Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumafuna Mutakhala Munthu Wotani?

Kodi Mumafuna Mutakhala Munthu Wotani?

Kodi Mumafuna Mutakhala Munthu Wotani?

MKULU wa apolisi m’tauni ina ku Philippines anafunsa mpainiya wina kuti: “Kodi munthu ameneyu munamusintha bwanji.” Wapolisiyo analoza mulu wa mapepala n’kunena kuti: “Kodi mukudziwa kuti mapepala onsewa ndi a milandu imene munthuyu wakhala akupalamula? Pamenepatu mayi mwatithandiza chifukwa mkuluyu ankasowetsa mtendere kwambiri m’tauni yonseyi.” Munthu amene ankamunenayu m’mbuyomo anali chidakwa ndiponso kabwerebwere. Kodi n’chiyani chinam’chititsa kuti asinthe moyo wake choncho? Iyeyu anasintha chifukwa cha uthenga wa m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ouziridwa a Mulungu.

Anthu ambiri agwiritsira ntchito malangizo a mtumwi Paulo akuti: ‘Muvule umunthu wakale umene unkagwirizana ndi khalidwe lanu lakale, ndi kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.’ (Aef. 4:22-24) Zilibe kanthu kuti tiyenera kusintha pang’ono kapena kwambiri, koma mfundo ndi yakuti aliyense amene akufuna kukhala Mkhristu ayenera kuvala umunthu watsopano.

Komabe, kusintha mpaka kufika poyenerera kubatizidwa n’chiyambi chabe. Tikamafika pobatizidwa, timakhala ngati mtengo umene wasemedwa mofanana pang’ono ndi chinthu chinachake. Munthu angathe kuzindikira chimene chikusemedwacho, komabe panthawiyi chimakhala kuti chidakali patali kuti chimalizidwe. Kuti chosemacho chikongole, wosemayo ayenera kutha nthawi yaitali akuchikonzabe mwina ndi mwina. Tikamabatizidwa, timakhala tili ndi makhalidwe otithandiza kuti tikhale mtumiki wa Mulungu. Komabe panthawiyi timakhala titangoyamba kumene kusonyeza umunthu watsopano. Tiyenera kupitirizabe kukonza khalidwe lathu pena ndi pena kuti umunthuwu ufike poonekera bwino.

Paulo ankaona kuti anafunika kusintha zina ndi zina pa moyo wake. Iye anavomereza kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane.” (Aroma 7:21) N’zoonekeratu kuti Paulo ankadziwa khalidwe lake ndiponso ankadziwa khalidwe limene ankafunika kukhala nalo. Nanga bwanji ifeyo? Nafenso tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndine munthu wotani? Nanga ndimafuna nditakhala wotani?’

Kodi Ineyo Ndine Munthu Wotani?

Tikamakonza nyumba yakale yomwe mitengo yake yakudenga yawonongeka, sitimangothamangira kuipenta kunja basi. Kuchita zimenezi popanda kuikonza bwinobwino, kungathe kubweretsa mavuto patsogolo. Choncho tiyeneranso kudziwa kuti kuchita zinthu mwa chiphamaso sikungatithandize. Tiyenera kuganizira kwambiri umunthu wathu wamkati n’kuona zinthu zofunika kusintha. Tikapanda kutero, makhalidwe athu akale aja angathe kuyambanso kuonekera. Motero tonsefe tiyenera kudzifufuza bwino. (2 Akor. 13:5) Tiyenera kuona makhalidwe alionse oipa n’kuyesetsa kusintha. Kuti tithe kuchita zimenezi, Yehova watipatsa thandizo.

Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amapyoza mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheb. 4:12) Uthenga wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo, ungathe kusintha kwambiri moyo wathu. Mophiphiritsa tingati umapyoza kwambiri moyo wathu mpaka kufika m’mafuta amene amapezeka mkati mwenimweni mwa mafupa athu. Umatithandiza kuona maganizo athu ndi zolinga zathu, kuti tidziwe umunthu wathu weniweni wamkati, osati zimene zimangoonekera kunja kapena makhalidwe amene eniakefe timaganiza kuti tili nawo. Pamenepatu tingati Mawu a Mulungu amatithandiza kwambiri kuona mavuto athu.

Tikamakonza nyumba yakale, sitimangochotsa zinthu zowonongeka n’kuika zina. Kudziwa chimene chinachititsa kuti zinthuzo ziwonongeke kumatithandiza kupeza njira yopewera kuti zisadzachitikenso. Ifenso tikadziwa makhalidwe ofunika kusintha pa umunthu wathu, tiyenera kupeza chimene chimachititsa kapena kulimbikitsa makhalidwewo. Zimenezi zingatithandize kwambiri pa zofooka zathu. Pali zinthu zambiri zimene zimakhudza umunthu wathu. Zinthu zimenezi ndi monga kudziwika kwathu, ndalama zimene timapeza, kumene tikukhala, chikhalidwe chathu, makolo athu, anzathu ndiponso zipembedzo zimene takhalamo. Ngakhale mapulogalamu a pa TV ndiponso mafilimu amene timaonera komanso zinthu zina zosangalatsa, zimakhudza umunthu wathu. Kuzindikira zinthu zimene zimatha kuwononga umunthu wathu kumatithandiza kuti tizipewe.

Koma n’kutheka kuti mutakhala pansi n’kuganizira bwinobwino za umunthu wanu, munganene kuti, ‘Kungoti ineyo ndi mmene ndilili basi.’ Maganizo amenewa ndi olakwika. Ponena za anthu ena ku Korinto amene kale anali adama, ogonana ndi amuna anzawo, zidakwa, ndiponso ochita makhalidwe ena otero, Paulo anati: “Ena mwa inu munali otero. Koma mwasambitsidwa . . . ndi mzimu wa Mulungu.” (1 Akor. 6:9-11) Mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova, ifenso tingathe kusintha.

Taganizirani nkhani ya Marcos, * yemwe akukhala ku Philippines. Ponena za kale lake, iye anati: “Makolo anga ankangokhalira kukangana. N’chifukwa chake ineyo ndinalowerera nditafika zaka 19.” Marcos anatchuka chifukwa cha kutchova njuga ndiponso kuba ndi mfuti. Panthawi ina, iyeyo ndi anzake anakonza zolanda ndege, koma chiwembu chimenechi sichinatheke. Atakwatira, Marcos anapitirizabe khalidwe lakeli. Mapeto ake katundu wake yense anathera njuga. Pasanapite nthawi yaitali, Marcos anayamba kukhala limodzi ndi mkazi wake akamaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Poyamba, Marcos sankadziona kuti ndi woyenerera kukhala Mboni. Koma kugwiritsira ntchito zimene ankaphunzira ndiponso kupita kumisonkhano, kunam’thandiza kusintha makhalidwe akewo. Panopo Marcos ndi Mkhristu wobatizidwa ndipo nthawi zonse amachita nawo ntchito yophunzitsa ena kuti nawonso asinthe umunthu wawo.

Kodi Mumafuna Kukhala Munthu Wotani?

Kodi tingafunikire kusintha zinthu zotani kuti tiyambe kuonetsa kwambiri makhalidwe athu achikhristu? Paulo analangiza Akhristu kuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu, mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe; ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana. Musamanamizane wina ndi mnzake. Vulani umunthu wakale pamodzi ndi ntchito zake.” Paulo anapitiriza kunena kuti: “Muvale umunthu watsopano, umene kudzera mwa kudziwa zinthu molondola ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha Iye amene anaulenga.”​—Akol. 3:8-10.

Motero, cholinga chathu chachikulu chizikhala kuvula umunthu wakale n’kuvala watsopano. Kuti tichite zimenezi, kodi ndi makhalidwe otani amene tiyenera kuyesetsa kukhala nawo? Paulo anati: “Valani chifundo chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima. Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso. Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi, pakuti ndicho chomangira umodzi changwiro.” (Akol. 3:12-14) Kuchita khama kuti tikhale ndi makhalidwe amenewa kungachititse kuti ‘Yehova ndi anthu omwe azitikomera mtima.’ (1 Sam. 2:26) Yesu ali padziko lapansi anasonyeza makhalidwe amenewa kuposa munthu wina aliyense. Pophunzira za iye ndi kumutsanzira, nafenso tingathe kukhala anthu “otsanzira Mulungu,” ngati Khristuyo.​—Aef. 5:1, 2.

Njira inanso imene ingatithandize kuona makhalidwe amene tiyenera kusintha ndiyo kuphunzira za a anthu otchulidwa m’Baibulo, n’kuona makhalidwe awo amene tiyenera kutsanzira ndiponso amene tiyenera kupewa. Mwachitsanzo, taganizirani za Yosefe, mwana wa Yakobo. Ngakhale kuti Yosefe anazunzidwa popanda chifukwa, iye sanasiye mtima wake wabwino. (Gen. 45:1-15) Koma Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide, sanali munthu wa khalidwe labwino. Ngakhale kuti anthu ankamutama chifukwa cha kukongola kwake, iye ananamizira kuti ankadera nkhawa kwambiri anthu. Komatu kwenikweni Abisalomu anali munthu wachinyengo ndiponso wachiwembu. (2 Sam. 13:28, 29; 14:25; 15:1-12) Munthu sakhala wabwino chifukwa chonamizira kuchita zabwino kapena chifukwa cha kukongola kwake.

Tingathe Kusintha

Kuti tisinthe umunthu wathu n’kukhala okongola pamaso pa Mulungu, tiyenera kuganizira za umunthu wathu wamkati. (1 Pet. 3:3, 4) Choyamba tiyenera kudziwa makhalidwe ofunika kusinthawo, n’kupeza chimene chimachititsa kapena kulimbikitsa makhalidwewo. Kenako tiyesetse kukhala ndi makhalidwe a Mulungu. Kodi tinganene mosakayika kuti tingathe kusinthadi umunthu wathu ngati titachita khama motero?

Inde, chifukwa Yehova angathe kutithandiza kusintha zinthu zimenezo. Monga Wamasalmo tingapemphere kuti: “Mundilengere mtima woyera, Mulungu; mukonze mzimu wokhazikika mkati mwanga.” (Sal. 51:10) Tingapemphe mzimu woyera wa Mulungu kuti utithandize ndi kutilimbikitsa kuti tikhalebe ofunitsitsa kusintha moyo wathu mogwirizana ndi chifuniro chake. Inde, tingathe kusintha n’kukhala anthu okongola kwambiri pamaso pa Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Si dzina lake lenileni.

[Chithunzi patsamba 4]

Ngati nyumba yawonongeka ndi mvula ya mkuntho, kodi ndi bwino kungoipentapenta kunja basi?

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi panopo umunthu wanu uli ngati wa Khristu?