal. 16:8.

4 N’zoona kuti sitingagwire dzanja la Yehova n’kumayenda naye ngati mmene timachitira ndi anthu anzathu. Komabe, tingachite zimenezi mophiphiritsa. Kodi tingayende naye motani? Wamasalmo Asafu analemba kuti: “Ndikhala ndi Inu chikhalire: Mwandigwira dzanja langa la manja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu.” (Sal. 73:23, 24) Kunena mwachidule, timayenda ndi Yehova tikamatsatira kwambiri malangizo ake, amene timalandira kudzera m’Mawu ake ndiponso kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mat. 24:45; 2 Tim. 3:16.

5. Kodi Yehova amawayang’anira bwanji atumiki ake okhulupirika monga amachitira bambo wachikondi, ndipo kodi tizimuona bwanji?

5 Yehova amakonda anthu amene amayenda naye ndipo amawayang’anira monga amachitira bambo wachikondi kwa ana ake. Iye amawasamalira, kuwateteza ndiponso kuwaphunzitsa. Mawu a Mulungu amati: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Sal. 32:8) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimatha kudziona ndikuyenda ndi Yehova mophiphiritsa n’kumatsatira mawu ake anzeru ndiponso iye akundiyang’ana mwachikondi? Kodi zimene ndimaganiza, kulankhula ndiponso kuchita zimasonyeza kuti ndimadziwa kuti Mulungu aliko? Ndikachimwa, kodi ndimamuona Yehova ngati Mulungu wouma mtima kapena ndimamuonabe kuti ndi Tate wokoma mtima komanso wachifundo amene amafuna kuthandiza anthu olapa kuti akhale nayenso paubwenzi?’​—Sal. 51:17.

6. Kodi Yehova amaposa bwanji makolo athu?

6 Nthawi zina Yehova angatithandize tisanafike pochita choipa. Mwachitsanzo, angaone kuti mtima wathu wonyengawu wayamba kukhumba zinthu zoipa. (Yer. 17:9) Zikatere, angatithandize mwamsanga kuposa mmene makolo athu angachitire, chifukwa maso ake amatha kuona mu mtima mwathu ndi kusanthula maganizo athu. (Sal. 11:4; 139:4; Yer. 17:10) Taganizirani mmene Mulungu anachitira ndi Baruki, mlembi komanso mnzake wapamtima wa mneneri Yeremiya.

Mulungu Anali Tate Wachikondi kwa Baruki

7, 8. (a) Kodi Baruki anali ndani, ndipo anayamba kukhala ndi maganizo oipa otani? (b) Kodi Yehova anasonyeza bwanji chikondi kwa Baruki monga amachitira bambo?

7 Baruki anali mlembi amene anatumikira mokhulupirika ndi Yeremiya pantchito yovuta kwambiri yolengeza chiweruzo cha Yehova kwa Ayuda. (Yer. 1:18, 19) Baruki ayenera kuti anali wochokera kubanja lotchuka, ndipo nthawi ina anayamba kufuna “zinthu zazikulu.” Mwina anayamba kufuna kutchuka kapena chuma. Kaya Baruki ankafuna chiyani, komabe Yehova anaona kuti Baruki wayamba kukhala ndi maganizo oipa. Nthawi yomweyo, Yehova kudzera mwa Yeremiya anauza Baruki kuti: “Munati, Kalanga ine tsopano! pakuti Yehova wawonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.” Ndipo Mulungu anati: “Kodi udzifunira wekha zinthu zazikulu? Usazifune.”​—Yer. 45:1-5.

8 Ngakhale kuti Yehova analankhula mwamphamvu kwa Baruki, iye sanalankhule mwaukali koma analankhula naye monga amachitira bambo wachikondi. N’zoona kuti Baruki anali ndi maganizo oipa, koma Mulungu anaona kuti iye sanali ndi mtima woipa kapena wachinyengo. Yehova anadziwanso kuti Yerusalemu ndi Yuda anali m’masiku otsiriza, ndipo sanafune kuti Baruki afooke panthawi yovuta imeneyi. Choncho pothandiza mtumiki wakeyu, Yehova anamukumbutsa Baruki kuti awononga anthu onse oipa ndipo ngati iye achita zinthu mwanzeru, adzapulumuka. (Yer. 45:5) M’mawu ena, tingati Mulungu anauza Baruki kuti: ‘Kumbukira zimene zichitikire anthu oipa a ku Yuda ndi Yerusalemu posachedwapa. Pitirizabe kukhala wokhulupirika kuti upulumuke. Ndidzakuteteza.’ Mawu a Yehova amenewa ayenera kuti anamukhudza mtima Baruki popeza anasintha maganizo. Patapita zaka 17, Yerusalemu anawonongedwa ndipo iye anapulumuka.

9. Kodi mungayankhe bwanji mafunso a m’ndimeyi?

9 Pamene mukuganizira nkhani ya Baruki, onani mafunso ndi malemba otsatirawa: Kodi mmene Mulungu anachitira ndi Baruki zikusonyeza chiyani za Yehova ndiponso mmene amaonera atumiki ake? (Werengani Aheberi 12:9.) Popeza tikukhala m’masiku ovuta, kodi zimene Mulungu analangiza Baruki zikutiphunzitsa chiyani? Nanga kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Baruki anachita atalangizidwa? (Werengani Luka 21:34-36.) Potsanzira Yeremiya, kodi akulu achikhristu angasonyeze bwanji kuti Yehova amakonda atumiki ake?​—Werengani Agalatiya 6:1.

Mwana Amasonyeza Chikondi cha Atate Wake

10. Kodi n’chiyani chimamuthandiza Yesu pa udindo wake monga Mutu wa mpingo wachikhristu?

10 Chikhristu chisanayambe, Yehova ankasonyeza chikondi pa anthu ake kudzera mwa aneneri ndi atumiki ake okhulupirika. Masiku ano, amachisonyeza kwambiri kudzera mwa Yesu Khristu yemwe ndi Mutu wa mpingo wachikhristu. (Aef. 1:22, 23) N’chifukwa chake m’buku la Chivumbulutso, Yesu amayerekezeredwa ndi mwana wa nkhosa amene ali ndi “maso asanu ndi awiri. Maso amenewo akuimira mizimu ya Mulungu isanu ndi iwiri, imene yatumizidwa m’dziko lonse lapansi.” (Chiv. 5:6) Inde, popeza ali ndi mphamvu yonse ya mzimu woyera wa Mulungu, Yesu amadziwa zinthu zonse. Iyenso amaona mu mtima mwathu ndiponso amadziwa zonse zimene zikuchitika.

11. Kodi Khristu ali ndi ntchito yotani, ndipo kodi mmene amationera zikufanana bwanji ndi Atate ake?

11 Komabe, mofanana ndi Yehova, Yesu si wapolisi. Iye amatisanthula monga momwe bambo wachikondi amachitira. Yesu amatchedwanso kuti “Atate Wosatha,” ndipo dzina limeneli limatikumbutsa ntchito imene adzagwire yopereka moyo wosatha kwa anthu onse omukhulupirira. (Yes. 9:6) Komanso, monga Mutu wa mpingo wachikhristu, Yesu angachititse Akhristu okhwima mwauzimu, makamaka akulu kuti alimbikitse kapena alangize anthu ena.​—1 Ates. 5:14; 2 Tim. 4:1, 2.

12. (a) Kodi makalata 7 a ku mipingo ya ku Asia Minor amasonyeza chiyani za Yesu? (b) Kodi akulu amasonyeza bwanji mmene Khristu amaonera nkhosa za Mulungu?

12 Makalata amene Khristu analembera akulu a m’mipingo 7 ya ku Asia Minor amasonyeza kuti Khristu amakonda kwambiri nkhosa zake. (Chiv. 2:1–3:22) M’makalata amenewa, Yesu anasonyeza kuti ankadziwa zonse zimene zinkachitika mu mpingo uliwonse komanso kuti ankadera nkhawa kwambiri otsatira ake. Umu ndi mmenenso amachitira masiku ano mwinanso kuposa nthawi imeneyo, popeza masomphenya a m’Chivumbulutso akukwaniritsidwa “m’tsiku la Ambuye.” * (Chiv. 1:10) Nthawi zambiri, Khristu amasonyeza chikondi chake kudzera mwa akulu, amene amatumikira monga abusa auzimu mu mpingo. Iye angachititse “mphatso za amuna” zimenezi kuti zilimbikitse kapena zilangize anthu ena. (Aef. 4:8; Mac. 20:28; werengani Yesaya 32:1, 2.) Kodi zimene amachita amuna amenewa mumaziona kuti ndi umboni wakuti Khristu amakukondani?

Amatithandiza Panthawi Yoyenera

13-15. Kodi Mulungu angayankhe bwanji mapemphero athu? Perekani zitsanzo.

13 Kodi munayamba mwapempherapo kwambiri ndiyeno n’kulandira yankho kudzera mwa Mkhristu wokhwima mwauzimu amene anakulimbikitsani? (Yak. 5:14-16) Mwina yankho linabwera kudzera m’nkhani imene munamva pa misonkhano yachikhristu kapena imene munawerenga m’mabuku athu. Nthawi zambiri Yehova amayankha mapemphero m’njira zimenezi. Mwachitsanzo, mkulu wina atamaliza kukamba nkhani yake, mlongo wina amene anachitiridwa nkhanza kwambiri milungu ingapo m’mbuyomo anapita kukalankhula naye. M’malo modandaula za vuto lakelo, mlongoyo anayamikira kwambiri mfundo zina za m’Malemba zimene zinatchulidwa m’nkhaniyo. Mfundozo zinali zothandiza pavuto lakelo ndipo zinamulimbikitsa kwambiri. Mlongoyu anasangalala kwambiri kuti anapezeka pa msonkhanowo.

14 Chitsanzo china chosonyeza kuti pemphero n’lothandiza ndi cha amuna atatu amene anaphunzira choonadi ali m’ndende n’kukhala ofalitsa osabatizidwa. Chifukwa cha chiwawa chimene chinachitika m’ndendemo, akaidi onse analandidwa ufulu wina umene anali nawo poyamba. Zimenezi zinapangitsa akaidi onse kuukira. Akaidiwo anagwirizana kuti akadya chakudya cha m’mawa tsiku lotsatira, asakabweze mbale posonyeza kukwiya kwawo. Apa abale atatu aja anathedwa nzeru. Iwo anadziwa kuti ngati angachite zimene akaidiwo anagwirizana ndiye kuti sakumvera malangizo a Yehova a pa Aroma 13:1. Anadziwanso kuti ngati sachita nawo, anzawowo awaukira.

15 Popeza panalibe mpata woti atatuwa agwirizane zochita, aliyense anapempha Mulungu kuti amuthandize. M’mawa wa tsiku lotsatira, abale atatuwa anapezeka kuti aganiza chinthu chimodzi chakuti asakadye chakudyacho. Oyang’anira ndende atabwera kudzatolera mbale, anapeza kuti abalewo analibe mbale. Iwo anasangalala kwambiri kuti “Wakumva pemphero” anali nawo.​—Sal. 65:2.

Tisaope Zam’tsogolo

16. Kodi ntchito yolalikira imasonyeza bwanji kuti Yehova amakonda anthu onga nkhosa?

16 Ntchito yolalikira ya padziko lonse ndi umboni wina wosonyeza kuti Yehova amakonda anthu oona mtima, kulikonse kumene ali. (Gen. 18:25) Nthawi zambiri Yehova amagwiritsa ntchito angelo kutsogolera atumiki ake kwa anthu onga nkhosa ngakhale atakhala kuti amakhala m’madera amene uthenga wabwino sunafikeko. (Chiv. 14:6, 7) Mwachitsanzo, mwa mngelo wake, Mulungu anatsogolera Filipo, mlaliki wa m’nthawi ya atumwi kukapezana ndi mdindo wa ku Aitiopiya kuti akam’fotokozere Malemba. Kodi zinthu zinayenda bwanji? Munthuyo anamvetsera uthenga wabwino ndipo anabatizidwa n’kukhala wotsatira wa Yesu. *​—Yoh. 10:14; Mac. 8:26-39.

17. Kodi n’chifukwa chiyani sitifunika kudera nkhawa kwambiri zam’tsogolo?

17 Pamene dongosolo lino la zinthu likupita ku mapeto, “masautso” adzapitirizabe. (Mat. 24:8) Mwachitsanzo, mitengo ya zakudya ikupitiriza kukwera chifukwa cha kuchuluka kwa anthu, kusokonekera kwa nyengo ndi mavuto a zachuma. Anthu ambiri akusowa ntchito ndipo amene ali pantchito akumagwira ntchito maola ambiri. Mulimonse mmene zinthu zingakhalire, anthu amene amaika zinthu za Ufumu patsogolo komanso amene ali ndi ‘diso lolunjika chimodzi’ samada nkhawa kwambiri. Iwo amadziwa kuti Mulungu amawakonda ndipo adzawasamalira. (Mat. 6:22-34) Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yehova anasamalirira Yeremiya panthawi imene Yerusalemu amawonongedwa mu 607 B.C.E.

18. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankakonda Yeremiya panthawi imene Yerusalemu ankawonongedwa?

18 Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, Yeremiya anamangidwa m’bwalo la akaidi. Kodi anapeza bwanji chakudya? Akanakhala kuti sanamangidwe, akanatha kupita kokafuna chakudya. Atamangidwa, amene akanatha kum’patsa chakudya anali anthu amene anali nawo pafupi, koma ambiri anali adani ake. Komabe, Yeremiya sanadalire anthu, anadalira Mulungu amene analonjeza kuti adzamusamalira. Kodi Yehova anamusamaliradi? Inde, anamusamalira. Mulungu anaonetsetsa kuti tsiku lililonse Yeremiya walandira “mkate . . . mpaka unatha mkate wonse wa m’mudzi.” (Yer. 37:21) Panthawiyi, Yeremiya, Baruki, Ebedi-Meleki ndi anthu ena, anapulumuka njala, matenda ndiponso imfa.​—Yer. 38:2; 39:15-18.

19. Kaya tikumane ndi zotani kutsogoloku, kodi tiyenera kutsimikiza mtima za chiyani?

19 Ndithudi, “maso a Yehova ali pa olungama, ndipo amatchera khutu pembedzero lawo.” (1 Pet. 3:12) Kodi mumasangalala kudziwa kuti Atate wathu wakumwamba amatiyang’ana? Kodi mumaona kuti ndinu wotetezeka podziwa kuti Mulungu akukuyang’anani ndi zolinga zabwino? Motero kaya m’tsogolo muli zotani, tiyeni titsimikize mtima kupitiriza kuyenda ndi Mulungu. Tikhale ndi chidaliro kuti Yehova apitiriza kuyang’anira mwachikondi atumiki ake okhulupirika.​—Sal. 32:8; werengani Yesaya 41:13.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Ngakhale kuti makalatawa ankalembera otsatira a Khristu odzozedwa, mfundo zake n’zothandiza kwa atumiki onse a Mulungu.

^ ndime 16 Chitsanzo china chosonyeza kuti Mulungu amatsogolera ntchito yolalikira chili pa Machitidwe 16:6-10. Pamenepa, timawerenga kuti ‘mzimu woyera unaletsa’ Paulo ndi anzake ena kulalikira ku Asiya ndi Bituniya. Komano, anauzidwa kuti akalalikire ku Makedoniya, kumene anthu ofatsa anamvetsera uthenga wabwino.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti ‘tikuyenda ndi Mulungu’?

• Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankakonda Baruki?

• Monga Mutu wa mpingo wachikhristu, kodi Yesu amasonyeza bwanji makhalidwe a Atate ake?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Mulungu m’nthawi zovuta zino?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Masiku ano, akulu achikhristu amasonyeza chikondi cha Yehova, monga mmene Yeremiya anachitira kwa Baruki

[Chithunzi patsamba 10]

Kodi Yehova angatithandize motani panthawi yoyenera?