Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mpukutu Wotchedwa “Nyimbo ya Panyanja” Umatithandiza Kudziwa Zinthu Zakale

Mpukutu Wotchedwa “Nyimbo ya Panyanja” Umatithandiza Kudziwa Zinthu Zakale

Mpukutu Wotchedwa “Nyimbo ya Panyanja” Umatithandiza Kudziwa Zinthu Zakale

PA 22 May 2007, ku nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi mumzinda wa Yerusalemu ku Israel, kunachitika chionetsero cha mbali ina ya mpukutu wa Chiheberi womwe unalembedwa mu 600 kapena 700 C.E. Mpukutuwu ndi wa Eksodo 13:19–16:1, ndipo muli nyimbo imene imatchedwa “Nyimbo ya Panyanja.” Iyi ndi nyimbo imene Aisiraeli anaimba posangalala kuti apulumutsidwa mozizwitsa pa Nyanja Yofiira. Kodi n’chifukwa chiyani chionetsero cha mpukutuwu chinali chofunika?

Tingadziwe kufunika kwake ngati titaganizira za nthawi imene mpukutuwu unalembedwa. Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa inalembedwa m’zaka za pakati pa 300 B.C.E ndi 100 C.E. Anthu anatulukira mipukutu imeneyi zaka 60 zapitazo. Mipukutu imeneyi isanatulukiridwe anthu ankangodziwa za mipukutu ya Chiheberi yotchedwa Aleppo imene inalembedwa cha m’ma 930 C.E. Pali mipukutu yochepa chabe yomwe inalembedwa kalekale chonchi imene anthu anaipeza.

Ponena za mpukutu wa “Nyimbo ya Panyanja,” mkulu wa pa nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi mumzinda wa Yerusalemu dzina lake James S. Snyder anati: “Umatithandiza kudziwa zinthu zakale zimene zinachitika mipukutu ya ku Nyanja Yakufa italembedwa . . . koma wa Aleppo usanalembedwe.” Malinga ndi zimene iye analemba, mipukutu yotereyi imatithandiza kudziwa kuti mabuku a m’Baibulo “anasungidwa popanda kusinthamo zina ndi zina.”

Mpukutu umenewu ndi umodzi mwa mipukutu yambiri imene inapezeka kumapeto kwa zaka za m’ma 1800 m’kachisi wa mu mzinda wa Cairo ku Egypt. Komabe munthu wina amene anagula ndi kusunga mipukutu ya Chiheberiyi, sanadziwe kufunika kwa mpukutuwu mpaka pamene anakumana ndi katswiri wina cha m’ma 1970. Ataupeza mpukutuwu anauyeza kuti adziwe nthawi imene unalembedwa, kenako anausunga mpaka nthawi imene unaonetsedwa m’nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ku Israel.

Mkulu wina dzina lake Adolfo Roitman, amene amayang’anira nyumba yosungiramo zinthu zochititsa chidwi ya Shrine of the Book ndi ya Israel Museum ndiponso amasamalira Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa, anafotokoza kufunika kwa mpukutuwu. Iye anati: “Mpukutu wa Nyimbo ya Panyanja umatsimikizira kuti anthu okopera Baibulo anagwira ntchito yawo mokhulupirika. N’zochititsa chidwi kuona kuti mawu a Nyimbo ya Panyanja adakali chimodzimodzi ndi mmene analili m’ma 600 ndi 700 C.E.”

Baibulo ndi Mawu a Mulungu ouziridwa ndipo Yehova amaonetsetsa kuti mawu akewo asungidwa bwino. Nawonso alembi anakopera Malembawa mosamala kwambiri. Motero, Baibulo limene tikuwerenga masiku anoli ndi lodalirika.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Courtesy of Israel Museum, Jerusalem