Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndaona Mboni za Yehova Zikuwonjezereka ku Korea

Ndaona Mboni za Yehova Zikuwonjezereka ku Korea

Ndaona Mboni za Yehova Zikuwonjezereka ku Korea

Yosimbidwa ndi Milton Hamilton

“Tikufuna kukudziwitsani kuti boma la Korea lakana kupereka ziphaso za amishonale nonse zokulolezani kukhala m’dzikolo ndipo lanena kuti musapitenso m’dzikomo. . . . chifukwa cha zimenezi, tikutumizani kaye ku Japan.”

INE ndi mkazi wanga tinalandira kalata imeneyi kuchokera ku Brooklyn, ku America, chakumapeto kwa chaka cha 1954. Kumayambiriro kwa chaka chimenechi tinamaliza maphunziro a kalasi ya nambala 23 ku Sukulu ya Gileadi, ku New York. Panthawi imene timalandira kalatayi n’kuti tikutumikira ku Indianapolis mu mzinda wa Indiana.

Ine ndi mkazi wanga Liz, tinali kalasi imodzi ku sekondale. Kenako tinakwatirana mu 1948. Liz ankakonda utumiki wa nthawi zonse, koma sankafuna kuchoka ku America kuti akatumikire ku dziko lina. Kenako iye anasintha maganizo amenewa.

Liz analola kupita nane ku msonkhano wa anthu ofuna kupita ku Sukulu ya Gileadi. Msonkhano umenewu unachitika panthawi ya msonkhano wa mayiko, womwe unachitikira ku Yankee Stadium, ku New York, m’chaka cha 1953. Pamapeto pa msonkhano wolimbikitsa umenewu tinalemba mafomu ofunsira Sukulu ya Gilead. Tinasangalala kumva kuti taitanidwa kuti tikayambe sukuluyi mwezi wa February mu 1954.

Titamaliza maphunzirowa anatiuza kuti tikatumikire ku Korea. Panthawiyi dzikoli linali litawonongedwa kwambiri chifukwa cha nkhondo ya zaka zitatu imene inatha mu 1953. Koma tinayamba kaye tapita ku Japan monga mmene anatilangizira m’kalata yochokera ku Brooklyn ija. Tinakafika ku Japan mu January chaka cha 1955 pamodzi ndi amishonale anzathu okwana 6 amenenso anatumizidwa ku Korea. Tinayenda ulendowu kwa masiku 20 pa sitima ya panyanja. M’bale Lloyd Barry, yemwe ankayang’anira nthambi ya ku Japan pa nthawi imeneyo, anakatichingamira ku doko, 6 koloko m’mawa. Kenako tinapita ku nyumba ya amishonale ku Yokohama. Ndipo tsiku lomwelo tinapita kokalalikira.

Ulendo wa ku Korea

Patapita nthawi tinapeza ziphaso zolowera m’dziko la Korea. Pa March 7, 1955, tinanyamuka pa bwalo la ndege la Haneda ku Tokyo, ndipo tinayenda maola atatu kukafika pa bwalo la ndege la Yoido, mu mzinda wa Seoul. Titatsika ndege tinalandiridwa ndi Mboni za ku Korea zoposa 200 ndipo tinasangalala kwambiri. Panthawi imeneyi ku Korea kunali Mboni zokwana 1,000 zokha. Ife tinkaganiza ngati mmene anthu ambiri a ku Ulaya amaganizira, kuti anthu onse a ku Asia amaoneka mofanana ndiponso amachita zinthu zofanana. Koma pasanapite nthawi yaitali tinazindikira kuti zimenezi si zoona. Anthu a ku Korea ali ndi chilankhulo ndiponso afabeti yawoyawo, kaphikidwe kawokawo ka zakudya, kavalidwe ndi maonekedwe awoawo. Anthu a ku Korea amasiyana ndi anthu a ku Asia pa zinthu zinanso zambiri monga kamangidwe ka nyumba.

Vuto lathu lalikulu linali kuphunzira chinenero cha ku Korea chifukwa kunalibe mabuku a chinenerochi. Tinazindikira kuti n’zosatheka kulankhula mawu a Chikoleya potsatira katchulidwe ka Chingelezi. Kuti munthu athe kulankhula bwino Chikoleya ayenera kugwiritsa ntchito afabeti ya chilankhulochi.

Komabe nthawi zina tinkalakwitsa. Mwachitsanzo, Liz anafunsa mwininyumba ngati anali ndi Baibulo, ndipo mwininyumbayo anamuyang’ana modabwa kenako anapita kukatenga kabokosi ka machesi. Apa vuto linali lakuti m’malo motchula mawu akuti sungkyung omwe amatanthauza “Baibulo,” iye anatchula mawu akuti sungnyang omwe amatanthauza machesi.

Patapita miyezi yochepa anatiuza kuti tikakhale ku Pusan, mzinda womwe unamangidwa pa doko kum’mwera kwa dziko la Korea. Ifeyo ndi alongo ena awiri, tinachita lendi nyumba ya zipinda zitatu. Zipindazi zinalibe mipopi komanso chimbuzi chamadzi. Chifukwa chakuti madzi ankavuta, tinkatunga mmamawa kwambiri. Kuti madziwa akhale abwino kumwa, tinkawaphitsa kapena kuwathira mankhwala opha tizilombo.

Panalinso mavuto ena amene tinkakumana nawo. Mphamvu ya magetsi inali yochepa kwambiri moti sitinkatha kusita kapena kugwiritsa ntchito matchini ochapira. Tinalibe khitchini ndipo tinkaphika pa sitovu ya palafini. Koma pasanapite nthawi tinazolowera ndipo aliyense amatha kuphika chakudya patsiku limene wapatsidwa. Patapita zaka zitatu, ine ndi Liz tinayamba kudwala matenda a chiwindi. Amishonale ambiri ankadwala matenda amenewa. Tinadwala miyezi yambiri, ndipo titachira tinayamba kudwala matenda enanso.

Tinawalimbikitsa Abale a ku Korea

Kwa zaka 55 zapitazi, dziko la Korea lakhala lili pa mavuto aakulu a zandale. Kuyenda makilomita 55 kuchokera ku Seoul, likulu la dziko la Korea, kulowera ku mpoto timapeza malire a dziko la South ndi North Korea kumene mayikowa anagwirizana kuti asamamenyeko nkhondo. Malo amenewa ndi malo otetezedwa kwambiri padziko lonse. M’bale Frederick Franz, yemwe anachokera ku Brooklyn, atabwera kudzationa mu 1971, ndinamuperekeza kukaona malo amenewa. Kwa zaka zambiri akuluakulu a bungwe la United Nations, akhala akukambirana ndi akuluakulu a maboma awiriwa pamalo amenewa.

Ifeyo sitimalowerera nawo ndale, ndipo sitinalowerere ngakhale pang’ono m’mikangano ya za ndale ku Korea. (Yoh. 17:14) Ndipo Mboni zoposa 13,000 zakhala zikutumizidwa ku ndende chifukwa chokana kulowa usilikali. Kuphatikiza zaka zimene anthu amenewa akhala kundende, zonse pamodzi zikukwana 26,000. (2 Akor. 10:3, 4) Achinyamata a Mboni za Yehova akakwanitsa zaka zinazake amatumizidwa kundende pachifukwa chimenechi, koma sabwerera m’mbuyo. Chifukwa chakuti timakana kumenya nkhondo komanso kulowa ndale, boma la Korea limati ifeyo ndi “zigawenga.”

Mu 1944, panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, inenso ndinakana kulowa usilikali ndipo ndinamangidwa kwa zaka ziwiri ndi theka ku ndende ya ku Lewisburg, mu mzinda Pennsylvania ku America. Choncho, ndimamvetsa mavuto amene abale achinyamata a ku Korea akukumana nawo. Abale ambiri analimbikitsidwa atadziwa kuti ena mwa amishonalefe tinakumanapo ndi mavuto otere.​—Yes. 2:4.

Tinakumana ndi Mavuto ku Korea

M’chaka cha 1977, nafenso tinakumana ndi mavuto chifukwa chosalowerera ndale. Akuluakulu a boma ankaganiza kuti ifeyo ndi amene tikuletsa achinyamata a ku Korea kulowa usilikali. Choncho boma linakhazikitsa lamulo loti m’mishonale aliyense amene anatuluka m’dzikoli pa chifukwa chilichonse, asabwererenso. Lamulo limeneli linakhala likugwira ntchito kuyambira mu 1977 mpaka mu 1987. Pazaka zonsezi sitinkapita kwathu kukaona anthu, chifukwa tikanangotuluka m’dzikoli sitikanaloledwa kubwereranso.

Nthawi zambiri tinkapita kwa akuluakulu a boma kukawafotokozera kuti sitimalowerera ndale chifukwa chakuti timatsatira Khristu. Kenako iwo anaona kuti ife sitingagonje, choncho patatha zaka 10 lamulo lija linachotsedwa. Pazaka zimenezi, amishonale ena anabwerera kwawo chifukwa cha matenda ndi zifukwa zina, koma enafe tinakhalabe m’dzikoli. Tikuona kuti tinachita bwino kusachoka m’dzikoli.

Cha m’ma 1980, anthu otsutsa ntchito yathu anayamba kunena kuti gulu lathu limaphunzitsa achinyamata kuti azikana kulowa usilikali. Zimenezi zinachititsa kuti boma liitane anthu otsogolera ntchito ya Mboni za Yehova ku Korea kuti likawafunse mafunso. Pa January 22, 1987, khoti linalamula kuti mlanduwo unalibe umboni. Zimenezi zinathandiza kuti anthu a ku Korea asamatikayikire.

Mulungu Akudalitsa Ntchito Yathu

Ntchito yathu yolalikira yakhala ikutsutsidwa kwambiri ku Korea chifukwa chakuti timakana kulowa usilikali. Ndipo zinkavuta kwambiri kupeza malo abwino ochitirako misonkhano ikuluikulu. Choncho, abale anayesetsa kumanga malo ochitira misonkhano ku Pusan. Malo amenewa anali oyamba kumangidwa ku Asia konse. Pa April 5, 1976, ineyo ndinakamba nkhani yopatulira malowa ndipo kunabwera anthu okwana 1,300.

Kuyambira mu 1950, asilikali ambiri a ku United States akhala akutumizidwa ku Korea. Asilikali ena amaphunzira choonadi ndipo akabwerera kwawo amakakhala Mboni zolimbikira. Nthawi zambiri amatilembera makalata ndipo timasangalala kuti tinawathandiza kudziwa Yehova.

Pa September 26, 2006, mkazi wanga wokondedwa anamwalira. Ndimamusowa kwambiri. Pa zaka 51 zimene anakhala ku Korea kuno, iye ankalolera kuchita utumiki uliwonse ndipo sankadandaula. Sananenepo chilichonse chosonyeza kuti akufuna kubwerera ku United States, ngakhale kuti poyamba sankafuna kuchokako kuti apite dziko lina.

Pakali pano, ndikutumikira pa Beteli ya ku Korea. Poyamba pa ofesi ya nthambi ya ku Korea panali anthu ochepa chabe, koma panopa pali anthu okwana 250. Ndine wosangalala kwambiri kutumikira mu Komiti ya Nthambi ya ku Korea, yomwe ili ndi abale 7.

Nthawi imene ndinkafika ku Korea, dzikoli linali losauka kwambiri koma panopa ndi limodzi la mayiko olemera kwambiri padziko lapansi. Pakali pano, ku Korea kuli Mboni zoposa 95,000, ndipo pafupifupi abale ndi alongo 40 pa 100 alionse amachita upainiya wokhazikika kapena wothandiza. Zinthu zimenezi zachititsa kuti nditumikire Mulungu mosangalala. Ndipo ndakhala ndi mwayi woona Mboni za Yehova zikuwonjezereka ku Korea.

[Chithunzi patsamba 24]

Titangofika kumene ku Korea limodzi ndi amishonale ena

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Tikutumikira ku Pusan

[Chithunzi patsamba 25]

Ndili ndi m’bale Franz mu 1971, kumalire a dziko la North ndi South Korea

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi Liz, patangotsala nthawi yochepa kuti amwalire

[Chithunzi patsamba 26]

Ofesi ya nthambi ya ku Korea, kumene ndikutumikira