Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Athandizeni Kubwerera Mwamsanga

Athandizeni Kubwerera Mwamsanga

Athandizeni Kubwerera Mwamsanga

“Tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.”​—YOHANE 6:68.

1. Kodi Petulo ananena chiyani kwa Yesu, ophunzira ake ambiri atam’thawa?

PANTHAWI ina, ophunzira ambiri a Yesu Khristu anam’thawa chifukwa choti sanagwirizane ndi mfundo ina imene iye anaphunzitsa. Yesu anafunsa atumwi ake kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” Ndipo Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:51-69) N’zoonadi, panalibenso kwina koti atumwiwo akanapita. Chipembedzo chachiyuda chinalibe “mawu amoyo wosatha.” Masiku anonso “mawu a moyo wosatha” sapezeka mu Babulo Wamkulu, womwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. Aliyense amene wachoka m’gulu la nkhosa la Mulungu ndipo akufuna kusangalatsa Yehova, ayenera kudziwa kuti tili mu ‘ola lakuti adzuke ku tulo’ n’kubwerera m’gulu.​—Aroma 13:11.

2. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani pankhani zofunika chinsinsi kapena chiweruzo?

2 Yehova anasonyeza kuti ankadera nkhawa nkhosa zosochera za mtundu wa Isiraeli. (Werengani Ezekieli 34:15, 16.) Akulu mumpingo nawonso amafunitsitsa kuthandiza anthu onga nkhosa amene achoka m’gulu. Iwo amachita zimenezi chifukwa amadziwa kuti umenewu ndi udindo wawo. Kodi wofalitsa amene akulu amusankha kuti aphunzire ndi munthu amene anafooka, angatani ngati atadziwa kuti munthuyo anachita tchimo lalikulu? Chifukwa choti nkhani zotere zingafunike chiweruzo kapena chinsinsi, wofalitsayo asayambe kupereka malangizo, m’malomwake alimbikitse wofookayo kuti adziwitse akulu za nkhaniyo. Koma wofookayo akalephera kuchita zimenezi, wofalitsayo awauze yekha akulu nkhaniyo.​—Lev. 5:1; Agal. 6:1.

3. Kodi munthu amene anali ndi nkhosa 100 anatani atapeza nkhosa imodzi imene inasochera?

3 Nkhani yapitayi, inatchula za fanizo la Yesu la munthu amene anali ndi nkhosa 100. Nkhosa imodzi itasowa, iye anasiya nkhosa 99 zija n’kuyamba kuifunafuna. Ataipeza anasangalala kwambiri. (Luka 15:4-7) Nafenso timasangalala kwambiri nkhosa ya Mulungu ikabwerera m’gulu. N’kutheka kuti akulu ndi anthu ena mumpingo anali atayenderapo munthu wofookayo chifukwa cha chikondi. Nawonso akufuna kuti munthuyo abwerere m’gulu lankhosa kuti Mulungu azimuthandiza, kumuteteza, ndi kum’dalitsa. (Deut. 33:27; Sal. 91:14; Miy. 10:22) Kodi iwo ayenera kutani ngati pali munthu wofunika kumuthandiza m’njira imeneyi?

4. Kodi lemba la Agalatiya 6:2, 5 likutithandiza kuzindikira chiyani?

4 Angamulimbikitse mwachikondi wofookayo kuti abwerere mumpingo pomuthandiza kuzindikira kuti Yehova amakonda nkhosa zake. Angamuthandizenso kudziwa kuti zinthu zimene Yehova amafuna kuti tizichita n’zotheka kuzikwanitsa. Zina mwa zinthuzo ndi monga kuwerenga Malemba, kupita kumisonkhano, ndi kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Zingakhale bwino kuwerenga Agalatiya 6:2, 5 n’kufotokoza kuti Akhristu amathandizana ponyamula mitolo yawo, koma pankhani ya udindo wathu kwa Yehova, “aliyense ayenera kunyamula katundu wakewake.” Kukhala wokhulupirika kwa Mulungu si chinthu choti winawake angatichitire.

Kodi Mwina Afooka Chifukwa cha “Nkhawa za Moyo”?

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumvetsera mosamala Akhristu ofooka akamatiuza zimene zikuwavutitsa mumtima? (b) Kodi mungathandize bwanji ofooka kuona kuti kusiya kusonkhana ndi anthu a Mulungu kwawabwezera m’mbuyo kwambiri?

5 Mkhristu wofooka akamafotokoza zimene akuvutika nazo mumtima mwake, akulu ndiponso ofalitsa ena okhwima mwauzimu ayenera kumvetsera mwatcheru kuti apeze njira yabwino yom’thandizira. Tiyerekezere kuti inuyo, monga mkulu, mukuchezera banja limene lakhala lisakupezeka kumpingo chifukwa cha “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Mwina bambo ndi mayiyo anafooka mwauzimu chifukwa cha mavuto azachuma kapena chifukwa cha kukula kwa ntchito yosamalira banja. Iwo anganene kuti anasiya kusonkhana pofuna kuti apepukidwe. Koma afotokozereni kuti kusiya kusonkhana sikungawathandize kuti apeze mpumulo. (Werengani Miyambo 18:1.) Pezani njira yabwino yowafunsira mafunso monga akuti: “Kodi mukuona kuti mwayamba kusangalala chifukwa chosiya kupita ku misonkhano? Kodi panopo banja lanu layamba kuyendako bwino? Kodi panopo mukupezabe chimwemwe chimene munali nacho panthawi imene munkatumikira Yehova?”​—Neh. 8:10.

6 Mafunso amenewa angathandize ofookawo kuganiza mofatsa n’kuona kuti, chifukwa chosiya kupita kumisonkhano, ubwenzi wawo ndi Yehova sukuyenda bwino ndiponso kuti chimwemwe chawo chachepa. (Mat. 5:3; Aheb. 10:24, 25) Mwinanso mungawathandize kuzindikira kuti sakupezanso chimwemwe chifukwa chosiya kulalikira uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Ndiyeno kodi chinthu chanzeru chimene ofookawo ayenera kuchita n’chiyani?

7. Kodi anthu amene achoka m’gulu la nkhosa tingawalimbikitse kuchita chiyani?

7 Yesu anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi kudya kwambiri, kumwa kwambiri, ndi nkhawa za moyo . . . Chotero khalani maso, muzipemphera mopembedzera nthawi zonse, kuti mudzathe kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika.” (Luka 21:34-36) Anthu amene achoka m’gulu la nkhosa koma akufuna kukhalanso osangalala monga kale, angathe kulimbikitsidwa kupempherera mzimu woyera ndiponso thandizo la Mulungu komanso kuti azichita zinthu zogwirizana ndi mapemphero awo.​—Luka 11:13.

Kodi Mwina Anakhumudwitsidwa?

8, 9. Kodi mkulu angathandize bwanji munthu amene wakhumudwitsidwa?

8 Chifukwa choti ndife opanda ungwiro, nthawi zina tingathe kusiyana maganizo n’kukhumudwitsana. Anthu ena anakhumudwa ataona munthu amene amamulemekeza kwambiri mumpingo atachita zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Ngati zimenezi n’zimene zinam’chitikira wofookayo, mkulu amene wamuyendera ayenera kumufotokozera kuti Yehova si amene amachititsa kuti munthu akhumudwe. Ndiye palibe chifukwa choti munthu athetsere ubwenzi wake ndi Mulungu kapena anthu ake. M’malomwake ndi bwino kupitirizabe kutumikira Mulungu podziwa kuti “Woweruza wa dziko lonse” akudziwa zonse zimene zinachitika ndipo adzachita zinthu m’njira yoyenerera. (Gen. 18:25; Akol. 3:23-25) Munthu akapunthwa n’kugwa, samangokhala pompo osayesa n’komwe kudzuka.

9 Pofuna kum’thandiza munthuyo mwauzimu, mkulu angatchule kuti pakapita nthawi, munthuyo angaone kuti zinthu zimene zinamukhumudwitsa alibe nazonso ntchito. N’kuthekanso kuti panopo vuto limene anakhumudwa nalolo linatha. Ngati munthuyo anakhumudwa chifukwa chopatsidwa chilango, kupemphera ndiponso kuganizira nkhaniyo bwinobwino kungam’thandize kuona kuti iyeyo analakwadi penapake ndipo sanachite bwino pokhumudwa ndi chilangocho.​—Sal. 119:165; Aheb. 12:5-13.

Kodi Mwina Sanagwirizane ndi Mfundo Inayake ya M’malemba?

10, 11. Kodi mungathandize bwanji munthu amene anafooka chifukwa chosagwirizana ndi mfundo inayake ya m’Malemba?

10 N’kutheka kuti anthu ena anasiyana ndi gulu la nkhosa la Mulungu chifukwa choti sanagwirizane ndi mfundo inayake ya m’Malemba. Aisiraeli atalanditsidwa ku Iguputo “anaiwala ntchito” zimene Mulungu anawachitira ndipo “sanalindira uphungu wake.” (Sal. 106:13) Mungachite bwino kukumbutsa wofookayo kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupereka chakudya chauzimu chabwino kwambiri. (Mat. 24:45) Mukumbutseni kuti zimenezo ndi zimene zinamuthandiza kuphunzira choonadi poyamba. Motero ndi bwino kuti ayesetse kuyambiranso kuyenda m’choonadi.​—2 Yoh. 4.

11 Mkulu akamayesetsa kuthandiza munthu amene wachoka m’gulu la nkhosa la Mulungu angapereke chitsanzo cha ophunzira amene anasiya Yesu chifukwa chosagwirizana ndi zimene iye anaphunzitsa. (Yoh. 6:53, 66) Atasiya kuyenda ndi Yesu komanso ophunzira ake okhulupirika, anthu amenewa anasiya kuona kuti zinthu zauzimu n’zofunika ndipo sanalinso osangalala. Kodi pali kwina kumene anthu amenewa angapeze chakudya chauzimu chabwino? Ayi ndithu palibe.

Kodi Mwina Anachita Tchimo Lalikulu?

12, 13. Kodi mungathandize bwanji munthu wosochera amene wavomereza kuti anachita tchimo lalikulu?

12 Anthu ena amasiya kulalikira ndi kusonkhana chifukwa choti anachita tchimo lalikulu. Iwo amaopa kuti akaulula kwa akulu achotsedwa mumpingo. Komatu ngati atalapa n’kusiya khalidwe loipalo si zoona kuti angachotsedwe. (2 Akor. 7:10, 11) Iwo akhoza kulandiridwa bwino ndipo akulu angawathandize mwauzimu.

13 Ngati ndinu wofalitsa wokhwima mwauzimu, akulu angakupempheni kuti muthandize munthu wofooka. Ndiyeno kodi mungatani ngati munthuyo atakuuzani kuti anachita tchimo linalake lalikulu? Monga tanenera poyamba paja, imeneyi si nkhani yoti muthane nayo nokha koma mulimbikitseni munthuyo kuti akauze akulu. Ngati sakufuna kukanena, tsatirani malangizo a Mulungu pankhaniyi n’cholinga choti muyeretse dzina la Yehova komanso mpingo wake. (Werengani Levitiko 5:1.) Akuluwo angaone mmene angathandizire munthuyo, amene akufuna kubwerera m’gulu n’kuyamba kuchita chifuniro cha Mulungu. Mwina angafunike kum’patsa chilango mwachikondi. (Aheb. 12:7-11) Ngati wavomereza kuti anachimwira Mulungu, koma wasiya khalidwe loipalo ndipo walapadi, akulu ayenera kumuthandiza ndipo Yehova angathe kumukhululukira.​—Yes. 1:18; 55:7; Yak. 5:13-16.

Anasangalala Mwana Wolowerera Atabwerera

14. Fotokozani fanizo la Yesu la mwana wolowerera.

14 Munthu amene wapemphedwa kuti athandize nkhosa yosochera angagwiritse ntchito fanizo la Yesu la pa Luka 15:11-24. M’fanizo limeneli mwana wina analowerera n’kusakaza chuma chake chonse chifukwa cha khalidwe lake loipa. Patapita nthawi, anayamba kudzimvera chisoni ndipo atavutika ndi njala komanso atasowa abale ake, anaganiza zobwerera kwawo. Bambo ake atamuona akubwera poteropo, anamuthamangira, kumukumbatira n’kumupsompsona mwachikondi ndipo anasangalala kwambiri. Kuganizira fanizo limeneli kungalimbikitse munthu amene wasochera kuti abwerere m’gulu la nkhosa. Popeza dongosolo lino la zinthu liwonongedwa posachedwapa, iye ayenera kubwerera mwamsanga.

15. N’chifukwa chiyani anthu ena amatengeka pang’onopang’ono n’kuchoka mumpingo?

15 Anthu ambiri amene asiyana ndi mpingo sali ngati mwana wolowerera uja. Iwo amayamba kubwerera m’mbuyo pang’onopang’ono ngati boti limene likutengedwa ndi mphepo mwapang’onopang’ono n’kumalowera mkati mwa nyanja. Anthu ena anafooka chifukwa cha nkhawa moti saona kufunika kwa zinthu zauzimu. Komanso anthu ena amakhumudwa chifukwa cha zochita za winawake mumpingo, kapena amasiya kusonkhana chifukwa chosagwirizana ndi mfundo inayake ya m’Malemba. Palinso ena ochepa amene amasiya kusonkhana chifukwa choti achita zinazake zosemphana ndi Malemba. Koma mfundo zimene tafotokoza pa zifukwa zonsezi zingakuthandizeni pothandiza anthu amene achoka m’gulu, kaya pa zifukwa zimenezi kapenanso pa zifukwa zina. Ngati mutatero anthuwo angathe kubwerera mwamsanga, nthawi isanathe.

“Ndasangalala Kwambiri Kuti Mwabwera”

16-18. (a) Kodi mkulu wina anathandiza bwanji m’bale amene anafooka kwa zaka zambiri? (b) Fotokozani chimene chinafooketsa m’baleyu, mmene anam’thandizira, ndiponso mmene mpingo unamulandirira.

16 Mkulu wina mumpingo anati: “Bungwe la akulu la mumpingo wathu limayesetsa kuyendera anthu amene anafooka. Ndinakumbukira m’bale wina amene ndinkaphunzira naye Baibulo n’kumuthandiza kudziwa choonadi. Iyeyu anachoka m’gulu kwa zaka pafupifupi 25 ndipo panthawi imene ndinakumana naye anali pa mavuto aakulu. Ndinam’fotokozera kuti kugwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo kungam’thandize. Patapita nthawi, m’baleyu anayambanso kubwera ku Nyumba ya Ufumu, kuphunzira Baibulo ndiponso anachita khama kwambiri kuti abwerere m’gulu la nkhosa.”

17 Kodi chinachitika n’chiyani kuti m’baleyu afooke? Iye anati: “Ndinayamba kuganizira kwambiri zinthu za m’dzikoli kuposa zinthu zauzimu. Kenaka ndinasiya kuphunzira Baibulo, kulalikira, ndiponso kusonkhana. Ndiye mapeto ake ndinapezeka kuti ndasiyana ndi mpingo wachikhristu. Koma ndinabwereranso chifukwa choti mkuluyo anasonyeza kuti amandiganizira kwambiri.” M’baleyu anayambanso kuphunzira Baibulo ndipo zinthu zinayambanso kumuyendera bwino. Iye anati: “Ndinaona kuti pamoyo wanga ndinkasowa chikondi ndiponso malangizo amene Yehova ndi gulu lake amapereka.”

18 Kodi m’bale ameneyu analandiridwa bwanji mumpingo? Iye anati: “Zimene zinandichitikira n’zofanana ndi za mwana wolowerera wa m’fanizo la Yesu uja. Nditapita kumisonkhano, ndinakumana ndi mlongo wina amene analipo zaka 30 zapitazo ndipo akutumikirabe Yehova mokhulupirika. Mlongoyu anandiuza kuti: ‘Ndasangalala kwambiri kuti mwabwera, takhala tikukusowani kwambiri.’ Mawu amenewa anandikhudza mtima kwambiri. Apa ndinaona kuti ndafikadi kwathu. Ndikufuna kuthokoza ndi mtima wonse mkuluyo komanso mpingo chifukwa chondiganizira, kundisonyeza chikondi ndiponso kundilezera mtima. Anthu amenewa anandithandiza kwambiri kubwerera m’gulu chifukwa choti amakonda Yehova ndiponso anansi awo.”

Alimbikitseni Kubwerera Mwamsanga

19, 20. Kodi mungalimbikitse bwanji ofooka kuti abwerere mwamsanga m’gulu la nkhosa ndipo mungawathandize bwanji kuzindikira mfundo yakuti zimene Mulungu amafuna kuti tizichita n’zoti tingazikwanitse?

19 Tikukhala m’masiku otsiriza, ndipo mapeto a dongosolo lino la zinthu ayandikira. Motero, limbikitsani anthu ofooka kuti azibwera kumisonkhano. Athandizeni kuzindikira kuti ayenera kuchita zimenezi mwamsanga. Akumbutseni kuti Satana amafuna kuwononga ubwenzi wawo ndi Mulungu powachititsa kuona kuti akasiya kulambira koona, moyo wawo ukhala wofewerapo. Athandizeni kumvetsa mfundo yakuti sangapeze chimwemwe chenicheni popanda kutsatira Yesu mokhulupirika.​—Werengani Mateyo 11:28-30.

20 Kumbutsani ofooka mfundo yakuti zimene Mulungu amafuna kuti tizichita n’zoti tingazikwanitse. Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa, mlongo wake wa Lazaro, Mariya, anam’dzoza Yesuyo mafuta amtengo wapatali. Ophunzira ena anam’dzudzula. Koma Yesu anati: “Mulekeni. . . . Wachita zimene angathe.” (Maliko 14:6-8) Yesu anayamikiranso mayi wamasiye wosauka amene anapereka ndalama yochepa kwambiri kukachisi. Mayiyu anachitanso zimene akanatha. (Luka 21:1-4) Ambirife timakwanitsa kufika kumisonkhano yachikhristu ndi kuchita nawo ntchito yolalikira. Zimenezi zikusonyeza kuti, mothandizidwa ndi Yehova, n’zothekanso kuti ambiri mwa anthu amene panopo ali ofooka azitha kufika kumisonkhano.

21, 22. Kodi anthu amene akubwerera kwa Yehova mungawatsimikizire za chiyani?

21 Anthu ena akachoka m’gulu la nkhosa safuna kubwerera poopa kuti abale sakawalandira bwino. Alimbikitseni powauza kuti mpingo umasangalala kwambiri munthu akabwerera m’gulu la nkhosa, monga mmene anthu anasangalalira mwana wolowerera uja atabwerera. Zimasangalatsa kwambiri anthu akamabwerera mumpingo. Alimbikitseni kuti panopa ayesetse kutsutsa Mdyerekezi ndi kuyandikira kwa Mulungu.​—Yak. 4:7, 8.

22 Anthu amene akubwerera kwa Yehova ayenera kuyembekezera kulandiridwa ndi manja awiri. (Maliro 3:40) Anthu amenewa akabwerera, amasangalala ngati mmene ankasangalalira panthawi imene ankatumikira Mulungu. Palinso madalitso osaneneka amene anthu amene akubwerera mwamsanga m’gulu la nkhosa adzapeze m’tsogolo.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi mungathandize bwanji Mkhristu amene anafooka chifukwa chokhumudwitsidwa?

• Kodi ndi mfundo zotani zimene tingam’thandizire munthu amene anasiya gulu la nkhosa la Mulungu chifukwa chosagwirizana ndi mfundo inayake ya m’Malemba?

• Kodi tingathandize bwanji munthu amene akuzengereza kubwerera mumpingo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Mvetserani mwatcheru Mkhristu wofooka akamakufotokozerani zimene akuvutika nazo mumtima mwake

[Chithunzi patsamba 15]

Kuganizira fanizo la Yesu la mwana wolowerera kungachititse ena kukhudzidwa mtima n’kubwerera m’gulu la nkhosa