Kutumikira Mulungu ndi “Mtima Umodzi ndi Maganizo Amodzi”
Kutumikira Mulungu ndi “Mtima Umodzi ndi Maganizo Amodzi”
AYUDA ndiponso anthu amene anatembenukira ku Chiyuda anasonkhana mozungulira atumwi a Yesu Khristu. Apa panali pa Phwando la Pentekosite ndipo alendowa anabwera ku Yerusalemu kuchokera kutali kwambiri. Ena anachokera chakumadzulo, ku Roma ndipo ena anachokera kum’mawa ku Pati. Kenaka khamu la anthuli linayamba kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Komatu ophunzira a Yesu amene anali kulankhula nawo anali Agalileya. Podabwa, ena mwa alendowo anafunsa kuti: “Nanga zikutheka bwanji kuti aliyense wa ife akumva chinenero chimene anabadwa nacho?”—Mac. 2:8.
Mac. 2:41) Ngakhale kuti mpingo unakula mwamsangamsanga, unapitirizabe kukhala wogwirizana. Luka analemba kuti: “Onse amene anakhulupirira anakhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.”—Mac. 4:32.
Ndiyeno mtumwi Petulo anaimirira n’kufotokoza chimene chinachititsa kuti zodabwitsazi zichitike. Nthawi yomweyo anthuwo anakhulupirira uthengawo moti anthu ambirimbiri anabatizidwa. (Anthu ambirimbiri amene anabatizidwa pa Pentekoste mu 33 C.E., anaganiza zoti asafulumire kuchoka ku Yerusalemu kuti aphunzire kaye zinthu zina zokhudza chikhulupiriro chawo chatsopanocho. Komatu popita ku Yerusalemuko iwowa sanakonzekere kuti akakhalako kwa nthawi yaitali ndithu. Motero anasonkhetsa ndalama ndipo Akhristu ena anaganiza zogulitsa zinthu zawo zina n’kupereka ndalamazo kwa atumwi kuti zithandizire osowawo. (Mac. 2:42-47) Apatu anasonyeza mtima wachikondi ndiponso kuwolowa manja.
Akhristu oona akhala akusonyeza mtima umenewu kuyambira kalekale. Panopo mpingo wachikhristu ukupitirizabe kutumikira Yehova ndi “mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” Akhristu ambirimbiri amasonyeza kuwolowa manja popereka nthawi yawo, mphamvu zawo, ndiponso ndalama zawo kuti athandize pa ntchito yolalikira uthenga wabwino ndiponso popititsa patsogolo Ufumu wa Mulungu.—Onani bokosi lakuti “Njira Zimene Ena Amaperekera.”
[Bokosi pamasamba 6, 7]
NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA
ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE
Ambiri amachita bajeti, kapena kuti amaika padera ndalama zoti aziponya m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Ntchito ya Padziko Lonse.”
Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha ndalama zimene mukufuna kupereka ku Accounting Office, Watch Tower Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.
MPHATSO ZINA
Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu zopititsira patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:
Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.
Maakaunti a ku Banki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu a ku banki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.
Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo mu kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.
Malo ndi Nyumba: Mungapereke mphatso monga, malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo panthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.
Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ku boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.
Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapenanso mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.
Accounting Office
Watch Tower Society
P. O. Box 30749
Lilongwe 3
Malawi
Telefoni: 01 762 111