Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Umphumphu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Umphumphu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusunga Umphumphu?

“Mundiweruze, Yehova, monga mwa . . . ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga uli mwa ine.”​—SAL. 7:8.

1, 2. Kodi ndi zochitika zina ziti zimene kawirikawiri zimayesa umphumphu wa Mkhristu?

TAGANIZIRANI zochitika zitatu izi: Mnyamata wina akunyozedwa ndi anzake a kusukulu. Anzakewo, akumuyamba dala kuti awatukwane kapena kuti amenyane nawo. Kodi iye adzachitadi zimenezo kapena adzadziletsa n’kungochokapo? Mwamuna wina ali yekha m’nyumba mwake ndipo akufufuza zinthu zina pa Intaneti. Kenako pakompyutapo pakuoneka mawu ena oitanira zithunzi zolaula. Kodi iye adzakopeka n’kuona zimenezo, kapena adzayesetsa kupewa kuti asazione? Mlongo wina akucheza ndi alongo anzake, kenako machezawo akusintha ndipo anzakewo akuyamba kudya miseche mlongo wina wa mumpingo. Kodi iye adzayankhira misecheyo kapena adzasintha nkhaniyo n’kuyambitsa ina?

2 Zochitikazi n’zosiyana koma zikufanana chinthu chimodzi. Pazochitika zonsezi Mkhristu aliyense akuyesedwa pankhani yosunga umphumphu. Kodi mumaganizira za umphumphu wanu mukakumana ndi vuto linalake kapena posankha zochita pamoyo wanu? Tsiku lililonse anthu amaganizira za maonekedwe awo, thanzi lawo, zochita za anzawo, za munthu amene amam’konda, komanso mavuto ena pamoyo wawo. Anthufe timatanganidwa kwambiri ndi zinthu zimenezi. Koma kodi ndi chiyani chimene Yehova amafuna akamasanthula mitima yathu? (Sal. 139:23, 24) Iye amafuna umphumphu wathu.

3. Kodi Yehova watipatsa mwayi wotani ndipo tikambirana zotani m’nkhani ino?

3 Yehova, yemwe amapereka “mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro,” wapatsa munthu aliyense mphatso zosiyanasiyana. (Yak. 1:17) Iye watipatsa mphatso monga thupi, nzeru, thanzi lomwe tili nalo komanso luso losiyanasiyana. (1 Akor. 4:7) Koma Yehova sakakamiza munthu aliyense kusunga umphumphu. Iye watipatsa mwayi wosankha tokha kukulitsa khalidwe limeneli. (Deut. 30:19) Choncho m’pofunika kuti tikambirane tanthauzo la umphumphu. Tikambirananso zifukwa zitatu zosonyeza kuti khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri.

Kodi Umphumphu N’chiyani?

4. Kodi mawu akuti umphumphu amatanthauza chiyani, nanga tikuphunzira chiyani pa lamulo la Yehova lokhudza nyama zoperekedwa nsembe?

4 Anthu ambiri samvetsa tanthauzo la mawu akuti umphumphu. Mwachitsanzo, ena amaganiza kuti munthu amene amachita zinthu moona mtima ndiye kuti amasunga umphumphu. Koma ngakhale kuti khalidwe la kuona mtima ndi lofunika, palokha si umphumphu. M’Baibulo mawu oti umphumphu amatanthauza kukhala ndi makhalidwe abwino mwachikwanekwane. M’Chiheberi mawu amene amatanthauza “umphumphu” amanena za chinthu chabwino, chathunthu kapena chopanda chilema. Ndipo ena mwa mawu amenewa anagwiritsidwa ntchito pofotokoza za nsembe zoperekedwa kwa Yehova. Nyama yoti iperekedwe nsembe, inkakhala yovomerezeka kwa Yehova pokhapokha ngati ili yabwino komanso yopanda chilema. (Werengani Levitiko 22:19, 20.) Yehova anadzudzula mwamphamvu anthu amene ankanyalanyaza mwadala malangizo ake n’kumapereka nsembe ya nyama zopunduka, zodwala ndi zakhungu.​—Mal. 1:6-8.

5, 6. (a) Perekani zitsanzo zosonyeza kuti anthufe timafunitsitsa zinthu zathunthu. (b) Kodi anthu amafunika kukhala angwiro kuti asunge umphumphu? Fotokozani.

5 Si zachilendo kufuna kupeza chinthu chomwe ndi chathunthu. Tiyerekeze kuti munthu wina akufufuza buku linalake ndipo walipeza bukulo pa shelefu, koma ndi lothothoka masamba ena ofunika kwambiri. Iye angakhumudwe kwambiri ndipo akhoza kungolibwezera pa shelefupo. Tiyerekezenso kuti mayi wina akufuna kugula mazira pamsika. Kodi iye angasankhe mazira otani? N’zosachita kufunsa kuti angasankhe osasweka. Mofananamo, Yehova amafuna anthu amene amam’tumikira kwathunthu kapena kuti ndi mtima wonse.​—2 Mbiri 16:9.

6 Mwina mungafunse kuti, kodi munthu amafunika kukhala wangwiro kuti asunge umphumphu? Chifukwa choti tonsefe ndi opanda ungwiro ndipo timachimwa, tingadziyerekezere ndi buku lothothoka masamba ena kapena dzira losweka. Kodi nthawi zina inuyo mumadziona choncho? Ngati mumatero, upezeni mtima chifukwa Yehova satiyembekezera kuti tizichita zinthu mwangwiro. Zimene amayembekezera ndi zoti tingakwanitse kuchita. * (Sal. 103:14; Yak. 3:2) Komabe amafuna kuti tisunge umphumphu. Ndiye kodi ungwiro ndi wosiyana ndi umphumphu? Inde. Kuti timvetse zimenezi taganizirani chitsanzo ichi: Mnyamata wina amakonda kwambiri mtsikana amene akufuna kudzakwatirana naye. Sichingakhale chinthu chanzeru kuganiza kuti mtsikanayo ayenera kukhala wangwiro. Komabe mnyamatayo angachite bwino kutsimikizira kuti mtsikanayo amam’konda iye yekha ndi mtima wonse. N’chimodzimodzi ndi Yehova. Iye ndi “Mulungu wansanje.” (Eks. 20:5) Ngakhale kuti satiyembekezera kuti tichite zinthu mwangwiro, iye amafuna kuti tizim’konda ndi mtima wonse ndiponso tizilambira iye yekha basi.

7, 8. (a) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pankhani ya kusunga umphumphu? (b) Kodi Malemba amatanthauza chiyani akamanena za umphumphu?

7 Taganizirani yankho limene Yesu anapereka atafunsidwa za lamulo loyamba pa onse. (Werengani Maliko 12:28-30.) Yesu sanangotchula lamulolo koma analitsatira. Iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhani yokonda Yehova ndi maganizo, mtima, moyo ndi mphamvu zake zonse. Iye anasonyeza kuti umphumphu umaonekera m’zinthu zabwino zimene munthu amachita, ali ndi zolinga zabwino osati kungolankhula chabe. Motero kuti tisunge umphumphu tiyenera kutsatira mapazi a Yesu.​—1 Pet. 2:21.

8 Apatu tsopano tadziwa zimene Malemba amatanthauza akamanena za umphumphu. Amatanthauza kudzipereka ndi mtima wonse kwa Yehova Mulungu wakumwamba komanso ku zolinga zake. Motero kuti tisunge umphumphu, cholinga chathu chachikulu chiyenera kukhala kukondweretsa Yehova Mulungu tsiku lililonse. Zinthu zimene timaziika patsogolo m’moyo wathu ziyenera kusonyeza kuti timagwirizana ndi zolinga za Yehova. Tiyeni tikambirane zifukwa zitatu zosonyeza kuti zimenezi ndi zofunika kwambiri.

1. Umphumphu Wathu Umasonyeza kuti Timavomereza Ulamuliro wa Yehova

9. Kodi umphumphu wathu umakhudza bwanji nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse?

9 Ulamuliro wa Yehova ndi woyenera, wamuyaya, wachilengedwe chonse ndiponso sudalira umphumphu wa zolengedwa zake. Ulamuliro wake sungasinthe ngakhale zolengedwa zina zitalankhula kapena kuchita zotani. Komatu ulamuliro wa Mulungu watsutsidwa kumwamba ndi padziko lapansi. Motero pafunika kutsimikizira kuti iye amalamulira zolengedwa zonse moyenera, mwachilungamo komanso mwachikondi. Monga Mboni za Yehova timasangalala kukambirana ndi anthu achidwi nkhani zokhudza ulamuliro wa Mulungu wachilengedwe chonse. Koma kodi zochita zathu zingasonyeze bwanji kuti tili ku mbali ya Yehova pankhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse? Kodi timasonyeza bwanji kuti timasankha Yehova monga wolamulira wathu? Tingachite zimenezi posunga umphumphu.

10. Tchulani mawu achipongwe amene Satana amanena okhudza umphumphu wa anthu, ndipo kodi inuyo mudzatani ndi zimene Satana akukunenerani?

10 Taganizirani mmene nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse imakhudzira umphumphu wanu. Satana amanena kuti palibe munthu amene angamvere ulamuliro wa Mulungu, ndipo palibe amene angatumikire Yehova ali ndi zolinga zabwino. Mdyerekezi anauza Yehova pamaso pa angelo ambirimbiri kuti: “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Onani kuti m’lembali Satana sananene za Yobu yekha, koma anati munthu kutanthauza aliyense. N’chifukwa chake Baibulo limati Satana ndi “woneneza abale athu.” (Chiv. 12:10) Iye amatonza Yehova kuti Akhristu onse kuphatikizapo inuyo sangakhale okhulupirika. Satana amati mungasiye kumvera Yehova pofuna kupulumutsa moyo wanu. Kodi inu mumamva bwanji ndi mawu achipongwe amenewa omwe Satana amakunenerani? Kodi simungakonde kupeza njira yomuyankhira Satana ku bodza limeneli? Ngati musunga umphumphu mudzasonyeza kuti Satana ndi wabodza.

11, 12. (a) Tchulani zitsanzo zosonyeza kuti zosankha zathu za tsiku ndi tsiku zimakhudza umphumphu wathu. (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kusunga umphumphu ndi mwayi waukulu?

11 Nkhani yosunga umphumphu ndi yofunika kwambiri pa zimene timasankha ndi kuchita tsiku lililonse. Taganiziraninso zochitika zitatu zimene tazitchula poyamba zija. Kodi anthuwa akanatani kuti asunge umphumphu? Mnyamata amene akunyozedwa ndi anzake angafune kubwezera, koma akhoza kungochokapo chifukwa chokumbukira malangizo akuti: “Musabwezere choipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu; pakuti Malemba amati: ‘Kubwezera ndi kwanga; ndidzawabwezera ndine, atero Yehova.’” (Aroma 12:19) Mwamuna amene akufufuza zinthu pa Intaneti angayesedwe kuti aonere zinthu zolaula koma kenako akukumbukira mfundo ya m’mawu a Yobu akuti: “Ndinapangana ndi maso anga, potero ndipenyerenji namwali?” (Yobu 31:1) Iyenso sangalole maso ake kuona zinthu zoipazo chifukwa zili ngati poizoni. Mlongo amene akucheza ndi anzake uja, ataona kuti ayamba kukamba zamiseche, iye sakuyankhira chifukwa chokumbukira malangizo akuti: “Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.” (Aroma 15:2) Iye angaone kuti nkhani zimenezo si zolimbikitsa. Akuona kuti zimenezo zingaipitse mbiri ya mlongo wonenedwayo komanso zingakhumudwitse Atate wake wakumwamba. Motero, angadziletse ndipo angasinthe nkhaniyo n’kuyambitsa ina.

12 Pa zochitika zonsezi Mkhristu akusankha zinthu zimene zikusonyeza kuti iye amati: ‘Yehova ndiye amalamulira moyo wanga. Choncho ndiyesetsa kuchita zinthu zoti zimusangalatse.’ Kodi inunso mumakhala ndi maganizo amenewa posankha zochita? Ngati mumatero ndiye kuti mumatsatira mawu olimbikitsa amene ali pa Miyambo 27:11 akuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” Tili ndi mwayi waukulu wokondweretsa mtima wa Mulungu. Motero tiyeni tiyesetse kuchita zonse zimene tingathe kuti tisunge umphumphu.

2. Yehova Amaweruza Anthu Mogwirizana ndi Umphumphu Wawo

13. Kodi mawu a Yobu ndi Davide amasonyeza bwanji kuti Yehova amatiweruza mogwirizana ndi kuti tikusunga umphumphu kapena ayi?

13 Monga taonera, umphumphu umatithandiza kusonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova. Motero Mulungu angatiweruze mogwirizana ndi kuti tikusunga umphumphu kapena ayi. Yobu ankaidziwa bwino mfundo imeneyi. (Werengani Yobu 31:6.) Iye ankadziwa kuti Mulungu amagwiritsa ntchito mfundo zake zolungama ngati ‘muyeso wabwino,’ pofuna kudziwa umphumphu wathu. Davide nayenso ananena kuti: “Yehova aweruza anthu mlandu: Mundiweruze, Yehova, monga mwa chilungamo changa, ndi ungwiro [“umphumphu,” NW] wanga uli mwa ine . . . Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.” (Sal. 7:8, 9) Timadziwa kuti Mulungu angathe kuona umunthu wathu wamkati, umene ndi “mitima ndi impso” zophiphiritsira. Koma ndi bwino kudziwanso zimene amayang’ana mumtima mwathumu. Monga ananenera Davide, Yehova amatiweruza mogwirizana ndi kuti tikusunga umphumphu kapena ayi.

14. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti sitingasunge umphumphu chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro?

14 Taganizirani kuti Yehova Mulungu akusanthula mitima ya anthu mabiliyoni ambiri masiku ano. (1 Mbiri 28:9) Kodi ndi kangati pamene amapeza Mkhristu yemwe akusunga umphumphu? Si kawirikawiri. Komabe tisaganize kuti ndife olephera kwambiri moti sitingasunge umphumphu. M’malo mwake tiyenera kukhala ndi maganizo amene Davide ndi Yobu anali nawo akuti, Yehova amaona kuti tikusunga umphumphu ngakhale kuti ndife opanda ungwiro. Kumbukirani kuti kukhala wangwiro si kumene kungatichititse kuti tisunge umphumphu. Pa anthu atatu angwiro amene anakhalapo padzikoli, awiri omwe ndi Adamu ndi Hava, sanasunge umphumphu. Koma anthu mamiliyoni ambiri opanda ungwiro akhala akusunga umphumphu. Motero nanunso mungathe kusunga umphumphu.

3. Kusunga Umphumphu N’kofunika Kwambiri pa Chiyembekezo Chathu

15. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti kusunga umphumphu n’kofunika kwambiri pa chiyembekezo chathu?

15 Popeza Yehova amatiweruza mogwirizana ndi umphumphu wathu, khalidwe limeneli ndi lofunika kwambiri pa chiyembekezo chathu. Davide ankaidziwa bwino mfundo imeneyi. (Werengani Salmo 41:12.) Iye anali ndi chiyembekezo chakuti Mulungu adzamusamalira kwamuyaya. Mofanana ndi Akhristu oona masiku ano, Davide anali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha. Panthawi yonse yamoyo wake iye ankatumikira Yehova Mulungu ndipo anapitirizabe kumuyandikira. Davide ankadziwa kuti ayenera kupitiriza kusunga umphumphu kuti chiyembekezo chake chikwaniritsidwe. Nafenso masiku ano, Yehova amatichirikiza, kutiphunzitsa, kutitsogolera komanso kutidalitsa tikamasunga umphumphu.

16, 17. (a) N’chifukwa chiyani nthawi zonse tiyenera kukhala otsimikiza mtima kusunga umphumphu? (b) Kodi tikambirana mafunso ati m’nkhani yotsatira?

16 Chiyembekezo chimatithandiza kuti tizikhala osangalala. Chimatipatsa chimwemwe chomwe chimatithandiza kupirira mavuto, komanso chimateteza maganizo athu. Tisaiwale kuti Baibulo limayerekezera chiyembekezo ndi chisoti. (1 Ates. 5:8) Mofanana ndi chisoti chimene chimateteza mutu wa msilikali pankhondo, chiyembekezo chimateteza maganizo athu kuti tisamadzione ngati anthu osanunkha kanthu. Satana ndi amene amalimbikitsa maganizo amenewa m’dziko limene likupitali. Popanda chiyembekezo moyo wathu umakhala wopanda tanthauzo. Tiyenera kudzifufuza moona mtima kuti tidziwe ngati timasungadi umphumphu komanso ngati tili ndi chiyembekezo. Tisaiwale kuti tikamasunga umphumphu timasonyeza kuti tili ku mbali ya ulamuliro wa Yehova ndiponso timateteza chiyembekezo chathu chamtengo wapatali. Ndiyetu tiyeni tipitirize kusunga umphumphu nthawi zonse.

17 Popeza umphumphu ndi wofunika kwambiri, ndi bwino kuti tikambirane mafunso awa: Kodi tingatani kuti tikhale anthu osunga umphumphu? Nanga tingatani kuti tisasiye kusunga umphumphu? Kodi munthu angatani ngati panthawi ina walephera kusunga umphumphu? Nkhani yotsatira iyankha mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Yesu ananena kuti: “Chifukwa chake khalani angwiro, monga Atate wanu wa kumwamba ali wangwiro.” (Mat. 5:48) Iye ankadziwa kuti ngakhale anthu opanda ungwiro angathe kuchita zinthu zabwino. Tingathe kusangalatsa Mulungu pomvera lamulo loti tizikonda anzathu ndi mtima wonse. Yehova ndi amene ali ndi ungwiro wosayerekezeka. Malemba akamanena za “umphumphu” wake amatanthauza kuti iye ndi wangwiro.​—Sal. 18:30.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi umphumphu n’chiyani?

• Kodi umphumphu wathu umakhudza bwanji nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse?

• Kodi kusunga umphumphu kumagwirizana bwanji ndi chiyembekezo chathu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 5]

Tsiku lililonse timakumana ndi zinthu zimene zingayese umphumphu wathu