Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba

Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba

Samalirani Thanzi Lanu M’njira Yogwirizana ndi Malemba

“Uzikonda Yehova Mulungu wako . . . ndi maganizo ako onse, ndi mphamvu zako zonse.”​—MALIKO 12:30.

1. Kodi Mulungu anali ndi cholinga chotani polenga anthu?

POLENGA anthu, Yehova Mulungu analibe cholinga choti anthuwo azidwala ndiponso kufa. Mulungu anaika Adamu ndi Hava m’munda wa Edene, kapena kuti m’paradaiso wosangalatsa, “kuti aulime nauyang’anire,” osati kwa zaka 70 kapena 80 zokha, koma kosatha. (Gen. 2:8, 15; Sal. 90:10) Iwowa sakanadzadwala, kukalamba kapenanso kufa akanati apitirizebe kukhala okhulupirika kwa Yehova n’kumagonjera ulamuliro wake chifukwa chomukonda.

2, 3. (a) Kodi m’buku la Mlaliki, zochitika pa ukalamba zimayerekezedwa ndi chiyani? (b) Kodi ndani amachititsa imfa yomwe inachokera kwa Adamu, ndipo kodi zimenezi zidzathetsedwa motani?

2 M’chaputala 12 cha buku la Mlaliki, Baibulo limalongosola momveka bwino za mavuto amene anthu opanda ungwirofe timakumana nawo pa “masiku oipa” aukalamba. (Werengani Mlaliki 12:1-7.) Limayerekezera imvi ndi maluwa a mtengo wa “mchiwu.” Miyendo ndi “amuna olimba” amene tsopano amayenda mowerama ndiponso mwapendapenda. Maso amene akulephera kuona limawayerekezera ndi akazi amene amapita pa windo pofuna kuwala koma m’malo mwake amangoona mdima wokhawokha. Kutha mano m’kamwa limakuyerekezera ndi azimayi ‘opera amene aleka kupera chifukwa choti atsalapo ochepa.’

3 N’zoonekeratu kuti sichinali cholinga cha Mulungu kuti anthu aziyamba kufooka miyendo, kusaona bwino, ndiponso kutha mano m’kamwa. Ndiponsotu imfa yomwe inachokera kwa Adamu ndi imodzi mwa “ntchito za Mdyerekezi” zimene Mwana wa Mulungu ‘adzaziwononge’ pogwiritsira ntchito Ufumu wa Mesiya. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mwana wa Mulungu anaonekera, kuti awononge ntchito za Mdyerekezi.”​—1 Yohane 3:8.

Sikulakwa Kuganizira Moyenerera za Thanzi Lathu

4. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova amaganizira moyenerera za thanzi lawo, koma kodi ndi mfundo iti imene sayenera kuiwala?

4 Pakali pano, atumiki ena a Yehova amadwala ndiponso kukalamba monga momwe anthu onse opanda ungwiro amachitira. Motero, mwachibadwa timada nkhawa poganizira thanzi lathu. Ndipotu uku sikulakwa ayi chifukwa timafuna kutumikira Yehova ‘ndi mphamvu zathu zonse.’ (Maliko 12:30) Komabe, ngakhale kuti timafuna thanzi labwino, tisamaganize kuti pali zinazake zimene tingachite kuti tisiyiretu kudwala kapena kukalamba.

5. Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene atumiki okhulupirika a Yehova anachita atadwala?

5 Atumiki ambiri okhulupirika a Yehova anavutika ndi matenda osiyanasiyana. Mmodzi wa iwo anali Epafurodito. (Afil. 2:25-27) Panalinso Timoteyo, mnzake wokhulupirika wa Paulo, yemwe ankadwaladwala m’mimba. Chifukwa cha vutoli Paulo anamuuza kuti azimwa “vinyo pang’ono.” (1 Tim. 5:23) Nayenso Paulo anali ndi vuto limene analitcha kuti “munga m’thupi.” N’kutheka kuti linali vuto la maso kapena vuto lina limene linali losachiritsika panthawiyo. (2 Akor. 12:7; Agal. 4:15; 6:11) Paulo anapempha Yehova mochokera pansi pamtima kuti amuchotsere ‘mungawo m’thupi mwake.’ (Werengani 2 Akorinto 12:8-10.) Mulungu sanachite chozizwitsa n’kumuchotsera Paulo “munga m’thupi.” Koma anangomulimbikitsa kuti apirire. Motero mphamvu za Yehova zinaonekera pa kufooka kwa Paulo. Kodi tingaphunzirepo kanthu pa nkhaniyi?

Pewani Kumangoganizira za Thanzi Lanu Nthawi Zonse

6, 7. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kumangoganizira za thanzi lathu nthawi zonse?

6 Monga mukudziwa, Mboni za Yehova zimavomera kulandira chithandizo chamankhwala chosiyanasiyana. Nthawi zambiri magazini ya Galamukani! imakhala ndi nkhani zokhudza thanzi lathu, ngakhale kuti siilangiza odwala za mankhwala kapena chithandizo chimene ayenera kulandira. Komabe timayamikira kwambiri achipatala akatithandiza mmene tikufunira. Inde, tikudziwa kuti pakali pano n’zosatheka kukhala ndi thanzi langwiro, motero n’chinthu chanzeru kupewa kumangoganizira za thanzi lathu nthawi zonse. Pankhaniyi, tizisiyana ndi anthu “opanda chiyembekezo,” omwe amaganiza kuti moyo ndi wokhawu basi, moti amalolera kulandira chithandizo chilichonse pofuna kuchiza matenda awo. (Aef. 2:2, 12) Koma ife sitilola ngakhale pang’ono kukhumudwitsa Yehova chifukwa chongofuna kupulumutsa moyo wathu wa panowu. Sitilola kuchita zimenezi chifukwa sitikayika ngakhale pang’ono kuti tikapitiriza kukhala okhulupirika kwa Mulungu, ‘tidzagwira zolimba moyo weniweniwo,’ womwe ndi moyo wosatha m’dongosolo latsopano limene iye analonjeza.​—1 Tim. 6:12, 19; 2 Pet. 3:13.

7 Palinso chifukwa china chimene tiyenera kupewera kuganizira za thanzi lathu monyanyira. Chifukwa chake n’chakuti kuchita zimenezi kungapangitse munthu kumangoganizira za iyeyo basi. Paulo anachenjeza Afilipi kuti apewe mzimu umenewu powauza kuti: “Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.” (Afil. 2:4) Inde, kudzisamalira n’kofunika, koma ndi bwino kupewa kumangoganizira za thanzi lathu nthawi zonse. Tingapewe zimenezi posonyeza chidwi abale athu ndiponso anthu amene timawauza “uthenga wabwino uwu wa Ufumu.”​—Mat. 24:14.

8. Kodi tikamangoganizira za thanzi lathu nthawi zonse tingayambe kuchita zotani?

8 Mkhristu angathe kumaganizira kwambiri za thanzi lake mpaka kufika ponyalanyaza zinthu zokhudza Ufumu. Kuganizira za thanzi monyanyira kungatipatsenso mtima wokakamiza ena kutsatira maganizo athu pa nkhani za kufunika kwa zakudya zinazake kapena mankhwala enaake. Pankhani imeneyi, taganizirani mfundo imene Paulo ananena m’mawu ake akuti: “Mutsimikizire kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, kotero kuti mukhale opanda cholakwa ndi osakhumudwitsa ena, kufikira tsiku la Khristu.”​—Afil. 1:10.

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

9. Tchulani chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zomwe sitiyenera kuzinyalanyaza, ndipo n’chifukwa chiyani sitiyenera kutero?

9 Tikadziwa kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti, timachita khama pantchito yochiza anthu mwauzimu. Timachita ntchito imeneyi polalikira ndi kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Ntchito yosangalatsa imeneyi imatipindulitsa ifeyo komanso anthu amene timawaphunzitsawo. (Miy. 17:22; 1 Tim. 4:15, 16) Nthawi zina m’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumakhala nkhani za abale, ndi alongo amene ali ndi matenda aakulu. Nkhanizi zimafotokoza zimene abale ndi alongowo amachita nthawi zina kuti apirire kapena aiwaleko mavuto awo n’kumathandiza anzawo kudziwa Yehova ndi malonjezo ake osangalatsa. *

10. N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha chithandizo chamankhwala?

10 Mkhristu aliyense wamkulu akadwala ayenera “kunyamula katundu wakewake” wa udindo wosankha chithandizo cha mankhwala. (Agal. 6:5) Komabe tisaiwale kuti nkhaniyi imam’khudzanso Yehova. ‘Timasala magazi’ chifukwa cholemekeza mfundo za m’Baibulo, moteronso tiyenera kupewa chithandizo cha mankhwala chimene chingativulaze mwauzimu kapena kutiwonongera ubwenzi wathu ndi Yehova. (Mac. 15:20) Njira zina zodziwira matenda amene munthu akudwala ndiponso zochizira matendawo n’zokhudzana kwambiri ndi kukhulupirira mizimu. Yehova sanasangalale ndi Aisiraeli opanduka amene ankachita “mphulupulu,” kapena kuti zinthu zokhulupirira mizimu, ndipo anawauza kuti: “Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi sabata, kumema masonkhano, sindingalole mphulupulu ndi masonkhano.” (Yes. 1:13) Tikadwala m’pamene makamaka tiyenera kupewa kwambiri kuchita zinthu zolepheretsa mapemphero athu kufika kwa Mulungu ndiponso zinthu zowononga ubwenzi wathu ndi iye.​—Maliro 3:44.

M’pofunika “Kukhala a Maganizo Abwino”

11, 12. Kodi “kukhala a maganizo abwino” kungatithandize bwanji tikamasankha chithandizo chamankhwala?

11 Tikadwala, sitiyembekezera kuti Yehova atichiritsa mozizwitsa koma timapemphera kuti atipatse nzeru zosankha bwino chithandizo. Komabe, posankha chithandizocho tizigwiritsira ntchito mfundo za m’Malemba ndiponso tiziganiza bwino. Matendawo akakhala aakulu, ngati n’kotheka ndi bwino kuonana ndi madokotala angapo odziwa bwino matendawo. Zimenezi n’zogwirizana ndi lemba la Miyambo 15:22, lomwe limati: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake “kukhala a maganizo abwino ndi a chilungamo ndi odzipereka kwa Mulungu m’dongosolo lino la zinthu.”​—Tito 2:12.

12 Moyo wa anthu ambiri masiku ano uli ngati moyo wa mayi wina m’nthawi ya Yesu. Pa Maliko 5:25, 26 timawerenga kuti: “Panali mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12, ndipo ochiritsa ambiri anam’chititsa kumva zopweteka zambiri, ndipo anawononga chuma chake chonse koma osapindula kanthu, m’malo mwake matendawo anangokulirakulira.” Yesu anam’chiritsa mayiyo, ndipo anachita zimenezo mwachifundo. (Maliko 5:27-34) Chifukwa chothedwa nzeru ndi matenda awo, Akhristu ena asankha njira zosemphana ndi mfundo za kupembedza koyera pofuna kudziwa kapena kuchiza matenda omwe akudwala.

13, 14. (a) Kodi Satana angayese bwanji kukhulupirika kwathu tikamafuna kusankha chithandizo chamankhwala? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kupeweratu chilichonse chokhudzana ndi zamizimu?

13 Satana amachita chilichonse chimene angathe kuti atisokoneze pa kupembedza koona. Iye amafooketsa ena pogwiritsa ntchito chiwerewere ndiponso kukonda chuma, koma amayesanso kuwononga chikhulupiriro cha ena powakopa kuti aziyesa kuchiza matenda awo pogwiritsira ntchito njira zokayikitsa zomwe zingakhale zokhudzana ndi zamatsenga ndiponso zamizimu. Timapemphera kuti Yehova atilanditse kwa “woipayo” ndi kuti atilanditse ku “mkhalidwe wa kusamvera malamulo kwa mtundu uliwonse.” Motero tisamasewere m’manja mwa Satana pochitira dala zinthu zokhudzana kwambiri ndi zamizimu ndiponso zamatsenga.​—Mat. 6:13; Tito 2:14.

14 Yehova analetsa Aisiraeli kuwombeza maula kapena kuchita zamatsenga. (Deut. 18:10-12) Ponena za “ntchito za thupi,” Paulo anatchulaponso “kukhulupirira mizimu.” (Agal. 5:19, 20) Komanso, “ochita za mizimu” sadzalowa m’dongosolo latsopano la Yehova. (Chiv. 21:8) Motero, n’zoonekeratu kuti Yehova amadana ndi chilichonse chokhudzana ndi kukhulupirira mizimu.

“Kulolera Kwanu Kudziwike”

15, 16. N’chifukwa chiyani timafunikira nzeru posankha chithandizo chamankhwala, ndipo kodi bungwe lolamulira linapereka malangizo otani m’nthawi ya atumwi?

15 Poganizira zimene takambiranazi, ngati mukukayikira njira inayake yodziwira kapena yochizira matenda anu, ndi bwino kukana njira imeneyo. Komabe, sikuti munthu ukapanda kumvetsa mmene njira inayake yothandizira odwala imagwirira ntchito, uzingoti basi njira imeneyo n’njokhudza kukhulupirira mizimu. Timafunika nzeru zochokera kwa Mulungu kuti tithe kuona nkhani ya chithandizo chamankhwala m’njira yogwirizana ndi Malemba. Komanso timafunika kuiganizira bwinobwino nkhaniyo. M’chaputala 3 cha buku la Miyambo, timapeza mawu olimbikitsa akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzawongola mayendedwe ako. . . . Sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira; ndipo mtima wako udzatengapo moyo, ndi khosi lako chisomo.”​—Miy. 3:5, 6, 21, 22.

16 Motero, ngakhale kuti timayesetsa kukhala athanzi, tiyenera kusamala kuti tisachite zinthu zotidanitsa ndi Mulungu chifukwa chongofuna kuchira matenda amene tikudwala kapena kuthana ndi mavuto enaake aukalamba. Pankhani ya matenda, monganso nkhani zina, tiziyesetsa kuti “kulolera kwathu kudziwike” pochita zinthu motsatira mfundo za m’Baibulo. (Afil. 4:5) M’kalata yofunika kwambiri imene bungwe lolamulira linalembera Akhristu m’nthawi ya atumwi, bungweli linawalangiza kuti apewe kupembedza mafano, magazi ndi chigololo. M’malangizowo anawatsimikiziranso kuti: “Ngati mupewa zinthu zimenezi mosamalitsa, mudzachita bwino.” (Mac. 15:28, 29) M’njira yotani?

Kusamalira Thanzi Mogwirizana ndi Chiyembekezo Choti Tidzakhala Angwiro

17. Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kwatithandiza m’njira zotani?

17 Ndi bwino kuti aliyense azidzifunsa kuti: ‘Kodi ndikuzindikira zabwino zonse zimene ndapeza chifukwa chotsatira mosamala mfundo za m’Baibulo zoletsa magazi ndi chigololo?’ Taganiziraninso madalitso amene talandira chifukwa chochita khama poyesetsa “kuchotsa chilichonse choipitsa cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akor. 7:1) Potsatira kwambiri mfundo za m’Baibulo zokhudza ukhondo, tapewa matenda ambiri. Ndife athanzi ndiponso olimba mwauzimu chifukwa timapewa kusuta fodya ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kudya ndi kumwa modziletsa kumatithandizanso kwambiri. (Werengani Miyambo 23:20; Tito 2:2, 3.) Inde, pali zinthu zina zomwe zatithandizanso kukhala athanzi, monga kupuma mokwanira ndiponso kuchita zinthu zolimbitsa thupi. Koma chimene tapindula nacho kwambiri mwakuthupi komanso mwauzimu ndicho kutsatira malangizo a m’Malemba.

18. Kodi tiziganizira kwambiri za chiyani, ndipo ndi ulosi uti wonena za thanzi umene tiyenera kuuyembekezera?

18 Koposa zonse, tiyenera kusamalira kwambiri thanzi lathu lauzimu ndi kulimbitsa ubwenzi wathu wamtengo wapatali ndi Atate wathu wakumwamba, yemwe ali Kasupe wa “moyo uno ndi umene ukubwerawo” m’dziko latsopano limene walonjeza. (1 Tim. 4:8; Sal. 36:9) M’dongosolo latsopano la Mulungu, anthu adzakhululukidwa machimo kudzera mu nsembe ya dipo ya Yesu motero adzachiritsidwa matenda onse auzimu ndiponso akuthupi. Khristu Yesu, yemwe ndi Mwanawankhosa wa Mulungu, adzatisonyeza “akasupe a madzi a moyo,” ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse pamaso pathu. (Chiv. 7:14-17; 22:1, 2) Panthawiyi, ulosi wodabwitsa wa pa Yesaya 33:24 udzakwaniritsidwa. Ulosiwu umati: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”​—Yes. 33:24.

19. Ngakhale kuti tiyenera kuyesetsa ndithu kusamalira thanzi lathu, kodi sitiyenera kukayika za chiyani?

19 Sitikayikira ngakhale pang’ono kuti chipulumutso chathu chayandikira. Tikuyembekeza mwachidwi tsiku limene Yehova adzachotse matenda ndi imfa. Pakali pano, sitikayikanso kuti Atate wathu wachikondiyu atithandiza kupirira zopweteka zosiyanasiyana zimene matenda amabweretsa. Tikudziwa zimenezi chifukwa choti iye ‘amasamala za ife.’ (1 Pet. 5:7) Motero tiyeni nthawi zonse tizisamala thanzi lathu, mogwirizana ndi malangizo omveka bwino amene ali m’Mawu a Mulungu ouziridwa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 9 Mungapeze ndandanda ya nkhani zoterezi pa bokosi la patsamba 17 mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2003.

Tibwereze

• Kodi ndani anayambitsa matenda ndipo ndani adzatichotsere mavuto obwera chifukwa cha uchimo?

• Ngakhale kuti tonsefe timaganizira za thanzi lathu kodi tiyenera kupewa chiyani?

• N’chifukwa chiyani zimene tasankha pa chithandizo cha mankhwala zimam’khudza Yehova?

• Pankhani ya thanzi lathu, kodi tingapindule bwanji potsatira mfundo za m’Baibulo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Mulungu sanalenge anthu kuti azidwala ndiponso kukalamba

[Chithunzi patsamba 25]

Ngakhale kuti atumiki a Yehova amadwala, iwo amasangalala pochita utumiki